Kodi Ndani Adzamvetsera Uthenga Wathu?
1 Kuposa ndi kale lonse m’mbiri ya anthu, anthu akulandira mauthenga ambirimbiri, amene ochuluka a iwo ali achabechabe ndipo ngakhale osokeretsa. Choncho, ambiri amathedwa nzeru, ndipo kumakhala kovuta kwa ife kuti tiwachititse kumvetsera uthenga wonena za Ufumu wa Mulungu. Iwo samadziŵa zotulukapo zabwino kwambiri zimene angakhale nazo ngati amvetsera Mawu a Mulungu.—Luka 11:28.
2 Tili achimwemwe kuti m’mbali zambiri za dziko, anthu zikwi makumi ambiri akumvetsera uthenga umenewo ndipo akulandira pempho lathu la maphunziro a Baibulo apanyumba. Komabe, m’magawo ena, ambiri samamvetsera. Ambiri a maulendo amene timapanga mu utumiki samakhala ndi zotulukapo zabwino, ndipo mwinamwake tingadzifunse ngati pali amene adzamvetsera uthenga wathu.
3 Tiyenera kupeŵa kulefulidwa. Paulo anafotokoza kuti: “Amene aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka. Ndipo iwo adzaitana bwanji pa Iye . . . amene sanamva za Iye? Ndipo adzamva bwanji wopanda wolalikira? . . . monganso kwalembedwa, Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira Uthenga Wabwino wa zinthu zabwino.” (Aroma 10:13-15) Ngati tifesa mbewu za Ufumu mwakhama, Mulungu adzazikulitsa mwa awo oona mtima.—1 Akor. 3:6.
4 Mfungulo Yake Ndiyo Kupanga Maulendo Obwereza Nthaŵi Zonse: M’magawo amene amaoneka kuti ndi anthu ochepa amene amamvetsera uthenga wathu, tifunikira kusumika maganizo athu pa kukulitsa chidwi chamtundu uliwonse chimene tipeza, kaya tigaŵira mabuku kapena ayi. Nkugamuliranji mwamsanga kuti palibe chimene chidzachitika? Pamene tifesa mbewu, sitimadziŵa pamene zidzalola bwino. (Mlal. 11:6) Ngati tili okonzekera pamene tibwererako kukagaŵana nawo kanthu kenakake ka m’Malemba, ngakhale ngati ndi mwachidule chabe, mwinamwake tingafike mtima wa munthuyo. Tingasiye trakiti kapena kupereka magazini atsopano. M’kupita kwa nthaŵi, tingakhoze kusonyeza kachitidwe ka phunziro la Baibulo. Tidzadabwa mokondwa kuona mmene Yehova amadalitsira zoyesayesa zathu.—Sal. 126:5, 6.
5 Trakiti linasiyidwa kwa mkazi wina amene anasonyeza chidwi chaching’ono. Sanapezedwenso panyumba mpaka patapita miyezi iŵiri, komano anali wotanganitsidwa kwambiri kwakuti sakanakambitsirana. Anamsiyiranso trakiti limodzimodzilo. Ngakhale kuti wofalitsayo analimbikira kupita kunyumba kwake, panapitanso miyezi ina itatu kuti aonane naye, koma anampeza kuti ngwodwala. Mlongoyo anafikanso mlungu wotsatira, ndipo anakambitsirana mwachidule ponena za trakitilo. Pamene mlongoyo anabwererako mlungu wotsatira, mkaziyo anasonyeza chidwi chenicheni pa uthenga wa Ufumu. Kusintha kwa mikhalidwe m’moyo wake kunamchititsa kuzindikira zosoŵa zake zauzimu. Phunziro la Baibulo linayambidwa, ndipo pambuyo pake anali kuphunzira mofunitsitsa mlungu uliwonse.
6 Monga mmene zimakhalira ndi chilichonse chimene timafuna kuchiona chikukula, kaya ndi maluŵa, ndiwo zamasamba, kapena chidwi pa uthenga wa Ufumu, kulimirira nkofunikira. Zimenezo zimatenga nthaŵi, kulimbikira, mzimu wosamala, ndi kutsimikiza mtima kusaleka. Chaka chatha, anthu oposa 333,300 mwa amene mbewu za Ufumu zinazika mizu anabatizidwa! Ngati tipitirizabe kulalikira, tidzapezadi ena ambiri amene adzamvetsera uthenga wathu.—Yerekezerani ndi Agalatiya 6:9.