Mkupiti Wachipambano wa Uthenga wa Ufumu
“NCHIFUKWA Ninji Moyo Uli ndi Mavuto Ochuluka Motere?—Kodi Paradaiso Wopanda Mavuto Ali Wotheka?” Umenewu unali mutu wa Uthenga wa Ufumu Na. 34, trakiti la masamba anayi limene linagaŵiridwa kwa anthu padziko lonse m’zinenero 139 mu April ndi May wa chaka chatha. Mboni za ku Jamaica zinatcha mkupiti wautumiki umenewu “chimodzi cha zinthu zapadera za chakachi.” Mboni za ku Belgium zinautcha kuti “magwero aakulu a chimwemwe kwa abale.” Ku Czech Republic imeneyi inali nthaŵi yoyamba kuti Mboni za Yehova zikhale ndi mwaŵi wa kugaŵira Uthenga wa Ufumu. Nthambi yake ikusimba kuti: “Mkupitiwo unadzetsa mzimu wa changu ndi kutenthedwa maganizo.” Ndemanga zofanana nazo zinamveka kuchokera kumaiko ena ambiri.
Uthenga wa Ufumu Na. 34 unali ndi uthenga wapadera kwa aja akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zochitidwa m’dzina la chipembedzo. (Ezekieli 9:4) Unali ndi chitonthonzo kwa aja amene amavutika ndi moyo chifukwa cha “nthaŵi zoŵaŵitsa” zimene sangazilamulire. (2 Timoteo 3:1) Posonyeza Baibulo, trakitilo linanena kuti mavuto a moyo adzathetsedwa posachedwapa. Paradaiso wopanda mavuto adzafikadi. (Luka 23:43) Ambiri amene anaŵerenga Uthenga wa Ufumu anakopedwa ndi uthenga wake. Mwamuna wina ku Togo anauza Mboni ina kuti: “Zimene mwanena nzosatsutsika.”
Kunena zoona, kugaŵiridwa kwa Uthenga wa Ufumu umenewu kunachititsa ambiri kukhala ndi chidwi chapadera. Mwini nyumba wina ku Denmark anayankha Mboni imene inali kumgaŵira trakiti kuti: “Ndangobwerera kumene kuchokera ku United States. Ndisanachoke, winawake anandipatsa trakiti lanuli. Tsopano ndangofika kumene kuno, ndipo nthaŵi yomweyo ndapatsidwa trakitili m’Chidanishi!”
Chichirikizo Chotentha pa Mkupiti
Mboni za Yehova padziko lonse zinagwirizana motenthedwa pantchito ya kugaŵira trakitilo. Austria, El Salvador, Haiti, Hungary, Italy, New Caledonia, anali ena a maiko ambiri amene anapereka lipoti la chiŵerengero chapamwamba koposa cha ofalitsa m’miyezi pamene Uthenga wa Ufumu unali kugaŵiridwa.
Ku Zambia woyang’anira dera wina waphunzitsa mwana wake wamkazi Deborah wazaka zitatu, kugaŵira mabuku kunyumba ndi nyumba. Mkati mwa mkupiti wa Uthenga wa Ufumu Na. 34, Deborah anagaŵira makope 45 a trakitilo. Amake anayamba kuchititsa maphunziro ndi ena amene analandira Uthenga wa Ufumu kwa Deborah.
Ku South Africa msungwana wina anagaŵira trakiti kwa mnzake wakusukulu wotchedwa Cashia. Cashia anaŵerenga trakitilo nati: “Zimenezi nzosangalatsadi kwambiri—kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso wapadziko lapansi! Kodi nchifukwa ninji sindinauzidwe zimenezi poyamba?” Phunziro la Baibulo linayambidwa. Sabata lisanathe Cashia analandira trakiti lina. Lachiŵirilo linachokera kwa bwenzi lake la Roma Katolika lolemberana nalo makalata, limene limakhala ku Cyprus. Bwenzilo linafotokoza kwa Cashia chifukwa chake ziphunzitso za Tchalitchi cha Roma Katolika zili zonama ndi kumuuza kuti akufuna kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova. Zoonadi, zimenezo zinalimbitsa kwambiri chitsimikizo cha Cashia cha kupitiriza phunziro lake.
Mnyamata wina wazaka khumi ku Switzerland anali kugaŵira trakitilo ndi amake. Anagaŵira kope limodzi kwa msungwana wina ndi kumlimbikitsa kuliŵerenga mosamala. Msungwanayo anafunsa mnyamatayo ngati anakhulupiriradi zimene chithunzithunzi cha pachikuto chinasonyeza—moyo wopanda mapeto padziko lapansi. Yankho la mnyamatayo? “O, inde, ndikukhulupiriradi kwambiri.” Ndiyeno msungwanayo anavumbula kuti anali kufunafuna chikhulupiriro choona chifukwa chakuti panali kuwombana kwa zinthu zochuluka m’chipembedzo chake. Paulendo wobwereza, phunziro la Baibulo linayambidwa.
Kuchitapo Kanthu Panthaŵi Yomweyo
Nthaŵi zina Uthenga wa Ufumu unachititsa aja amene anauŵerenga kuchitapo kanthu panthaŵi yomweyo. Ataŵerenga trakiti, msungwana wina wazaka 11 ku Belgium anaulula kwa mmodzi wa Mboni za Yehova kuti anakhala akumaba m’sitolo ina. Amake a msungwanayo anafuna kubisa nkhaniyo, koma chikumbumtima cha msungwanayo chinasonkhezereka ndi zimene anaŵerenga, ndipo anaumirira zopita kukaonana ndi manijala wa sitoloyo. Potsirizira pake amake anavomereza mwana wawoyo kupita kusitoloyo ndi Mboni. Manijala wake anadabwa pa kudziulula kwake. Pamene anamva kuti Uthenga wa Ufumu ndiwo unamsonkhezera kuchita motero, iye mwiniyo anatenga kope kuti aone zimene zinalimo zimene zinali ndi mphamvu kwambirizo. Msungwanayo tsopano akuchita phunziro la Baibulo lopita patsogolo.
Mboni ina ku Cameroon inasiya kope la Uthenga wa Ufumu kwa mwamuna wina ndipo ikusimba kuti: “Pamene tinabwererako, tinapeza kuti anali atalichonga ndipo anali ndi mafunso ambiri. Atayankhidwa mokhutiritsa, anati: ‘Nzoonadi kuti chipembedzo chathandizira kubweretsa chisoni pa anthu. Trakiti lanu landithandiza kumvetsetsa zochuluka, koma ndikufuna kudziŵa zambiri.’” Tsopano iye ali ndi phunziro lokhazikika la Baibulo.
Mboni ina imene inali mu ntchito ya kunyumba ndi nyumba ku Uruguay inagaŵira trakiti kwa mwamuna wina. Mboniyo inapitiriza ntchito yake ya kulalikira kunyumba ndi nyumba ndi kufola kuseri kwa mdadada kufikira atatulukiranso kukhomo lakumbuyo la nyumba ya mwamunayo. Anadabwa pamene anapeza mwamunayo akumuyembekezera, trakitilo lili m’manja. Anali ataliŵerenga kale ndipo anali kufuna chidziŵitso chinanso. Phunziro linayambidwa nthaŵi yomweyo.
Anthu Athandizira Kugaŵirako
Mboni ina yachichepere ku Japan inafikira mwamuna wina wazaka za ma 50 ndi kumsonyeza trakiti. Mwamunayo anafunsa kuti: “Kodi ungachitenji ndi pepalali ngati utakumana ndi anthu osaona?” Mboniyo inanena kuti siidziŵa. Mwamunayo anamuuza kuyembekezera pang’ono napita m’nyumba mwake. Anabwera ndi kope la Uthenga wa Ufumu nati: “Ndalandira kale pepalali. Ndinaganiza kuti muli chidziŵitso chokondweretsa ndi chofunika, chotero ndinalitembenuzira mu Braille. Chonde kagaŵire kwa anthu akhungu.” Mwamunayo anali atathera maola ambiri akumatembenuza Uthenga wa Ufumu m’kalembedwe ka Braille kuti akhungu asaphonye zimene unali nazo.
Ku Slovakia mwamuna wina anakonda kwambiri trakitilo kwakuti anapangitsa makope 20, ndipo anagaŵira makope a maonekedwe akuda ndi oyera iye mwiniyo. Wofalitsa wina ku Switzerland anasiyira banja lina Uthenga wa Ufumu ndi kupitiriza kugwira ntchitoyo zipinda zapamwamba za nyumba imene banjalo linali kukhala. Atatsika, anakumana ndi mnyamata wina wa m’banjamo, amene anapempha makope ena 19 a trakitilo. Kusukulu kwa mnyamatayo, ophunzira anali atauzidwa kulemba za mavuto ndi kufufuza zothetsera zake. Anafuna makope a Uthenga wa Ufumu okapatsa a m’kalasi anzake onse.
Palibe Amene Anaphonyedwa
Awo amene anakhala ndi phande mu mkupitiwo anayesayesa zolimba kutsimikizira kuti palibe amene anaphonyedwa. Ku New Caledonia Mboni ziŵiri zinali kupita kugawo lokhalako mtundu wina wakutali kuti zikagaŵire Uthenga wa Ufumu. Ali m’njira, anaona kanjira kamene kanachita ngati kosagwiritsiridwa ntchito, komabe iwo anafuna kuti akaone ngati pali munthu amene amakhala kumapeto kwake. Atatuluka m’galimoto, anatsatira kanjirako, akumawoloka mifuleni mpaka anapeza nyumba ina. Okwatirana amene anali asanamvepo za Mboni za Yehova anali kukhala pamenepo, ndipo analandira kope la Uthenga wa Ufumu. Pambuyo pake ofalitsawo anabwererako ndipo anadabwa kupeza kuti okwatiranawo anakonza msewuwo ndi milatho ingapo kuti Mbonizo zifike ndi galimoto lawo panyumbapo. Phunziro la Baibulo lokhazikika linayambidwa.
Ku Poland Mboni ina inadutsa pamalo ena amene anali kumangapo kuti ikagaŵire kope la Uthenga wa Ufumu kwa mwini nyumba. Antchito anayang’ana pamene anali kudutsanso pamalo omangapowo. Potsirizira pake, wantchito wina anamuitana, akumampempha kuti asawaiŵale. Pamene anafika kwa iwo, analekeza namvetsera mosamalitsa ulaliki wa trakitilo. Analandira makope a Uthenga wa Ufumu ndiponso magazini ndipo pambuyo pake, paulendo wobwereza, analandira mabuku.
Mamiliyoni mazana ambiri a Uthenga wa Ufumu Na. 34 unagaŵiridwa m’zinenero zambiri. Uthenga wake wayamba kale kusonkhezera anthu mwamphamvu. Ambiri azindikira kuti paradaiso wopanda mavuto ngwotheka. Tikupempherera kuti anthu oona mtima apitirizebe kulabadira ndipo potsirizira pake kukhala pakati pa “ofatsa” amene “adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:11.
[Bokosi patsamba 31]
Pitirizani Kugaŵira Magazini!
April ndi May 1995 anali ndi mkupiti wachipambano wa kugaŵira Uthenga wa Ufumu Na. 34. M’miyezi iŵiri imeneyo, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! anagaŵiridwanso kwambiri. Mwachitsanzo, mbale wina ku Czech Republic akusimba kuti anagaŵira makope a Uthenga wa Ufumu 250 ndi magazini 750. Ku Guadeloupe, Loŵeruka, April 15, linasankhidwa kukhala tsiku lapadera la magazini. Pafupifupi wofalitsa aliyense m’dzikolo anakhala ndi phande mu utumiki tsikulo! Slovakia anali ndi chiŵerengero chapamwamba chatsopano pa kugaŵira magazini mu April. Malipoti ofanana nawo anachokera ku maiko ena ambiri.
Chotero bwanji osapanga April ndi May 1996 kukhala miyezi yapadera ya kugaŵira magazini? Mipingo ingalinganize masiku apadera a magazini. Munthu aliyense payekha angachite nawo upainiya wothandiza. Mwa njira zimenezi ndi zina, kugaŵira magazini kungalimbikitsidwe, ndipo uthenga wofunika wolengezedwa mu Uthenga wa Ufumu Na. 34 udzapitiriza kuwanditsidwa. Ndiyeno, monga momwe zinachitikira chaka chatha, Yehova adzadalitsadi mzimu wachangu umene tikusonyeza.—2 Timoteo 4:22.