Zopereka ku Ntchito ya Sosaite Yapadziko Lonse Zichirikiza Kufutukuka
MONGA momwe kunanenedweratu pa Yesaya 54:2, 3, kulambira koyera kwa Yehova kukupitirizabe kufutukuka padziko lonse lapansi. Kumeneku kukuphatikizapo maiko osiyanasiyana pa kontinenti ya Afirika ndi zisumbu zapafupi. Mkati mwa zaka khumi zapitazi, ziletso pa ntchito ya Ufumu zachotsedwa m’malo monga Angola, Cameroon, Equatorial Guinea, Ethiopia, Madagascar, Malaŵi, Mozambique, ndi Togo. M’maiko ameneŵa ndi m’maiko ena mmene nthaŵi ya kukolola yafika, amishonale a ku Gileadi, omaliza maphunziro a Sukulu Yophunzitsa Utumiki, a banja la Beteli, ndi ena apita kukagwirirako ntchito.—Mat. 9:37, 38.
Mwachionekere, kuwonjezereka kwa alambiri oona m’gulu la Yehova kukufuna kumangidwa kwa mazana a Nyumba za Ufumu zatsopano. Kwakhalanso koyenera kupanga makonzedwe a Nyumba za Misonkhano ndi kumanga nthambi zatsopano kapena kuzifutukula. Kupereka ndalama kuntchito zimenezi limodzi ndi kupititsabe patsogolo ntchito za Ufumu osati mu Afirika mokha komanso m’mbali zina za dziko kwagwiritsira ntchito kwambiri zopereka za ntchito ya padziko lonse ya Sosaite.
Zithunzithunzi zojambulidwa ndi zapamanja zimene zili pamasamba aŵiri a mphatika ino zikukupatsani chithunzi cha zimene Sosaite yakhala ikuyesetsa kuchita m’munda wa mu Afirika. Zimene zasonyezedwa ndizo zimango zina zimene tsopano zili mkati ndi ntchito zimene zidzayamba posachedwapa.
Mwa kupenda tchati cha utumiki wa m’munda mu 1996 Yearbook, mungakhale ndi chithunzi chabwino cha zimene ofalitsa akuchita mu utumiki m’maiko ameneŵa. M’maiko ambiri mwakhala kuwonjezereka kwakukulu, ndipo umboni wakuti padzakhala kuwonjezerekabe ukuonekera m’ziŵerengero zapadera za opezeka pa Chikumbutso. Pamene tikumbukira zimene zikuchitidwa monga mbali ya ntchito ya padziko lonse ya kulalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira m’makontinenti ena, zimatikumbutsa kuti tilidi ndi mwaŵi waukulu wa kuchirikiza mwakuthupi chifuno cha kulambira koona.—Luka 16:9; 1 Tim. 6:18.
[Chithunzi patsamba 3]
Nyumba ya Ufumu ku KwaZulu-Natal, South Africa, yomangidwa m’masiku 9
[Chithunzi patsamba 3]
Nyumba ya Ufumu yomangidwa pamtengo wotsika ku Nigeria
[Chithunzi patsamba 3]
Nyumba ya Misonkhano ku Mozambique yokhala ndi mipando 1,500, yomwe idzamalizidwa kumapeto kwa 1996
[Chithunzi patsamba 3]
Nthambi ya ku Mozambique, yomwe idzayamba kugwira ntchito kumapeto kwa 1996
[Chithunzi patsamba 3]
Nthambi ya ku Sierra Leone, yomwe yalinganizidwa kumalizidwa chilimwe chino
[Chithunzi patsamba 4]
Nyumba ya Misonkhano yomalizidwa yopanda makoma ku Mauritius, limodzi ndi nthambi, yomwe idzamalizidwa m’ngululu ya 1997
[Chithunzi patsamba 4]
Nthambi ya Zimbabwe imene ikumangidwa
[Chithunzi patsamba 4]
Nyumba ya Misonkhano yopanda makoma ndi nthambi yatsopano imene ikumangidwa ku Senegal
[Chithunzi patsamba 4]
Nthambi ya ku Kenya, m’likulu, Nairobi
[Chithunzi patsamba 4]
Nthambi ya Madagascar, imene idzamalizidwa posachedwa
[Chithunzi patsamba 4]
Nthambi ya Malaŵi yomwe idzayamba kumangidwa