Ntchito Yomanga Nyumba za Ufumu Ikuyenda Bwino
1 Ku United States, pa Msonkhano Wachigawo wachaka cha 1983 wakuti, “Mgwirizano wa Ufumu,” analengeza kuti akhazikitsa thumba la ndalama lapadera loti lithandize pomanga ndi kukonzetsera Nyumba za Ufumu ku United States ndi ku Canada. Panthaŵiyo sitinkadziŵa madalitso amene tingapeze pa chiyambi chochepa chimenecho. Tinayamba kuona bwinobwino zimene Salmo 92:4 limanena momveka bwino kuti: “Popeza Inu, Yehova, munandikondweretsa ndi kuchita kwanu. Ndidzafuula mokondwera pa ntchito ya manja anu.”
2 Tsopano tikusangalala kwambiri ndi zimene zikuchitika. Masiku ano ntchito yomanga Nyumba za Ufumu mofulumira kwambiri ili mkati padziko lonse. Tonse tili ndi mwayi wogwira nawo ntchitoyi m’njira ina yake. Timachita zimenezi mwa kupereka ndalama zambiri kapena zochepa zoti zithandizire ntchito yomangira malo ambiri olambiriramo padziko lonse. Abale ambirinso amathandiza mwa kugwiritsa ntchito zida zawo komanso nthaŵi ndiponso luso lawo pantchito zimenezi. Ntchitoyi ikuyenda bwino chifukwa chakuti Yehova akuitsogolera, kuichirikiza ndiponso chifukwa chogwira ntchito mogwirizana.—Sal. 127:1.
3 Nthambi zambiri zatsatira dongosolo limene poyambirira linali la mipingo ya ku United States. Pa Nyumba za Ufumu m’mayiko ambiri, pamakhala bokosi limene ofalitsa amaikamo zopereka za Nyumba ya Ufumu. Ku United States, Utumiki Wathu wa Ufumu wa March 1997 unalengeza za kusintha kwa pulogalamu imeneyi. Anati: “Kuyambira mu 1983 pamene ku United States anakhazikitsa Thumba la Sosaite la Ndalama za Nyumba za Ufumu, abale akhala akupereka mooloŵa manja, ndipo zimenezi zathandiza kuti azikongoza ndalama zomangira Nyumba za Ufumu. Mipingo pafupifupi 2,700 m’dziko limeneli yapindula kale ndi thumbali. Mipingo yambiri sikanatha kumanga Nyumba za Ufumu zatsopano kapena kukonzetsa nyumba zakale pakanapanda thumba limeneli. Pakalipano pakufunika kwambiri kugwiritsa ntchito zina mwa ndalama zimenezi kukongoza mipingo ya m’mayiko osauka. Sosaite ndiponso mipingo imene imapindula ndi zopereka zanu imayamikira kwambiri kupitiriza kwanu kuthandiza dongosolo limeneli.”
4 Zimene analengezazi zinalimbikitsa kuthandiza nawo ntchito yomanga Nyumba za Ufumu mofulumira kwambiri. Thumba la Ndalama za Nyumba za Ufumu limenelo linali kudzathandizanso abale athu m’mayiko ena komanso kupitiriza kukongoza ndalama zomangira Nyumba za Ufumu mu United States. Nkhani ina ya mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 1997 wa ku United States inati: “Padziko lonse pakufunikabe Nyumba za Ufumu. M’chaka cha utumiki chathachi, anakhazikitsa mipingo yatsopano 3,288. Yambiri mwa mipingo imeneyi ili mu Africa, Asia, Central America ndi South America, ndiponso kum’mawa kwa Ulaya.”
5 Kodi pachitika zotani kuyambira nthaŵi imeneyo? Yearbook ya 2001 inati: “Chifukwa cha dongosolo limeneli, m’mayiko okwana 30, panopo amaliza kumanga Nyumba za Ufumu 453, ndipo zina 727 akuzimanga. Alimbikitsa kwambiri kamangidwe katsopano ka Nyumba za Ufumu m’dziko lililonse mogwiritsa ntchito zinthu zomangira za kumeneko. Ku Kenya, amamangira miyala; ku Togo, Malaŵi ndi m’mayiko ena, n’kofala kumangira njerwa; ku Cameroon n’kofala kumangira konkire ndipo akatha amapaka pulasitala. Mwanjira imeneyi, abale amaphunzira msanga luso lofunika kuti agwire ntchitoyo m’dziko lawolo.”
6 Umboni wakuti Yehova akudalitsa ntchito imeneyi ukuoneka ku kontinenti yathu ino ya Africa. Mukamaona zina mwa zithunzi za Nyumba za Ufumu zimene zamangidwa, lingalirani momwe zimenezi zakhudzira ntchito ya Mboni za Yehova. Izi zathandiza m’mbali zitatu—zagwirizanitsa abale padziko lonse, zalimbikitsa anthu am’deralo, ndiponso anthu pa misonkhano ya mpingo amachuluka. Ngakhale kuti mphatika ino ikukamba za Nyumba za Ufumu za ku Africa kuno, Utumiki Wathu wa Ufumu ukubwerawo udzakamba za mmene ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ikuyenderanso bwino m’zigawo zina padziko lapansi.
[Zithunzi patsamba 3]
CENTRAL AFRICAN REPUBLIC
Bimbo, Bangui
Begoua, Bangui
[Zithunzi patsamba 4]
Ukonga, Tanzania
[Chithunzi patsamba 4]
Accra, Ghana
[Chithunzi patsamba 4]
Salala, Liberia
[Chithunzi patsamba 4]
Karoi, Zimbabwe
[Zithunzi patsamba 4, 5]
Allada, Benin—Nyumba ya Ufumu yakale
Allada, Benin—Nyumba ya Ufumu yatsopano
[Chithunzi patsamba 5]
Kpeme, Togo
[Chithunzi patsamba 5]
Sokodé, Togo
[Zithunzi pamasamba 4, 5]
Fidjrosse, Benin
[Chithunzi patsamba 6]
Lyenga, Zambia—Nyumba ya Ufumu yakale
[Chithunzi patsamba 6]
Lyenga, Zambia—Nyumba ya Ufumu yatsopano
[Chithunzi patsamba 6]
Kinshasa, Congo
[Chithunzi patsamba 6]
Musambira, Rwanda