Mutu 116
Kukonzekeretsa Atumwi Kaamba ka Kuchoka Kwake
CHAKUDYA cha chikumbutso chatha, komabe Yesu ndi atumwi ake adakali m’chipinda chapamwamba. Ngakhale kuti Yesu adzakhala atapita mwamsanga, iye adakali ndi zinthu zambiri za kuzinena. “Mtima wanu usavutike,” iye akuwatonthoza motero. “Mukhulupilira Mulungu.” Koma iye akuwonjezera kuti: “Khulupilirani inenso.”
“M’nyumba ya Atate wanga alimo malo okhalamo ambiri,” Yesu akupitiriza. “Pakuti ndipita kukukonzerani inu malo . . . kuti kumene kuli ineko, mukakhale inunso. Ndipo kumene ndinkako ine, mudziŵa njira yake.” Atumwiwo sakuzindikira kuti Yesu akunena za kupita kumwamba, chotero Tomasi akufunsa kuti: “Ambuye, sitidziŵa kumene munkako; tidziŵa njira bwanji?”
“Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo,” Yesu akuyankha. Inde, kuli kokha mwa kumvomereza ndi kutsanzira njira yake ya moyo kuti munthu angakhoze kuloŵa nyumba yakumwamba ya Atate chifukwa chakuti, monga momwe Yesu akunenera: “Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa ine.”
“Ambuye, tiwonetsereni ife Atate,” Filipo akupempha motero, “ndipo chitikwanira.” Mwachiwonekere Filipo akufuna kuti Yesu apereke chisonyezero chowoneka cha Mulungu, chonga ngati chimene chinaperekedwa m’nthaŵi zakale m’masomphenya kwa Mose, Eliya, ndi Yesaya. Koma, ndithudi, atumwiwo ali ndi kanthu kena kabwino kwambiri kuposa masomphenya amtundu umenewo, monga mmene Yesu akunenera kuti: “Kodi ndiri ndi inu nthaŵi yaikulu yotere, ndipo sunandizindikira Filipo? Iye amene wandiwona ine wawona Atate.”
Yesu amasonyeza mwanjira yangwiro umunthu wa Atate wake kotero kuti kukhala naye ndi kumvetsera kwa iye kuli, m’chenicheni, kofanana ndi kuwonadi Atate. Komabe, Atate ngwamkulu kwa Mwana, monga mmene Yesu akuvomerezera kuti: “Mawu amene ndinena ine kwa inu sindilankhula kwa ine ndekha.” Moyenerera Yesu akupereka thamo lonse kaamba ka ziphunzitso zake kwa Atate wake wakumwamba.
Nkolimbikitsa chotani nanga mmene kuyenera kukhalira kwa atumwiwo kumva Yesu tsopano akuwauza kuti: “Wokhulupilira ine, ntchito zimene ndichita ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi!” Yesu sakutanthauza kuti otsatira ake adzachita zozizwitsa zazikulu zamphamvu koposa zimene iye anachita. Ayi, koma iye akutanthauza kuti iwo adzachita uminisitalawo kwanthaŵi yotalikirapo, m’dera lokulirapo, ndi kwa anthu ochuluka kwambiri.
Yesu sadzasiya ophunzira ake atachoka. “Chirichonse mukafunse m’dzina langa,” iye akulonjeza motero, “ndidzachichita.” Ndiponso, iye akuti: “Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani inu nkhoswe ina, kuti akhale ndi inu kunthaŵi yonse, ndiye mzimu wa chowonadi.” Pambuyo pake, atakwera kumwamba, Yesu akutsanulira mzimu wake woyera pa ophunzira, ndiyo nkhoswe inayo.
Kuchoka kwa Yesu kuli pafupi, monga momwe iye akunenera kuti: “Katsala kanthaŵi, ndipo dziko lapansi silindiwonanso ine.” Yesu adzakhala cholengedwa chauzimu chimene munthu sangathe kuwona. Koma kachiŵirinso Yesu akulonjeza atumwi ake okhulupirikawo kuti: “Inu mundiwona, popeza ine ndiri ndi moyo inunso mudzakhala ndi moyo.” Inde, sikokha kuti Yesu adzawonekera kwa iwo mumpangidwe waumunthu pambuyo pa chiukiriro chake koma m’nthaŵi yokwanira iye adzawaukitsira kumoyo kukakhaka naye kumwamba monga zolengedwa zauzimu.
Yesu tsopano akunena lamulo losavuta iri: “Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda ine; koma wondikonda ine adzakondedwa ndi Atate wanga, ndipo ine ndidzamkonda, ndipo ndidzadziwonetsa ndekha kwa iye.”
Pamenepo mtumwi Yudase, wotchedwanso Tadeyo, akudodometsa kuti: “Ambuye, chachitika chiyani kuti muziti mudziwonetsa nokha kwa ife, koma sikwadziko lapansi?”
“Ngati wina akonda ine,” Yesu akuyankha, “adzasunga mawu anga; ndipo Atate wanga adzamkonda, . . . Wosandikonda ine sasunga mawu anga.” Mosafanana ndi otsatira ake omvera, dziko likunyalanyaza ziphunzitso za Kristu. Chotero sakudzivumbula kwa iwo.
Mkati mwa uminisitala wake wa padziko lapansi, Yesu waphunzitsa atumwi ake zinthu zambiri. Kodi iwo adzakumbukira motani zonsezo, makamaka popeza kuti, ngakhale kufikira pamphindi imeneyi, iwo akulephera kuzindikira zochuluka? Mwachimwemwe, Yesu akulonjeza kuti: “Nkhosweyo, mzimu woyera, amene Atate adzamtuma m’dzina langa, iyeyo adzaphunzitsa inu zonse, nadzakumbutsa inu zinthu zonse zimene ndinanena kwa inu.”
Kachiŵirinso powatonthoza, Yesu akuti: “Mtendere ndikusiyirani inu, mtendere wanga ndikupatsani; . . . Mtima wanu usavutike, kapena usachite mantha.” Ndithudi, Yesu akuchoka, koma iye akufotokoza kuti: “Mukadandikonda ine, mukadakondwera kuti ndipita kwa Atate; pakuti Atate ali wamkulu ndi ine.”
Nthaŵi yotsala ya Yesu ya kukhala nawo njayifupi. “Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu,” iye akutero, “pakuti mkulu wadziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa ine.” Satana Mdyerekezi, amene anali wokhoza kuloŵa mwa Yudase ndi kumgonjetsa, ndiye wolamulira wa dziko. Koma mwa Yesu mulibe kufooka kwa uchimo kumene Satana angakugwiritsire ntchito kumpatutsa pakutumikira Mulungu.
Kusangalala ndi Unansi Wathithithi
Pambuyo pa chakudya cha chikumbutso, Yesu wakhala akulimbikitsa atumwi ake mwa kukambitsirana nawo mawu ndi mtima wonse. Kungakhale kwakuti pakati pa usiku papita. Chotero Yesu akufulumiza kuti: “Nyamukani, tizimuka kuchokera kuno.” Komabe, asanachoke Yesu, mosonkhezeredwa ndi chikondi chake kwa iwo, akupitiriza kulankhula, akumapereka fanizo losonkhezera maganizo.
“Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate wanga ndiye wammunda,” iye akuyamba motero. Mlimi Wamkuluyo, Yehova Mulungu, anabzala mpesa wophiphiritsira umenewu pamene iye anadzoza Yesu ndi mzimu woyera pa ubatizo wake m’mphakasa ya 29 C.E. Koma Yesu akupitiriza kusonyeza kuti mpesawo umaphiphiritsira zoposa iye yekha, akumanena kuti: “Nthambi iriyonse ya mwa ine yosabala chipatso, ayichotsa; ndi iriyonse yakubala chipatso, aisadza, kuti ikabale chipatso chochuluka. . . . Monga nthambi siingathe kubala chipatso pa yokha, ngati siikhala mwampesa; motere mulibe inunso ngati simukhala mwa ine. Ine ndine mpesa, inu ndinu nthambi zake.”
Pa Pentekoste, masiku 51 pambuyo pake, atumwiwo ndi ena akukhala nthambi za mpesa pamene mzimu woyera utsanuliridwa pa iwo. Potsirizira pake, anthu okwanira 144,000 akukhala nthambi za mpesa wophiphiritsira. Limodzi ndi tsinde la mpesawo, Yesu Kristu, ameneŵa amapanga mpesa wophiphiritsira umene umatulutsa zipatso za Ufumu wa Mulungu.
Yesu akufotokoza mfungulo ya kubala chipatso kuti: “Wakukhala mwa ine, ndi ine mwa iye, ameneyo abala chipatso chambiri; pakuti kopanda ine simungathe kuchita kanthu.” Komabe, ngati munthu alephera kubala chipatso, Yesu akuti: “Watayika kunja monga nthambi, nafota; ndipo azisonkhanitsa nazitaya kumoto, nazitentha.” Kumbali ina, Yesu akulonjeza kuti: “Ngati mukhala mwa ine, ndi mawu anga akhala mwa inu, pemphani chimene chirichonse muchifuna ndipo chidzachitika kwa inu.”
Ndiponso, Yesu akuti kwa atumwi ake: “Mwa ichi alemekezedwa Atate wanga, kuti mubale chipatso chambiri; ndipo mudzakhala akuphunzira anga.” Chipatso chimene Mulungu amafuna m’nthambizo ndicho kusonyeza mikhalidwe yonga ya Kristu, makamaka chikondi. Ndiponso, popeza kuti Kristu anali wolengeza wa Ufumu wa Mulungu, chipatso chofunidwacho chimaphatikizanso ntchito yawo ya kupanga ophunzira monga mmene iye anachitira.
“Khalani m’chikondi changa,” Yesu akufulumiza motero tsopano. Komabe, kodi ndimotani mmene atumwi ake angachitire motero? “Ngati musunga malamulo anga,” iye akutero, “mudzakhala m’chikondi changa.” Popitiriza, Yesu akufotokoza kuti: “Lamulo langa ndi ili, kuti mukondane wina ndi mnzake monga ndakonda inu. Palibe munthu ali nacho chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.”
M’maola oŵerengeka, Yesu adzasonyeza chikondi choposa chimenechi mwa kupereka moyo wake mmalo mwa atumwi ake, ndiponso mwa ena onse amene adzaika chikhulupiliro chawo mwa iye. Chitsanzo chake chiyenera kusonkhezera otsatira ake kukhala ndi chikondi chodzipereka nsembe kaamba ka wina ndi mnzake chofananacho. Chikondi chimenechi chidzaŵazindikiritsa, monga momwe Yesu ananenera poyambirirapo kuti: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”
Podziŵitsa mabwenzi ake, Yesu akuti: “Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu. Sinditchanso inu akapolo; chifukwa kapolo sadziŵa chimene mbuye wake achita. Koma ndatcha inu abwenzi; chifukwa zonse zimene ndazimva kwa Atate wanga ndakudziŵitsani.”
Ndiunansi wamtengo wapatali chotani nanga wa kukhala nawo—kukhala mabwenzi apamtima a Yesu! Koma kuti apitirize kusangalala ndi unansi umenewu, otsatira ake ayenera “kubala chipatso.” Ngati atero, Yesu akuti, “chirichonse mukapempha Atate m’dzina langa iye [adzakupatsani].” Ndithudi imeneyo ndiyo mphotho yaikulu ya kubala chipatso cha Ufumu! Atatha kufulumizanso atumwi ake ‘kukondana wina ndi mnzake,’ Yesu akufotokoza kuti dziko lidzawada. Komabe, iye akuwatonthoza kuti: “Ngati dziko lapansi lida inu, mudziŵa kuti lidada ine lisanayambe kuda inu.” Yesu kenako akuvumbula chifukwa chake dziko limada otsatira ake, akumati: “Koma popeza simuli a dziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu.”
Pofotokozanso chifukwa chimene dziko likawadera, Yesu akupitiriza kuti: “Izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziŵa [Yehova Mulungu] wondituma ine.” Ntchito zozizwitsa za Yesu, m’chenicheni, zimaimba mlandu awo amene amamuda, monga mmene iye akunenera kuti: ‘Ngati sindikanachita ntchito pakati pawo zimene palibe aliyense anazichita, sakanakhala ndi tchimo; koma tsopano ponse paŵiri iwo awona ndi kuda ine ndi Atate wanga.’ Motero, monga mmene Yesu akunenera, lembalo likukwaniritsidwa: “Anandida ine kopanda chifukwa.”
Monga mmene anachitira poyambirirapo, kachiŵirinso Yesu akuwatonthoza mwa kuwalonjeza kuwatumizira wothandiza, mzimu woyera, umene uli mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. “Iyeyu adzandichitira ine umboni. Ndipo inunso, muchita umboni.”
Chilangizo Chowonjezereka cha Kutsazikana
Yesu ndi atumwiwo akonzekera kuchoka m’chipinda chapamwamba. “Izi ndalankhula ndi inu kuti mungakhumudwitsidwe,” iye akupitiriza motero. Ndiyeno iye akupereka chenjezo lapadera kuti: “Adzakutulutsani m’masunagoge; koma ikudza nthaŵi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikira Mulungu.”
Mwachiwonekere atumwiwo akuvutika maganizo kwambiri ndi chenjezo limeneli. Ngakhale kuti Yesu anali atanena poyambirirapo kuti dziko likawada, iye sanaulule mwachindunji motero kuti iwo akaphedwa. “Koma izi sindinanena [zimenezi] kwa inu kuyambira pachiyambi,” Yesu akufotokoza, “chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.” Komabe, nkwabwino chotani nanga kuwakonzekeretsa pasadakhale ndi chidziŵitso chimenechi iye asanachoke!
“Koma tsopano,” Yesu akupitiriza, “ndimuka kwa iye wondituma ine; ndipo palibe wina mwa inu andifunsa ine kuti, Mumka kuti?” Kuchiyambiyambi madzulowo, iwo anali atafufuza mwa kufunsa za kumene iye anali kupita, koma tsopano iwo achita kakasi ndi zimene iye wawauza kotero kuti iwo akulephera kufunsa zowonjezereka ponena za zimenezi. Monga momwe Yesu akunenera kuti: “Chifukwa ndalankhula izi ndi inu chisoni chadzala mumtima mwanu.” Atumwiwo achititsidwa chisoni osati kokha chifukwa chakuti azindikira kuti adzavutika ndi chizunzo chowopsa ndi kuphedwa komanso chifukwa chakuti Mbuye wawo akuwasiya.
Motero Yesu akufotokoza kuti: “Kuyenera kwa inu kuti ndichoke ine; pakuti ngati sindichoka, nkhosweyo sadzadza kwa inu; koma ngati ndipita ndidzamtuma iye kwa inu.” Monga munthu, Yesu angakhale kokha pamalo amodzi panthaŵi imodzi, koma pamene ali kumwamba, iye angatumize wothandizayo, mzimu woyera wa Mulungu, kwa otsatira ake kulikonse kumene iwo angakhale padziko lapansi. Chotero kuchoka kwa Yesu kudzakhala kopindulitsa.
Mzimu woyerawo, Yesu akutero, “adzatsutsa dziko lapansi za machimo, ndi za chilungamo, ndi za chiŵeruziro.” Tchimo la dziko, kulephera kwake kukhulupilira Mwana wa Mulungu, lidzavumbulidwa. Ndiponso, umboni wokhutiritsa wa chilungamo cha Yesu udzasonyezedwa mwa kukwera kwake kwa Atate. Ndipo kulephera kwa Satana ndi dziko lake loipa kuswa umphumphu wa Yesu ndiko umboni wokhutiritsa wakuti wolamulira wa dziko watsutsidwa.
“Ndiri nazo zambirinso zakunena kwa inu,” Yesu akupitiriza motero, “koma simungathe kuzisenza tsopano lino.” Chifukwa chake Yesu akulonjeza kuti pamene atsanulira mzimu woyera, umene uli mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, udzawatsogolera kukuzindikira zinthu zimenezi mogwirizana ndi luso lawo la kuzimvetsetsa.
Atumwiwo kwakukulukulu akulephera kuzindikira kuti Yesu adzafa ndiyeno kuwonekera kwa iwo ataukitsidwa. Chotero akufunsana kuti: “Ichi nchiyani chimene anena ndi ife, Kanthaŵi ndipo simundiwona; ndiponso kanthaŵi, ndipo mudzandiwona; ndipo, chifukwa ndimuka kwa Atate?”
Yesu akuzindikira kuti iwo akufuna kumfunsa, chotero iye akufotokoza kuti: “Indetu, indetu, ndinena ndi inu, kuti mudzalira ndi kubuma maliro inu, koma dziko lapansi lidzakondwera; mudzachita chisoni, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe.” Pambuyo pake tsiku limenelo, masana, pamene Yesu waphedwa, atsogoleri achipembedzo adyera akukondwera, koma ophunzirawo akumva chisoni. Komabe, chisoni chawocho chikusandulika chisangalalo, pamene Yesu waukitsidwa! Ndipo chisangalalo chawocho chikupitirirabe pamene iye akuwapatsa mphamvu pa Pentekoste ya kukhala mboni zake mwa kutsanulira pa iwo mzimu woyera wa Mulungu!
Poyerekezera mkhalidwe wa atumwi ndi uja wa mkazi mkati mwa zoŵaŵa zake za kubala, Yesu akuti: “Mkazi pamene akuti abale ali nacho chisoni, chifukwa yafika nthaŵi yake.” Koma Yesu akunena kuti mkaziyo samakumbukiranso mavuto ake pamene mwana wake wabadwa, ndipo akulimbikitsa atumwi ake, kuti: “Inu tsono muli nacho chisoni tsopano lino, koma ndidzakuwonaninso [pamene ndaukitsidwa], ndipo mtima wanu udzakondwera, ndipo palibe wina adzachotsa kwa inu chimwemwe chanu.”
Kufikira panthaŵi ino, atumwiwo sanapange konse mapempho m’dzina la Yesu. Koma tsopano iye akuti: “Ngati mudzapempha Atate kanthu, adzakupatsani inu m’dzina langa. . . . Pakuti Atate yekha akonda inu, chifukwa inu mwandikonda ine, ndi kukhulupilira kuti ine ndinatuluka kwa Atate. Ndinatuluka mwa Atate, ndipo ndadza kudziko lapansi: ndilisiyanso dziko lapansi, ndipo ndipita kwa Atate.”
Mawu a Yesu ngachilimbikitso chachikulu kwa atumwiwo. “Mwa ichi tikhulupilira kuti munatuluka kwa Mulungu,” iwo akutero. “Kodi mukhulupilira tsopano?” Yesu akufunsa. “Wonani! ikudza nthaŵi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya pa ndekha.” Zosakhulupirika monga momwe zingawonekerere, zimenezi zikuchitika usikuwo kusanache!
“Zinthu izi ndalankhula ndi inu, kuti mwa ine mukhale nawo mtendere.” Yesu akumaliza: “M’dziko lapansi mudzakhala nacho chivuto, koma limbikani mtima; ndalilaka dziko lapansi.” Yesu analaka dziko mwa kukwaniritsa mokhulupirika chifuno cha Mulungu mosasamala kanthu za zinthu zonse zimene Satana ndi dziko lake anayesa kuchita kuswa umphumphu wa Yesu.
Pemphero Lotsiriza m’Chipinda Chapamwamba
Mosonkhezeredwa ndi chikondi chachikulu kaamba ka atumwi ake, Yesu wakhala akuwakonzekeretsa kaamba ka kuchoka kwake kumene kwayandikira koposa. Tsopano atawadandaulira ndi kuwatonthoza kwanthaŵi yaitali, akugadamira kumwamba ndi kupempha Atate wake kuti: “Lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akalemekeze inu, monga mwampatsa ulamuliro pathupi lirilonse, kuti onse amene mwampatsa iye, awapatse iwo moyo wosatha.”
Ndimutu wankhani wothutsa mtima chotani nanga umene Yesu akutchula—moyo wosatha! Pokhala atapatsidwa “ulamuliro pathupi lirilonse,” Yesu angapereke mapindu a nsembe yake ya dipo kumtundu wonse womafa wa anthu. Komabe, iye amapereka “moyo wosatha” kwa awo okha amene Atate amavomereza. Poumba nkhaniyo pamutu umenewu wa moyo wosatha, Yesu akupitiriza pemphero lake:
“Moyo wosatha ndi uwu, kuti adziŵe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” Inde, chipulumutso chimadalira pakuloŵetsa kwathu chidziŵitso cha onse aŵiriwo Mulungu ndi Mwana wake. Koma zowonjezereka zimafunika koposa kokha chidziŵitso chammutu.
Munthu ayenera kufikira pakuwadziŵa monga mabwenzi, akumakulitsa unansi waubwenzi ndi iwo. Munthuyo ayenera kulingalira monga mmene iwo amachitira pa zinthu ndi kuwona zinthu monga momwe iwo amawonera. Koposa zonse, munthu ayenera kuyesayesa kutsanzira mikhalidwe yawo yosayerekezereka pochita ndi ena.
Kenako Yesu akupemphera kuti: “Ine ndalemekeza inu padziko lapansi, mmene ndinatsiriza ntchito imene munandipatsa ndichite.” Pokhala atakwaniritsa gawo lake motero kufikira pamlingo uno ndi kukhala wotsimikizira chipambano chake chamtsogolo, iye akupempha kuti: “Atate, lemekezani ine ndi inu nokha ndi ulemelero umene ndinali nawo ndi inu lisanakhale dziko lapansi.” Inde, iye tsopano akupempha kubwezeretsedwera kuulemelero wake woyambilira wakumwamba mwanjira ya chiukiliro.
Ponena mwachidule ntchito yake yaikulu padziko lapansi, Yesu akuti: “Ndaliwonetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa ine m’dziko lapansi; anali anu, ndipo mwandipatsa ine iwo; ndipo adasunga mawu anu.” Yesu anagwiritsira ntchito dzina la Mulungu, Yehova, muuminisitala wake ndipo anasonyeza matchulidwe ake olondola, komatu iye anachita zowonjezereka kuposa zimenezo kupangitsa dzina la Mulungu kudziŵika kwa atumwi ake. Iye anakulitsanso chidziŵitso chawo ndi kuyamikira Yehova, umunthu wake, ndi zifuno zake.
Potamanda Yehova monga mbuyake, Amene amamtumikira, Yesu modzichepetsa akuvomereza kuti: “Mawu amene munandipatsa ine ndinapatsa iwo; ndipo analandira, nazindikira kowona kuti ndinatuluka kwa inu, ndipo anakhulupilira kuti inu munandituma ine.”
Posiyanitsa otsatira ake ndi otsala onse a mtundu wa anthu, Yesu kenako akupemphera kuti: “Ndiwapempherera iwo; sindipempherera dziko lapansi, koma iwo amene mwandipatsa ine . . . Pamene ndinakhala nawo ine, ndinalikuwasunga . . . , ndipo ndinawasunga, ndipo sanatayika mmodzi yense wa iwo, koma mwana wa chitayiko,” ndiko kuti, Yudase Isikariote. Panthaŵi yeniyeni imeneyi, Yudase ali pa ulendo wake wachiwembu chopanda nzerucho cha kupereka Yesu. Motero, Yudase mosadziŵa akukwaniritsa Malemba.
“Dziko lapansi linadana nawo,” Yesu akupitiriza kupemphera motero. “Sindipempha kuti muwachotse iwo m’dziko lapansi, koma kuti muwasunge iwo kuletsa woipayo. Siali a dziko lapansi monga ine sindiri wa dziko lapansi.” Otsatira a Yesu ali m’dziko, chitaganya cha anthu cholinganizidwa ichi cholamuliridwa ndi Satana, koma iwo ali ndipo nthaŵi zonse ayenera kukhala olekana nalo ndi kuipa kwake.
“Patulani iwo m’chowonadi,” Yesu akupitiriza motero, “mawu anu ndichowonadi.” Panopa Yesu akutchula Malemba ouziridwa Achihebri, kumene anagwirako mawuwo mopitirizabe kuti “chowonadi.” Koma zimene anaphunzitsa ophunzira ake ndi zimene iwo pambuyo pake analemba mwachiuziro monga Malemba Achikristu Achigiriki nazonso ziri “chowonadi.” Chowonadi chimemechi chingayeretse munthu, kusintha moyo wake kotheratu, ndi kumpanga kukhala munthu wolekana ndi dziko.
Tsopano Yesu akupemphera “koma sindipempherera iwo okha, komanso iwo akukhulupilira [iye] chifukwa cha mawu awo.” Motero Yesu akupempherera awo amene adzakhala otsatira ake odzozedwa ndi ophunzira ena amtsogolo amene adzasonkhanitsidwabe mu “khola limodzi.” Kodi iye akupemphereranji onseŵa?
“Kuti akakhale amodzi, monga mmene inu Atate mwa ine, ndi ine mwa inu, . . . kuti akhale amodzi, monga ife tiri amodzi.” Yesu ndi Atate wake saali kwenikweni munthu mmodzi, koma iwo amagwirizana pazinthu zonse. Yesu akupempherera kuti otsatira ake akhale ndi umodzi wofanana umenewu kutsata “kuti dziko lapansi lizindikire kuti inu munandituma ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda ine.”
Yesu tsopano akupempherera, awo amene akakhala otsatira ake odzozedwa kwa Atate wake wakumwamba. Za chiyani? “Kuti, kumene ndiri ine, iwonso akhale pamodzi ndi ine; kuti ayang’anire ulemelero wanga, umene mwandipatsa ine pakuti munandikonda ine lisanakhazikike dziko lapansi,” ndiko kuti, Adamu ndi Hava asanabale ana awo. Kalekale anawo asanabadwe, Mulungu anakonda Mwana wake wobadwa yekha, amene anadzakhala Yesu Kristu.
Pomaliza pemphero lake, kachiŵirinso Yesu akugogomezera kuti: “Ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa; kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo ndi ine mwa iwo.” Kwa atumwiwo, kuzindikira dzina la Mulungu kwaphatikizapo kudziŵa mwachindunji chikondi cha Mulungu. Yohane 14:1–17:26; 13:27, 35, 36; 10:16; Luka 22:3, 4; Eksodo 24:10; 1 Mafumu 19:9-13; Yesaya 6:1-5; Agalatiya 6:16; Salmo 35:19; 69:4; Miyambo 8:22, 30.
▪ Kodi Yesu akumka kuti, ndipo kodi ndiyankho lotani limene Tomasi akulandira ponena za njira yomka kumeneko?
▪ Mwapempho lake, kodi Filipo mwachiwonekere akufuna kuti Yesu aperekenji?
▪ Kodi nchifukwa ninji munthu amene wawona Yesu wawonanso Atate?
▪ Kodi otsatira a Yesu adzachita ntchito zokulirapo kuposa zimene iye anachita motani?
▪ Kodi Satana alibe ulamuliro pa Yesu m’lingaliro lotani?
▪ Kodi ndiliti pamene Yehova anabzala mpesa wophiphiritsira, ndipo ndiliti ndipo ndimotani mmene ena amakhalira mbali ya mpesawo?
▪ Potsirizira, kodi ndinthambi zingati zimene mpesa wophiphiritsirawo uli nazo?
▪ Kodi ndichipatso chotani chimene Mulungu amafuna kuchokera pa nthambizo?
▪ Kodi ndimotani mmene tingakhalire mabwenzi a Yesu?
▪ Kodi nchifukwa ninji dziko limada otsatira a Yesu?
▪ Kodi ndichenjezo lotani lonenedwa ndi Yesu limene likuvutitsa maganizo a atumwi ake?
▪ Kodi nchifukwa ninji atumwiwo akulephera kufunsa Yesu za kumene akupita?
▪ Kodi nchiyani chimene atumwiwo makamaka akulephera kudziŵa?
▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akusonyezera kuti mkhalidwe wa atumwiwo udzasintha kuchokera kuchisoni kumka kuchisangalalo?
▪ Kodi nchiyani chimene Yesu akunena kuti atumwiwo adzachita mwamsanga?
▪ Kodi Yesu akulaka dziko motani?
▪ Kodi ndim’lingaliro lotani m’limene Yesu akupatsidwa “ulamuliro pathupi lirilonse”?
▪ Kodi kuloŵetsa chidziŵitso cha Mulungu ndi Mwana wake kumatanthauzanji?
▪ Kodi ndim’njira zotani zimene Yesu akupangitsa dzina la Mulungu kudziŵika?
▪ Kodi “chowonadi” nchiyani, ndipo kodi ‘chimayeretsa’ Mkristu motani?
▪ Kodi ndimotani mmene Mulungu, Mwana wake, ndi olambira onse owona aliri amodzi?
▪ Kodi ndiliti pamene “dziko lapansi linakhazikika”?