Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 111
  • Chizindikiro cha Masiku Otsiriza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chizindikiro cha Masiku Otsiriza
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Chidaliro Mkati mwa Masiku Otsiriza
  • Anamwali Ochenjera ndi Opusa
  • Fanizo la Matalente
  • Pamene Kristu Afika m’Mphamvu Yaufumu
  • Anamwali Anzeru ndi Opusa
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Fanizo la Anamwali Limatiphunzitsa Kufunika Kokhala Tcheru
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kuunika Kaamba ka “Mapeto a Dongosolo la Zinthu”
    Chisungiko cha Padziko Lonse mu Ulamuliro wa “Kalonga wa Mtendere”
  • Fanizo la Matalente
    Nsanja ya Olonda​—1990
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 111

Mutu 111

Chizindikiro cha Masiku Otsiriza

POFIKA tsopano ndi Lachiŵiri masana. Yesu ali khale pa Phiri la Azitona, akuyang’ana kachisi chamunsimo, Petro, Andreya, Yakobo, ndi Yohane akudza kwa iye mwamtseri. Iwo ali odera nkhaŵa ndi kachisiyo, pakuti Yesu wangoneneratu kumene kuti mwala sudzasiidwa pamwala unzake pakachisipo.

Koma mwachiwonekere iwo alidi nzambiri m’maganizo mwawo pamene akufika kwa Yesu. Milungu ingapo yapitayo, iye adalankhula za ‘kukhalapo’ kwake, mkati mwa nthaŵi imene ‘Mwana wa munthu adzavumbulutsidwa.’ Ndipo pachochitika choyambirira, iye adawafotokozera za “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” Chotero atumwiwo ngachidwi kwambiri.

“Mutiuze ife,” iwo akutero, “zija zidzawoneka liti [kuchitika kwa chiwonongeko cha Yerusalemu ndi kachisi wake]? ndipo chizindikiro cha kufika kwanu [kukhalapo kwanu, NW], nchiyani, ndi cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano?” M’chenicheni, funso lawolo nlambali zitatu. Choyamba, iwo akufuna kudziŵa za mapeto a Yerusalemu ndi kachisi wake, ndiyeno yonena za kukhalapo kwa Yesu m’mphamvu Yaufumu, ndipo potsiriza ponena za mapeto a dongosolo lonse la zinthu.

Muyankho lake lalitali, Yesu akuyankha mbali zonse zitatu za funsolo. Akupereka chizindikiro chimene chikusonyeza pamene dongosolo la zinthu Lachiyuda lidzatha; koma iye akutchula zowonjezereka. Iye akuperekanso chizindikiro chimene chidzagalamutsa ophunzira ake amtsogolo kuti adziŵe kuti iwo akukhala ndi moyo mkati mwa kukhalapo kwake ndipo ali pafupi ndi mapeto a dongosolo lonse la zinthu.

Pamene zakazo zikupita, atumwiwo akuwona kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu. Inde, zinthu zenizenizo zimene ananeneratu zikuyamba kuchitika m’tsiku lawo. Motero, Akristu amene ali ndi moyo zaka 37 pambuyo pake, mu 70 C.E., sakudzidzimutsidwa ndi chiwonongeko cha dongosolo Lachiyuda ndi kachisi wake.

Komabe, kukhalapo kwa Kristu ndi chimaliziro cha dongosolo la zinthu sizikuchitika mu 70 C.E. Kukhalapo kwake m’mphamvu Yaufumu kukuchitika nthaŵi yaitali pambuyo pake. Koma kodi ndiliti? Kupenda kwa ulosi wa Yesu kumavumbula zimenezi.

Yesu akuneneratu kuti padzakhala “nkhondo, ndi mbiri za nkhondo.” “Mtundu umodzi wa anthu udzaukirana ndi mtundu wina,” iye akutero, ndipo padzakhala kupereŵera kwa chakudya, zivomezi, ndi miliri. Ophunzira ake adzadedwa ndi kuphedwa. Aneneri onyenga adzauka ndi kusokeretsa ambiri. Kusayeruzika kudzawonjezereka, ndipo chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala. Panthaŵi imodzimodziyo, mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu idzalalikidwa monga mboni kumitundu yonse.

Ngakhale kuti ulosi wa Yesu uli ndi kukwaniritsidwa kokhala ndi malire chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. chisanachitike, kukwaniritsidwa kwake kwakukulu kukuchitika mkati mwa kukhalapo kwake ndi mkati mwa mapeto a dongosolo la zinthu. Kupenda mosamalitsa zochitika za dziko chiyambire 1914 kumavumbula kuti ulosi wosaiŵalikawo wa Yesu wakhala ndi kukwaniritsidwa kwake kwakukulu chiyambire chakacho.

Mbali ina ya chizindikiro chimene Yesu akupereka ndiyo kuwonekera kwa “chonyansa cha kupululutsa.” Mu 66 C.E. chonyansa chimenechi chiwonekera mumpangidwe wa ‘magulu a ankhondo ozinga’ a Roma amene akweteza Yerusalemu ndi kugwetsa linga la kachisi. ‘Chonyansacho’ chikuima pa malo amene sichinayenera kuimapo.

M’kukwaniritsidwa kwakukulu kwa chizindikirocho, chonyansacho ndicho Chigwirizano cha Amitundu ndi choloŵa m’malo chake, Mitundu Yogwirizana. Gulu lochirikiza mtendere wadziko limeneli limalingaliridwa ndi Chikristu Chadziko kukhala loloŵa m’malo mwa Ufumu wa Mulungu. Nchonyansa chotani nanga! Chifukwa chake, m’kupita kwa nthaŵi, maulamuliro a ndale zadziko mogwirizana ndi UN adzatembenukira Chikristu Chadziko (Yerusalemu wophiphiritsira) nadzachipululutsa.

Chotero Yesu akuneneratu kuti: ‘Padzakhala chisautso chachikulu, monga sipadakhale chotero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.’ Pamene kuli kwakuti chiwonongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. chiridi chisautso chachikulu, chokhala ndi oposa miliyoni imodzi osimbidwa kukhala ataphedwa, sichiri chisautso chokulirapo kuposa Chigumula chapadziko lonse cha m’tsiku la Nowa. Chotero kukwaniritsidwa kwakukulu kwa mbali imeneyi ya ulosi wa Yesu kukachitikabe mtsogolo.

Chidaliro Mkati mwa Masiku Otsiriza

Pamene Lachiŵirilo, Nisani 11, liri pafupi kutha, Yesu akupitiriza kukambitsirana ndi atumwi ake ponena za chizindikiro cha kukhalapo kwake m’mphamvu Yaufumu ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu. Akuwachenjeza za kusalondola Akristu onyenga. Zoyesayesa zidzapangidwa, iye akutero, “kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe.” Koma, mofanana ndi miimba yowona patali, osankhidwa ameneŵa adzasonkhana kumene chakudya chenicheni chauzimu chikapezekako, ndiko kuti, ndi Kristu weniweni pakukhalapo kwake kosawoneka. Sadzasochezedwa ndi kusonkhanitsidwira pamodzi kwa Kristu wonyenga.

Akristu onyenga angawoneke m’thupi chabe. Mosiyana, kukhalapo kwa Yesu kudzakhala kosawoneka. Kudzachitika mkati mwa nthaŵi yochititsa mantha m’mbiri ya anthu, monga momwedi Yesu akunenera kuti: “Dzuŵa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzawonetsa kuŵala kwake.” Inde, imeneyi idzakhala nyengo yamdima wa ndiweyani yoposa zonse m’mbiri ya anthu. Kudzakhala monga ngati kuti dzuŵa linadetsedwa m’nthaŵi yamasana, ndipo monga ngati kuti mwezi sunawonetse kuŵala kwake usiku.

“Mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka,” Yesu akupitiriza. Chotero iye akusonyeza kuti miyamba yeniyeniyo idzakhala malo ochititsa mantha. Miyamba sidzakhala malo a mbalame chabe, koma idzadzala ndi ndege zankhondo, maroketi, ndi masiteshoni a openda za mlengalenga. Mantha ndi chiwawa zidzaposa zirizonse zochitika m’mbiri ya anthu yapitayo.

Monga chotulukapo, Yesu akuti, padzakhala “chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pamkukumo wake wa nyanja ndi mafunde ake; anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zirinkudza kudziko lapansi.” Ndithudi, nyengo yamdima wa ndiweyani imeneyi ya kukhalapo kwa anthu idzatsogolera kunthaŵi imene, monga momwe Yesu akunenera kuti, “padzawoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa munthu; ndipo mitundu yonse ya pa dziko lapansi idzadziguguda pachifuwa.”

Komabe sionse amene adzadziguguda pachifuwa pamene ‘Mwana wa munthu adza ndi mphamvu’ kudzawononga dongosolo loipa la zinthuli. “Osankhidwawo,” a 144,000 amene adzakhala ndi phande limodzi ndi Kristu mu Ufumu wake wakumwamba, sadzadziguguda pachifuwa, ngakhalenso atsamwali awo, amene Yesu poyambirirapo anatcha “nkhosa zina” sadzatero. Mosasamala kanthu za kukhala ndi moyo mkati mwa nyengo yamdima wa ndiweyani koposa yonse m’mbiri ya anthu, ameneŵa amalabadira chilimbikitso cha Yesu chakuti: “Poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.”

Kuti ophunzira ake amene akakhala ndi moyo mkati mwa masiku otsiriza akakhoze kuzindikira kuyandikira kwa mapetowo, Yesu akupereka fanizo ili: “Wonani mkuyu, ndi mitengo yonse: pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja liri pafupi pomwepo. Inde chotero inunso, pakuwona zinthu izi zirikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Indetu ndinena ndinu, mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitachitika.”

Chotero, pamene ophunzira ake awona mbali zambiri zosiyanasiyana za chizindikiro zikukwaniritsidwa, ayenera kuzindikira kuti mapeto a dongosolo la zinthu ayandikira ndi kuti Ufumu wa Mulungu mwamsanga udzachotsa kuipa konse. Kunena zowona, mapetowo adzachitika mkati mwa nthaŵi ya moyo wa anthu amene akuwona kukwaniritsidwa kwa zinthu zonse zimene Yesu akuneneratu! Podandaulira ophunzira amene akakhala ndi moyo mkati mwa masiku otsiriza osaiŵalikawo, Yesu akuti:

“Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi. Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa munthu.”

Anamwali Ochenjera ndi Opusa

Yesu wakhala akuyankha funso la atumwi ake la chizindikiro cha kukhalapo kwake m’mphamvu Yaufumu. Tsopano iye akupereka mbali zina zowonjezereka za chizindikirocho m’miyambi itatu, kapena mafanizo.

Kukwaniritsidwa kwa fanizo lirilonse kukawonedwa ndi okhala ndi moyo mkati mwa kukhalapo kwake. Iye akuyamba loyambalo ndi mawu akuti: “Pomwepo ufumu wa kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi, amene anatenga nyali zawo, natuluka kukakomana ndi mkwati. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera.”

Mwa mawuwo “ufumu wa kumwamba udzafanizidwa ndi anamwali khumi,” Yesu sakutanthauza kuti theka la awo amene akulandira Ufumu wa kumwamba ali anthu opusa ndipo theka ali ochenjera! Ayi, koma iye akutanthauza kuti mu Ufumu wa kumwamba, muli mbali yofanana ndi iyi kapena inayo, kapena kuti zochitika zogwirizanitsidwa ndi Ufumuwo zidzakhala zofanana motere ndiponso motere.

Anamwali khumiwo amaphiphiritsira Akristu onse amene ali mumzera kapena amene amadzinenera kukhala mumzera wa Ufumu wakumwamba. Panali pa Pentekoste 33 C.E. pamene mpingo Wachikristu unatomeredwa ndi Mkwati wovekedwa ulemelero woukitsidwayo, Yesu Kristu. Koma ukwatiwo unali kudzachitikira kumwamba panthaŵi yosadziŵika mtsogolomo.

M’fanizolo, anamwali khumi akutuluka ndi chifuno cha kukachingamira mkwati ndi kukagwirizana nawo m’dzoma laukwati. Pamene afika, iwo adzaunikira njira ya aukwatiwo ndi nyali zawo, motero kumlemekeza pamene akubweretsa mkwatibwi wake kunyumba yokonzedwera mkwatibwiyo. Komabe, Yesu akufotokoza kuti: “Opusawo, mmene anatenga nyali zawo, sanadzitengeranso mafuta; koma anzeruwo anatenga mafuta m’nsupa zawo, pamodzi ndi nyali zawo. Ndipo pamene mkwati anachedwa, onsewo anawodzera, nagona tulo.”

Kuchedwa kwambiri kwa mkwatiyo kumasonyeza kuti kukhalapo kwa Kristu monga Mfumu yolamulira kudzakhala mtsogolo. Iye potsilizira pake akudza pampando wake wachifumu m’chaka cha 1914. Mkati mwa usiku wautaliwo chakacho chisanafike, anamwali onse agona tulo. Koma iwo sakutsutsidwira kutero. Kutsutsidwa kwa anamwali opusawo kuli kaamba ka kusakhala kwawo ndi mafuta m’nsupa zawo. Yesu akufotokoza mmene anamwaliwo akudzukira mkwatiyo asanafike kuti: “Koma pakati pa usiku panali kufuula, Wonani, mkwati! tulukani kukakomana naye. Pomwepo anauka anamwali onse amenewo, nakonza nyali zawo. Ndipo opusa anati kwa ochenjera, Tipatseniko ena a mafuta anu; chifukwa nyali zathu zirikuzima. Koma ochenjera anayankha nati, Kapena sangakwanire ife ndi inu; koma makamaka mukani kwa ogulitsa malonda, mukadzigulire inu nokha.”

Mafuta amaphiphiritsira chimene chimapangitsa Akristu owona kukhala oŵala monga zounikira. Chimenechi ndicho Mawu a Mulungu ouziridwa, amene Akristu amagwiritsitsa zolimba, limodzi ndi mzimu woyera, umene umawathandiza kumvetsetsa Mawuwo. Mafuta auzimuwo amatheketsa anamwali ochenjera kuunikira pochingamira mkwati mkati mwa ligubo lomka kuphwando laukwati. Koma kagulu ka anamwali opusawo kalibe, mafuta auzimu ofunikawo m’nsupa zawo. Chotero Yesu akufotokoza zimene zikuchitika motere:

“Ndipo pamene iwo [anamwali opusawo] analikumuka kukagula [mafuta], mkwati anafika; ndipo okonzekawo analoŵa naye pamodzi muukwati; ndipo anatseka pakhomo. Koma pambuyo pake anadzanso anamwali enawo, nati, Mbuye, Mbuye, mutitsegulire ife. Koma iye anayankha nati, Indetu ndinena kwa inu, sindikudziŵani.”

Pamene Kristu afika mu Ufumu wakumwamba, kagulu ka anamwali ochenjera ka Akristu odzozedwa owona kakugalamuka ku mwaŵi wawo wa kuŵalitsira kuunika m’dziko ili lokanthidwa ndi mdima mwa kutamanda Mkwati amene wabwerayo. Koma awo amene akuphiphiritsiridwa ndi anamwali opusa ngosakonzekera kupereka chitamando cha kuchingamira chimenechi. Chotero pamene nthaŵi ifika, Kristu sakuwatsegulira khomo loloŵera kuphwando laukwati kumwamba. Iye akuwasiya kunja mumdima wa usiku wakuda bii wa dzikoli, kuti awonongeke limodzi ndi ena onse ochita kusayeruzika. “Chifukwa chake dikirani,” Yesu akumaliza motero, “pakuti simudziŵa tsiku lake, kapena nthaŵi yake.”

Fanizo la Matalente

Yesu akupitiriza kukambitsirana kwake ndi atumwi pa Phiri la Azitona mwa kuwauza fanizo lina, lachiŵiri mumpambo wa atatuwo. Masiku angapo apitawo, pamene anali ku Yeriko, iye anapereka fanizo la ndalama khumi kusonyeza kuti Ufumu unali chikhalirebe kutali m’nthaŵi yamtsogolo. Fanizo limene akusimba tsopano, pamene kuli kwakuti liri ndi mbali zingapo zofanana, limafotokoza m’kukwaniritsidwa kwake zochitika mkati mwa kukhalapo kwa Kristu m’mphamvu Yaufumu. Limafotokoza mwafanizo kuti ophunzira ake ayenera kugwira ntchito pamene adakali padziko lapansi kuwonjezera “chuma chake.”

Yesu akuyamba kuti: “Pakuti [ndiko kuti, mikhalidwe yogwirizanitsidwa ndi Ufumu iri] monga munthu, wakumka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake.” Yesu ndiye munthuyo, amene, asanapite paulendo wakutali wa kumwamba, apereka kwa akapolo ake—ophunzira oyembekezera Ufumu wakumwamba—chuma chake. Chuma chimenechi sichiri chuma chakuthupi, koma chimaimira munda wolimidwa muumene iye wakulitsa kuthekera kwa kutulutsamo ophunzira owonjezereka.

Yesu akuikizira chuma chake kwa akapolo ake mwamsanga asanakwere kumwamba. Kodi akuchita zimenezo motani? Mwa kuwalangiza kupitirizabe kugwira ntchito m’munda wolimidwawo mwa kulalikira uthenga Waufumu kumalekezero a dziko lapansi. Monga momwe Yesu akunenera kuti: “Mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziŵiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zawo; namuka iye.”

Motero matalente asanu ndi atatu—chuma cha Kristu— akugaŵiridwa molingana ndi maluso, kapena mwamphamvu yauzimu, ya akapolo. Akapolowo akuimira timagulu ta ophunzira. Mwachiwonekere m’zaka za zana loyamba, kagulu kamene kanalandira matalente asanu kanaphatikizapo atumwi. Yesu akupitiriza kusimba kuti akapolo onse aŵiri amene analandira matalente asanuyo ndi wina aŵiri anawawonjezera kuŵirikiza kaŵiri mwa kulalikira kwawo Ufumu ndi kupanga ophunzira. Komabe, kapolo amene analandira talente limodzi analibisa pansi.

“Itapita nthaŵi yaikulu,” Yesu akupitiriza, “anabwera mbuye wa akapolo awo, naŵerengera nawo pamodzi.” Sikunali kufikira m’zaka za zana la 20, pafupifupi zaka 1,900 pambuyo pake, pamene Kristu anabwera kudzaŵerengera ndalamazo, chotero, kunalidi, “itapita nthaŵi yaikulu.” Pamenepo Yesu akufotokoza kuti:

“Ndipo uyo amene adalandira ndalama za matalente zisanu anadza, ali nazo ndalama zina zisanu, nanena, Mbuye, munandipatsa ndalama za matalente zisanu, wonani ndapindulapo ndalama zisanu zina. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing’ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; loŵa iwe m’chikondwero cha mbuye wako.” Kapolo amene analandira matalente aŵiri mofananamo anachulukitsa matalente ake kuŵirikiza kaŵiri, ndipo analandira thamo limodzimodzilo ndi mphotho.

Komano, kodi akapolo okhulupirika ameneŵa akuloŵa motani m’chikondwero cha Mbuye wawo? Eya, chikondwero cha Mbuyawo, Yesu Kristu, ndicho cha kulandira chuma cha Ufumu pamene anapita kutali kwa Atate wake kumwamba. Ponena za akapolo okhulupirika m’nthaŵi zamakono, iwo ali ndi chikondwero chachikulu cha kuikiziridwa mathayo owonjezereka Aufumu, ndipo pamene amaliza njira yawo ya padziko lapansi, adzakhala ndi chikondwero chachikulu cha kuukitsidwira ku Ufumu wakumwamba. Koma bwanji nanga za kapolo wachitatu?

“Mbuye, ndinakudziŵani inu kuti ndinu munthu wouma mtima,” kapoloyu akudandaula motero. “Ndinawopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi ndalama yanu: wonani, siyi yanu.” Kapoloyo anakana mwadala kugwira ntchito m’munda wolimidwa mwa kulalikira ndi kupanga ophunzira. Chotero mbuyeyo akumutcha “woipa ndi waulesi” napereka chiweruzo kuti: “Chotsani kwa iye ndalamayo . . . Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake ku mdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.” Awo a kagulu ka kapolo woipa ameneyu, oponyeredwa kunja, amamanidwa chikondwero chauzimu chirichonse.

Zimenezi zikupereka phunziro lamphamvu kwa onse amene amadzinenera kukhala otsatira a Kristu. Ngati ati alandire chiyamikiro chake ndi mphotho, ndi kupeŵa kuponyedwa kunja kumdima ndipo potsirizira pake chiwonongeko, iwo ayenera kugwirira ntchito kuwonjezera chuma cha Mbuye wawo wakumwamba mwa kukhala ndi phande mokwanira m’ntchito yolalikira. Kodi inu muli wakhama m’ntchitoyi?

Pamene Kristu Afika m’Mphamvu Yaufumu

Yesu adakali ndi atumwi ake pa Phiri la Azitona. Poyankha funso lawo la chizindikiro cha kukhalapo kwake ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu, iye tsopano akuwasimbira lomalizira mumpambo wa mafanizo atatuwo. “Pamene Mwana wa munthu adzadza muulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye,” Yesu akuyamba motero, “pomwepo iye adzakhala pachimpando cha kuŵala kwake.”

Anthu sangathe kuwona angelo muulemerero wawo wakumwamba. Chotero kufika kwa Mwana wa munthu, Yesu Kristu, limodzi ndi angelo kuyenera kukhala kosawoneka ndi maso aumunthu. Kufikako kukuchitika m’chaka cha 1914. Koma kodi kuli kaamba ka chifuno chotani? Yesu akufotokoza kuti: “Adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere.”

Pofotokoza zimene zidzachitikira olekanitsidwira kumbali yoyanjidwa, Yesu akuti: “Pomwepo Mfumuyo idzanena kwa iwo a ku dzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu Ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.” Nkhosa za m’fanizo ili sizidzalamulira limodzi ndi Kristu kumwamba koma zidzalandira Ufumuwo m’lingaliro la kukhala nzika zake zapadziko lapansi. “Chikhazikiro chake cha dziko lapansi” chinachitika poyambapo pamene Adamu ndi Hava anabala ana amene akakhoza kupindula ndi makonzedwe a Mulungu a kuwombola anthu.

Koma kodi nchifukwa ninji nkhosazo zikulekanitsidwira kudzanja lamanja la chiyanjo la Mfumu? “Pakuti ndinali ndi njala,” mfumuyo ikuyankha motero, “ndipo munandipatsa ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza ine; wamaliseche ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi ine; ndinali m’nyumba yandende, ndipo munadza kwa ine.”

Popeza kuti nkhosazo ziri padziko lapansi, izo zifuna kudziŵa mmene zikanakhala zitachitira Mfumu yawo yakumwambayo ntchito zabwino zotero. “Ambuye tinakuwonani inu liti wanjala, ndi kukudyetsani,” iwo akufunsa motero, “kapena waludzu, ndi kukumwetsani? Ndipo tinawona inu liti mlendo, ndi kukucherezani? kapena wamaliseche, ndi kukuvekani? Ndipo tinakuwonani inu liti wodwala, kapena m’nyumba yandende, ndipo tinadza kwa inu?”

“Indetu ndinena kwa inu,” Mfumuyo ikuyankha motero, “chifukwa munachitira ichi mmodzi wa abale anga, ngakhale ang’onong’ono aŵa, munandichitira ichi ine.” Abale a Kristu ndiwo otsalira padziko lapansi a 144,000 amene adzalamulira limodzi naye kumwamba. Ndipo kuwachitira zabwino, Yesu akutero, kuli kofanana ndi kumchitira iye zabwino.

Kenako, Mfumuyo ikulankhula kwa mbuzi. “Chokani kwa ine otembereredwa inu, kumoto wa nthaŵi zonse wokolezedwera Mdyerekezi ndi amithenga ake: pakuti ndinali ndi njala, ndipo simunandipatsa ine kudya: ndinali ndi ludzu, ndipo simunandimwetsa ine: ndinali mlendo, ndipo simunandilandira ine; wamaliseche ndipo simunandiveka ine; wodwala, ndi m’nyumba yandende, ndipo simunadza kundiwona ine.”

Komabe, mbuzizo zikudandaula kuti: “Ambuye, tinakuwonani liti wanjala, kapena waludzu, kapena mlendo, kapena wamaliseche, kapena m’nyumba yandende, ndipo ife sitinakutumikirani inu?” Mbuzizo zikuweruzidwa mosayanjidwa pamaziko amodzimodziwo amene nkhosazo zikuweruzidwa moyanjidwa. “Chifukwa munalibe kuchitira ichi mmodzi wa aŵa ang’onong’ono [a abale anga],” Yesu akuyankha, “munalibe kundichitira ichi ine.”

Chotero kukhalapo kwa Kristu m’mphamvu Yaufumu, mwamsanga mapeto a dongosolo ili loipa la zinthu pachisautso chachikulu asanachitike, kudzakhala nthaŵi yachiweruzo. Mbuzi ‘zidzachoka kumka kukudulidwa kosatha; koma olungama [nkhosazo] kuloŵa m’moyo wosatha.’ Mateyu 24:2–25:46; 13:40, 49; Marko 13:3-37; Luka 21:7-36; 19:43, 44; 17:20-30; 2 Timoteo 3:1-5; Yohane 10:16; Chivumbulutso 14:1-3.

▪ Kodi nchiyani chisonkhezera funso la atumwilo, koma mwachiwonekere nchiyaninso chimene ali nacho m’maganizo mwawo?

▪ Kodi ndimbali iti ya ulosi wa Yesu imene ikukwaniritsidwa mu 70 C.E., koma nchiyani chimene sichikuchitika panthaŵiyo?

▪ Kodi ndiliti pamene ulosi wa Yesu ukukhala ndi kukwaniritsidwa koyamba, koma ndiliti pamene ukukhala ndi kukwaniritsidwa kwakukulu?

▪ Kodi nchiyani chimene chiri chonyansa m’kukwaniritsidwa kwake koyamba ndi kotsirizira?

▪ Kodi nchifukwa ninji chisautso chachikulu sichinakwaniritsidwe kotheratu pachiwonongeko cha Yerusalemu?

▪ Kodi ndimikhalidwe yotani yadziko imene ikusonyeza kukhalapo kwa Kristu?

▪ Kodi ndiliti pamene ‘mitundu yonse ya padziko lapansi idzalira ndi kudziguguda pachifuwa,’ koma kodi otsatira a Kristu adzakhala akuchita chiyani?

▪ Kodi ndifanizo lotani limene Yesu akupereka kuthandiza ophunzira ake amtsogolo kuzindikira pamene mapeto ayandikira?

▪ Kodi ndichilangizo chotani chimene Yesu akupereka kwa ophunzira ake amene akakhala ndi moyo mkati mwa masiku otsiriza?

▪ Kodi anamwali khumi amaphiphiritsira ayani?

▪ Kodi ndiliti pamene mpingo Wachikristu unatomeredwa ndi mkwati, koma kodi ndiliti pamene mkwatiyo akufika ndi kutengera mkwatibwi wake kuphwando laukwati?

▪ Kodi mafuta akuimira chiyani, ndipo kodi kukhala nawo kukutheketsa anamwali ochenjerawo kuchitanji?

▪ Kodi nkuti kumene phwando laukwati likuchitikira?

▪ Kodi ndimphotho yaikulu yotani imene anamwali opusa akutayikiridwa nayo, ndipo cholandira chawo nchiyani?

▪ Kodi ndiphunziro lotani limene fanizo la matalente limapereka?

▪ Kodi akapolowo ndayani, ndipo chuma chimene iwo aikizidwira nchiyani?

▪ Kodi ndiliti pamene mbuyeyo adza kudzaŵerengera ndalamazo, ndipo kodi iye akupezanji?

▪ Kodi nchikondwero chotani chimene akapolo okhulupirika akuloŵamo, ndipo nchiyani chikuchitikira kapolo wachitatu, woipayo?

▪ Kodi nchifukwa ninji kukhalapo kwa Kristu kuyenera kukhala kosawoneka, ndipo ndintchito yanji imene iye akuichita panthaŵiyo?

▪ Kodi ndimlingaliro lotani m’limene nkhosa zikuloŵa Ufumuwo?

▪ Kodi ndiliti pamene “chikhazikiro cha dziko lapansi” chinachitika?

▪ Kodi ndipamaziko otani pa amene anthu akuweruzidwapo monga nkhosa kapena monga mbuzi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena