Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 4/1 tsamba 16-21
  • “Tamandani ya, Anthu Inu!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Tamandani ya, Anthu Inu!”
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Taonani Mfumu Yaumesiya!
  • Kodi “Chimaliziro” Chidzafika Motani?
  • Nthaŵi ya Kutamanda Ya
  • Tamandani Ya Chifukwa cha Ziweruzo Zake
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Tamandani Mfumu Yamuyaya!
    Nsanja ya Olonda—1996
  • Chilanditso pa Vumbulutso la Yesu Kristu
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Chiwonongeko cha Dziko Chonenedweratucho Chidzadza Liti?
    Mtendere Weniweni ndi Chisungiko—Kodi Mungazipeze Motani?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 4/1 tsamba 16-21

“Tamandani ya, Anthu Inu!”

“Zonse zakupuma [zitamande, NW] Yehova.”​—SALMO 150:6.

1, 2. (a) Kodi Chikristu choona chinafalikira kufikira pati m’zaka za zana loyamba? (b) Kodi ndi chenjezo liti lapasadakhale limene atumwi anapereka? (c) Kodi mpatuko unayamba motani?

YESU anasonkhanitsa ophunzira ake ndi kupanga mpingo wachikristu, umene unafutukuka m’zaka za zana loyamba. Ngakhale kuti panali chitsutso choŵaŵa cha achipembedzo, ‘uthenga wabwino . . . unalalikidwa cholengedwa chonse cha pansi pa thambo.’ (Akolose 1:23) Koma pambuyo pa imfa ya atumwi a Yesu Kristu, Satana mwamachenjera anayambitsa mpatuko.

2 Atumwiwo anachenjezeratu za zimenezi. Mwachitsanzo, Paulo anauza akulu a ku Efeso kuti: “Tadzichenjerani nokha, ndi gulu lonse, pamenepo mzimu woyera anakuikani oyang’anira, kuti muŵete [mpingo, NW] wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa [Mwana wake wayekha, NW]. Ndidziŵa ine kuti, nditachoka ine, adzaloŵa mimbulu yosautsa, yosalekerera gululo; ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.” (Machitidwe 20:28-30; onaninso 2 Petro 2:1-3; 1 Yohane 2:18, 19.) Chotero, m’zaka za zana lachinayi, Chikristu champatuko chinayamba kugwirizana ndi Ufumu wa Roma. Zaka mazana angapo pambuyo pake, Ufumu Wopatulika wa Roma, wogwirizana ndi papa wa Roma, unayamba kulamulira chigawo chachikulu cha anthu. M’kupita kwa nthaŵi, gulu la Kukonzanso Kwachiprotesitanti linapandukira zochita zoipitsitsa za Tchalitchi cha Katolika, koma linalephera kubwezeretsa Chikristu choona.

3. (a) Kodi ndi liti ndipo ndi motani mmene uthenga wabwino unalalikidwira cholengedwa chonse? (b) Kodi ndi ziyembekezo ziti zozikidwa pa Baibulo zimene zinakwaniritsidwa mu 1914?

3 Komabe, pamene mapeto a zaka za zana la 19 anayandikira, kagulu kena koona mtima ka ophunzira Baibulo kanachitanso changu kulalikira ndi kupereka kwa ‘cholengedwa chonse cha pansi pa thambo chiyembekezo cha uthenga wabwino.’ Malinga ndi zimene kaguluko kanaphunzira mu ulosi wa Baibulo, iko kanasonya mtsogolo zaka zoposa 30 pasadakhale kuti 1914 ndiye mapeto a “nthaŵi zawo za anthu akunja,” nyengo ya “nthaŵi zisanu ndi ziŵiri,” kapena zaka 2,520, zimene zinayamba pa chiwonongeko cha Yerusalemu mu 607 B.C.E. (Luka 21:24; Danieli 4:16) Mogwirizana ndi zimene anayembekezera, 1914 inakhaladi posinthira zinthu m’zochita za munthu padziko lapansi. Ngakhalenso kumwamba kunachitika zinthu zazikulu. Panthaŵiyo mpamene Mfumu yamuyaya inakhazika Yesu Kristu, Mfumu yake yachiŵiri kwa iye, pa mpando wachifumu kumwamba, kukonzekera kudzasesa kuipa konse pankhope ya dziko lapansi ndi kukhazikitsanso Paradaiso.​—Salmo 2:6, 8, 9; 110:1, 2, 5.

Taonani Mfumu Yaumesiya!

4. Kodi ndi motani mmene Yesu anachitira mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lakelo Mikayeli?

4 Mu 1914 Yesu, Mfumu Yaumesiyayo, anayamba kuchitapo kanthu. M’Baibulo amatchedwanso Mikayeli, kutanthauza kuti “Ndani Ali Ngati Mulungu?,” popeza kuti ali wofunitsitsa kutsimikiziritsa uchifumu wa Yehova. Monga momwe kwalembedwera pa Chivumbulutso 12:7-12, mtumwi Yohane anafotokoza m’masomphenya zimene zinali kudzachitika: “Munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjokanso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezekanso malo awo m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.” Kunalidi kugwa kwakukulu kumeneko!

5, 6. (a) Itayamba 1914, kodi ndi chilengezo chiti chosangalatsa chimene chinaperekedwa kuchokera kumwamba? (b) Kodi Mateyu 24:3-13 akugwirizana motani ndi zimenezi?

5 Pamenepo mawu amphamvu anamveka kumwamba akumalengeza kuti: “Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku. Ndipo iwo [Akristu okhulupirika] anamlaka iye chifukwa cha mwazi wa Mwanawankhosa [Kristu Yesu], ndi chifukwa cha mawu a umboni wawo; ndipo sanakonda moyo wawo kungakhale kufikira imfa.” Zimenezi zikutanthauza chilanditso kwa osunga umphumphu, amene asonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya dipo ya Yesu yamtengo wapatali.​—Miyambo 10:2; 2 Petro 2:9.

6 Mawu aakuluwo kumwamba anapitiriza kulengeza kuti: “Chifukwa chake, kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” “Tsoka” limenelo loloseredwa padziko lapansili laonekera m’nkhondo zadziko, njala, miliri, zivomezi, ndi kusaweruzika kumene kwasakaza dziko lapansi m’zaka za zana lino. Malinga ndi Mateyu 24:3-13, Yesu ananeneratu kuti zimenezi zidzakhala mbali ya ‘chizindikiro cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.’ Mogwirizana ndi ulosiwo, anthu chiyambire 1914 aona masoka padziko lapansi amene sanachitikepo m’mbiri yonse ya anthu yapitayo.

7. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimalalikira mwachangu?

7 M’nyengo ino ya masoka ausatana, kodi anthu angapeze chiyembekezo cha mtsogolo? Ndithudi, pakuti Mateyu 12:21 amati ponena za Yesu: “Ndipo akunja [adzayembekeza, NW] dzina lake”! Mikhalidwe yosautsa imene ili pakati pa mitundu simangosonyeza ‘chizindikiro cha mathedwe a nthaŵi ya pansi pano’ komanso ‘chizindikiro cha [kukhalapo, NW] kwa Yesu’ monga Mfumu yakumwamba ya Ufumu Waumesiya. Ponena za Ufumuwo, Yesu akunenanso kuti: “Uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi, ukhale umboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” (Mateyu 24:14) Kodi ndi anthu okha ati padziko lapansi lerolino amene akulalikira za chiyembekezo chabwino cha ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu? Mboni za Yehova! Mwachangu, iwo amalalikira poyera ndi kunyumba ndi nyumba kuti Ufumu wa Mulungu wolungama ndi wamtendere uli pafupi kuyamba kuyendetsa zinthu padziko lapansi. Kodi mukuchita nawo utumiki umenewu? Simungakhale ndi mwaŵi wina woposa umenewu!​—2 Timoteo 4:2, 5.

Kodi “Chimaliziro” Chidzafika Motani?

8, 9. (a) Kodi chiweruzo chinayambira motani “panyumba ya Mulungu”? (b) Kodi Dziko Lachikristu laswa motani Mawu a Mulungu?

8 Anthu aloŵa m’nyengo ya chiweruzo. Tikuuzidwa pa 1 Petro 4:17 kuti chiweruzo chinayambira “panyumba ya Mulungu”​—chiweruzo cha magulu odzitcha achikristu chimene chakhala chikuchitika chiyambire pamene “masiku otsiriza” anayamba ndi kupha kwa m’Nkhondo Yadziko I mu 1914-18. Kodi Dziko Lachikristu lachita motani pa chiweruzo chimenechi? Eya, talingalirani kaimidwe ka matchalitchi pakuchirikiza nkhondo chiyambire 1914. Kodi atsogoleri achipembedzo sali okhathamira ndi “mwazi wa miyoyo ya aumphaŵi osachimwa” amene anawalalikira kuti apite kunkhondo?​—Yeremiya 2:34.

9 Malinga ndi Mateyu 26:52, Yesu anati: “Onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” Zimenezi zachitikadi m’nkhondo za m’zaka za zana lino! Atsogoleri achipembedzo asonkhezera anyamata kuti apululutse anyamata ena, ngakhale a m’chipembedzo chawo​—Akatolika kupha Akatolika ndi Aprotesitanti kupha Aprotesitanti. Utundu wakwezedwa pamwamba kuposa Mulungu ndi Kristu. Posachedwapa, m’mitundu ina ya mu Afirika, ubale waufuko waikidwa patsogolo pa mapulinsipulo a Baibulo. Ku Rwanda, kumene anthu ochuluka ndi Akatolika, anthu osachepera theka la miliyoni anaphedwa m’chiwawa cha mafuko. Papa anavomereza m’nyuzipepala ya Vatican ya L’Osservatore Romano kuti: “Kumeneku ndi kupululutsana kwenikweni kwa mafuko, kumene mwatsoka ngakhale Akatolika omwe alimo ndi mbali.”​—Yesaya 59:2, 3; Mika 4:3, 5.

10. Kodi ndi chiweruzo chotani chimene Yehova adzapereka pa chipembedzo chonyenga?

10 Kodi Mfumu yamuyaya imaona motani zipembedzo zimene zimalimbikitsa anthu kuphana kapena zimene zimangopenya pamene nkhosa zawo zikupha zinzake? Ponena za Babulo Wamkulu, gulu la padziko lonse la chipembedzo chonyenga, Chivumbulutso 18:21, 24 chimatiuza kuti: “Mngelo wolimba ananyamula mwala, ngati mphero yaikulu, naiponya m’nyanja, nanena, Chotero Babulo, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse. Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.”

11. Kodi ndi zonyansa ziti zimene zakhala zikuchitika m’Dziko Lachikristu?

11 Kukwaniritsa ulosi wa Baibulo, zinthu zonyansa zakhala zikuchitika m’Dziko Lachikristu. (Yerekezerani ndi Yeremiya 5:30, 31; 23:14.) Makamaka chifukwa cha mkhalidwe wolekerera zinthu wa atsogoleri achipembedzo, nkhosa zawo zadzala kuipa kokhakokha. Ku United States, mtundu umene amati ndi wachikristu, pafupifupi theka la maukwati onse amathera m’chisudzulo. Mimba za atsikana ndi mathanyula zili zofala pakati pa anthu a tchalitchi. Ansembe akugona ana​—osatinso kangapo chabe. Zamveka kuti malipiro olamulidwa ndi makhoti a milandu imeneyi akhoza kutayitsa Tchalitchi cha Katolika ku United States madola zikwi mamiliyoni ambiri pazaka khumi. Dziko Lachikristu lanyalanyaza chenjezo la mtumwi Paulo pa 1 Akorinto 6:9, 10: “Kapena simudziŵa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasocheretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa ufumu wa Mulungu.”

12. (a) Kodi Mfumu yamuyaya idzachitapo kanthu motani pa Babulo Wamkulu? (b) Mosiyana ndi Dziko Lachikristu, kodi ndi pachifukwa chiti chimene anthu a Mulungu adzaimbira nyimbo za “Haleluya”?

12 Posachedwapa, Mfumu yamuyayayo, Yehova, ikumachitapo kanthu mwa Kazembe wake wa Nkhondo wakumwamba, Kristu Yesu, idzatsegulira chisautso chachikulu. Choyamba, Dziko Lachikristu ndi mbali zina zonse za Babulo Wamkulu zidzalandira chilango cha chiweruzo cha Yehova. (Chivumbulutso 17:16, 17) Iwo asonyeza kuti sayenera chipulumutso chimene Yehova wapereka mwa nsembe ya dipo ya Yesu. Iwo achitira mwano dzina loyera la Mulungu. (Yerekezerani ndi Ezekieli 39:7.) Ha, ndi kutonyola kotani nanga kumene iwo amachita pamene aimba kuti “Haleluya” m’matchalitchi awo omangidwa mochititsa kaso! Iwo amachotsa dzina lamtengo wapatali la Yehova m’Mabaibulo amene iwo amatembenuza namachita ngati sakuona kuti “Haleluya” amatanthauza kuti “Tamandani Ya”​—“Ya” kukhala chidule cha “Yehova.” Moyenerera, Chivumbulutso 19:1-6 chili ndi nyimbo za “Haleluya” zoimbidwa kukondwerera chiweruzo cha Mulungu choperekedwa pa Babulo Wamkulu.

13, 14. (a) Kodi ndi zochitika zazikulu ziti zimene zikutsatira? (b) Kodi padzakhala zotulukapo zotani zokondweretsa kwa anthu owopa Mulungu?

13 Chimene chidzatsatira ndicho ‘kudza’ kwa Yesu kudzalengeza ndi kupereka chiweruzo pa mitundu ndi anthu. Iye yekha analosera kuti: “Pamene Mwana wa munthu [Kristu Yesu] adzadza mu ulemerero wake, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo iye adzakhala pa chimpando [choweruzira] cha kuŵala kwake: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse [padziko lapansi]; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi; nadzakhalitsa nkhosa kudzanja lake lamanja, koma mbuzi kulamanzere. Pomwepo mfumuyo idzanena kwa iwo akudzanja lake lamanja, Idzani kuno inu odalitsika a Atate wanga, loŵani mu ufumu wokonzedwera kwa inu pa chikhazikiro chake cha dziko lapansi.” (Mateyu 25:31-34) Vesi 46 likupitiriza kufotokoza kuti a gulu la mbuzi “adzachoka kumka ku chilango cha nthaŵi zonse; koma olungama ku moyo wa nthaŵi zonse.”

14 Buku la Baibulo la Chivumbulutso limafotokoza mmene “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,” Ambuye wathu wakumwamba, Yesu Kristu, adzaloŵera m’nkhondo panthaŵiyo ya Armagedo, akumawononga magulu onse andale ndi amalonda a dongosolo la Satana. Motero Kristu adzakhala atatsanulira “ukali wa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse” pa ufumu wonse wa padziko lapansi wa Satana. Pamene ‘zoyambazi zipita,’ anthu owopa Mulungu adzaloŵetsedwa m’dziko latsopano laulemerero mmene Mulungu “adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo.”​—Chivumbulutso 19:11-16; 21:3-5.

Nthaŵi ya Kutamanda Ya

15, 16. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kwa ife kulabadira mawu a Yehova aulosi? (b) Kodi aneneri ndi atumwi amasonyeza kuti tiyenera kuchitanji kuti tipulumuke, ndipo zimenezi zingatanthauzenji lerolino kwa namtindi wa anthu?

15 Tsikulo la kupereka chiweruzo layandikira! Chotero, tikuchita bwino kulabadira mawu aulosi a Mfumu yamuyaya. Kwa aja omwe ali omangikabe ndi ziphunzitso ndi miyambo ya chipembedzo chonyenga, mawu akumwamba akulengeza kuti: “Tulukani mmenemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake.” Koma kodi othaŵawo ayenera kupita kuti? Pali choonadi chimodzi chabe, nchifukwa chake pali chipembedzo chimodzi chokha choona. (Chivumbulutso 18:4; Yohane 8:31, 32; 14:6; 17:3) Kuti tipeze moyo wamuyaya zimadalira pa kupeza chipembedzocho ndi kumvera Mulungu wake. Baibulo limatiuza za iye pa Salmo 83:18, lomwe limati: “Inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wam’mwambamwamba padziko lonse lapansi.”

16 Komabe, tifunikira kuchita zambiri kuposa kungodziŵa dzina la Mfumu yamuyaya. Tifunikira kuphunzira Baibulo ndi kudziŵa mikhalidwe yake yaikulu ndi zifuno zake. Ndiyeno tifunikira kuchita chifuniro chake cha panthaŵi ino, monga momwe Aroma 10:9-13 amanenera. Mtumwi Paulo anagwira mawu aneneri ouziridwa nati: “Amene aliyense adzaitana pa dzina la [Yehova, NW] adzapulumuka.” (Yoweli 2:32; Zefaniya 3:9) Kupulumuka? Inde, pakuti namtindi wa anthu omwe lerolino amasonyeza chikhulupiriro m’makonzedwe a Yehova a dipo mwa Kristu adzalanditsidwa pa chisautso chachikulu chikudzacho, pamene chiweruzo chidzaperekedwa padziko loipa la Satana.​—Chivumbulutso 7:9, 10, 14.

17. Kodi ndi chiyembekezo chiti chabwino kwambiri chimene chiyenera kutisonkhezera kutsagana nawo kuimba nyimbo ya Mose ndi ya Mwanawankhosa?

17 Kodi chifuniro cha Mulungu nchotani kwa awo oyembekezera kupulumuka? Nchakuti titengemo mbali ngakhale tsopano m’kuimba nyimbo ya Mose ndi ya Mwanawankhosa, kutamanda Mfumu yamuyaya poyembekezera chilakiko chake. Timachita zimenezi mwa kuuza ena za zifuno zake zaulemerero. Pamene chidziŵitso chathu cha Baibulo chikula, timapatulira moyo wathu kwa Mfumu yamuyaya. Zimenezi zidzachititsa kuti tidzakhale ku umuyaya wonse m’kakonzedwe kamene Mfumu yamphamvu imeneyi ikufotokoza, kopezeka pa Yesaya 65:17, 18: “Pakuti taonani, ndilenga kumwamba kwatsopano [Ufumu Waumesiya wa Yesu] ndi dziko lapansi latsopano [chitaganya chatsopano cha anthu olungama]; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kuloŵa mumtima. Koma khalani inu okondwa ndi kusangalala ku nthaŵi zonse ndi ichi ndichilenga.”

18, 19. (a) Kodi mawu a Davide m’Salmo 145 ayenera kutisonkhezera kuchitanji? (b) Kodi nchiyani chimene ife mwachidaliro tingayembekezere kwa Yehova?

18 Wamasalmo Davide anafotokoza Mfumu yamuyayayo m’mawu awa: “Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ndi ukulu wake ngwosasanthulika.” (Salmo 145:3) Ukulu wake ngwosasanthulikadi monga malekezero a mlengalenga ndi umuyaya! (Aroma 11:33) Pamene tikupitiriza kuloŵetsa chidziŵitso cha Mlengi wathu ndi makonzedwe ake a dipo mwa Mwana wake, Kristu Yesu, tidzafunikira kutamanda kwambiri Mfumu yathu yamuyaya. Tidzafunikira kuchita zimene Salmo 145:11-13 likunena: “Adzanenera ulemerero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu; kudziŵitsa ana a anthu zamphamvu zake, ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake. Ufumu wanu ndiwo ufumu womka muyaya, ndi kuweruza kwanu kufikira mibadwo yonseyonse.”

19 Tingayembekezere ndi chidaliro kuti Mulungu wathu adzakwaniritsa chilengezo chakuti: “Muoloŵetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” Mfumu yamuyaya idzatitsogoza mokoma mtima mpaka ku mapeto a masiku ano otsiriza, pakuti Davide anatilonjeza kuti: “Yehova asunga onse akukondana naye; koma oipa onse adzawawononga.”​—Salmo 145:16, 20.

20. Kodi mukulabadira motani chiitano cha Mfumu yamuyaya, choperekedwa m’masalmo asanu omalizira?

20 Lililonse la masalmo asanu omalizira m’Baibulo limayamba ndi kutha ndi chiitano chakuti “Haleluya.” Chotero, Salmo 146 likutiitanira kuti: “Haleluya [“Tamandani Ya, anthu inu!” NW]; ulemekeze Yehova, moyo wanga. Ndidzalemekeza Yehova m’moyo mwanga; ndidzaimbira zolemekeza Mulungu wanga pokhala ndi moyo ine.” Kodi mudzalabadira chiitanocho? Ndithudi mufunikira kumtamanda iye! Mukhaletu pakati pa aja onenedwa pa Salmo 148:12, 13 kuti: “Anyamata ndiponso anamwali; okalamba pamodzi ndi ana: alemekeze dzina la Yehova; pakuti dzina lake lokha ndi lokwezeka; ulemerero wake uli pamwamba pa dziko lapansi ndi thambo.” Tiyeni tilabadire ndi mtima wonse chiitano chakuti: “Tamandani Ya, anthu inu!” Mogwirizana, tiyeni titamande Mfumu yamuyaya!

Kodi Mukutipo Bwanji?

◻ Kodi atumwi a Yesu anachenjezeratu za chiyani?

◻ Chiyambire 1914, kodi ndi zochitika zazikulu zotani zimene zakhalapo?

◻ Kodi ndi ziweruzo zotani zimene Yehova ali pafupi kupereka?

◻ Kodi nchifukwa ninji ino ndiyo nthaŵi ya nthaŵi zonse ya kutamanda Mfumu yamuyaya?

[Bokosi patsamba 19]

Nyengo Ino ya Masoka ndi ya Chipwirikiti

Ambiri avomereza kuti nyengo yachipwirikiti inayamba kuchiyambi kwa zaka za zana la 20. Mwachitsanzo, m’mawu oyamba a buku lakuti Pandaemonium, lolembedwa ndi Phungu wa m’Nyumba ya Malamulo ya United States Daniel Patrick Moynihan, lofalitsidwa mu 1993, mawu onena za “tsoka la 1914” amati: “Nkhondo inafika ndipo dziko linasintha​—kusinthiratu. Lerolino pali maboma asanu ndi atatu okha padziko lapansi amene analiko mu 1914 ndi amenenso mtundu wa boma lawo sunasinthidwe ndi chiwawa chiyambire nthaŵiyo. . . . Pa maboma enawo pafupifupi 170 omwe alipo, ena apangidwa dzulodzuloli kwakuti sanaonepo chipwirikiti chochuluka chaposachedwapa.” Ndithudi, nyengo yokhalako chiyambire 1914 yaona masoka ambirimbiri!

Buku lina limenenso linafalitsidwa mu 1993 nlakuti Out of Control​—Global Turmoil on the Eve of the Twenty-First Century. Mlembi wake ndi Zbigniew Brzezinski, amene anali mkulu wa National Security Council ya United States. Iye analemba kuti: “Chiyambi cha zaka za zana la makumi aŵiri chinathokozedwa m’ndemanga zambiri monga chiyambi chenicheni cha Nyengo ya Nzeru. . . . Mosiyana ndi zimene zinalonjeza, zaka za zana la makumi aŵiri zakhala zaka zokhetsa mwazi kwenikweni ndi zodzala ndi udani, zaka za ndale zachinyengo ndi za kuphana kwauchinyama. Nkhanza inachitika mwadongosolo pamlingo umene sunachitikepo, kupha anthu ochuluka nthaŵi imodzi kunachitika molinganizidwa pamlingo waukulu koposa. Kusiyana kwa mphamvu ya sayansi yakuchita zabwino ndi kuipa kwa ndale kumene kwenikweni kunatulukapo nkowopsa. M’mbiri yonse yakale kuphana sikunakhalepo kofala kwambiri motero padziko lonse, sikunawonongepo miyoyo yambiri motero, kupululutsa anthu sikunachitikepo mwakhama chotero kaamba ka zonulirapo zopanda pake ndi zodzikuza.” Zimenezotu nzoonadi!

[Chithunzi patsamba 17]

Mikayeli anaponya Satana ndi magulu ake kudziko lapansi Ufumu uthakazikitsidwa mu 1914

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena