Tamandani Mfumu Yamuyaya!
“Yehova ndiye Mfumu ku nthaŵi yamuyaya.”—SALMO 10:16.
1. Kodi pakubuka mafunso otani ponena za umuyaya?
UMUYAYA—kodi inu mumaganiza kuti ndiwo chiyani? Kodi muganiza kuti nthaŵi ingapitirizedi kwamuyaya? Chabwino, sitikayikira konse kuti nthaŵi imamka muyaya kupita kumbuyo. Chotero ingalekerenji kumka muyaya kupita kutsogolo? Inde, Baibulo la New World Translation limatchula kuti Mulungu adzatamandidwa “kuyambira nthaŵi yosadziŵika ndi kufika ku nthaŵi yosadziŵika.” (Salmo 41:13) Kodi mawu ameneŵa amatanthauzanji? Tingathandizidwe kuwamvetsa ngati tingapende nkhani yofanana—mlengalenga.
2, 3. (a) Kodi ndi mafunso ati amene akukhudza mlengalenga, akumatithandiza kuzindikira umuyaya? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kulambira Mfumu yamuyaya?
2 Kodi mlengalenga ngwaukulu motani? Kodi uli ndi malire alionse? Kuyambira kale mpaka zaka 400 zapitazo, anthu ankalingalira kuti dziko lathu lapansi linali pakati pa chilengedwe chonse. Ndiyeno Galileo anapanga telesikopo, akumapereka mpata wakuti mbali yaikulu ya miyamba izionedwa. Panthaŵiyo Galileo anakhoza kuona nyenyezi zambiri ndipo anakhoza kusonyeza kuti dziko lapansi ndi mapulaneti ena amazungulira dzuŵa. Mlalang’amba wa Milky Way sunalinso wachimbuuzi. Unapezeka kukhala mlalang’amba wa nyenyezi, pafupifupi mamiliyoni zikwi zana limodzi. Sititha kuŵerenga nyenyezi zochuluka motero imodziimodzi, ngakhale m’moyo wathu wonse. Pambuyo pake, openda zakuthambo anapezabe milalang’amba ina mamiliyoni zikwi zambiri. Zimenezi zimamka muyaya m’mlengalenga, kufikira pamene matelesikopo amphamvu koposa atha kufika. Zikuoneka kuti mlengalenga ulibe malire. Ndi mmenenso umuyaya wakhalira—ulibe malire.
3 Maubongo athu aumunthu okhala ndi malire satha kulimvetsa lingaliro la umuyaya. Komabe, alipo Wina amene amalimvetsetsa. Iye atha kuŵerenga, inde, ngakhale kutcha maina, miyandamiyanda yosaŵerengeka ya nyenyezi m’milalang’amba mamiliyoni zikwi zambiri! Iyeyo amati: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, Amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse maina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka. Kodi iwe sunadziŵe? Kodi sunamve? Mulungu wachikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zake sizisanthulika.” (Yesaya 40:26, 28) Iye ali Mulungu wodabwitsadi! Kunena zoona, iye ndiye Mulungu amene tiyenera kulambira!
“Mfumu ku Nthaŵi Yomka Yamuyaya”
4. (a) Kodi Davide anasonyeza motani chiyamikiro kwa Mfumu yamuyaya? (b) Kodi mmodzi wa asayansi otchuka kwambiri m’mbiri ananenanji pa magwero a chilengedwe chonse?
4 Pa Salmo 10:16, Davide akunena za Mlengiyo, Mulungu kuti: “Yehova ndiye Mfumu ku nthaŵi yamuyaya.” Ndipo pa Salmo 29:10, iye akubwereza mawuwo kuti: “Yehova akhala mfumu ku nthaŵi yomka muyaya.” Inde, Yehova ndiye Mfumu yamuyaya! Ndiponso, Davide akupereka umboni wakuti Mfumu yokwezeka imeneyi ndiyo Mlinganizi ndi Mpangi wa zonse zomwe tiona m’mlengalenga, akumati pa Salmo 19:1: “Zakumwamba zimalalikira ulemerero wa Mulungu; ndipo thambo lionetsa ntchito ya manja ake.” Patapita zaka pafupifupi 2,700, wasayansi womveka Sir Isaac Newton anavomereza zimene Davide ananena, akumalemba kuti: “Dongosolo limeneli lapamwamba koposa la madzuŵa, mapulaneti ndi nyenyezi zamchira liyenera kuti linakhalako mwa chifuno ndi uchifumu wa munthu wina wamphamvu ndi wanzeru.”
5. Kodi Yesaya ndi Paulo analembanji ponena za Magwero a nzeru?
5 Kuyenera kutichepetsa chotani nanga kudziŵa kuti Ambuye Mfumu Yehova, amene ngakhale ‘thambo ndi m’mwambamwamba motakata zichepa kumulandira,’ ali wamuyaya! (1 Mafumu 8:27) Yehova, wofotokozedwa pa Yesaya 45:18 kukhala “amene analenga kumwamba, . . . amene anaumba dziko lapansi, nalipanga,” ndiye Magwero a nzeru yopambana kwenikweni imene maubongo omafa aumunthu satha kuzindikira. Yehova anati, monga momwe 1 Akorinto 1:19 ikusonyezera: “Ndidzawononga nzeru za anzeru, ndi kuchenjera kwa ochenjera ndidzakutha.” Pa zimenezi, mtumwi Paulo anawonjezapo m’vesi 20 kuti: “Ali kuti wanzeru? Mlembi ali kuti? Ali kuti wotsutsana wa nthaŵi ya pansi pano? Kodi Mulungu sanaipusitsa nzeru ya dziko lapansi?” Inde, malinga ndi zimene Paulo anapitiriza kunena, pa chaputala 3, vesi 19, “nzeru ya dziko lino lapansi ili yopusa kwa Mulungu.”
6. Kodi Mlaliki 3:11 amasonyezanji ponena za “zamuyaya”?
6 Zinthu zakuthambo zili mbali ya chilengedwe chimene Mfumu Solomo anatchula kuti: “Chinthu chilichonse [Mulungu] anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.” (Mlaliki 3:11) Ndithudi, chikhumbo chinaikidwa mumtima wa munthu chakuti apeze tanthauzo la “zamuyaya,” ndiko kuti, umuyaya. Koma kodi iye angachipeze nkomwe chidziŵitso chotero?
Chiyembekezo cha Moyo Chabwino Koposa
7, 8. (a) Kodi ndi chiyembekezo cha moyo chiti chabwino koposa chimene chili mtsogolo mwa anthu, ndipo angachipeze motani? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukondwa kuti maphunziro aumulungu adzapitiriza ku umuyaya wonse?
7 M’pemphero lake kwa Yehova Yesu Kristu anati: “Moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziŵe inu Mulungu woona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.” (Yohane 17:3) Kodi chidziŵitso chotero tingachipeze motani? Tifunikira kuphunzira Mawu a Mulungu, Baibulo Lopatulika. Mwanjira imeneyo tingapeze chidziŵitso cholongosoka cha zifuno zazikulu za Mulungu, kuphatikizapo makonzedwe opangidwa mwa Mwana wake a moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Umenewo udzakhala “moyo weniweniwo” wotchulidwa pa 1 Timoteo 6:19. Udzagwirizana ndi chimene Aefeso 3:11 amafotokoza kukhala “[chifuno chomka muyaya, NW] chimene [Mulungu] anachita mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”
8 Inde, ife anthu ochimwa tingapeze moyo wosatha mwa maphunziro aumulungu ndi chikhulupiriro m’nsembe ya dipo ya Yesu. Kodi maphunziro ameneŵa adzapitiriza kufikira liti? Adzapitiriza ku umuyaya wonse pamene anthu adzaphunzitsidwa pang’onopang’ono nzeru ya Mlengi wathu. Nzeru ya Yehova ilibe malire. Pozindikira zimenezi, mtumwi Paulo anadzuma kuti: “Ha! Kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake nzosalondoleka!” (Aroma 11:33) Indetu, nkoyenera kuti 1 Timoteo 1:17 amatcha Yehova “Mfumu yosatha”!
Nzeru ya Kulenga ya Yehova
9, 10. (a) Kodi ndi ntchito zazikulu ziti zimene Yehova anachita pokonza dziko lapansi monga mphatso yake kwa anthu? (b) Kodi nzeru yopambana ya Yehova imasonyezedwa motani ndi zolengedwa zake? (Onani bokosi.)
9 Talingalirani choloŵa chokongola koposa chimene Mfumu yamuyaya yapereka kwa anthufe. Salmo 115:16 limatiuza kuti: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” Kodi simukuganiza kuti dziko lili choikizira chabwino kopambana? Ntheradi! Ndipo timayamikira kwambiri chotani nanga kuoneratu patali kwapadera kwa Mlengi wathu pokonza dziko lapansi monga mudzi wathu!—Salmo 107:8.
10 Zinthu zodabwitsa kwambiri zinachitika padziko lapansi mu “masiku” asanu ndi limodzi akulenga a mu Genesis chaputala 1, tsiku lililonse likumatenga zaka zikwi zambiri. Potsirizira pake, ntchito za kulenga za Mulungu zimenezi zinali kudzakuta dziko lapansi ndi udzu wobiriŵira wogudira bwino, nkhalango zokongola ndi maluŵa amaonekedwe abwino. Linali kudzadzala ndi zamoyo zambirimbiri za m’nyanja zochititsa kaso, magulu a mbalame zokongola, ndi nyama zochuluka zamitundumitundu zoŵeta ndi zakuthengo, zonse zomaswana “monga mwa mitundu yawo.” Pambuyo pofotokoza za kulengedwa kwa mwamuna ndi mkazi, Genesis 1:31 amasimba kuti: “Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu.” Ha, ndi malo osangalatsa chotani nanga amene anazinga anthu oyamba aja! Kodi sititha kuona nzeru, kuoneratu patali, ndi chisamaliro cha Mlengi wachikondi m’zolengedwa zonsezi?—Yesaya 45:11, 12, 18.
11. Kodi Solomo anaikuza motani nzeru ya kulenga ya Yehova?
11 Munthu wina amene anachita chidwi kwambiri ndi nzeru ya Mfumu yamuyaya anali Solomo. Iye mobwerezabwereza anatchula nzeru ya Mlengi. (Miyambo 1:1, 2; 2:1, 6; 3:13-18) Solomo akutitsimikizira kuti “dziko lingokhalabe masiku onse.” Iye anayamikira zodabwitsa zambiri za chilengedwe, kuphatikizapo ntchito ya mitambo ya mvula pa kutsitsimula dziko lathu lapansi. Chotero, iye analemba kuti: “Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.” (Mlaliki 1:4, 7) Ndi mmene zimakhalira kuti pamene mvula ndi mitsinje yatsitsimula dziko lapansi, madzi ake amatengedwa kuchoka m’nyanja kubwereranso m’mitambo. Kodi dziko lapansili likanakhala lotani, ndipo tikanakhala kuti, popanda kuyeretsedwa ndi kubwezeretsedwa kwa madzi kumeneku?
12, 13. Kodi tingasonyeze motani chiyamikiro kaamba ka chilengedwe cha Mulungu?
12 Kuyamikira kwathu zamoyo ndi malo ake okhala kuyenera kuchirikizidwa ndi ntchito, monga momwe Mfumu Solomo ananenera m’mawu omaliza a Mlaliki kuti: “Mawu atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, [n]usunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi. Pakuti Mulungu adzanena mlandu wa zochita zonse, ndi zobisika zonse, ngakhale zabwino ngakhale zoipa.” (Mlaliki 12:13, 14) Tiyenera kuwopa kuchita kanthu kalikonse kosakondweretsa Mulungu. M’malo mwake, tiyenera kuyesayesa kumumvera ndi mantha aulemu.
13 Inde, tiyenera kutamanda Mfumu yamuyaya kaamba ka ntchito zake zodabwitsa za chilengedwe! Salmo 104:24 limati: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.” Mwachimwemwe, tiyeni tigwirizane ndi vesi lomaliza la salmo limeneli mwa kunena kwa ife eni ndi ena kuti: “Yamika Yehova, moyo wanga. Haleluya.”
Cholengedwa Chopambana cha Padziko Lapansi
14. Kodi cholengedwa chaumunthu cha Mulungu chimapambaniratu nyama motani?
14 Chilengedwe chonse cha Yehova chinapangidwa mwaukatswiri. Koma cholengedwa cha padziko lapansi chodabwitsa koposa ndife—anthufe. Adamu ndiyeno Hava, anali zolengedwa zomaliza patsiku lakulenga la Yehova lachisanu ndi chimodzi—zolengedwa zapamwamba kwambiri kuposa nsomba, mbalame, ndi zinyama! Pamene zambiri za zimenezi zili ndi nzeru yachibadwa, anthu ali ndi mphamvu ya kulingalira, chikumbumtima chimene chikhoza kusiyanitsa chabwino ndi choipa, nzeru ya kukonzekera za mtsogolo, ndi chikhumbo chachibadwa cha kulambira. Kodi zonsezi zinachitika motani? M’malo mwa kusandulika kuchokera ku zilombo zosalingalira, munthu analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. Chifukwa chake, munthu ndiye yekha amene akhoza kusonyeza mikhalidwe ya Mlengi wathu, amene anadzidziŵikitsa kukhala “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi waukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.”—Eksodo 34:6.
15. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kutamanda Yehova modzichepetsa?
15 Tiyeni timtamande ndi kumthokoza Yehova kaamba ka mmene anapangira matupi athu modabwitsa. Mwazi wathu, wofunika kwambiri pa moyo, umazungulira m’thupi lonse pamasekondi 60 alionse. Monga momwe Deuteronomo 12:23 amanenera, “mwazi ndiwo moyo”—moyo wathu—wamtengo wapatali kwa Mulungu. Mafupa olimba, minofu yofeŵa, ndi minyewa yatcheru yonyamula mauthenga, zili ndi ubongo pamwamba pake woposeratu ubongo uliwonse wa nyama, ndipo uli ndi mphamvu yaikulu kuposeratu mphamvu imene kompyuta yaikulu ngati nyumba yaitali yosanja ingakhale nayo. Kodi zimenezi sizimakuchititsani kudzichepetsa? Ziyeneradi kutero. (Miyambo 22:4) Ndipo talingaliraninso izi: Mapapu athu, kholingo, lilime, mano, ndi kamwa zimagwirira ntchito pamodzi kutulutsa mawu m’chilichonse cha zinenero zikwi zambiri. Davide anaimbira Yehova nyimbo yoyenera, kuti: “Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.” (Salmo 139:14) Tiyeni tigwirizane ndi Davide pa kutamanda Yehova mwachiyamiko, Mlinganizi wathu wodabwitsa ndi Mulungu wathu!
16. Kodi ndi nyimbo yotani imene woimba nyimbo wotchuka analemba kutamanda Yehova, ndipo ndi pempho losonkhezera liti limene tiyenera kulabadira?
16 Buku la nyimbo za m’zaka za zana la 18 lolembedwa ndi Joseph Haydn limati potamanda Yehova: “Myamikeni Iye, inu ntchito Zake zonse zodabwitsa! Imbani ulemu Wake, imbani ulemerero Wake, dalitsani Dzina Lake ndi kulikuza! Chitamando cha Yehova chikhala kosatha, Amen, Amen!” Ndipo oposa kukoma kwake ndi mawu ouziridwa obwerezedwabwerezedwa m’Masalmo, monga pempho loperekedwa kanayi m’Salmo 107:8, 15, 21, 31 lakuti: “Ayamike Yehova chifukwa cha chifundo chake, ndi zodabwitsa zake za kwa ana a anthu!” Kodi mumatengamo mbali m’chitamandocho? Muyenera kutero, pakuti Yehova, Mfumu yamuyaya, ndiye magwero a zinthu zonse zotizinga zokongolazo.
Akuchitabe Ntchito Zokulirapo
17. Kodi ‘nyimbo ya Mose ndi ya Mwanawankhosa’ imamkweza motani Yehova?
17 Pazaka zikwi zisanu ndi chimodzi zapitazo, Mfumu yamuyaya yachitabe ntchito zazikuludi. M’buku lomaliza la Baibulo, pa Chivumbulutso 15:3, 4, timaŵerenga za aja amene ali kumwamba amene alaka adani auchiŵanda kuti: “Aimba nyimbo ya Mose kapolo wa Mulungu, ndi nyimbo ya Mwanawankhosa, nanena, Ntchito zanu nzazikulu ndi zozizwitsa, [Yehova, NW] Mulungu, Wamphamvuyonse; njira zanu nzolungama ndi zoona, Mfumu inu ya nthaŵi zosatha. Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalemekeza dzina lanu [Yehova, NW]? Chifukwa inu nokha muli [wokhulupirika, NW]; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.” Kodi nchifukwa ninji imeneyi ikutchedwa ‘nyimbo ya Mose ndi ya Mwanawankhosa’? Tiyeni tione.
18. Kodi ndi ntchito yaikulu iti imene imakumbukika m’nyimbo ya mu Eksodo chaputala 15?
18 Zaka pafupifupi 3,500 zapitazo, pamene magulu a nkhondo amphamvu a Farao anawonongedwa pa Nyanja Yofiira, Aisrayeli moyamikira anatamanda Yehova ndi nyimbo. Timaŵerenga zotere pa Eksodo 15:1, 18: “Pamenepo Mose ndi ana a Israyeli anaimbira Yehova nyimbo iyi, nanena, ndi kuti, Ndidzaimbira Yehova pakuti wapambanatu; kavalo ndi wokwera wake anawaponya m’nyanja. Yehova adzachita ufumu nthaŵi yomka muyaya.” Zolungama za Mfumu yamuyaya imeneyi zinasonyezedwa pa kupereka kwake chiweruzo ndi chiwonongeko pa adani amene anapandukira uchifumu wake.
19, 20. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova anapanga mtundu wa Israyeli? (b) Kodi Mwanawankhosa ndi ena ayankha motani chinenezo cha Satana?
19 Kodi nchifukwa ninji zimenezi zinali zofunikira? Munali m’munda wa Edene pamene Njoka yochenjerayo inachititsa makolo athu oyamba kuchimwa. Zimenezi zinachititsa kupanda ungwiro kwauchimo kuyambukira anthu onse. Komabe, mwamsanga, Mfumu yamuyayayo inachitapo kanthu mogwirizana ndi chifuno chake choyambirira, zimene zidzachititsa adani ake onse kuchotsedwa padziko lapansi ndi kubwezeretsa mikhalidwe ya paradaiso. Mfumu yamuyaya inapanga mtundu wa Israyeli nipereka Chilamulo chake kuti ichitire chithunzi mmene idzakwanitsira zimenezo.—Agalatiya 3:24.
20 Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, Israyeli analoŵerera m’kusakhulupirika, ndipo mkhalidwe womvetsa chisoni umenewu unafika poipitsitsa pamene atsogoleri ake anapereka Mwana wobadwa yekha wa Mulungu kwa Aroma kuti amzunze mwankhalwe ndi kumupha. (Machitidwe 10:39; Afilipi 2:8) Komabe, umphumphu wa Yesu wofika ku imfa, monga “Mwanawankhosa wa Mulungu” wansembe, unatsutsiratu chinenezo chimene Mdani wakalekale wa Mulungu, Satana, anapereka—chakuti palibe munthu padziko lapansi amene angakhalebe wokhulupirika kwa Mulungu poyesedwa koŵaŵa. (Yohane 1:29, 36; Yobu 1:9-12; 27:5) Ngakhale kuti anthu ena mamiliyoni amene amawopa Mulungu ali ndi choloŵa cha kupanda ungwiro kuchokera kwa Adamu, iwo atsatira mapazi a Yesu mwa kusunga umphumphu poyang’anizana ndi ziukiro zausatana.—1 Petro 1:18, 19; 2:19, 21.
21. Mogwirizana ndi Machitidwe 17:29-31, kodi nchiyani chidzafotokozedwa m’nkhani yotsatira?
21 Tsopano lafika tsiku lakuti Yehova apereke mfupo kwa okhulupirikawo ndi kuweruza adani onse a choonadi ndi chilungamo. (Machitidwe 17:29-31) Kodi zimenezi zidzachitika motani? Nkhani yathu yotsatira idzasimba zimenezo.
Bokosi la Kubwereramo
◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova moyenerera akutchedwa ‘Mfumu yamuyaya’?
◻ Kodi nzeru ya Yehova imaoneka motani mwa zimene analenga?
◻ Kodi ndi motani mmene anthu alili olengedwa mwaukatswiri?
◻ Kodi ndi ntchito zotani zimene zimafuna ‘nyimbo ya Mose ndi ya Mwanawankhosa’?
[Bokosi patsamba 12]
Nzeru Yopambana ya Yehova
Nzeru ya Mfumu yamuyaya imaoneka mwanjira zosiyanasiyana m’ntchito zake padziko lapansi. Tamverani mawu a Aguri: “Mawu onse a Mulungu ali oyengeka; ndiye chikopa cha iwo amene amkhulupirira.” (Miyambo 30:5) Ndiyeno Aguri akutchula zolengedwa zambiri za Mulungu, zazikulu ndi zazing’ono. Mwachitsanzo, m’Proverbs 30 mavesi 24 mpaka 28, akufotokoza “zinayi zili zazing’ono padziko; koma zipambana kukhala zanzeru [“zili ndi nzeru yachibadwa,” NW].” Zimenezo ndizo nyerere, mbira, dzombe, ndi buluzi.
“Zili ndi nzeru yachibadwa”—inde, nyama zinalengedwa motero. Sizimalingalira pa zinthu monga amachitira anthu koma zimadalira pa nzeru yoikika. Kodi munayamba mwadabwapo ndi zimenezi? Izo zilidi zolengedwa zadongosolo kwambiri! Mwachitsanzo, nyerere nzolinganizidwa m’magulumagulu, okhala ndi mmanthu, antchito, ndi amuna. M’mitundu ina, nyerere zantchito zimaŵeta tizilombo timene timamwa madzi a zomera m’mafamu omwe zimamanga. Mmenemo zimakama tizilomboto pamene asilikali ake amapitikitsa adani alionse obwera. Miyambo 6:6 imapereka chilangizo ichi: “Pita kunyerere, wolesi iwe, penya njira zawo nuchenjere.” Kodi zitsanzo zotero siziyenera kutisonkhezera anthufe kukhala “akuchuluka mu ntchito ya Ambuye”?—1 Akorinto 15:58.
Munthu wapanga ndege zazikulu kwambiri. Komatu mbalame, kuphatikizapo ija ya hummingbird, imene kulemera kwake sikufika pa magalamu 30, nzokhoza kusintha mosavuta kuposa ndegezo! Ndege ya Boeing 747 iyenera kunyamula mafuta okwana malita 180,000, kuyendetsedwa ndi kagulu kophunzitsidwa, ndi kugwiritsira ntchito njira zocholoŵana zopimira maulukidwe kuti iyende ulendo wodutsa nyanja. Komabe, hummingbird yaing’onong’onoyo imadalira pa mafuta ake a m’thupi okwana galamu imodzi kuti iyende ulendo wonse kuchokera ku North America, kudutsa Gulf of Mexico, ndi kuloŵa mu South America. Siifunikira mtolo wolemera wa mafuta, siifunikira maphunziro a kaulukidwe, siifunikira matchati kapena makompyuta ocholoŵana! Kodi luso limeneli linakhalapo mwa ngozi ya chisinthiko? Kutalitali! Mbalame yaing’onong’onoyi ili ndi nzeru yachibadwa, yoikidwamo ndi Mlengi wake, Yehova Mulungu.
[Chithunzi patsamba 10]
Zolengedwa zamitundumitundu za ‘Mfumu yamuyaya’ zimakweza ulemerero wake
[Chithunzi patsamba 15]
Monga momwe Mose ndi Israyeli yense anakondwerera chilakiko cha Yehova pa Nyanja Yofiira, padzakhala chikondwerero chachikulu pambuyo pa Armagedo