Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w93 1/1 tsamba 3-5
  • Mlengi Wathu Wamkulu ndi Ntchito Zake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mlengi Wathu Wamkulu ndi Ntchito Zake
  • Nsanja ya Olonda—1993
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito Yaukatswiri ya Chilengedwe cha Mulungu
  • Kukoma Mtima Kwachikondi kwa Mlengi Wathu
  • Tamandani Mfumu Yamuyaya!
    Nsanja ya Olonda—1996
  • “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
    “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano”
  • Mlengi Aika Okhala pa “Chombo cha m’Mlengalenga Dziko Lapansi”
    Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
  • Kulinganizira Anthu Malo Okhala Achimwemwe
    Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1993
w93 1/1 tsamba 3-5

Mlengi Wathu Wamkulu ndi Ntchito Zake

NZAZIKULU CHOTANI NANGA! Mathithi ochita mabingu aku Iguaçú kapena aku Niagara, zigwa zakuya zaku Arizona kapena Hawaii, maphompho okongola aku Norway kapena New Zealand​—zodabwitsa za chilengedwe zimenezi zimachititsa mfuu zochititsa chidwi chotani nanga! Koma kodi izo zinakhalako mwa wotchedwa chotero kuti Amayi Chilengedwe? Ayi, izo ziri zoposa kwambiri zimenezo! Izo ziri ntchito zochititsa mantha za Mlengi Wamkulu, Atate wakumwamba wa chikondi amene Mfumu Solomo analemba za iye kuti: ‘Chinthu chirichonse anachikongoletsa pa mphindi yake; ndipo waika zamuyaya m’mitima yawo ndipo palibe munthu angalondetse ntchito Mulungu wazipanga chiyambire mpaka chitsiriziro.’ (Mlaliki 3:11) Ndithudi, kukatenga nthaŵi yamuyaya kuti anthu afufuze ntchito zonse zaulemerero zimene Mlengi wathu wadzaza m’chilengedwe chonse.

Tiri ndi Mlengi Wamkulu chotani nanga! Ndipo tiri okondwera chotani nanga kuti Mulungu Wamphamvuyonse ameneyu ‘pamapeto amasiku ano walankhula nafe kudzera mwa Mwana, amene wamuika woloŵa nyumba wa zinthu zonse, ndi kupyolera mwa amene anapanga madongosolo azinthu.’ (Ahebri 1:2) Mwana ameneyu, Yesu Kristu, anayamikira zinthu zabwino zolengedwa ndi Atate wake. Kaŵirikaŵiri iye anasonya kuzinthuzo pofotokoza mwafanizo zifuno za Atate wake ndi polankhula mawu olimbikitsa kwa omvetsera ake. (Mateyu 6:28-30; Yohane 4:35, 36) “Ndi chikhulupiriro” ambiri azindikira kuti zodabwitsa za chilengedwe ‘zinakonzedwa ndi mawu a Mulungu.’ (Ahebri 11:3) Miyoyo yathu ya tsiku ndi tsiku iyenera kusonyeza chikhulupiriro chotero.​—Yakobo 2:14, 26.

Ndithudi, zolengedwa za Mulungu wathu ziri zazikulu. Zimasonyeza modabwitsa nzeru yake, mphamvu yake, chilungamo chake, ndi chikondi chake. Mwachitsanzo, iye anapendamika dziko lathu lapansili nalichititsa kuyenda mozungulira dzuŵa kotero kuti cholengedwa chake chamtsogolo, munthu, chikakhoze kusangalala ndi zungulirezungulire wa nyengo. Mulungu anati: ‘Pakukhalabe masiku a dziko lapansi, nthaŵi yakubzala ndi yakukunkha, chisanu ndi mafundi, malimwe, ndi msakasa, usana ndi usiku sizidzalekayi.’ (Genesis 8:22) Ndiponso, Mulungu anayika m’nthaka ya dziko lathu lapansi miyala yamtengo wapatali yochuluka. Makamaka, iye anapereka madzi ambiri, amene pambuyo pake akakhala mbali yofunika ndi yochirikizira miyoyo ya zamoyo zonse za padziko lapansi.

M’kutsatizana kwake kwa dongosolo la ‘masiku akulenga’ asanu ndi limodzi, lirironse lokhala ndi utali wazaka zikwi zingapo, ‘mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu’ inapitirizabe kukonza dziko lapansi kuti lidzakhalidwe ndi munthu. Kuunika kumene timawona nako, mpweya umene timapuma, mtunda umene timakhalapo, zomera, kutsatizana kwa usana ndi usiku, nsomba, mbalame, zinyama​—zonsezo zinalengedwa motsatizanatsatizana ndi Mlengi wathu Wamkulu chifukwa cha ubwino ndi chisangalalo cha munthu. (Genesis 1:2-25) Ndithudi, tingathe kugwirizana ndi wamasalmo podzuma kuti: ‘Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.’​—Salmo 104:24.

Ntchito Yaukatswiri ya Chilengedwe cha Mulungu

Pamene “tsiku” lachisanu ndi chimodzi lakulenga linali pafupi kutha, Mulungu anapanga mwamuna ndiyeno womthandiza wake, mkazi. Anali matsirizidwe aukatswiri chotani nanga achilengedwe cha dziko lapansi, abwinodi kwambiri kuposa zolengedwa zakuthupi zonse zimene zidalengedwa kale! Salmo 115:16 limatiuza kuti: “Kunena za kumwamba, kumwamba ndiko kwa Yehova; Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.” Mogwirizana ndi zimenezi, Yehova analinganiza anthufe kotero kuti tikakhoze kupeza ponse paŵiri chikondwerero ndi kugwiritsira ntchito zimene analenga poyambirira za padziko lapansi. Tiyenera kukhala othokoza chotani nanga kaamba ka maso athu​—ocholoŵana kwambiri kuposa kamera yabwino kopambana​—amene akhoza kuwona zinthu zotizinga zamawonekedwe amitundumitundu okongola! Tiri ndi makutu athu​—abwino kwambiri kuposa chiwiya chirichonse chopangidwa ndi munthu choyezera phokoso​—otithandiza kusangalala ndi makambitsirano, nyimbo ndi nyimbo zokondweretsa za mbalame. Tiri ndi mpangidwe wachibadwa wakulankhula, kuphatikizapo lirime logwira ntchito zosiyanasiyana. Maselo olaŵira alirime, limodzi ndi mphamvu zathu zakununkhiza, zimaperekanso chikondwerero m’kulaŵa ndi kununkhiza zakudya zamitundumitundu. Ndipo timayamikira chotani nanga kukhudza kwa dzanja la wokondedwa! Ndithudi, tingathe kuyamikira Mlengi wathu, monga momwe anachitira wamasalmo amene anati: ‘Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu nzodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.’​—Salmo 139:14.

Kukoma Mtima Kwachikondi kwa Mlengi Wathu

Wamasalmo analemba kuti: ‘Yamikani Yehova pakuti ndiye wabwino . . . ; amene yekha achita zodabwitsa zazikulu: pakuti chifundo chake nchosatha.’ (Salmo 136:1-4) Kukoma mtima kwachikondi kumeneko tsopano kukumsonkhezera kuchita zinthu zodabwitsa kwambiri kuposa zolengedwa zonse zimene tangofotokoza kumene. Inde, ngakhale pamene akupuma pakulenga zinthu zakuthupi, iye akulenga zinthu zauzimu. Iye akuchita izi moyankha chitokoso cha woipa chimene chinalunjikitsidwa mwamwano kwa iye. Motani?

Mwamuna woyamba ndi mkazi anaikidwa m’paradaiso waulemerero, mu Edene. Komabe, mngelo wopanduka, Satana, anadziika kukhala mulungu natsogolera anthu aŵiriwo kupandukira Yehova. Molungama, Mulungu anawaweruzira kuimfa, nchotulukapo chakuti ana awo, fuko lonse laumunthu, abadwira mumkhalidwe wauchimo, wakumafa. (Salmo 51:5) Nkhani ya m’Baibulo yonena za Yobu imasonyeza kuti Satana anatokosa Mulungu, akumanena kuti palibe munthu angathe kusunga umphumphu kwa Iye pakuyesedwa. Koma Yobu anatsimikizira Satana kukhala wonama bodza lamkunkhuniza, monga momwe achitira atumiki ena okhulupirika a Mulungu m’nthaŵi za Baibulo ndi kufikira lerolino. (Yobu 1:7-12; 2:2-5, 9, 10; 27:5) Yesu, monga munthu wangwiro, anapereka chitsanzo chakusunga umphumphu chosayerekezereka.​—1 Petro 2:21-23.

Chotero, Yesu anakhoza kunena, “Wolamulira wa dziko [Satana] alibe ulamuliro pa ine.” (Yohane 14:30, NW) Komabe, kufikira lerolino “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Pokhala atatsutsa kuyenera kwa ulamuliro wa Yehova, Satana wapatsidwa zaka pafupifupi 6,000 kuti asonyeze ngati ulamuliro wake pa anthu ungapeze chipambano. Iye walephera momvetsa chisoni chotani nanga, monga momwe mikhalidwe yadziko yomanyonyotsoka ikupitirizira kuchitira umboni! Mulungu wathu wachikondi, Yehova, mwamsanga adzachotsa chitaganya chadziko chosalungama chimenechi, akumatsimikizira ulamuliro wake woyenera padziko lapansi. Ndimpumulo wosangalatsa chotani nanga umene zimenezo zidzazetsa kwa anthu olakalaka ulamuliro wa mtendere ndi wolungama!​—Salmo 37:9-11; 83:17, 18.

Komabe, sizokhazo! Kukoma mtima kwachikondi kwa Mulungu kudzasonyezedwanso mogwirizana ndi mawu a Yesu pa Yohane 3:16 kuti: “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi [la anthu] kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Kubwezeretsa pa anthu chiyembekezo cha moyo wosatha padziko lapansi kumeneku kumaphatikizapo kulengedwa kwa zinthu zatsopano. Kodi zimenezi nchiyani? Kodi zimapindulitsa motani anthu obuula? Nkhani yathu yotsatira idzasimba.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena