Mutu 51
Kupha Mwambanda pa Phwando la Tsiku Lakubadwa
PAMBUYO pa kupereka malangizo kwa atumwi ake, Yesu akuwatuma m’gawo aŵiriaŵiri. Mwinamwake abalewo Petro ndi Andreya amkira limodzi, monga momwe akuchitira Yakobo ndi Yohane, Filipo ndi Bartolomeyo, Tomasi ndi Mateyu, Yakobo ndi Tadeyo, ndipo Simoni ndi Yudase Isikariote. Timagulu tisanu ndi kamodzi ta aŵiriaŵiri ta alaliki tikulalikira mbiri yabwino ya Ufumuwo ndipo tikuchita machiritso ozizwitsa kulikonse kumene apitako.
Pakali pano, Yohane Mbatizi akali chikhalirebe m’ndende. Iye wakhala mmenemo pafupifupi zaka ziŵiri tsopano. Mungathe kukumbukira kuti Yohane ananena poyera kuti kunali kulakwa kuti Herode Antipa atenge Herodiya, mkazi wa mbale wake Filipo, kukhala wake. Popeza kuti Herode Antipa adanena kuti anali wotsatira Chilamulo cha Mose, moyenerera Yohane anasonyeza kulakwa kwa ukwati wachigololo umenewu. Chotero Herode anaponya Yohane m’ndende, mwinamwake mochirikizidwa ndi Herodiya.
Herode Antipa akuzindikira kuti Yohane ndimwamuna wolungama ndipo akumumvetseradi ndi chisangalalo. Chifukwa chake, iye sakudziŵa chimene angachite naye. Kumbali ina, Herodiya, akuda Yohane ndipo akupitirizabe kufunafuna kuti amuphe. Potsirizira pake, mwaŵi umene wakhala akuyembekezera ukufika.
Mwamsanga Paskha wa 32 C.E. asanachitike, Herode akuchita makonzedwe a phwando lalikulu la tsiku lake lakubadwa. Osonkhana kaamba ka phwandolo ndiwo nduna zapamwamba za Herode ndi akazembe ankhondo, kudzanso nzika zolemekezeka za m’Galileya. Pamene madzulowo akupitirizabe, Salome, mwana wamkazi wachichepere wa Herodiya mwa mwamuna wake woyambilirayo Filipo, akutumidwa kukavinira alendo. Amuna owonererawo akuchita chidwi ndi kavinidwe ka msungwanayo.
Herode wakondwera kwambiri ndi Salome. “Tapempha kwa ine chirichonse uchifuna, ndidzakupatsa iwe,” iye akulengeza motero. Iye akufikira ngakhale pakulumbira kuti: “Chirichonse ukandipempha ndidzakupatsa, ngakhale kukugaŵira ufumu wanga.”
Asanayankhe, Salome akutuluka kukafunsa amake. “Ndidzapempha chiyani?” iye akufunsa motero.
Potsirizirapo mwaŵi wafika! “Mutu wake wa Yohane Mbatizi,” akuyankha motero Herodiya popanda kudodoma.
Mwamsanga Salome akubwerera kwa Herode ndipo akupempha kuti: “Ndifuna kuti mundipatse tsopano, mutu wake wa Yohane Mbatizi mumbizi.”
Herode akumva chisoni kwambiri. Komabe chifukwa chakuti alendo ake amva lumbiro lake, iye akuchita manyazi kusawupereka, ngakhale kuti izi zitanthauza kupha mwambanda munthu wosachimwa. Wopha munthu akutumidwa mwamsanga kundende atalangizidwa ndi malamulo okakalawo. Mwamsanga iye akubwera ndi mutu wa Yohane mumbizi, ndipo akuwupereka kwa Salome. Nayenso, akuwupititsa kwa amake. Pamene ophunzira a Yohane amva zimene zachitika, iwo akudza nachotsa mtembo wake nauika m’manda, ndipo pamenepo iwo akuuza nkhaniyo kwa Yesu.
Pambuyo pake, pamene Herode amva za kuchiritsa anthu kwa Yesu ndi kutulutsa ziŵanda, iye akuchita mantha, akumawopa kuti Yesu kwenikweni ndiye Yohane amene waukitsidwa kwa akufa. Pambuyo pake, iye akukhumba kwambiri kuti awone Yesu, osati kudzamva kulalikira kwake, koma kutsimikizira kuti kaya mantha akewo ali ndi maziko abwino kapena ayi. Mateyu 10:1-5; 11:1; 14:1-12; Marko 6:14-29; Luka 9:7-9.
▪ Kodi nchifukwa ninji Yohane ali m’ndende, ndipo kodi nchifukwa ninji Herode safuna kumupha?
▪ Kodi ndimotani mmene potsirizira pake Herodiya ali wokhoza kuphetsa Yohane?
▪ Pambuyo pa imfa ya Yohane, kodi nchifukwa ninji Herode akufuna kuwona Yesu?