Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 121
  • Pamaso pa Sanhedrin, Ndiyeno kwa Pilato

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pamaso pa Sanhedrin, Ndiyeno kwa Pilato
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Pamaso pa Bwalo la Akulu, Kenaka kwa Pilato
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • Khoti la Sanihedirini Linaweruza Mlandu wa Yesu Kenako Anapita Naye kwa Pilato
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Pilato Anapereka Yesu Ndipo Anthu Anamutenga Kuti Akamuphe
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Aperekedwa Natengedwa
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 121

Mutu 121

Pamaso pa Sanhedrin, Ndiyeno kwa Pilato

USIKUWO uli pafupi kutha. Petro wakana Yesu kwanthaŵi yachitatu, ndipo ziŵalo za Sanhedrin zatha kuzenga mlandu kwawo kwa chiphamaso ndipo amwazikana. Komabe, mwamsanga pamene kukufikira kukhala mbandakucha wa Lachisanu mmaŵa, iwo akusonkhananso, panthaŵi ino kunyumba yawo ya Sanhedrin. Mwachiwonekere chifuno chawo ndicho kupereka kawonekedwe kalamulo kumlandu wozengedwa usikuwo. Pamene Yesu abweretsedwa pamaso pawo, iwo akuti, monga momwe adanenera usikuwo: “Ngati uli Kristu, utiuze.”

“Ndikakuuzani, simudzavomereza,” Yesu akuyankha. “Ndikakufunsani kanthu, simudzayankha.” Komabe, molimba mtima Yesu akunena amene iye ali, akumati: “Kuyambira tsopano Mwana wa munthu adzakhala padzanja lamanja lamphamvu ya Mulungu.”

“Umo mutero, muli mwana wa Mulungu kodi?” onsewo akufuna kudziŵa.

“Munena kuti ndine,” Yesu akuyankha.

Kwa amuna ameneŵa okhala ndi cholinga chambanda, yankho limeneli nlokwanira. Akulilingalira kukhala kuchitira mwano Mulungu. “Tifuniranjinso mboni?” iwo akufunsa. “Pakuti ife tokha tinamva mkamwa mwa iye mwini.” Chotero iwo akumanga Yesu, nachoka naye, ndi kukampereka kwa Pontiyo Pilato kazembe wa Roma.

Yudase, wopereka Yesu, wakhala akupenyetsetsa zochitikazo. Pamene iye awona kuti Yesu waŵeruziridwa kuimfa, akumva chisoni. Chotero iye akupita kwa akulu ansembe ndi akulu ena kukabwezera zidutswa za ndalama za siliva 30, akumafotokoza kuti: “Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa.”

“Tiri nacho chiyani ife? udziwonera wekha,” iwo akuyankha mwankhalwe. Chotero Yudase akutayira zidutswa za silivazo m’kachisi nachoka kukayesa kudzipachika. Komabe, mwachiwonekere nthambi imene Yudase akumangirirako chingwe ikuthyoka, ndipo thupi lake likugwera pathathwe, pamene likuphulika.

Akulu ansembe saali otsimikizira chimene angachite ndi zidutswa za ndalama za silivazo. “Sikuloledwa kuziika m’chosonkhera ndalama za Mulungu,” iwo akutero, “chifukwa ndizo mtengo wamwazi.” Chotero, pambuyo pakufunsana, iwo akugula ndi ndalamazo munda wa woumba mbiya kuikamo maliro a alendo. Chotero mundawo ukufikira kutchedwa kuti “Munda wa Mwazi.”

Ukali chikhalirebe mmamaŵa pamene Yesu akutengeredwera ku pretorio ya kazembe. Koma Ayuda amene apita naye akukana kuloŵa chifukwa akhulupirira kuti kuyandikana ndi Amitundu koteroko kudzawadetsa. Chotero mowagonjera, Pilato akutuluka. “Chifukwa chanji mwadza nacho cha munthu uyu?” iye afunsa motero.

“Akadakhala wosachita zoipa uyu sitikadampereka iye kwa inu,” iwo akuyankha.

Pofuna kupeŵa kuphatikizidwa, Pilato akuyankha kuti: “Mumtenge iye inu, ndi kumuŵeruza iye monga mwa chilamulo chanu.”

Akumasonyeza cholinga chawo cha kuchita mbanda, Ayudawo akuti: “Tiribe ulamuliro wakupha munthu ali yense.” Ndithudi, ngati iwo akapha Yesu pa Phwando la Paskha, mwinamwake kukachititsa chipolowe mwa anthu, popeza kuti ambiri amalemekeza Yesu. Koma ngati iwo angachititse Aroma kumupha pachinenezo cha ndale zadziko, izi zikawachotsera thayolo pamaso pa anthu.

Chotero atsogoleri achipembedzo, mosatchula kuzenga kwawo mlandu koyambirira kumene anaweruza motsutsa Yesu kuti akuchitira mwano Mulungu, tsopano akupeka zinenezo zosiyana. Iwo akupanga zinenezo zambali zitatu: ‘Tinapeza munthu uyu [1] ali kupandutsa anthu a mtundu wathu, [2] akuwaletsa kukhoma msonkho kwa Kaisara, [3] nadzinenera kuti iye ndiye Kristu mfumu.’

Chiri chinenezo chakuti Yesu akudzitcha mfumu chimene Pilato akudera nacho nkhaŵa. Chifukwa chake, iye, akuloŵanso m’pretorio, naitana Yesu kwa iye, namfusa kuti: “Iwe ndiwe mfumu ya Ayuda kodi?” Mwamawu ena, kodi waswa lamulo mwa kudzilengeza iwe mwini kukhala mfumu motsutsana ndi Kaisara?

Yesu akufuna kudziŵa kuti Pilato wamva zochuluka motani ponena za iye, chotero iye akufunsa kuti: “Kodi munena ichi mwa inu nokha, kapena kodi anakuuzani za ine?”

Pilato akusonyeza ngati kuti sadziŵa kanthu za iye ndipo ali ndi chikhumbo cha kufuna kumva zenizeni. “Ndiri ine Myuda kodi?” iye akuyankha. “Mtundu wako ndi akulu ansembe anakupereka kwa ine; achita chiyani?”

Mwanjira iriyonse Yesu sakuyesa kuzemba nkhaniyo, imene iri ya kukhala kwake mfumu. Mosakayikira yankho limene Yesu apereka tsopano likudabwitsa Pilato. Luka 22:66–23:3; Mateyu 27:1-11; Marko 15:1; Yohane 18:28-35; Machitidwe 1:16-20.

▪ Kodi Sanhedrin ikusonkhananso mmamaŵa kaamba ka chifuno chotani?

▪ Kodi Yudase akufa bwanji, ndipo kodi chikuchitika nchiyani ndi zidutswa 30 zasiliva?

▪ Mmalo mwakumupha iwo eni, kodi nchifukwa ninji Ayuda akufuna kuti Aroma aphe Yesu?

▪ Kodi ndizinenezo zotani zimene Ayuda akupanga motsutsa Yesu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena