Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w94 6/1 tsamba 8-12
  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?
  • Nsanja ya Olonda—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Tingadziŵe Motani Lingaliro la Mulungu?
  • Kodi Onse Amene Amagwiritsira Ntchito Baibulo Ali Olondola?
  • Zizindikiro Zodziŵira Chipembedzo Choona
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kulondola Chipembedzo Choyera Kaamba ka Chipulumutso
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Mmene Mungacidziwire Cipembedzo Coona
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi Ndingachidziwe Bwanji Chipembedzo Cholondola?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1994
w94 6/1 tsamba 8-12

Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?

“Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo.”​—YAKOBO 1:27.

1, 2. (a) Malinga ndi kuganiza kwa anthu ambiri, kodi nchiyani chimene chimasonyeza kaya ngati chipembedzo chawo chili cholondola? (b) Kodi nchiyani chimene chiyenera kulingaliridwa mwamphamvu popima chipembedzo?

TIKUKHALA m’nyengo imene anthu ambiri ali okhutira ndi mbali yochepa imene chipembedzo chili nayo m’miyoyo yawo. Iwo angakhale akumapezeka pa misonkhano yachipembedzo, koma ndi oŵerengeka chabe amene amatero nthaŵi zonse. Anthu ochuluka samakhulupirira kuti zipembedzo zina zonse zili zolakwa ndi kuti chawo ndicho cholondola. Iwo angangolingalira kuti chipembedzo chawo nchowayenerera.

2 Polingalira zimenezi, kodi funso lakuti, Kodi mwapeza chipembedzo cholondola? limangotanthauza kuti, Kodi mwapeza chipembedzo chimene mumakonda? Kodi nchiyani chimene chimasonyeza zimene mumakonda? Banja lanu? Mabwenzi anu? Malingaliro anu? Kodi mwaliganizirapo mwamphamvu motani lingaliro la Mulungu pa nkhaniyi?

Kodi Tingadziŵe Motani Lingaliro la Mulungu?

3. (a) Ngati titi tidziŵe lingaliro la Mulungu, kodi tiyenera kukhala ndi chiyani? (b) Kodi ndi mafunso otani amene tiyenera kufunsa ponena za chifukwa chake ife pa tokha timakhulupirira kuti Baibulo nlochokera kwa Mulungu?

3 Ngati titi tidziŵe zimene Mulungu mwiniyo amaganiza, pamenepo payenera kukhala vumbulutso lochokera kwa iye. Baibulo ndi buku lakale koposa limene limadzinenera kukhala louziridwa ndi Mulungu. (2 Timoteo 3:16, 17) Koma kodi kunganenedwe moonadi kuti buku limeneli, mosiyana ndi ena onse, lili ndi uthenga wa Mulungu kaamba ka mtundu wonse wa anthu? Kodi mungayankhe motani funso limenelo, ndipo nchifukwa ninji? Kodi nchifukwa chakuti makolo anu anakhulupirira zimenezo? Kodi nchifukwa cha zimene mabwenzi anu amaganiza? Kodi inu mwininu mwapenda umboniwo? Bwanji osachita zimenezo tsopano lino, mukumagwiritsira ntchito maumboni anayi otsatirawa?

4. Ponena za kupezeka kwake, kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Baibulo, mmalo mwa buku lina lililonse, nlochokera kwa Mulungu?

4 Kupezeka kwake: Uthenga wochokeradi kwa Mulungu umene uli wa banja lonse laumunthu uyenera kulandiridwa ndi onse. Kodi ndi mmene zilili ndi Baibulo? Talingalirani izi: Baibulo, lathunthu kapena mbali yake, likufalitsidwa tsopano m’zinenero zoposa 2,000. Malinga ndi American Bible Society, pafupifupi zaka khumi zapitazo zinenero zimene Baibulo linasindikizidwamo zinachititsa kuti anthu pafupifupi 98 peresenti a padziko lonse akhale nalo. Monga momwe Guinness Book of World Records inanenera, Baibulo mosakayikira ndilo “buku lofalitsidwa kopambana padziko.” Izi nzimene tingayembekezere ponena za uthenga wochokera kwa Mulungu kaamba ka anthu a mafuko onse ndi mitundu ndi manenedwe. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 14:6.) Palibe buku lina lililonse m’dziko limene lafalitsidwa monga ilo.

5. Kodi nchifukwa ninji maziko a mbiri ya Baibulo ali ofunika kwambiri?

5 Kuona kwa mbiri yake: Kupenda mosamalitsa nkhani za Baibulo kumavumbula njira ina imene Baibulo lilili losiyana ndi mabuku ena amene amadzinenera kukhala opatulika. Baibulo lili ndi zochitika zenizeni za m’mbiri, osati nthano zosatsimikizirika. Irwin Linton, amene pokhala loya anali ndi chizoloŵezi cha kupenda zimene zinali kufunika monga umboni wa m’bwalo la milandu, analemba kuti: “Pamene kuli kwakuti nkhani zolembedwa, nthano zopekedwa ndiponso umboni wonama zimakhala zaluso kugwirizanitsa zochitika zosimbidwazo ndi malo akutali ndi nthaŵi zosadziŵika, . . . nkhani za Baibulo zimatchula molondola bwino lomwe deti ndi malo a zinthu zonenedwazo.” (Mwachitsanzo, onani 1 Mafumu 14:25; Yesaya 36:1; Luka 3:1, 2.) Kwa anthu amene amatembenukira ku chipembedzo kaamba ka choonadi osati kaamba kothaŵa mavuto, mfundo imeneyi n’njofunika kwambiri.

6. (a) Kodi ndimotani mmene Baibulo limathandiziradi munthu pa mavuto a moyo? (b) Kodi ndi mwanjira zitatu ziti zimene Baibulo limathandizira munthu kulimbana ndi mavuto enieni?

6 Kugwira kwake ntchito: Awo amene amapenda Baibulo mosamalitsa amazindikira msanga kuti malamulo ndi miyezo yake sizili zowalima pamsana. Mmalo mwake, zimasonyeza njira ya moyo imene imadzetsa mapindu kwa awo amene amazimamatira kwambiri. (Yesaya 48:17, 18) Chitonthozo chimene limapereka kwa awo amene akuvutika sichili chonyenga, chozikidwa pa nthanthi zachabe. Mmalo mwake, limathandiza anthu kulimbana ndi mavuto enieni a moyo. Motani? Mwa njira zitatu: (1) mwa kupereka uphungu wabwino wosonyeza mmene angachitire ndi zovuta, (2) mwa kufotokoza mmene tingalandirire chichirikizo chachikondi chimene Mulungu amapereka kwa atumiki ake lerolino, ndipo (3) mwa kuvumbula mtsogolo mwabwino koposa mmene Mulungu wasungira awo amene amamtumikira, ndi kuwapatsa zifukwa zabwino zokhalira ndi chidaliro m’malonjezo ake.

7. (a) Mwa kugwiritsira ntchito malemba osonyezedwa m’mawu amtsinde, fotokozani yankho la Baibulo pa imodzi ya nkhani zazikulu zimene zimadetsa nkhaŵa anthu lerolino. (b) Sonyezani mmene uphungu wa Baibulo umatitetezerera kapena kutithandiza kulimbana ndi mkhalidwe wovutitsa.

7 Ngakhale kuti uphungu wa Baibulo sumalandiridwa kaŵirikaŵiri ndi awo amene amakana ulamuliro ndi kulondola moyo wokhutiritsa zikhumbo zawo, ambiri afikira pa kuzindikira kuti moyo wotero sunawadzetsere chimwemwe chenicheni. (Agalatiya 6:7, 8) Baibulo limapereka mayankho olondola ponena za kutaya mimba, chisudzulo, ndi kugonana kwa ofanana ziŵalo. Uphungu wake umatitetezera pa kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka ndi zakumwa zoledzeretsa ndi kuyambukiridwa ndi AIDS kupyolera m’mwazi wokhala ndi kachilombo kake kapena uchiwerewere. Limatisonyeza mmene tingakhalire ndi mabanja achimwemwe. Limapereka mayankho amene amakhozetsa munthu kulimbana ndi mikhalidwe yovutitsa koposa m’moyo, kuphatikizapo kukanidwa ndi ziŵalo zabanja zapamtima, nthenda yalizunzo, ndi imfa ya wokondedwa. Limatithandiza kuzindikira zinthu zathu zofunika koposa kotero kuti miyoyo yathu idzale ndi tanthauzo mmalo mwa chisoni.a

8, 9. (a) Kodi ndi ulosi uti umene inu pa nokha umakuchititsani chidwi monga umboni wa kuuziridwa kwa Baibulo? (b) Kodi maulosi a m’Baibulo amasonyezanji ponena za magwero awo?

8 Ulosi: Baibulo ndilo buku lapadera la ulosi, buku limene limasimba zimene zidzachitika mtsogolo, ndipo limatero mwatsatanetsatane. Linaneneratu za chiwonongeko cha Turo wakale, kugwa kwa Babulo, kumangidwanso kwa Yerusalemu, kuyamba kulamulira ndi kugwa kwa mafumu a Amedi ndi Aperisi ndi Grisi, ndi zochitika zambiri m’moyo wa Yesu Kristu. Ndiponso linaneneratu mwatsatanetsatane za mikhalidwe ya dziko imene yabuka m’zaka za zana lino, ndipo limafotokoza tanthauzo lake. Limasonyeza mmene mavuto amene athetsa nzeru olamulira aumunthu adzathetsedwera, ndipo limadziŵikitsa Wolamulira amene adzadzetsera mtundu wa anthu mtendere wosatha ndi chisungiko chenicheni.b​—Yesaya 9:6, 7; 11:1-5, 9; 53:4-6.

9 Kwakukulukulu, Baibulo limasonyeza kukhoza kwa kuneneratu molondola za mtsogolo kukhala umboni wa Umulungu. (Yesaya 41:1–46:13) Amene angachite zimenezo kapena amene angauzire ena kuchita zimenezo sangakhale konse fano lopanda moyo. Sali munthu wopembedza ayi. Ali Mulungu woona, ndipo buku limene lili ndi ulosi wotero ndilo Mawu ake.​—1 Atesalonika 2:13.

Kodi Onse Amene Amagwiritsira Ntchito Baibulo Ali Olondola?

10, 11. Malinga ndi mmene Yesu anasonyezera, ngakhale kuti mtsogoleri wachipembedzo angagwiritsire ntchito Baibulo, kodi nchiyani chimene chingachititse chipembedzo chimene amachirikiza kukhala chopanda pake?

10 Pamenepa, kodi kuli kwanzeru​—makamaka, kodi kuli Kwamalemba​—kunena kuti magulu onse achipembedzo amene amanena kuti amagwiritsira ntchito Baibulo amaphunzitsa chipembedzo choona? Kodi aliyense amene amanyamula kapena kugwira mawu a Baibulo amachita chipembedzo cholondola?

11 Atsogoleri achipembedzo ambiri, ngakhale kuti ali ndi Baibulo, amagwiritsira ntchito chipembedzo monga njira yopezera ulemerero waumwini. Iwo amaluluza choonadi choyera mwa miyambo ndi nthanthi zaumunthu. Kodi kulambira kwawo kuli kovomerezedwa ndi Mulungu? Kwa atsogoleri achipembedzo a Yerusalemu wa m’zaka za zana loyamba amene anali kuchitadi zimenezo, Yesu Kristu moyenerera anagwiritsira ntchito chilengezo cha Mulungu kupyolera mwa mneneri Yesaya, akumati: “Anthu aŵa andilemekeza ine ndi milomo yawo; koma mtima wawo uli kutali ndi ine. Koma andilambira ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.” (Mateyu 15:8, 9; 23:5-10) Mwachionekere, chipembedzo chamtundu wotero sichili chipembedzo choona.

12, 13. (a) Kodi ndimotani mmene khalidwe la ziŵalo za tchalitchi lingathandizire munthu kudziŵa kaya ngati chipembedzo chawo chili cholondola? (b) Kodi Mulungu adzakuona bwanji kulambira kwathu ngati tisankha kuyanjana ndi awo amene iye amakana? (2 Mbiri 19:2)

12 Bwanji ngati zipatso zotulutsidwa ndi ziphunzitso za zipembedzo zina, zosonyezedwa m’miyoyo ya ziŵalo zake zimene zili ndi malo oyanjidwa, zili zoipa? Mu Ulaliki wake wa pa Phiri, Yesu anachenjeza kuti: “Yang’anirani mupeŵe aneneri onyenga, . . . Mudzawazindikira ndi zipatso zawo. . . . Mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa.” (Mateyu 7:15-17) Nzoona kuti anthu angachite cholakwa nafunikira kuwongoleredwa. Koma mkhalidwe umakhala wosiyana pamene ziŵalo za tchalitchi, ngakhale atsogoleri achipembedzo, achita dama ndi chigololo, kumenyana, kuledzera, umbombo, kunama, kukhulupirira mizimu, kulambira mafano​—chimodzi cha izi kapena zonse​—komabe palibe chilango chimene chimaperekedwa, ndipo awo amene amapitiriza ndi njira imeneyi samachotsedwa mumpingo. Baibulo limafotokoza bwino lomwe kuti awo amene amachitachita zinthu zotero ayenera kuchotsedwa mumpingo; sadzakhala ndi malo mu Ufumu wa Mulungu. (Agalatiya 5:19-21) Kulambira kwawo sikukondweretsa Mulungu, ngakhale kulambira kwathu sikumakondweretsa Mulungu ngati tisankha kuyanjana ndi awo amene iye amakana.​—1 Akorinto 5:11-13; 6:9, 10; Chivumbulutso 21:8.

13 Kuli koonekeratu kuti si magulu onse amene amagwiritsira ntchito Baibulo amene akuchita chipembedzo choona chimene limafotokoza. Pamenepa, kodi nziti zimene Baibulo limatchula kukhala zizindikiro zodziŵira chipembedzo choona?

Zizindikiro Zodziŵira Chipembedzo Choona

14. (a) Kodi ziphunzitso zonse za chipembedzo choona nzozikidwa pa chiyani? (b) Kodi ziphunzitso za Dziko Lachikristu zikuchita motani pa muyeso wonena za Mulungu ndi moyo?

14 Ziphunzitso zake zili zozikidwa zolimba pa Malemba ouziridwa. “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.” (2 Timoteo 3:16) Koma kodi m’pati pamene Baibulo Loyera limanena za Utatu wa Dziko Lachikristu? Ndipo kodi m’pati pamene Baibulo limaphunzitsa, monga momwe amachitira atsogoleri achipembedzo, kuti anthu ali ndi moyo umene umapulumuka imfa ya thupi? Kodi munapemphapo mtsogoleri wachipembedzo kukusonyezani ziphunzitso zimenezo m’Baibulo lanu? The New Encyclopædia Britannica imati: “Ngakhale liwu lakuti Utatu kapena chiphunzitso chomvekera sichimapezeka m’Chipangano Chatsopano.” (1992, Micropædia, Voliyumu 11, tsamba 928) Ndipo New Catholic Encyclopedia imavomereza kuti: “Pakati pa Abambo Autumwi, panalibedi lingaliro kapena kaonedwe kotero mpang’ono pomwe.” (1967, Voliyumu XIV, tsamba 299) Ponena za chikhulupiriro cha Dziko Lachikristu cha moyo umene umalekana ndi thupi pa imfa, akatswiri a tchalitchi amavomereza kuti anatengera lingalirolo ku nthanthi Zachigiriki. Komabe, chipembedzo choona sichimapambuka pa choonadi cha Baibulo ndi kutenga nthanthi zaumunthu.​—Genesis 2:7; Deuteronomo 6:4; Ezekieli 18:4; Yohane 14:28.

15. (a) Kodi Baibulo limadziŵikitsa motani Uyo yekha amene ayenera kulambiridwa? (b) Kodi olambira oona amamva motani ponena za kuyandikana ndi Yehova?

15 Chipembedzo choona chimachirikiza kulambira Mulungu woona yekha, Yehova. (Deuteronomo 4:35; Yohane 17:3) Akumafotokoza mwachidule Deuteronomo 5:9 ndi 6:13, Yesu Kristu ananena motsimikiza kuti: “[Yehova, NW] Mulungu wako udzamgwadira, ndipo iye yekhayekha udzamlambira.” (Mateyu 4:10) Mogwirizana ndi zimenezo, Yesu anadziŵikitsa dzina la Atate wake kwa ophunzira ake. (Yohane 17:26) Kodi chipembedzo chanu chakuphunzitsani kulambira Yehova? Kodi mwafika pa kumdziŵa Munthuyo wotchedwa ndi dzina limenelo​—zifuno zake, zochita zake, mikhalidwe yake​—kotero kuti mukulingalira kuti mungayandikire kwa iye mwachidaliro? Ngati chipembedzo chanu chili choona, yankho nlakuti inde.​—Luka 10:22; 1 Yohane 5:14.

16. Kodi chikhulupiriro mwa Kristu chimatanthauzanji kwa awo amene amachita chipembedzo choona?

16 Mbali yofunika kwambiri ya kulambira kumene kumakondweretsa Mulungu ndiyo chikhulupiriro mwa Mwana wake, Yesu Kristu. (Yohane 3:36; Machitidwe 4:12) Zimenezi sizimatanthauza kungokhulupirira kuti anakhalako kapena kuti anali munthu wapadera. Zimaphatikizapo kuyamikira zimene Baibulo limaphunzitsa ponena za mtengo wa nsembe ya moyo wangwiro waumunthu wa Yesu ndi kuzindikira malo ake amene ali nawo lerolino monga Mfumu yakumwamba. (Salmo 2:6-8; Yohane 3:16; Chivumbulutso 12:10) Ngati mumayanjana ndi awo amene amachita chipembedzo choona, mumadziŵa kuti m’moyo wawo wa tsiku ndi tsiku amayesayesa mwakhama kumvera Yesu, kutsanzira chitsanzo chake, ndi kukhala ndi phande mwaumwini ndi mwachangu m’ntchito imene anagaŵira ophunzira ake. (Mateyu 28:19, 20; Yohane 15:14; 1 Petro 2:21) Ngati zimenezo sizili choncho ndi awo amene mumalambira nawo, mufunikira kupita kwina.

17. Kodi nchifukwa ninji olambira oona amasamala kukhala osachititsidwa maŵanga ndi dziko, ndipo kodi zimenezo zimaphatikizapo chiyani?

17 Kulambira koona sikumaipitsidwa ndi kuloŵerera m’ndale ndi m’mikangano ya dziko. (Yakobo 1:27) Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Yesu anati ponena za atsatiri ake: “Siali a dziko lapansi monga ine sindili wa dziko lapansi.” (Yohane 17:16) Yesu sanadziloŵetse m’ndale zadziko, ndipo analetsa atsatiri ake kugwiritsira ntchito zida. (Mateyu 26:52) Awo amene amalabadira zimene Mawu a Mulungu amanena ‘samaphunziranso nkhondo.’ (Yesaya 2:2-4) Ngati chipembedzo chilichonse chimene mumagwirizana nacho ngakhale mwa dzina lokha sichiyenerera mafotokozedwe amenewo, ndi bwino kuleka kugwirizana nacho.​—Yakobo 4:4; Chivumbulutso 18:4, 5.

18. (a) Kodi nchiyani chimene lemba la Yohane 13:35 limasonyeza kukhala mkhalidwe wapadera wa chipembedzo choona? (b) Kodi ndimotani mmene mungathandizire wina kudziŵa gulu limene limatsatira Yohane 13:35?

18 Chipembedzo choona chimaphunzitsa ndi kusonyeza chikondi chopanda dyera. (Yohane 13:35; 1 Yohane 3:10-12) Chikondi chotero sichimangotchulidwa m’maulaliki okha. Chimaloŵetsadi anthu a m’mafuko onse, mikhalidwe yonse ya zachuma, manenedwe onse, ndi mitundu yonse, mu ubale weniweni. (Chivumbulutso 7:9, 10) Chimalekanitsa Akristu oona ndi dziko lowazinga. Ngati simunaterobe, fikano pa misonkhano pa Nyumba Yaufumu ya Mboni za Yehova, limodzinso ndi pa misonkhano yawo yaikulu. Zipenyeni pamene zikugwirira ntchito pamodzi kumanga imodzi ya Nyumba zawo Zaufumu. Onani mmene zimachitira ndi achikulire (kuphatikizapo akazi amasiye) ndi achichepere (kuphatikizapo awo amene ali ndi kholo limodzi kapena amene alibe). (Yakobo 1:27) Yerekezerani zimene mwaonazo ndi zimene mwaona m’chipembedzo china chilichonse. Ndiyeno dzifunseni kuti, ‘Kodi ndani amene amachita chipembedzo choona?’

19. (a) Kodi ndi yankho liti la mavuto a mtundu wa anthu limene chipembedzo choona chimachirikiza? (b) Kodi nchiyani chimene ziŵalo za gulu limene lili ndi chipembedzo choona ziyenera kumachita?

19 Chipembedzo choona chimachirikiza Ufumu wa Mulungu monga yankho lachikhalire la mavuto a mtundu wa anthu. (Danieli 2:44; 7:13, 14; 2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:4, 5) Kodi tchalitchi chilichonse cha Dziko Lachikristu chimachita zimenezo? Kodi ndi liti pamene munamva mtsogoleri wachipembedzo akufotokoza Ufumu wa Mulungu ndi zimene Malemba amasonyeza kuti udzakwaniritsa? Kodi gulu limene mulimo limakulimbikitsani kuuza ena za Ufumu wa Mulungu, ndipo ngati limatero, kodi ziŵalo zonse zimachita zimenezo? Yesu anachita umboni wotero; ophunzira ake oyambirira anatero. Nanunso mungakhale ndi mwaŵi wa kuchitako ntchito imeneyi. Ndiyo ntchito yofunika kwambiri imene ikuchitidwa pa nkhope ya dziko lapansi lerolino.​—Mateyu 24:14.

20. Kuwonjezera pa kudziŵa chipembedzo cholondola, kodi tiyenera kuchitanji?

20 Ngakhale kuti pali zipembedzo zikwi zambiri, Baibulo limatithandiza mofulumira kuchotsa msokonezowo kuti tidziŵe chipembedzo choona. Koma tifunikira kuchita zambiri kuposa kungochidziŵa. Nkofunika kwa ife kuchichita. Zophatikizidwa m’kuchita zimenezi zidzapendedwa bwino lomwe m’nkhani yathu yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

a Kutaya mimba: Machitidwe 17:28; Salmo 139:1, 16; Eksodo 21:22, 23. Chisudzulo: Mateyu 19:8, 9; Aroma 7:2, 3. Kugonana kwa ofanana ziŵalo: Aroma 1:24-27; 1 Akorinto 6:9-11. Kugwiritsira ntchito molakwa anamgoneka ndi zakumwa zoledzeretsa: 2 Akorinto 7:1; Luka 10:25-27; Miyambo 23:20, 21; Agalatiya 5:19-21. Mwazi ndi uchiwerewere: Machitidwe 15:28, 29; Miyambo 5:15-23; Yeremiya 5:7-9. Banja: Aefeso 5:22–6:4; Akolose 3:18-21. Kukanidwa: Salmo 27:10; Malaki 2:13-16; Aroma 8:35-39. Nthenda: Chivumbulutso 21:4, 5; 22:1, 2; Tito 1:2; Salmo 23:1-4. Imfa: Yesaya 25:8; Machitidwe 24:15. Zinthu zofunika koposa: Mateyu 6:19-34; Luka 12:16-21; 1 Timoteo 6:6-12.

b Kuti mupeze zitsanzo za maulosi otero ndi kukwaniritsidwa kwawo, onani mabuku awa Baibulo​—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?, masamba 117-61; ndi Kukambitsirana za m’Malemba, masamba 54-6, 374-80, 260-8. Onse aŵiri amafalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

Kodi Mungayankhe Motani?

◻ Pofuna kudziŵa chipembedzo choona, kodi ndi lingaliro la yani limene lili lofunika koposa?

◻ Kodi ndi maumboni anayi ati amene amasonyeza Baibulo kukhala Mawu a Mulungu?

◻ Kodi nchifukwa ninji si zipembedzo zonse zimene zimagwiritsira ntchito Baibulo zimene zili zovomerezedwa ndi Mulungu?

◻ Kodi zizindikiro zisanu ndi chimodzi zodziŵira chipembedzo chimodzi chokha cholondola nziti?

[Bokosi patsamba 10]

Mboni za Yehova . . .

◆ Ziphunzitso zawo zonse nzozikidwa pa Baibulo.

◆ Zimalambira Mulungu woona yekha, Yehova.

◆ Zimachita mogwirizana ndi chikhulupiriro chawo mwa Yesu Kristu.

◆ Sizimadziloŵetsa m’ndale ndi mikangano yadziko.

◆ Zimafuna kusonyeza chikondi chopanda dyera m’moyo wa tsiku ndi tsiku.

◆ Zimachirikiza Ufumu wa Mulungu monga yankho lachikhalire la mavuto a mtundu wa anthu.

[Chithunzi patsamba 9]

BAIBULO​—kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti lili ndi uthenga wa Mulungu kwa mtundu wa anthu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena