Mutu 14
Mmene Mungacidziwire Cipembedzo Coona
1. Kodi ncifukwa ninji kuli kwamaziko ndiponso Kwamalemba kunena kuti pali cipembedzo cimodzi cokha coona?
MWAMMAZIKO panayenera kukhalapo cipembedzo cimodzi cokha coona. Ici ciri cogwirizana ndi ceniceni cakuti Mulungu woona ndiye Mulungu, osati “wacisokonezeko koma wa mtendere.” (1 Akorinto 14:33) Kuonjezerapo, Yesu Kristu analankhula za awo amene amacigwiritsira nchito cipembedzo coteroco kukhala akumalambira mulungu “mumzimu ndi m’coonadi,” ndipo nthawi zonse coonadi sicimaombana cokha. (Yohane 4:23, 24) Koma kodi alambiri oona amenewa ndani lerolino? Kodi ndi motani mmene mungawadziwire iwo ndi kudziwadi kuti kulambira kwao kuli ndithudi kobvomerezedwa ndi Mulungu?
2. (a) Kodi onse amene amadzisonyeza kukhala Akristu amacicita cipembedzo coona? (b) Kodi ndi muyezo wotani umene Yesu anaupereka mwa umene tingawalekanitsire atumiki oona a Mulungu ndi onyenga?
2 Ici sicingazindikiridwe kokha pa maziko a zimene anthu ndi magulu amadzinenera kukhala. Mu ulaliki wace wa pa phiri, Yesu ananena kuti ambiri adzamucha iye “Ambuye, Ambuye,” akumanena kuti anacita zinthu zodziwika bwino m’dzina lace. Komabe iye adzanena kwa iwo kuti: “Sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika.” Osati mau okha komanso maonekedwe angakhale acinyengo kwambiri. Yesu ananena kuti aneneri onyenga adzadza atabvala zikopa za nkhosa, koma mkati mwao iwo anali mimbulu yolusa. Komabe, iye anatipatsa ife mlingo umene tingalekanitsire atumiki oona a Mulungu ndi onyengawo, kumati: “Mudzawazindikira ndi zipatso zao.” Iye anasonyeza kuti cimene kwenikweni cimatsimikizira ngati ife tiri alambiri oona a Mulungu siciri kokha kudzinenera kwathu kapena ngakhale nchito zathu zoyamikirika, koma kucicita kwathu cifuniro ca Atate wakumwambayo.—Mateyu 7:15-23.
3. Kodi ndi cenjezo lotani lokhazikitsidwa ndi mtumwi Paulo limene limasonyeza za kufunika kwa kusamala?
3 Mtsatiri wokhulupirika wa Yesu, mtumwi Paulo, nayenso anasonyeza za kufunika kwa kusamala. Iye anacenjeza kuti anthu ena adzaonekera kukhala ngati aministara a cilungamo ndipo komabe adzakhala Akristu onyenga. Mwa kuonekera kukhala ngati aministara a cilungamo ndipo komabe adzakhala Akristu onyenga. Mwa kuonekera kwao kwa kunja iwo sangaonekere kukhala oipa. Koma pamene ayezedwa mogwirizana ndi mmene Mau a Mulungu Baibulo, amanenera, iwo amaonekera kukhala atumiki a mdani wa Mulungu, Satana, pakuti nchito zao kwenikweni zimakhala zotsutsana ndi cifuniro ca Mulungu. (2 Akorinto 11:13-15) Kucitsatira kwathu citsogolero ca Akristu onyenga oterowo kungangotsogolera ku kutaya moyo wamuyaya.
KUGWIRITSIRA NCHITO MLINGOWO
4. Kodi cizindikiro cacikuru kwambiri ndi cotani ca alambiri oona a Mulungu?
4 Pamenepo, kodi ndi zina ziti za zizindikiro zowadziwikitsa alambiri oona a Mulungu? Kodi ndi zipatso zabwino zotani zimene iwo adzazibala? Baibulo limatiuza ife kuti “Mulungu ndiye cikondi.” Mogwirizana ndi ici, Yesu anasonyeza kuti cizindikiro cacikurukuru ca awo amene amacitsatira citsanzo cace m’kulambira Mulungu ndico cakuti iwo adzakhala ndi cikondi pakati pao. Iye anati: “Mwa ici adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli naco cikondano wina ndi mnzace.” (1 Yohane 4:8; Yohane 13:35) Kuti cikondi coteroco cikhaledi cizindikiro codziwikitsa, sicikangokhala kokha kumayesa kusonyeza kukhala wabwino kwa munthu wina ndi mnzace, kodi zingatero? Ciyenera kukhala cikondi cimene cimaiyambukira kwakukuru mbali iriyonse ya moyo wa munthu wa tsiku ndi tsiku. Ico ciyenera kumtsogoza munthuyo ponena za mmene amawakhalitsira mamemba enawo a m’banja lace. Ico ciyenera kukayambukira kalingaliridwe ka munthuyo kulinga kwa anthu a mitundu yina ndi mafuko. Alambiri oona a Mulungu amasonyeza cikondi, osangoti m’mau okha, komanso m’macitidwe. Iwo amafunafuna zimene ziridi zabwino kwa ena.—1 Yohane 3:18.
5. Kodi magulu a cipembedzo ndi mamemba ao akuoneka motani lerolino ponena za cizindikiro cacikuru cimeneci ca cipembedzo coona?
5 Kodi magulu a zipembedzo amene inuyo mumawadziwa alinaco cizindikiro ici ca kuwadziwikitsira? Kodi izo zimakhomereza mwa mamemba awo cikondi cimene ciri camphamvu kwambiri kwakuti cimakhalabe colimba ngakhale mu nthawi zobvuta? Mwacitsanzo, kodi nciani cimene izo zimacicita pamene kutukutira kwa pakati pa mitudndu yaudziko kutsogolera ku nkhondo? Zenizenizo zimasonyeza kuti kufikira tsopano zambirimbiri za izo zakhala zofunitsitsa kuti mamemba ao apite pa mabwalo a nkhondo ndi kukawapha akhulupiriri anzao a mtundu wina mwa kulamulira kwa anthu audziko. Kodi mukulingalira kuti kacitidwe kameneko kali kogwirizana ndi Mau a Mulungu ndipo kamasonyezadi mzimu wa Mulungu?—1 Yohane 3:10-12; Mateyu 5:44.
6. (a) Kodi pali anthu amene asonyeza cikondi ceniceni Cacikristu ngakhale mu nthawi za nkhondo za dziko? (b) Kodi ndi motani mmene cikondi caoco cakhalira coposa ndi kungopewa kokha kuwabvulaza ena?
6 Komabe, monga mudziwa, sikuti ali aliyense amene wakatsatira kacitidwe kameneka. Ena akhala okhoza kunena mogwirizana ndi mtumwi Paulo kuti: “Pakuti pakuyendayenda m’thupi, siticita nkhondo monga mwa thupi, pakuti zida za nkhondo yathu siziri za thupi.” (2 Akorinto 10:3, 4) Iwo sanakhale olakwa mwa kumanena bodza lakumati, “Ndikonda Mulungu,” pamene akudana ndi mbale wao wa mtundu wina. (1 Yohane 4:20, 21) Awo amene amamtsanziradi Yesu, samangokupewa kokha kuwabvulaza ena, komanso amasonyeza cikondi mu njira zina. Motani? Mwa kugwirizana kwao ndi Akristu anzao m’maiko onse, mwa njira imene amakhalira ndi anzao oyandikana nawo ndi mwa njira ya zoyesayesa zao zacikondi za kuwathandiza ena kuphunzira za Mulungu.—Agalatiya 6:10.
7. Kodi ndi lingaliro lotani ponena za Baibulo limene cipembedzo coona cimalisonkhezera, ndipo kodi ndi motani mmene Mwana wa Mulungu anakhazikitsira citsanzo mu ici?
7 Cizindikiro cina ca cipembedzo coona ndi ca awo amene amacigwiritsira ico nchito ndico kulabadira Mau a Mulungu. Mwana wa Mulungu pamene anali pa dziko lapansi anakhazikitsa citsanzo mu ici mwa kumasonyeza kulabadira kwakukurukuru kaamba ka Malemba ouziridwa. Iye anawagwira iwo mau monga magwero okha otsimikizirika pa zinthu. Iye mosalekeza anali kuwatsogoza amvetseri ace ku Mau a Mulungu, akumawalimbikitsa iwo kuwawerenga ndi kuwagwiritsira iwo nchito. (Mateyu 19:4-6; Luka 24:44, 45) Iye anasonyeza kulimvera kwace kwakukuru Baibulo mwa kumakhala mogwirizana ndi ziphunzitso zace tsiku ndi tsiku. Kukwaniritsidwa kwa mau a Mulungu kunali kofunika kwambiri kwa iye koposa moyo wacewace. (Mateyu 26:53-56) Iye sanaliluluze konse Baibulo; koma m’malo mwace, iye anawatsutsa awo amene analephera kuphunzitsa mogwirizana nalo ndi amene anayesa kulicotsera mphamvu yace mwa ziphunzitso zao zao.—Marko 7:9-13.
8. Kodi ndi manenedwe otani a akulu a mpingo a mu Cikristu ca Dziko amene amasonyeza kuti iwo sakucitsatira citsanzo ca Mwana wa Mulungu limodzi ndi atumwi ace mu nkhani iyi?
8 Kodi nciani cimene tingacinene mu nsonga iyi ponena za magulu ambiri a carici a mu Cikristu ca Dziko lerolino? Pamene muwamva kapena kuwawerenga mau onenedwa ndi akulu a mpingo amene amazichula mbali zina za Baibulo kukhala “nthanthi,” kapena amene amakonda ciphunzitso ca cisinthiko koposa ndi ciphunzitso ca Baibulo ca cilengedwe, kodi munganene kuti iwo akuwalimbikitsa anthu kuti aziwamvera Mau a Mulungu? Kapena pamene muwawerenga malongosoledwe mu amene atsogoleri a carici oterowo amene amanena kuti kugonana ukwati usanacitike sikuti ndi kolakwika, kapena kuti ngakhale kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha kungakhale koyenera kwenikweni, kodi munganene kuti iwo akuwalimbikitsa anthu kuligwiritsira nchito Baibulo monga citsogozo cao? Iwo ndithudi sakucitsatira citsanzo ca Mwana wa Mulungu limodzi ndi atumwi ace.—Mateyu 15:18, 19; Agalatia 5:19-21; Aroma 1:24-27.
9. Kodi ncifukwa ninji kulambira ngakhale kwa anthu ambiri amene ali ndi Baibulo sikuli komkondweretsa Mulungu?
9 Kodi zipatso zimene zimasonyezedwa m’miyoyo ya mamemba a macarici amenewa zimasonyeza kuti iwo amawamveradi Mau a Mulungu? Kucokera pa zimene inuyo muzidziwa, kodi munganene kuti anthu ambiri amene amapita ku nyumba za macarici pa tsiku la Sande amagwiritsira nchito maprinsipulo a Baibulo m’moyo wao panyumba pao ndiponso m’macitidwe ao ndi ena pa tsiku Lolemba ndiponso mkati mwa masiku enawo a pakati pa mlungu? Mau a Mulungu amasonyeza kuti pali anthu amene angakhale nalo Baibulo ndipo ngakhale kumaliphunzira kumene koma amene nchito zao zimatsimikizira kuti iwo amamkana Mulungu amene iwo amanena kuti amamdziwayo. (Tito 1:16; Yohane 5:39, 40) Kalambiridwe kamene iwo amakacitako sikamakhala komkondweretsa Mulungu, cifukwa cakuti samawalola Mau ace kukhala ndi mphamvu yeniyeni m’miyoyo yao.—2 Timoteo 3:5.
10. (a) Kodi ndi motani mmene tingadziwire kuti zipatso zoipazo sizimangowadziwikitsa anthu okhawo, komanso gulu la cipembedzolo? (b) Kodi ndi cosankha cofunika kopambana cotani cimene munthu ayenera kucipanga ngati wapeza kuti ziphunzitso za carici cace sizimagwirizana ndi Baibulo?
10 Poyamba munthu angalingalire kuti ali m’ministara mmodzi yekha amene amalakwa kapena mamemba a carici ena amene samacita bwino. Koma bwanji ngati m’ministara amene amaliluluza Baibuloyo amapitirizabe kukhala pa malo ace a nchitowo? Ndipo bwanji ngati mamemba a cariciwo amene amalakwa apitirizabe kukhala obvomerezeka ndi caricico? Pamenepo iyo ndiyo nthawi ya kukumana naco motsimikizira ceneceni cakuti zipatso zoipa zimalidziwikitsa gulu lacipembedzolo. Ngati zimenezo ziri zoona, mosapatulapo ciriconse, inu mudzapeza kuti ziphunzitso za gululo zonse pamodzi sizimagwirizana ndi Baibulo. Ngati mwaiwerenga mitu yapitayo ya bukhu ili ndipo mwawalingalira malemba a Baibulo amene akupezeka m’menemo, inu cimene mwagwirizana naco. Ngati ndi conco, pamenepo muli naco cothetsa nzeru cacikuru kwambiri. Ciri cothetsa nzeru ca kucipanga cosankha kaya ca kucilandira coonadi ca Baibulo kapena kucikana ico ndi kugwirizana ndi ziphunzitso zimene Baibulo silimazicirikiza. (Macitidwe 17:11) Ndithudi, cimene mungacicite ciyenera kukhala cosankha canucanu. Komabe, muyenera kupenda zinthu mosamalitsa, popeza kuti cosankha cimene mungacipangeco cidzakayambukira kaimidwe kanu ndi Mulungu ndiponso ziyembekezo zanu za moyo wamuyaya mu dongosolo latsopano.
11. (a) Kodi ndi motani mmene cipembedzo coona cimalionera dzina la Mulungu, monga momwe kwasonyezedwera ndi Yesu Kristu? (b) Cotero ngati tifuna kupeza cipulumutso tiyenera kucitanji?
11 Cofunika coonjezereka ca cipembedzo coona ndico cakuti ico ciyenera kuliyeretsa dzina la Mulungu. Cifukwa ninji? Cifukwa cakuti pamene Yesu Kristu anawaphunzitsa atsatiri ace mmene angapempherere, iye anawasonyeza iwo kuti icico cinayenera kukhala cinthu coyambirira m’maganizo mwao. Iye anati: “Cifukwa cace pempherani inu comweci: Atate wathu wa kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Ici cimatanthauza kulisunga dzinalo kukhala lopatulika, kumacita nalo monga cinthu coyera. Yesu mwiniyo anacicitadi ici. Iye sanalephere kuligwiritsira nchito dzina la Atate wacelo, ndipo iye sanacite nalo monga losafunika. Mosiyana ndi cimeneco, m’pemphero kwa Atate wace, Yesu anati: “ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa.” (Yohane 17:26) Iye anadziwa kuti cinali cifuno ca Mulungu cakuti dzina lace lilemekezedwe m’dziko lonse lapansi, ndipo iye anakhazikitsa citsanzo m’kumalilengeza ndi kumalilemekeza dzina limenelo. (Yohane 12:28; Yesaya 12:4, 5) ndiponso, Malemba amasonyeza kuti cifuno cacikuru coukhazikitsira mpingo umene Mulungu wauitana kuturuka m’dziko ndico cakuti ukhale “anthu a dzina lace.” (Macitidwe 15:14) Ngati mufuna kupulumutsidwa, inuyo, nanunso, muyenera kulidziwa ndi kulilemekeza dzina la Mulungu.—Aroma 10:13, 14.
12. (a) Kodi macarici onse amacikwaniritsa cofunika ici ca kulambira koona? (b) Kodi alipo alionse amene amacitira umboni za dzina la Mulungu?
12 Tsopano, taimani ndi kudzifunsa nokha kuti: Kodi ndi gulu la cipembedzo liti limene liri lodziwika kopambana kaamba ka kumalifalitsa dzina la Mulungu, monga momwe Yesu anacitira? Macarici onse amapewa kugwiritsira nchito dzina lakuti Yehova; ndipo, ngakhale kuli kwakuti ena mwa iwo amanena kuti amakonda kukagwiritsira nchito kachulidwe kakuti “Yahweh,” iwonso sikuti amaligwiritsira nchito limenelo. Ena afikira pa kumalicotsa dzina la Mulungu m’Mabaibulo amene atembenuzidwa ndi iwo. Mwacitsanzo, Revised Standard Version, limene tsopano likufalitsidwa ndi cicirikizo ca Aprotestanti ndi Akatolika, dzina la Yehova linacotsedwamo kotheratu, ngakhale kuli kwakuti limaonekera m’malemba oyambirirawo Acihebri cifupifupi nthawi zikwi zisanu ndi ziwiri. Kodi magulu amenewa akuzikwaniritsa zofunika za cipembedzo coona? Kwenikwenidi, kodi ndi gulu liti limene limacitira umboni za dzina la Mulungu, monga momwe anacitira Yesu? (Cibvumbulutso 1:5; Yesaya 43:10-12) Ngati inu munali kulankhula ndi anthu okhala cifupi nanu ndipo munali kuchula mobwerezabwereza dzina lakuti Yehova, mukumaligwiritsira nchito dzina lace lopatulikalo, kodi mukugainza kuti iwo adzakugwirizanitsani inu ndi gulu liti? Limenelo sindilo funso lobvuta kuliyankha. Pali gulu la anthu limodzi lokha limene modziwika bwino limacitsatira citsanzo ca Yesu mu nsonga iyi.
13. (a) Kodi alambiri oona ayenera kubvomereza kuti ciyembekezo cokha ca mtundu wa anthu nciani? (b) Kodi amacicita ici motani?
13 Alambiri oona amaulengezanso ufumu wa Mulungu monga ciyembekezo cokha coona ca mtundu wa anthu. Iwo sangaleke kucita ici nakhalabe omamkondweretsa Yehova Mulungu, cifukwa cakuti iye walongosola momvekera bwino kuti Ufumuwo ndiwo makonzedwe ace a kulitsogozera dziko lapansi. (Danieli 2:44; 7:13, 14) Yesu anakhazikitsa cisanzo mu ici mwa kumapita ku mapeto ndi mapeto a dzikolo “akumalalikira ndi kumabukitsa mbiri yabwino ya ufumu wa Mulungu.” (Luka 8:1, NW) Iye limodzi ndi atumwi ace anacicita ici mwa kumapita ku mudzi ndi mudzi ndi “kunyumba ndi nyumba.” (Macitidwe 20:20, NW) Yesu ananeneratunso kuti ‘m’masiku otsiriza’ awa “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu” idzalalikidwa pa dziko lonse lapansi kaamba ka umboni.—Mateyu 24:14, NW.
14. (a) M’malo mwa kuubvomereza ufumu wa Mulungu, kodi kawirikawiri timawamva atsogoleri acipembedzo akumalankhula ndi kupempherera moyanja ciani? (b) Kodi ndi ayani amene amadza pa khomo lanu akulalikira za Ufumuwo monga ciyembekezo coona ca mtundu wa anthu?
14 Lerolino kwawirikawiri timawamva atsogoleri acipembedzo akumalankhula mocirikiza magulu a ndale za dziko monga ngati Mitundu Yogwirizana ndi kuwapempherera iwo. Koma kodi ndani amene akukucita kulalikira kwa mbiri yabwinoyo yonena za ufumu wa Mulungu monga momwe Yesu ananeneratu? Ngati wina adza pa khomo lanu kapena pa khomo la nyumba imene mwayandikana nayo ndipo mumumva iye akulankhula za ufumu wa Mulungu kukhala ciyembekezo cokha coona ca mtundu wa anthu, kodi munthu ameneyo mumamgwirizanitsa ndi gulu liti? Iye ndiyo nchito yaikuru ya awo amene amacicita kwenikweni cifuniro ca Atate wakumwambayo pomtsanzira Mwana wace Yesu.—1 Petro 2:21.
15. Tacichulani cofunika cina ca cimpembedzo coona, monga momwe kwalongosoledwera pa Yakobo 1:27.
15 Komabe cofunika cina ca cipembedzo coona ndico cakuti ico cimadzipatula ku dziko limodzi ndi zocitika zace. Baibulo, pa Yakobo 1:27, limasonyeza kuti, ngati kulambira kwathu kungakhale kopanda ucisi ndi kosadetsedwa pamaso pa Mulungu, ife tiyenera kukhala “opanda mawanga ndi dziko lapansi.” Iyi iri nkhani yofunika kwambiri, pakuti, “iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.” (Yakobo 4:4, NW) Inu mungazindikire mmene icico cakhalira cofunika kopambana pamene mukumbukira kuti Baibulo limanena kuti wolamulira wa dzikoli ali mdani wamkuru wa Mulungu, Satana Mdierekezi.—Yohane 12:31.
16. Kucokera pa zimene mwazionazo, kodi macarici a kwanuko, limodzi ndi mamemba ao, sialidi “a dziko lapansi”?
16 Kodi zenizeni zimasonyeza kuti macarici amene ali m’dera lanu amacilabadira cimeneci? Kodi akulu a mpingo, kuphatikizaponso mamemba a mipingoyo, salidi “a dziko lapansi,” monga momwe Yesu ananenera kuti atsatiri ace oona adzatero? (Yohane 15:19) Kapena kodi iwo alowa kwambiri mu zocitika za dziko ili, mu utundu wace, mu ndale zadziko zace ndi kulimbirana kwace kuchuka? Simukutofunikira wina kuti akuyankhireni mafunso amenewa. Zocita za macarici ziri zodziwika kwambirimbiri, ndipo mukudziwa zimene zikucitika m’menemo. Ngati muli anthu m’malo akwanuwo amene, cifukwa ca cipembedzo cao, amawakana macitacita amenewo, mosakaikira inu mukudziwanso za amene iwowo ali.
17. (a) Kuti cikhale cipembedzo coona, kodi cipembedzo ciyenera kugwirizana ndi zofunika zimenezi zingati? (b) Monga momwe kwasonyezedwa kucokera m’Baibulo, kodi pali zipembedzo zoona zingati?
17 Tsopano, titatha kuzichula zizindikiro zodziwikitsa zimenezi ponena za cipembedzo coona cimene Mulungu wacipereka kaamba ka ife m’Mau ace, kodi ife tidzacitanji? Nsonga yofunika imene tikuikambitsiranayo sindiyo kaya ngati gulu lina lacipembedzo limaonekera kuti likucikwaniritsa cimodzi kapena ziwiri za zofunika zimenezi, kapena kaya ngati zina za ziphunzitso zace zimagwirizana ndi Baibulo. Koposa zimenezo, cipembedzo coona ciyenera kuzikwaniritsa mbali zonsezi ndipo ziphunzitso zace zonse ziyenera kukhala zogwirizana ndi Mau a Mulungu. Kuli kokha mwa njira iyi kuti cipembedzo coteroco cingakhale comkondweretsa Yehova mulungu. Palibe zipembedzo zambiri zimene zimazikwaniritsa zofunika izi. Baibulo limasonyeza kuti pali “cikhulupiriro cimodzi” cokha.—Aefeso 4:5.
18. (a) Mogwirizana ndi umboni umene ulipowo, kodi bukhu ili limasonyeza kuti alambiri oona lerolino ndi ayani? Kodi zimenezo ndizo zimene inunso mumazikhulupirira? (b) Kodi njira ya kuzidziwira bwino mboni za Yehova ndi yotani?
18 Pamenepo, kodi ndi ayani amene amalipanga gulu la alambiri oona lerolino? Pa maziko a umboni, umene uli wodziwika kapena umene anthu ambiri ali nao m’mbali zonse za dziko lapansi, ife sitikukaikira kunena kuti iwo ali mboni Zacikristu za Yehova. Kuti inu mukhale ndi citsimikiziro coteroco inu mufunikira kuzolowerana nazo. Njira yabwino kwambiri ndiyo ya kupita pa misonkhano ya pa King’idomu Holo ya Mboni za Yehova. Mu njira iyi inu mungadzionere inu mwini za mmene gulu limeneli limagwirira nchito ndi njira mu imene awo amene ali ogwirizana nalo amawagwiritsirira nchito Mau a Mulungu m’miyoyo yao. Popeza kuti Mulungu amatitsimikizira ife kuti kumacigwiritsira nchito cipembedzo coona kumapereka cikhutiro cacikuru tsopanolino ndiponso kumalitsegula khomo la ku moyo wamuyaya mu dongosolo lace latsopano la zinthu, ndithudi kudzakhala kokupindulitsani inu kukupanga kufufuza koteroko. (Deuteronomo 30:19, 20) Ife tikukufunsani motenthedwa mtima kuti mutero. Bwanji osafufuzafufuza tsopano lino?