Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • tr mutu 2 tsamba 11-16
  • Cifukwa Cace Muyenera Kuciyesa Cipembedzo Canu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Cifukwa Cace Muyenera Kuciyesa Cipembedzo Canu
  • Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Nkhani Yofanana
  • Chipembedzo Chanu Chiridi Nkanthu
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kulambira Kumene Mulungu Amavomereza
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Mmene Mungacidziwire Cipembedzo Coona
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi Mwapeza Chipembedzo Cholondola?
    Nsanja ya Olonda—1994
Onani Zambiri
Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
tr mutu 2 tsamba 11-16

Mutu 2

Cifukwa Cace Muyenera Kuciyesa Cipembedzo Canu

1. (a) Popeza kuti Mulungu posacedwapa adzaliononga dongoili la zinthu, kodi ndi funso lotani limene ife tifunikira kulifunsa ponena za kulambira kwathu? (b) Ngati tifuna kukatsatira kacitidwe kamene Mulungu amakabvomereza, kodi tidzapita ku bukhu liti?

TIRI NDI cifukwa cabwino ca kulingalirira mosamalitsa ponena za kaimidwe kathu ndi Mulungu. Cifukwa ninji? Cifukwa cakuti umboniwo umatsimikizira kuti Mulungu posacedwapa adzawaononga oipa ndi kukhazikitsa dongosolo lace latsopano lolungama. Cotero tifunikira kufunsa kuti: “Kodi ndikumlambira Mulungu mu njira imene iye amaibvomereza?” Sali munthu aliyense, koma Mulungu, amene ali wocisankha cimene cimamkondweretsa iye. Kuti tikhale ndi lingaliro la Mulungu, tifunikira kupita ku Baibulo. Kumeneko iye amatiuza ife mwacimvekere za njira imene tingaitsatire ngati tifuna kupeza moyo wamuyaya. (Miyambo 3:1, 2) Ngati ticikumbukira cimene iye amanena ndi kucigwiritsira ico nchito m’miyoyo yathu, ico cidzatidzetsera ife madalitso ozizwitsa, ponse pawiri tsopano ndi mu nthawi imene ikudzayo.

2. Kodi ndi kalongosoledwe kotani m’Baibulo kamene kamasonyeza kuti siziri zipembedzo zonse zimene zimamkondweretsa Mulungu?

2 Pamene ticipenda cimene Baibulo limanena pa nkhani imeneyi, kodi tikupezanji? Kodi limaphunzitsa kuti mazana mamiliyoni ocuruka a anthu amene amacigwiritsira nchito cipembedzo mu njira zocuruka zosiyanasiyana onsewo ali omkondweretsa Mulungu? Kodi limasonyeza kuti cipembedzo ciriconse ciri cabwino? Kutitheketsa ife kuti tidziwe mmene iye amailingalirira nkhaniyo, Mulungu anawapangitsa mau omvekera bwino awa kulembedwa m’Mau ace: “Cipata ciri cacikuru, ndi njira ya kumuka nayo ku kuonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa ico. Pakuti cipata ciri copapatiza, ndi icepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akucipeza cimeneco ali owerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Ha, ndi motani nanga mmene mau amenewo akuwayankhira mafunso athuwo momvekera bwino! Iwo akusonyeza kuti anthu ambiri sakumlambira Mulungu mu njira imene imamkondweretsa iye. Ali owerengeka okha amene ali pa njira yopita ku moyo.

3. Kodi ziripo zinthu zocitidwa m’dzina la cipembedzo zimene zimumazibvomereza?

3 Mwina mwace inu mudzadzipeza inu mwini mukumabvomerezana ndi ceniceni cakuti zipembedzo zambiri siziri zobvomerezeka ndi Mulungu. Mosakaikira pali zinthu zambiri zimene zimacitidwa m’dzina la cipembedzo zimene inu simungazibvomereze. Mwacitsanzo, ngati muunguzaunguza m’macarici ndi kuwapenyerera anthu amene amakhala m’moyo wacisembwere koma namadzisonyeza kukhala olungama, inu mumadziwa kuti kanthu kena kali kolakwika. (2 Timoteo 3:4, 5) Ndipo pamene muwerenga mu nyuzipepa kuti akulu a mpingo ena akukubvomereza mwapoyera kugonana kwa pakati pa anthu awiri osakwatirana ndi kuti iwo akunena kuti kugonana amuna kapena akazi okhaokha kuli bwino pansi pa mikhalidwe ina, inu mumazindikira bwino lomwe kuti icico sindico cimene Mulungu amanena. Inu mungakumbukire kuti Mulungu anaononga mizinda yakale ya Sodomu ndi Gomora. Ndipo ncifukwa ninji? Cifukwa cakuti iwo anali kucita zinthu zimenezo! Cotero inu mukudziwa kuti Mulungu sadzacibvomereza cipembedzo cimene cimawauza anthu kuti kuli bwino kucita motero.—Yuda 7.

4. (a) Kuonjezera pa kukhala kwathu a cikhalidwe cabwino ndi okoma mtima, kodi ndi cinanso ciani cimene tiyenera kucilingalira ponena za cipembedzo cathu, pomalingalira za mau a Yesu a pa Yohane 4:23? (b) Ncifukwa ninji tifunikira kuzipenda ziphunzitso zimene taphunzitsidwa?

4 Komabe, mosakaikira inu mwawamva anthu akumanena kuti: “Palibe kanthu ponena za cimene mumacikhulupirira, kokha pamene mukhala ndi cikhalidwe cabwino ndi kucita mokoma mtima ndi okhala cifupi nanu.” Koma kodi ndi zokhazo zimene ziripo ponena za kumlambira Mulungu mu njira yobvomarezeka? Zinthu izi ziri zoyenerera, koma Mulungu amafuna zambiri. Ziphunzitso zikuphatikizidwaponso. Baibulo limatilangiza ife kuti “olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’coonadi.” (Yohane 4:23) Ngati kulambira kwanu kuti kukhale kobvomerezeka kwa Mulungu, uko kuyenera kuzikidwa mizu molimba m’Mau a Mulungu a coonadi. Yesu anawadzudzula anthu awo amene anali kuumirira kuti anali kutumikira Mulungu koma amene anadalira kwakukurukuru pa miyambo ya anthu ndi kusiya Mau a Mulungu. Iye anawagwiritsira nchito pa iwo Mau a Mulungu mwiniyo ocokera pa Yesaya 29:13, kumati: “Koma andilambira Ine kwacabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.” (Mateyu 15:9) Popeza kuti sitikufuna kuti kulambira kwathu kukhale kwacabe, kuli kofunika kuti aliyense wa ife acipende cipembedzo cace.

5. Kodi ncifukwa ninji tinayenera kupenda, osangoti kokha zikhulupiriro zathu zaumwini, komanso ziphunzitso za gulu lirilonse lacipembedzo limene tingakhale titagwirizana nalo?

5 Ife tifunikira kupenda, osangoti kokha cimene ife enife timacikhulupirira, komanso cimene cimaphunzitsidwa ndi gulu lirilonse lacipembedzo limene ifeyo tagwirizana nalo. Kodi ziphunzitso zace ziri zogwirizana kotheratu ndi Mau a mulungu, kapena kodi izo zazikidwa pa miyambo ya anthu? Ngati tiri okonda coonadi, palibe cimene tingaciope pa kupenda koteroko. Ciyenera kukhala cikhumbo coona mtima ca aliyense wa ife kuciphunzira cimene cifuniro ca Mulungu ciri kaamba ka ife, ndiyeno ndi kucicita ico.—Yohane 8:32.

6. (a) Kodi ceniceni cakuti Baiblulo limagwiritsiridwa nchito mwa kamodzikamodzi m’carici cimatsimikizira kuti ziphunzitso zonse za carici ziri zocokera m’Baibulo? (b) Kodi ncifukwa ninji cipembedzo cobvomerezedwa ndi Mulungu ciyenera kugwirizana mwa tsatanetsatane ndi Baibulo?

6 Ceniceni cokha cakuti mamemba a carici angakhale ndi Baibulo kapena kuti ilo mwa kamodzikamodzi limawerengedwera kwa iwo kucokera pa gome mwa iko kokha sikumatsimikizira kuti zinthu zonse zimene amaphunzitsidwa ziri zocokera m’Baibulo. Kuli bwino kukhala nalo Baibulo; munthu aliyense anayenera kukhala nalo. Komanso tiyenera kucidziwa cimene ilo limanena ndi kucikhulupirira. Ngati cipembedzo cimalilandiradi Baibulo monga mau a Mulungu, ico sicidzangogwiritsira nchito kokha mbali zina za ilo ndi kuzikana mbali zina. “Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa ciphunzitso, citsutsano, cikonzero, cilangizo ca m’cilungamo.” (2 Timoteo 3:16) Popeza kuti izi ziri tero, cipembedzo cimene ciri cobvomerezedwa ndi Mulungu ciyenera kukhala cogwirizana m’kacitidwe kace konse ndi Baibulo.

7. Monga momwe kwasonyezedwera ndi mtumwi Paulo, kodi kuona mtima kwa olambirawo mwa iko kokha kumasonyeza kuti cipembedzo cao ciri cobvomerezedwa ndi Mulungu?

7 Munthu amene amafuna kumkondweretsa Mulungu ayenera kukhala woona mtima. Koma kuona mtima kokha sikumacipangitsa cipembedzo ca munthuyo kukhala cobvomerezeka m’maso mwa Mulungu. Mtumwi Paulo anasonkhezeredwa ndi mzimu wa mulungu kulemba ponena za ena a m’tsiku lacelo: “Pakuti ndiwacitira iwo umboni kuti ali ndi cangu ca kwa Mulungu, koma si monga mwa cidziwitso. Paukuti pakusadziwa cilungamo ca kwa Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa cilungamo ca iwo okha, iwo sanagonja ku cilungamo ca Mulungu.” (Aroma 10:2, 3) Mwa coturukapo ca cimeneco, kuona mtima kwao kunali mu njira yolakwika. Cothetsa nzeru cao cinali cakuti iwo anali kuyembekezera ku njira yolakwika kaamba ka cilangizo. Iwo anamamatira ku dongosolo lacipembedzo Caciyuda, limene linali litamkana Mwana wa Mulungu ndipo nalonso linakanidwa ndi Mulungu.—Macitidwe 2:36, 40; Miyambo 14:12.

8. Kodi ndi motani mmene Yesu Kristu anasonyezera kuti siziri zipembedzo zonse zimene zimaumilira kukhala Zacikristu zimene zimabvomerezedwa ndi Mulungu?

8 Pamenepo, bwanji ponena za zipembedzo zimene zimaligwiritsira nchito dzina la Kristu ndi kusonyeza kuti zimamlandira iye kukhala mbuye wao? Kodi kulalikira kwaoko m’dzina lace kumatsimikizira kuti iwo amakhala ndi cibvomerezo ca Mulungu? Pomalingalira za malemba amene akambitsiridwa kalewo, kapena inu mwaona kuti iwo samakhala naco. Ngati kuli tero, pamenepo pa nkhani iyi inu mukubvomerezana ndi Yesu Kristu, amene Mulungu wamsankha kukhala woweruza wakumwamba; cifukwa cakuti iye amaticenjeza ife, kumati: “Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakucitayo cifunira ca Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye kodi sitinanenera mau m’dzina lanu . . .? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; cokani kwa Ine, inu akucita kusayeruzika.”—Mateyu 7:21-23.

9. Kuonjezera pa cidziwitso ca Baibulo ndi cianinso cimene cikufunika kuti cipembedzo ca munthu cikhale cokondweretsa kwa Mulungu?

9 Cidziwitso ca Baibulo ndi ca cifuniro ca Mulungu ciri cofunika kaamba ka cibvomerezo ca Mulungu. Koma, monga momwe Yesu ananenera, kuli kucicita cifuniro cimeneco kumene kuli kanthu. Munthu ayenera kukhala ndi nchito zimene ziri zogwirizana ndi cimene munthuyo waciphunzira. (Yakobo 2:26) Pamenepo, kuti Mulungu akondweretsedwe, cipembedzo ca munthuyo ciyenera kukhala cogwirizana kotheratu ndi Baibulo ndi kugwiritsidwa nchito mbali iri yonse ya moyo.—Luke 6:46-49.

10. Kodi ndi zipatso zotani zimene cipembedzo coona cidzazibala m’miyoyo ya awo amene amacicita ico?

10 Yesu ananena kuti inu mungazindikire ngati munthu akucicita cipembedzo coona mwa “zipatso” zace, ndiko kuti, zinthu zimene amazicita. (Mateyu 7:20) Mu njira imodzimodziyo, tingacizindikire cipembedzo mwa mtundu wa anthu umene ico cimawaturutsa. Cipembedzo coona ciyenera kuturutsa anthu—amuna okwatira ndi atate abwino, akazi okwatiwa ndi azimai abwino. Ico ciyenera kuwaturutsa anthu amene ali oona mtima, amene amasiyana ndi ena cifukwa cakuti iwo amacicita cimene ciri coyenera. Kodi cimeneco sindico cimene munayenera kuciyembekezera mu cipembedzo cimene cimamuyandikizitsa munthu cifupi ndi Mulungu? Mulungu amafunafunanso zinthu zimenezi, ndipo izo zimacitsimikizira ngati cipembedzo ciri cobvomerezeka ndi Mulungu kapena ai.

11. Kodi ndi kacitidwe kotani kamene kanatsatiridwa ndi Abereya akale kamene ife tidzacita bwino kukatsatira?

11 Ndithudi inu simukufuna kuikidwa pa mpambo umodzi ndi awo amene akukanizidwa kulowa mu ufumu wa Mulungu cifukwa ca kulephera kucicita cifuniro ca Mulungu. Pamenepo, kudzakhala kokupindulitsani inuyo, kuzolowerana ndi Baibulo. Bukhu limene mukuliwerenga tsopanoli lapangidwira kukuthandizani inu kuti mucicite cimeneco. Katsatireni kacitidwe ka Abereya akale amenewo amene Mau a Mulungu amawayamikira cifukwa cakuti iwo “analandira mau ndi kufunitsa kwa mtima wonse, nasanthula m’malembo masiku onse, ngati zinthu zinali zotero.”—Macitidwe 17:11.

12. (a) Kodi ndi motani mmene cikondi cathu kaamba ka Mulungu cingayesedwere, kapena ndi mabwenzi ndi acinansi? (b) Kodi nthawi zonse tinayenera kufunafuna cibvomerezo ca ndani?

12 Pamene muwapenda Mau a Mulungu, inu mudzazindikira kuti cikondi canu kaamba ka mulungu cidzayesedwa. Pangakhale anthu ena, kapena ngakhale mabwenzi enieni apamtima kapena anansi, amene sadzakubvomereza kuwapenda kwanu Malembako. (1 Petro 4:4; Mateyu 10:36, 37) Iwo angayese kukulefulani inu. Iwo angacicite ici moona mtima, cifukwa cakuti sakucidziwa coonadi cozizwitsa cimene cikupezeka m’Baibulo. Kapena mungawathandize iwo. Mu zocitika zina citsutsoco cingadzere kwa anthu amene samamkonda Mulungu. Ngati cimeneci citacitika, kumbukirani kuti, kukhala ndi cibvomerezo ca Mulungu kuli kofunika kopambana koposa ndi kukhala ndi cibvomerezo ca anthu. Ali Mulungu, osati munthu, amene adzakupatsani inu moyo wamuyaya ngati mumkonda iye koposa kanthu kalikonse ndiponso munthu aliyense.—Mateyu 22:37-39.

13. Ngati tifunafuna kucita cifuniro ca Mulungu, kodi tinayenera kupemphera za ciani?

13 Nthawi zonse yang’anani kwa Mulungu kaamba ka cithandizo cace ndi citsogozo. Pitirizanibe kupemphera, monga momwe anacitira wamasalmoyo: “Imvani pemphero langa, Yehova; . . . Mundiphunzitse cokonda Inu; popeza inu ndinu Mulungu wanga.” (Salmo 143:1, 10 [142:1, 10, Dy]) Ngati inu moona mtima mumafuna kucidziwa ndi kucicita cipembedzo cimene iye amacibvomereza, iye adzayankha pemphero lanulo. Ndipo iye adzakuyanjanitsani ndi awo amene amalambiradi “Atate mumzimu ndi m’coonadi.”—Yohane 4:23; onaninso Mateyu 7:7, 8.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena