Mutu 3
Chipembedzo Chanu Chiridi Nkanthu
1. Kodi anthu ena amakhulupiriranji ponena za chipembedzo?
ZIPEMBEDZO ZONSE nzabwino,’ anthu ambiri amatero. ‘Izo zangokhala misewu yosiyanasiyana yopita kumalo amodzi.’ Ngati zimenezi zikanakhala zowona, chipembedzo chanu sichikanakhaladi nkanthu, pakuti kukanatanthauza kuti zipembedzo zonse nzovomerekeza kwa Mulungu. Koma kodi nzotero?
2. (a) Kodi ndimotani mmene Afarisi anachitira ndi Yesu? (b) Kodi Afarisi anatcha yani kukhala atate wawo?
2 Pamene Yesu Kristu anali padziko lapansi, panali gulu lachipembedzo lotchedwa Afarisi. Iwo adapanga dongosolo la kulambira ndipo anakhulupirira kuti linali ndi chivomerezo cha Mulungu. Komabe, pa nthawi imodzimodziyo, Afarisi anali kuyesa kupha Yesu! Motero Yesu anawauza kuti: “Inu muchita ntchito za atate wanu.”M’kuyankha iwo anati: “Tiri naye Atate mmodzi ndiye Mulungu.”—Yohane 8:41.
3. Kodi Yesu ananenanji ponena za atate wa Afarisi?
3 Kodi Mulungu analidi atate wawo? Kodi Mulungu analandira mpangidwewawo wa chipembedzo? Kutalitali! Ngakhale kuli kwakuti Afarisi anali ndi Malemba naganiza kuti iwo anali kuwatsatira, iwo adasochezedwa ndi Mdyerekezi. Ndipo Yesu anawauza motero, kuti: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’chowonadi, . . . ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.”—Yohane 8:44.
4. Kodi ndimotani mmene Yesu anawonera chipembedzo cha Afarisi?
4 Mwachiwonekere, chipembedzo cha Afarisi chinali chonyenga. Chinatumikira zabwino za Mdyerekezi, osati Mulungu. Motero koposa ndi kuwona chipembedzo chawo kukhala chabwino, Yesu anachitsutsa. Kwa Afarisi achipembedzo amenewo iye anati: “Mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pawo; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo mwawaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.” (Mateyu 23:13) Chifukwa cha kulambira kwawo konyenga, Yesu anatcha Afarisi amenewo onyenga ndi njoka zaululu. Chifukwa cha njira yawo yoipa, iye ananena kuti iwo anali kupita ku chiwonongeko.—Mateyu 23:25-33.
5. Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera kuti zipembedzo zambirizo siziri chabe misewu yosiyanasiyana yopita kumalo amodzi?
5 Motero Yesu Kristu sanaphunzitse kuti zipembedzo zonse zangokhala misewu yosiyanasiyana yopita kumalo amodzi a chipulumutso. Mu Ulaliki wake wotchuka wa pa Phiri, Yesu anati: “Lowani pachipata chopapatiza; chifukwa chipata chiri chachikulu, ndi njira yakumuka nayo kukuwonongeka iri yotakata; ndipo ali ambiri amene alowa pa icho. Pakuti chipata chiri chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali owerengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Chifukwa chakuti iwo akulephera kulambira Mulungu m’njira yoyenera, anthu ochuluka ali panjiraya ku chiwonongeko. Owerengeka okha ali panjira yopita ku moyo.
6. Kodi tingaphunzirenji mwa kupenda kulambira kwa mtundu wa Israyeli?
6 Kupenda mmene Mulungu anachitira ndi mtundu wa Israyeli kumapangitsa kuwonekera bwino mmene kuliri kofunika kulambira Mulungu m’njira imene iye amavomereza. Mulungu anachenjeza Aisrayeli kuti asagwirizane ndi chipembedzo chonyenga cha mitundu yowazinga. (Deauteronomo 7:25) Anthu amenewo anapereka nsembe ana awo kwa milungu yawo, ndipo iwo anachita machitidwe onyansa akugonana, kuphatikizapo kugonana kwa amuna okhaokha. (Levitiko 18:20-30) Mulungu analamulira Aisrayeli kupewa machitidwe amenewa. Pamene iwo sanamvere ndi kulambira milungu ina, iye anawalanga. (Yoswa 24:20; Yesaya 63:10) Motero chipembedzo chawo chinalidi nkanthu.
CHIPEMBEDZO CHONYENGA LEROLINO?
7, 8. (a) Kodi ndilingaliro lotani limene chipembedzo chinatsatira mkati mwa nkhondo zadziko? (b) Kodi mukuganiza kuti Mulungu akumva bwanji ndi zimene chipembedzo chachita mkati mwa nthawi yankhondo?
7 Bwanji ponena za mazana ambiri a zipembedzo lerolino? Mwina mwake mukuvomereza kuti zinthu zambiri zochitidwa m’dzina la chipembedzo sizimavomerezedwa ndi Mulungu. Mkati mwa nkondo zadziko zaposachedwapa, zimene mamiliyoni ambiri a anthu okhala ndi moyo tsopano anapulumuka, zipembedzo kumbali ziwiri zonse zinalimbikitsa mtundu wawo kupha. “Iphani Ajeremani—apheni,” anatero bishopu wa ku London. Ndipo, ku mbali inayo, atchibishopu wa Cologne anauza Ajeremani kuti: “Tikukulamulirani m’dzina la Mulungu, menyani nkhondo kufikira dontho lotsiriza la mwazi wanu kaamba ka ulemu ndi ulemerero wa dziko.”
8 Motero Akatolika anapha Akatolika movomerezedwa ndi atsogoleri awo achipembedzo, ndipo Aprotesitanti anachita zomwezo. Mtsogoleri wachipembedzo Harry Emerson Fosdick anavomereza kuti: “Ngakhale m’matchalitchi athu taika mbendera zankhondo. . . Ndi mbali imodzi ya pakamwa pathu tatamanda Kalonga wa Mtendere ndipo ndi inayo talemekeza nkhondo.” Kodi mukuganiza kuti Mulungu akumva bwanji ndi chipembedzo chimene chimadzitcha kukhala chikuchita chifuniro chake koma chimalemekeza nkhondo?
9. (a) Kodi ndimotani mmene anthu ambiri alingalirira ponena za maupandu ochitidwa ndi ziwalo za zipembedzo zosiyanasiyana? (b) Pamene chipembedzo chidzipanga kukhala mbali ya dziko, kodi tiyenera kunenanji?
9 Chifukwa cha maupandu ochitidwa m’dzina la Mulungu ndi ziwalo za zipembedzo zambiri zosiyanasiyana mkati mwa mbiri yonse, mamiliyoni ambiri a anthu lerolino afulatira Mulungu ndi Kristu. Iwo amaimba Mulungu mlandu chifukwa cha nkhondo zowopsa zachipembedzo, monga ngati zija za pakati pa Akatolika ndi Asilamu zotchedwa Nkhondo Zamtanda, nkhondo za pakati pa Asilamu ndi Ahindu, ndi nkhondo za pakati pa Akatolika ndi Aprotesitanti. Iwo amasonya kuphedwa kwa Ayuda m’dzina la Kristu, ndi zilango Zachikatolika zankhanza. Komabe, ngakhale kuli kwakuti atsogoleri achipembedzo ochititsa maupandu owopsa oterowo anatcha Mulungu kukhala Atate wawo, kodi iwo sanali kwenikweni ana a Mdyerekezi mofanana ndi Afarisi amene Yesu anatsutsa? Popeza kuti Satana ndiye mulungu wa dziko lino lapansi, kodi sitiyenera kuyembekezera kuti iye amalamuliranso zipembedzo zochitidwa ndi anthu a dziko lapansi?—2 Akorinto 4:4; Chivumbulutso 12:9.
10. Kodi ndizinthu zina zotani zochitidwa m’dzina la chipembedzo zimene simukuzivomereza?
10 Mosakayikira pali zinthu zambiri zochitidwa m’dzina la chipembedzo lerolino zimene simukuganiza kuti nzabwino. Kawirikawiri mungamve ponena za anthu amene ali ndi mkhalidwe oipa kwambiri, koma amene ali ziwalo zolemekezeka za matchalitchi. Mungadziwedi atsogoleri achipembedzo amene ali ndi kakhalidwe koipa kwambiri, koma amene akulandiridwabe monga atsogoleri achipembedzo abwino m’matchalitchi awo. Atsogoleri ena achipembedzo anena kuti kugonana kwa amuna okhaokha ndi kugonana popanda kukwatirana sizolakwa. Koma mungadziwe kuti Baibulo silimatero. Kunena zowona, Mulungu anachititsa anthu ake a Israyeli kulangidwa ndi imfa chifukwa chakuti iwo anachita zinthu zoterozo. Kaamba ka chifukwa chimodzimodzicho iye anawononga Sodomu ndi Gomola. (Yuda 7) Posachedwapa iye adzachita zimodzimodzizo ku chipembedzo chonyenga chamakono. M’Baibulo chipembedzo choterocho chikuphiphiritsiridwa kukhala mkazi wachigololo chifukwa cha chigololo chake ndi “mafumu a dziko lapansi.”—Chivumbulutso 17:1, 2, 16.
KULAMBIRA KUMENE MULUNGU AMAVOMEREZA
11. Kodi nchiyani chimene chikufunika ngati kulambira kwathu kuti kukhale kolandirika kwa Mulungu?
11 Popeza kuti Mulungu samavomereza zipembedzo zonse, tifunikira kufunsa kuti: ‘Kodi ine ndikulambira Mulungu m’njira imene amavomereza?’ Kodi tingadziwe bwanji ngati tikutero? Simunthu aliyense, koma Mulungu, amene ali wodziwa chimene chiri kulanbira kowona. Motero ngati kulambira kwanthu kuti kulandiridwe ndi Mulungu, kuyenera kuzikidwa zolimba m’Mawu a Mulungu a chowonadi, Baibulo. Tiyenera kulingalira mofanana ndi wolemba Baibulo amene anati: “Mulungu akhale wowona, ndipo anthu onse akhale onama.”—Aroma 3:3, 4.
12. Kodi nchifukwa ninji Yesu ananena kuti kulambira kwa Afarisi sikunavomerezedwe ndi Mulungu?
12 Afarisi a m’zaka za zana loyamba sanalingalire motero. Iwo anakhazikitsa zikhulupiriro zawozawo ndi miyambo natsatira zimenezi koposa Mawu a Mulungu. Limodzi ndi chotulukapo chotani? Yesu anawauza kuti: “Inu mupeputsa mawu a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu. Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yawo; koma mtima wawo uli kutali ndi Ine. Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.” (Mateyu 15:1-9; Yesaya 29:13) Motero ngati tikufuna chivomerezo cha Mulungu, nkofunika kuti titsimikizire kuti zimene tikukhulupirira nzogwirizana ndi ziphunzitso za Baibulo.
13. Kodi Yesu anati tiyenera kuchitanji kuti tivomerezedwe ndi Mulungu?
13 Sikokwanira kwa ife kunena kuti timakhulupirira Kristu ndipo kenako nkuchita zimene ife tikuganiza kuti nzabwino. Nkofunika kotheratu kuti tidziwe chimene chifuniro cha Mulungu chiri pa nkhaniyo. Yesu anasonyeza zimenezi mu Ulaliki wake wa pa Phiri pamene anati: “Siyense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba.”—Mateyu 7:21.
14. Kodi nchifukwa ninji Yesu angatiyese “akuchita kusayeruzika” ngakhale kuli kwakuti tikuchita “ntchito zabwino”?
14 Tingakhaledi tikuchita zimene tikukhulupirira kukhala “ntchito zabwino,” ndi kukhala tikuchita zimenezi m’dzina la Kristu. Komabe zonsezi zikakhala zachabechabe ngati tinalephera kuchita chifuniro cha Mulungu. Tikakhala ofanana ndi anthu amene Kristu kenako akutchula: “Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenera mawu m’dzina lanu, ndi m’dzina lanunso kutulutsa mizimu yoipa, ndi kuchita m’dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziwani inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 7:22, 23) Inde, tingakhale tikuchita zinthu zimene tikuganiza kuti nzabwino—ndipo zimene anthu ena angatithokoze nazo ndipo ngakhale kutitamanda—koma ngati tilephera kuchita chimene Mulungu akunena kuti nchabwino tidzayesedwa ndi Yesu Kristu kukhala “akuchita kusayeruzika.”
15. Kodi nchifukwa ninji njira yotsatiridwa ndi anthu a mu Bereya wakale iri yanzeru kwa ife kutsatira?
15 Popeza kuti zipembedzo zambiri lerolino sizikuchita chifuniro cha Mulungu, sitingangoyerekezera kuti ziphunzitso za gulu lachipembedzo limene tirimo nzogwirizana ndi Mawu a Mulungu. Chenicheni chabe chakuti Baibulo limagwiritsiridwa ntchito ndi chipembedzo mwa icho chokha sichimatsimikizira kuti zinthu zonse zimene chimaphunzitsa ndi kuchita ziri m’Baibulo. Nkofunika kuti ife enife tipende kaya izo zirimo kapena ayi. Anthu a mu mzinda wa Bereya anatamandidwa chifukwa chakuti, mtumwi Wachikristu Paulo atawalalikira, iwo anapenda Malemba kuti atsimikizire kuti zinthu zimene iye anali kuwauza zinali zowona. (Machitidwe 17:10, 11) Chipembedzo chimene chikuvomerezedwa ndi Mulungu chiyenera kugwirizana ndi Baibulo m’mbali iriyonse; sichidzalandira mbali zina za Baibulo ndi kukana mbali zina.—2 Timoteo 3:16.
KUWONA MTIMA KOKHA SIKOKWANIRA
16. Kodi Yesu ananenanji kusonyeza kuti kuwona mtima kokha sikokwanira kuti munthu avomerezedwe ndi Mulungu?
16 Koma munthu wina angafunse kuti: ‘Ngati munthu ali wowona mtima m’zikhulupiriro zake, kodi Mulungu sakamvomereza ngakhale ngati chipembedzo chake chiri cholakwa?’ Eya, Yesu anati sakavomereza “akuchita kusayeruzika” ngakhale kuli kwakuti iwo anakhulupirira kuti iwo anali kuchita chimene chinali chabwino. (Mateyu 7:22, 23) Motero kuwona mtima kokha sikukavomerezedwanso ndi Mulungu. Pa nthawi ina Yesu anauza omtsatira kuti: “Ikudza nthawi imene yense wakupha inu adzayesa kuti atumikire Mulungu.” (Yohane 16:2) Akupha Akristu oterowo angakhulupirire mowona mtima kuti iwo anali kutumikira Mulungu mwakutero, koma mwachiwonekere iwo sanali. Mulungu sakuvomereza zimene iwo anachita.
17. Ngakhale kuli kwakuti Paulo anali wowona mtima, kodi iye anachitanji asanakhale Mkristu?
17 Asanakhale Mkristu, mtumwi Paulo anathandiza m’kupha Stefano. Pambuyo pake, iye anafunafuna njira zophera Akristu ena. (Machitidwe 8:1; 9:1, 2) Paulo anafotokoza kuti: “Ndinalondalonda mpingo wa Mulungu koposa, ndi kuupasula, ndipo ndinawaposa ndi kutsogola mwa Chiyuda ambiri a msinkhu wanga mwa mtundu wanga, ndipo ndinakhala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.” (Agalatiya 1:13, 14) Inde, Paulo anali wowona mtima, koma kumeneko sikunapangitse chipembedzo chake kukhala choyenera.
18. (a) Kodi chipembedzo cha Paulo chinali chiyani pamene iye anazunza Akristu? (b) Kodi nchifukwa ninji Paulo ndi ena m’nthawi yake anafunikira kusintha chipembedzo chawo?
18 Pa nthawiyo, Paulo anali chiwalo cha gulu lachipembedzo Lachiyuda, limene lidakana Yesu Kristu, ndipo motero ilo, nalonso, linakanidwa ndi Mulungu. (Machitidwe 2:36, 40; Miyambo 14:12) Motero kuti apeze chivomerezo cha Mulungu Paulo anafunikira kusintha chipembedzo chake. Iye analembanso ponena za ena amene anali ndi “changu cha kwa Mulungu”—amene anali owona mtima koma sanavomerezedwe ndi Mulungu chifukwa chakuti chipembedzo chawo sichinazikidwe pa chidziwitso cholongosoka cha zifuno za Mulungu.—Aroma 10:2, 3.
19.Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti chowonadi sichidzavomereza mitundu yosiyanasiyana ya chiphunzitso chachipembedzo?
19 Chowonadi sichidzavomereza mitundu yonse yosiyanasiyana ya chiphunzitso chachipembedzo m’dziko lapansi. Mwa chitsanzo, kaya anthu ali ndi moyo umene umapulumuka imfa ya thupi kapena iwo alibe. Kaya dziko lapansi lidzakhala kosatha kapena silidzatero. Kaya Mulungu adzachotsa kuipa kapena sadzatero. Zimenezi ndi zikhulupiriro zina zambiri ziri mwina zowona kapena zolakwa. Sipangakhale mipambo iwiri ya chowonadi pamene umodzi sukugwirizana ndi wina. Umodzi kapena winawo ngwowona, koma osati iwiri yonse. Kukhulupirira kanthu kena mowona mtima, ndi kutsatira chikhulupiriro chimenecho, sikudzakapangitsa kukhala kabwino ngati iko kwenikweni kali kolakwa.
20. Ponena za chipembedzo, kodi tingatsatire motani “mapu amsewu” oyenera?
20 Kodi muyenera kumva bwanji ngati umboni uperekedwa wakuti zimene mukukhulupirira nzolakwa? Mwa chitsanzo, tinene kuti munali m’galimoto, mukupita kwa nthawi yoyamba kumalo ena. Muli ndi mapu amsewu, koma simunapeze nthawi ya kuwapenda mosamala. Munthu wina wakuuzani msewu woti mutenge. Mumkhulupirira, mukumakhulupirira mowona mtima kuti njira imene iye wakulozerani njolondola. Koma tiyerekezere kuti siyolondola. Bwanji ngati munthu wina asonyeza cholakwa? Bwanji ngati iye, mwa kupita ku mapu anuwo, asonyeza kuti muli pamsewu wolakwika? Kodi kudzikuza kapena kuuma khosi kudzakulepheretsani kuvomereza kuti muli pamsewu wolakwika? Chabwino, pamenepa ngati muwona mwa kupenda Baibulo lanu kuti mukuyenda pamsewu wachipembedzo wolakwika, khalani wofunitsitsa kusintha. Pewani msewu wotakata wa ku chiwonongeko; lowani pamsewu wopapatiza wa ku moyo!
KUCHITA CHIFUNIRO CHA MULUNGU NKOFUNIKA
21. (a) Kuphatikiza pa kudziwa chowonadi, kodi nchiyani chimene chiri chofunika? (b) Kodi mudzachitanji ngati muphunzira kuti Mulungu samavomereza zinthu zina zimene mukuchita?
21 Nkofunika kudziwa zowonadi za Baibulo. Komabe chidziwitso chimenechi chimakhala chopanda pake ngati inu simulambira Mulungu m’chowonadi. (Yohane 4:24) Kutsatira chowonadi, kuchita chifuniro cha Mulungu, ndiko kumene kuli nkanthu. “Chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa,” Baibulo limatero. (Yakobo 2:26) Pamenepa, kuti mukondweretse Mulungu, chipembedzo chanu sichiyenera kokha kukhala chogwirizana kotheratu ndi Baibulo komanso chiyenera kugwiritsidwa ntchito m’zochita zirizonse za moyo. Chifukwa cha chimenecho, ngati muphunzira kuti mukuchita chimene Mulungu akunena kuti ncholakwa, kodi mudzakhala wofunitsitsa kusintha?
22. Kodi ndimaphindu otani amene tingalandire tsopano ndi mtsogolo, ngati titsatira chipembedzo chowona?
22 Pali madalitso akulu okuyembekezerani ngati muchita chifuniro cha Mulungu. Ngakhale tsopano mudzapindula. Kutsatira chipembedzo chowona kudzakupangani kukhala munthu wabwino kwambiri—mwamuna, mwamuna wokwatira kapena atate wabwino kwambiri, mkazi, mkazi wokwatibwa kapena amayi wabwino kwambiri, mwana wabwino kwambiri. Kudzapanga mwa inu mikhalidwe yabwino imene idzakuchititsani kuwonekera pakati pa ena chifukwa chakuti mukuchita chimene chiri chabwino. Koma ngakhale koposa, kudzatanthauza kuti inu mudzakhala woyenerera kulandira madalitso a moyo wosatha m’chimwemwe ndi thanzi langwiro padziko lapansi latsopano laparadaiso la Mulungu. (2 Petro 3:13) Palibe kukayikira ponena za iko—chipembedzo chanu chiridi nkanthu!
[Chithunzi patsamba 25]
Kodi atsogoleri achipembedzo amene anali kuyesa kupha Yesu anali kutumikira Mulungu?
[Zithunzi pamasamba 26, 27]
Anthu ochuluka ali pamsewu wotakata wa ku chiwonongeko, Yesu anatero. Owerengeka okha ali pamsewu wopapatiza wa ku moyo
[Chithunzi pamasamba 28, 29]
“Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana Iye.”—Tito 1:16.
M’mawu
M’kuchita
[Chithunzi patsamba 30]
Chifukwa cha kusiyana chipembedzo, Paulo anagwirizana nawo m’kuponyedwa miyala kwa wophunzira wa Kristu Stefano
[Chithunzi patsamba 33]
Ngati munali pamsewu wolakwika, kodi kudzikuza kapena kuuma khosi kudzakulepheretsani kuvomereza?