Mutu 118
Kuperekedwa ndi Kugwidwa
PAKATI pa usiku papita pamene Yudase akutsogolera khamu lalikulu la asilikali, akulu ansembe, Afarisi, ndi ena m’munda wa Getsemane. Ansembewo avomereza kulipira Yudase zidutswa 30 za siliva kuti apereke Yesu.
Pachiyambiyambi, pamene Yudase anachoka pachakudya cha Paskha, iye mwachiwonekere anapita mwachindunji kwa akulu ansembe. Ameneŵa nthaŵi yomweyo anasonkhanitsa maofesala awo, ndiponso kagulu ka asilikali. Mwinamwake Yudase choyamba anawatsogolera kumene Yesu ndi atumwi ake anali atachitirako Paskha. Atapeza kuti iwo anali atachokako, khamu lalikululo lokhala ndi zida ndiponso lonyamula nyali ndi miyuni linatsatira Yudase kutuluka m’Yerusalemu ndi kupyola Chigwa cha Kidroni.
Pamene Yudase akutsogolera anthuwo ku Phiri la Azitona, iye akutsimikizira kuti akudziŵa kumene angapeze Yesu. Mkati mwa sabata lapitalo, pamene Yesu ndi atumwi anali kuyenda mobwerezabwereza pakati pa Betaniya ndi Yerusalemu, iwo kaŵirikaŵiri ankaima mmunda wa Getsemane kuti apume ndi kucheza. Koma, tsopano, popeza mwinamwake Yesu wabisika mumdima mkati mwa mitengo ya azitona, kodi asilikaliwo adzamzindikira motani? Iwo angakhale asanamuwone kalelo. Chifukwa cha chimenecho Yudase akupereka chizindikiro, akumanena kuti: “Iye amene ndidzampsompsona, ndiyeyo; mumgwire iye.”
Yudase akutsogolera khamu lalikulu kuloŵa m’mundawo, nawona Yesu ali ndi atumwi ake, namlunjika. “Tikuwoneni, Rabi;” iye akutero nampsompsonetsa.
“Mnzanga, wafikiranji iwe?” Yesu akutero. Ndiyeno, poyankha funso la iye mwini, iye akuti: “Yudase, ulikupereka Mwana wa munthu ndi chimpsompsono kodi?” Koma atatsimikizira za womperekayo! Yesu akusunthira patsogolo pa kuŵala kwa miyuni yoyakayo ndi nyali nafunsa kuti: “Mufuna yani?”
“Yesu Mnazarayo,” yankholo likutero.
“Ndine,” Yesu akuyankha motero, pamene akuimirira molimba mtima pamaso pa iwo onse. Atadabwa ndi kulimba mtima kwake ndi kusadziŵa choti ayembekezere, amunawo akubwerera m’mbuyo nagwera pansi.
“Ndati ndine,” Yesu modekha akupitiriza. “Chifukwa chake ngati mufuna ine, lekani aŵa amuke.” Nthaŵi yochepa yapitayo asanakhale m’chipinda chapamwamba, Yesu anali atauza Atate wake m’pemphero kuti iye anali atasunga atumwi ake okhulupirika ndipo palibe mmodzi wa iwo amene anatayika “koma mwana wachitayiko.” Motero, kuti mawu ake akakwaniritsidwe, iye akupempha kuti otsatira ake asiyidwe.
Pamene asilikaliwo akudzilimbitsanso, iwo akuimilira, nayamba kumanga Yesu, atumwiwo akuzindikira zimene ziri pafupi kuchitika. “Ambuye, tidzakantha ndi lupanga kodi?” iwo akufunsa motero. Yesu asanayankhe, Petro, akulalira ndi limodzi la malupanga aŵiri amene atumwiwo abweretsa, nakantha nalo Malko, kapolo wa mkulu wa ansembe. Kukantha kwa Petro kukuphonya mutu wa kapoloyo koma kukudula khutu lake lamanja.
“Lolani kufikira kumene,” Yesu akutero pamene akuloŵerera. Pogwira khutu la Malko, iye akuchiritsa chirondacho. Pamenepo iye akuphunzitsa phunziro lofunika kwambiri, akumalamulira Petro kuti: “Tabweza lupanga lako m’chimakemo, pakuti onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga. Kapena uganiza kuti sindingathe kupemphera Atate wanga, ndipo iye adzanditumizira tsopano lino mabungwe a angelo oposa khumi ndi aŵiri?”
Yesu ali wofunitsitsa kumangidwa, pakuti iye akufotokoza kuti: “Malemba adzakwaniridwa bwanji, pakuti kuyenera chomwecho?” Ndipo iye akuwonjezera kuti: “Chikho chimene Atate wandipatsa ine sindimwera ichi kodi?” Iye ali m’chigwirizano chotheratu ndi chifuniro cha Mulungu kwa iye!
Pamenepo Yesu akulankhula ndi khamulo. “Kodi munatulukira kundigwira ine ndi malupanga ndi mikunkhu, ngati wachifwamba?” iye akufunsa motero. “Tsiku ndi tsiku ndimakhala m’kachisi kuphunzitsa, ndipo simunandigwira. Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniritsidwe.”
Pamenepo kagulu ka asilikaliko ndi kazembe wankhondo ndi maofesala a Ayuda akugwira Yesu ndi kum’manga. Pakuwona izi, atumwiwo akusiya Yesu nathaŵa. Komabe, mnyamata wina—mwinamwake iye ndiye wophunzira Marko—akutsalira pakhamulo. Iye angakhale anali kunyumba kumene Yesu anachitirako Paskha ndiyeno pambuyo pake nalondola khamulo kuchokera kumeneko. Komabe, tsopano, iye akuzindikiridwa, ndipo akuyesayesa kumgwira. Koma iye akusiya nsalu yake nathaŵa wamaliseke. Mateyu 26:47-56; Marko 14:43-52; Luke 22:47-53; Yohane 17:12; 18:3-12.
▪ Kodi nchifukwa ninji Yudase akutsimikizira kuti adzapeza Yesu mmunda wa Getsemane?
▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akusonyezera nkhaŵa kaamba ka atumwi ake?
▪ Kodi ndikachitidwe kotani kamene Petro akutenga kutchinjiriza Yesu, koma kodi Yesu akuuza chiyani Petro za chochitikacho?
▪ Kodi ndimotani mmene Yesu akuvumbulira kuti akuvomerezana kotheratu ndi chifuniro cha Mulungu kwa iye?
▪ Kodi ndani akutsala, pamene atumwi akusiya Yesu, ndipo nchiyani chimene chikumchitikira?