Mutu 114
Mgonero Wachikumbutso
YESU atatha kusambitsa mapazi a atumwi ake, akugwira mawu lemba la Salmo 41:9, kumati: “Iye wakudya mkate wanga anatsalimira pa ine chidendene chake.” Kenako, atavutika maganizo, akufotokoza kuti: “Mmodzi wa inu adzandipereka ine.”
Atumwiwo akuyamba kumva chisoni nanena mmodzi mmodzi kwa Yesu kuti: “Ndine kodi?” Ngakhale Yudase Isikariote akugwirizana nawo m’kufunsako. Yohane, amene waseyama pafupi ndi Yesu pagomepo, akuyedzamira kumbuyo pachifuwa pa Yesu nafunsa kuti: “Ambuye, ndiye yani?”
“Mmodzi wa khumi ndi aŵiriwo ndiye wakusunsa pamodzi ndi ine m’mbale,” Yesu akuyankha. “Pakuti Mwana wa munthu amukadi, monga kwalembedwa za iye; koma tsoka munthuyo amene apereka Mwana wa Munthu! Kukadakhala bwino kwa munthu ameneyo ngati sakadabadwa iye.” Zitatha zimenezo, Satana akuloŵanso mwa Yudase, akumapeza mpata wotseguka mumtima mwa Yudase, umene wakhala woipa. Pambuyo pake usikuwo, Yesu moyenerera akutcha Yudase “mwana wa chitayiko.”
Tsopano Yesu akuuza Yudase kuti: “Chimene uchita, chita msanga.” Palibe ngakhale mmodzi wa ena a atumwiwo amene akuzindikira zimene Yesu akutanthauza. Ena akulingalira kuti popeza Yudase ali ndi thumba landalama, Yesu akumuuza kuti: ‘Gula zimene tiribe paphwando,’ kapena kuti ayenera kupita ndi kupatsa kanthu kena kwa osauka.
Yudase atachoka, Yesu akuyambitsa phwando latsopano kotheratu, kapena chikumbutso, ndi atumwi ake okhulupirika. Iye akutenga mkate, nayamika, naunyema, nawapatsa, nanena kuti: “Tengani, idyani.” Iye akufotokoza kuti: “Ichi ndithupi langa lopatsidwa chifukwa cha inu; chitani ichi chikumbukiro changa.”
Aliyense atadya mkatewo, Yesu akutenga chikho cha vinyo, mwachiwonekere chikho chachinayi chogwiritsiridwa ntchito pa dzoma la Paskha. Akuperekanso pemphero la kuyamika, nachipereka kwa iwo, akumawapempha kumwa, nati: “Chikho ichi ndipangano latsopano m’mwazi wanga wothiridwa chifukwa cha inu.”
Chotero, kunena zowona, ichi ndichikumbutso cha imfa ya Yesu. Chaka chirichonse pa Nisani 14 chiyenera kubwerezedwa, monga momwe Yesu akunenera, pomkumbukira. Chidzakumbutsa ochita phwandowo zimene Yesu ndi Atate wake wakumwamba achita kupereka populumukira anthu kuchokera ku chitsutso cha imfa. Kwa Ayuda amene akukhala ophunzira a Kristu, phwandolo lidzaloŵa m’malo mwa Paskha.
Pangano latsopano, limene likuyamba kugwira ntchito mwa mwazi wokhetsedwa wa Yesu, likuloŵa mmalo pangano Lachilamulo lakale. Likuchitiridwa unkhoswe ndi Yesu Kristu pakati pa mbali ziŵiri—kumbali imodzi, Yehova Mulungu, ndi kumbali inayo, Akristu obadwa ndi mzimu a 144,000. Kuwonjezera pa kupereka mwaŵi wa chikhululukiro cha machimo, panganolo limalola kupangidwa kwa mtundu wakumwamba wa mafumu ndi ansembe. Mateyu 26:21-29; Marko 14:18-25; Luka 22:19-23; Yohane 13:18-30; 17:12; 1 Akorinto 5:7.
▪ Kodi ndiulosi uti Wabaibulo umene Yesu akugwira mawu ponena za bwenzi, ndipo kodi akuugwiritsira ntchito motani?
▪ Kodi nchifukwa ninji atumwiwo akufikira kukhala a chisoni kwambiri, ndipo kodi nchiyani chimene aliyense wa iwo akufunsa?
▪ Kodi Yesu akuuza Yudase kuchita chiyani, koma kodi ndimotani mmene atumwi enawo akutanthauzirira malangizo ameneŵa?
▪ Kodi Yesu akuyambitsa kuchitidwa kwa phwando lotani Yudase atachoka, ndipo kodi ndichifuno chotani chimene likutumikira?
▪ Kodi ndani amene akuphatikizidwa m’pangano latsopanolo, ndipo kodi panganolo limakwaniritsanji?