Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Muzilimbikira
    Galamukani!—2012 | October
    • Muzilimbikira

      Munthu amalimbikira kuchita chinachake ngati waona kuti n’chaphindu.

      KODI munthu angapindule bwanji ndi sukulu? Sukulu imathandiza kuti munthu adziwe zinthu kapena kuti akhale ndi nzeru ndipo Baibulo limanena kuti “nzeru zimateteza.” (Mlaliki 7:12) Kodi nzeru zimateteza bwanji? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyerekeze kuti mukudutsa malo enaake oopsa. Kodi mungasankhe kuyenda nokha kapena ndi anzanu amene angakutetezeni ngati mutakumana ndi zoopsa? Zinthu zimene mumaphunzira ku sukulu zili ngati anzanu amene angakuthandizeni pa moyo wanu wonse. Zina mwa zinthu zimenezi ndi izi:

      • Kuganiza bwino. Sukulu imathandiza munthu kuti azitha kuchita zimene Baibulo limanena kuti ndi “kudziwa zinthu komanso kuganiza bwino.” (Miyambo 3:21, Contemporary English Version) Zinthu zimenezi zikhoza kukuthandizani kuti muthane nokha ndi mavuto anu m’malo momangodalira anthu ena.

      • Kukhala bwino ndi anthu. Baibulo limalimbikitsa Akhristu kuti aziyesetsa kusonyeza makhalidwe abwino ngati kuleza mtima ndi kudziletsa. (Agalatiya 5:22, 23) Popeza munthu akakhala ku sukulu amachita zinthu ndi anthu osiyanasiyana, amakhala ndi mwayi wosonyeza makhalidwe ngati kulolera, kulemekeza ena komanso chifundo. Makhalidwe amenewa angadzamuthandizenso akadzakula.

      • Kukukonzekeretsani zam’tsogolo. Sukulu imathandiza munthu kuti adziwe kufunika kolimbikira ntchito, zomwe zingadzamuthandize kuti adzapeze ntchito mosavuta komanso kuti adzakhalitse pantchitopo. Kuwonjezera pamenepa, sukulu imathandizanso kuti munthu adzidziwe bwino komanso adziwe mfundo zimene amayendera. (Miyambo 14:15) Kudziwa zimenezi kungamuthandize kuti azilimba mtima kuuza ena mwaulemu zimene amakhulupirira.​—1 Petulo 3:15.

      Mfundo yofunika kuikumbukira: Monga taonera, sukulu ndiyofunika kwambiri. Koma mukamangoganizira zinthu zomwe sizikusangalatsani pa nkhani ya sukulu mukhoza kuyamba kudana nayo. Choncho, mungachite bwino kuganizira mfundo zimene tazifotokozazi komanso mfundo zina.

      Yambani kutsatira malangizo amenewa. Sankhani ndi kuyamba kutsatira mfundo imene ingakuthandizeni kuti muzilimbikira sukulu.

      Ana Amanyadira Mphunzitsi Wabwino

      “Aphunzitsi omwe ankatiphunzitsa phunziro la Economics anali ophunzira kwambiri moti akanatha kugwira ntchito yapamwamba m’makampani ena. Koma iwo anasankha kugwira ntchito yauphunzitsi, yomwe imaoneka ngati yotsika. Ana a sukulu akawafunsa chifukwa chake anasankha kudzaphunzitsa pasukulu yathu, iwo ankayankha kuti amakonda ntchito yauphunzitsi ndipo ankasangalala kwambiri kuphunzitsa pasukulu yathu kuposa malo ena alionse amene anagwirako ntchito. Nthawi zambiri ana a sukulu sakonda phunziro la Economics, koma tonse m’kalasi mwathu tinkakonda phunziroli chifukwa aphunzitsiwo ankayesetsa kuphunzitsa mosavuta komanso mosangalatsa. Ankatithandizanso kuona mmene nkhani zachuma zingatithandizire. Tinkawakonda kwambiri chifukwa ankatimvetsa, ankatidera nkhawa komanso ankatilimbikitsa. Nthawi ina anawaimbira foni mayi anga n’kuwauza kuti ndinakhoza bwino phunziro lawolo. Sindinakhaleponso ndi mphunzitsi wabwino ngati ameneyu.”​—Anatero Reyon, wa ku United States.

  • Muzichita Zinthu Mwadongosolo
    Galamukani!—2012 | October
    • Muzichita Zinthu Mwadongosolo

      Munthu akamayesetsa kuchita zinthu mwadongosolo, zinthu zimamuyendera bwino. Mwachitsanzo, amakhala ndi nthawi yambiri, sakhala ndi nkhawa komanso amakhoza bwino ku sukulu.

      AYEREKEZANI kuti mukufuna kugula chinachake musitolo, koma mutangolowa mwapeza kuti katundu sanalongedzedwe mwadongosolo. N’zachidziwikire kuti zingakutengereni nthawi yaitali kuti mupeze chimene mukufunacho. Koma simungavutike ngati katunduyo walongedzedwa mwadongosolo komanso ngati aika zikwangwani. N’chimodzimodzinso ndi sukulu. Kuti zinthu zizikuyenderani bwino, chinthu chimodzi chofunika ndi kuchita zinthu mwadongosolo. Ndiye kodi mungachite bwanji zimenezi?

      Muzikhala ndi ndandanda.

      Mnyamata wina wazaka 18 wa ku United States, dzina lake Zachary, ananena kuti: “Nthawi ina ndinakagona kwa mnzanga Loweruka ndi Lamlungu moti ndinaiwala zoti ndili ndi homuweki komanso kuti ndinkafunika kugwira ntchito zina zapakhomo. Nditapita kusukulu ndinachita kupempha aphunzitsi kuti andilole kubweretsa homuweki yanga mochedwa. Panopa ndimachita zinthu mwadongosolo chifukwa ndili ndi ndandanda ya zimene ndiyenera kuchita.”

      Kukhala ndi ndandanda kwathandizanso mtsikana wina wa ku Papua New Guinea, dzina lake Celestine. Pofotokoza zimene ankachita ali pa sukulu, iye anati: “Ndinkakhala ndi ndandanda ya zonse zimene ndikufunika kuchita monga kulemba homuweki komanso mayeso. Ndandandayi inandithandiza kuti ndikafuna kuchita zinthu, ndiziyamba ndi zofunika kwambiri komanso kuti ndizizichita pa nthawi yake.”

      Mfundo yothandiza: Lembani ndandanda yanu m’kope kapena mufoni yanu.

      Musamazengereze pochita zinthu.

      Anthu ali ndi chizolowezi chonena kuti: “Aa, ndipangabe.” Koma ndibwino kumachita zinthu nthawi yomweyo, makamaka ikakhala homuweki.

      Mfundo yothandiza: Muzilemberatu homuweki yanu mukangofika kunyumba. Musamaonere TV kapena kuchita zinthu zina musanalembe homuweki.

      Muzilongedzeratu za ku sukulu.

      Kodi zinayamba zakuchitikiranipo kuti mwafika m’kalasi n’kuona kuti mwaiwala kope, cholembera kapena mabuku? Kodi mungatani kuti zimenezi zisamakuchitikireni? Mnyamata wina wa ku Myanmar, dzina lake Aung Myo Myat, ananena zimene amachita kuti asamaiwale zinthu. Iye anati: “Nthawi zonse ndimalongedzeratu chikwama cha ku sukulu.”

      Mfundo yothandiza: Muzionetsetsa kuti mwalongedza chikwama chanu mwadongosolo kuti musamavutike kupeza zinthu.

      Mfundo yofunika kuikumbukira: Mukamachita zinthu mwadongosolo mumapewa mavuto amene amabwera chifukwa choiwala zinthu, kuchedwa komanso kusowa nthawi yochitira zinthu zina zofunika.

      Yambani kutsatira malangizo amenewa. Ganizirani chinthu chimodzi chimene mukuona kuti mufunika kumachichita mwadongosolo. Kenako mothandizana ndi kholo lanu kapena mnzanu, fufuzani njira zina zimene zingakuthandizeni kuti muyambe kuchita zinthu mwadongosolo.

  • Muzikhala ndi Okuthandizani
    Galamukani!—2012 | October
    • Muzikhala ndi Okuthandizani

      Kukhala ndi anthu amene angamakulangizeni komanso kukuthandizani n’kofunika pamene muli pa sukulu komanso mukadzamaliza sukulu.

      KODI ndani amene angakuthandizeni kuti zinthu zizikuyenderani bwino ku sukulu?

      Anthu am’banja mwanu.

      Mtsikana wina wazaka 18, wa ku Brazil, dzina lake Bruna, ananena kuti: “Homuweki ikakhala kuti yandivuta, bambo anga ankandifotokozera bwino kenako n’kundifunsa mafunso. Koma sankandiuzira mayankho chifukwa ankafuna kuti ndipeze ndekha.”a

      Mfundo yothandiza: Funsani makolo anu kuti anene mmene ankakhozera phunziro limene limakuvutanilo. Ngati ankakhoza bwino, ndiye kuti angakuthandizeni.

      Aphunzitsi.

      Aphunzitsi ambiri amasangalala akaona kuti mwana wasukulu akufunitsitsa kuti azikhoza bwino ndipo amayesetsa kuti amuthandize.

      Mfundo yothandiza: Mungachite bwino kuwauza aphunzitsi anu kuti: “Ndimafuna nditamakhoza bwino phunziroli koma limandivuta. Kodi mungandithandize bwanji?”

      Anthu ena okuthandizani.

      Mwina munthu wina amene mumamudalira akhoza kukuthandizani. Zimenezi zingakuthandizeni m’njira ziwiri izi: Choyamba, mungapeze thandizo limene mukufuna ndipo chachiwiri, mungaphunzire kudalira anthu ena, zomwenso zingadzakuthandizeni mukadzakula. Dziwani kuti munthu aliyense zimamuyendera bwino ngati anthu ena amuthandiza.​—Miyambo 15:22.

      Mfundo yothandiza: Afunseni makolo anu kuti akuuzeni anthu ena amene iwo akuganiza kuti akhoza kukuthandizani.

      Mfundo yofunika kuikumbukira: Palibe cholakwika ndi kupempha ena kuti akuthandizeni.

      Yambani kutsatira malangizo amenewa. Lembani mayina a anthu awiri kapena atatu amene ndi zitsanzo zabwino ndipo mumafuna mutatengera chitsanzo chawo. Mwina mmodzi wa anthu amenewa akhoza kukuthandizani pa nkhani ya sukulu.

      a Ngati muli ndi m’bale wanu wamkulu akhozanso kukuthandizani.

      “Mphunzitsi amene ankandisangalatsa”

      “Kale ndili pa sukulu, tinali ndi aphunzitsi enaake ovuta koma ana ankawalemekeza. Iwo ankakonda ntchito yawo kwambiri moti akamaphunzitsa ankayenda uku ndi uku m’kalasimo, uku akulankhula ndi manja. Iwo ankayesetsa kuti mwana aliyense azifotokoza maganizo ake. Nthawi zambiri ankakonda kutiuza kuti tizimasuka kuwafunsa mafunso. Iwo ankanena kuti kufunsa mafunso kungawathandize kudziwa zimene ifeyo sitikuzimvetsa komanso kuti akhale mphunzitsi wabwino. Ankasonyeza chidwi kwa mwana aliyense. Mwachitsanzo ukakhala kuti sunamvetse mfundo inayake, ankakufotokozera moleza mtima mpaka umvetse. Iwo anatiphunzitsa kwa chaka chimodzi phunziro la Accounts moti ana ambiri anasankha kuti adzagwira ntchito imeneyi.”​—Anatero Alana, wa ku Australia.

  • Muzisamalira Thanzi Lanu
    Galamukani!—2012 | October
    • Muzisamalira Thanzi Lanu

      Kusamalira thanzi lanu kungathandize kuti muzikhoza ku sukulu komanso kuti muzikhala osangalala.

      N’ZOYENERA kuti tizisamalira thupi lathu chifukwa ndi mphatso imene Mulungu anatipatsa. (Salimo 139:14) Mwachitsanzo, tayerekezerani kuti muli ndi galimoto koma simupeza nthawi yoti muziisamalira. Sipangapite nthawi yaitali isanawonongeke. N’chimodzimodzinso thupi lanu. Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite kuti muzilisamalira?

      Muzigona mokwanira.

      Ngati simugona mokwanira mukhoza kumasokonezeka maganizo, kukhala wofooka, komanso wotopa. Koma munthu amene amagona mokwanira amakhala ndi mphamvu, thupi lake limakula bwino, ubongo wake umagwira bwino ntchito, chitetezo cha m’thupi mwake chimakhala champhamvu komanso amakhala wosangalala. Choncho, kugona mokwanira kungakuthandizeni kuti mupeze zonsezi.

      Mfundo yothandiza: Ngati n’zotheka muzigona nthawi imodzimodzi tsiku lililonse.

      Muzidya zakudya zopatsa thanzi.

      Achinyamata amakula mwamsanga. Mwachitsanzo, anyamata akafika zaka zapakati pa 10 ndi 17, thupi lawo limayamba kusintha. N’chimodzimodzinso atsikana. Munthu akamakula thupi lake limafunika chakudya chokwanira komanso chopatsa mphamvu. Choncho, muziyesetsa kudya zakudya zopatsa thanzi.

      Mfundo yothandiza: Muzionetsetsa kuti mwadya chakudya cham’mawa. Kudya musanapite kusukulu kungathandize kuti muzikamvetsera bwino m’kalasi komanso kuti muzitha kukumbukira bwino zinthu.

      Muzichita masewera olimbitsa thupi.

      Baibulo limanena kuti: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Timoteyo 4:8) Kuchita masewera olimbitsa thupi kungathandize kuti musanenepe kwambiri ndiponso kuti mukhale ndi thupi komanso mafupa amphamvu. Kungathandizenso kuti ubongo wanu uzigwira bwino ntchito, chitetezo cha m’thupi mwanu chikhale champhamvu komanso kuti musamakhale ndi nkhawa. Komanso kuchita masewera olimbitsa thupi n’kosangalatsa chifukwa umakhala ukuchita zinthu zimene zimakusangalatsa.

      Mfundo yofunika kuikumbukira: Kugona mokwanira, kudya chakudya chopatsa thanzi komanso kuchita masewera olimbitsa thupi kungathandize kuti thupi lanu likhale lathanzi. Zimenezi zingachititse kuti muzikhoza m’kalasi.a

      Yambani kutsatira malangizo amenewa. Khalani ndi ndandanda yabwino yochitira masewera olimbitsa thupi. Kwa mwezi umodzi, fufuzani kuti mudziwe nthawi imene mukumagona komanso zakudya zimene mukudya. Kenako onani zimene mungafunike kusintha.

      “Ndimaona kuti ndikapita kokayenda ndimapeza mphamvu.”​—Anatero Jason, wa ku New Zealand.

      “Ndimaona kuti Mulungu analenga chakudya kuti chizitipatsa mphamvu, choncho ndikufuna kuti ndizidya chakudya chopatsa thanzi.”​—Anatero Jill, wa ku United States.

      “Ndimapita kothamanga katatu pa mlungu ndipo ndimakwera njinga kapena kupita koyenda kawiri pa mlungu. Kuchita masewera olimbitsa thupi kwandithandiza kuti ndizikhala ndi mphamvu komanso kuti ndisamakhale ndi nkhawa.”​—Anatero Grace, wa ku Australia.

      a Kuti mudziwe zambiri zokhudza mmene mungasamalilire thanzi lanu, werengani mutu 10 m’buku lachingelezi lakuti Questions Young People Ask​—Answers That Work, Volume 1, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

  • Muzikhala ndi Cholinga
    Galamukani!—2012 | October
    • Muzikhala ndi Cholinga

      Munthu amalimbikira komanso kusangalala ndi sukulu ngati akudziwa phindu lake.

      MUNTHU amene akuphunzira popanda cholinga chilichonse amakhala ngati munthu amene akungothamanga osadziwa kumene akupita. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “Salaza njira ya phazi lako,” kutanthauza kuti tizidziwa kumene tikupita. (Miyambo 4:26) Kukhala ndi cholinga kungakuthandizeni kuti mukadzamaliza sukulu musadzavutike kuzolowera moyo wapantchito. Ndiyeno mungatani kuti mukhale ndi cholinga?

      Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndizidzagwira ntchito yanji?’ Simuyenera kuzengereza kupeza yankho la funso limeneli chifukwa zingakuthandizeni kuyamba kukonzekera panopa. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kunyamuka ulendo winawake, choyamba mungafunike kudziwa kumene mukupita. Kenako mungafunike kuyang’ana pa mapu kuti mudziwe mmene mungakafikire kumaloko. Mungachitenso chimodzimodzi ndi sukulu. Choyamba, ganizirani ntchito imene mukufuna kuti mudzagwire kenako sankhani kosi yogwirizana ndi ntchito imene mukufunayo.

      Chenjezo: Achinyamata ambiri amafuna kudzagwira ntchito yokhayo imene amailakalaka, monga kudzakhala woimba wotchuka, ndipo amaona kuti sangagwire ntchito zina. Koma kodi tiyenera kuiona bwanji nkhani imeneyi?

      1. Ganizirani zinthu zimene mumakwanitsa. Mwachitsanzo, kodi mumasangalala kugwira ntchito zothandiza anthu? Kapena muli ndi luso la zopangapanga, la masamu, la zachuma kapena kukonza zinthu zowonongeka?

      2. Ganizirani ntchito zimene mungagwire. Kodi ndi ntchito ziti zimene zikugwirizana ndi zimene inuyo mumakwanitsa? Ganizirani ntchito zambirimbiri m’malo momangoganizira imene mumailakalaka. Komanso ngati mutati mwasamukira kudera lina, kodi ntchito imeneyo mungakaipeze mosavuta? Kodi kosi imene mukufuna ingachititse kuti mukhale ndi ngongole zambiri?

      3. Ganizirani amene angakulembeni ntchito. Mukasankha ntchito imene mukufuna kudzagwira, ganiziraninso amene angakulembeni ntchito m’dera lanu. Kodi mukudziwapo aliyense amene angadzakulembeni? Ngati alipo, kodi angalole kuti muzikagwirako ntchito pa nthawi imene muli pa sukulu? Kodi pali makampani amene amaphunzitsa ntchito imene mukufunayo?

      Mfundo yothandiza: Funsani makolo anu, aphunzitsi komanso anzanu achikulire. Mungakafufuzenso za ntchito imene mukufunayo ku laibulale kapena pa Intaneti.

      Mfundo yofunika kuikumbukira: Kukhala ndi cholinga kungakuthandizeni kuti muzilimbikira komanso kuti muzisankha zinthu mwanzeru.

      Yambani kutsatira malangizo amenewa. Pa nthawi imene mudakali pa sukulu, ganizirani mfundo zitatu zimene takambiranazi. Lembani zolinga zanuzo ndipo mukambirane ndi makolo anu.

      Mwina mwaona kuti m’nkhanizi muli malemba a m’Baibulo ofotokoza zimene munthu angachite kuti zinthu zizimuyendera ku sukulu. A Mboni za Yehova, omwe amafalitsa magaziniyi, amakhulupirira kuti Baibulo lili ndi malangizo “opindulitsa,” omwe amathandiza kuti zinthu zizitiyendera bwino pa moyo wathu. (2 Timoteyo 3:16) Lili ndi mfundo zimene zingatithandize pa moyo wathu kaya ndi ku sukulu, ku ntchito kapena m’banja.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena