Zimene Makolo Angachite Kuti Athandize Ana Awo
Masiku ano ana amaona zinthu zachiwawa komanso zinthu zina zoipa zimene anthu amachita. Choncho makolo ayenera kuteteza ana awo kuti asatengere makhalidwe amenewa. Koma kodi makolo angapeze kuti malangizo amene angathandizire ana awo? Makolo ambiri aona kuti Baibulo limathandiza kwambiri ndipo malangizo ake pa nkhani ya makhalidwe abwino ndi apamwamba moti sitingawayerekezere ndi malangizo ena alionse.
Pofuna kuthandiza makolo kupeza malangizo a mmene angalangizire ana awo, a Mboni za Yehova ali ndi buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Buku limeneli lili ndi mitu 48 ndipo ina mwa mitu imeneyi ndi monga, “Kumvera Kudzakuteteza,” “Chifukwa Chake Tiyenera Kukhululukira Ena,” “Chifukwa Chake Tiyenera Kupewa Bodza,” “Zimene Zingatithandize Kuthetsa Mantha” komanso “Chifukwa Chake Tifunikira Kugwira Ntchito.”