Zoti Banja Likambirane
Gwirizanitsani chithunzi ndi vesi lake
Werengani Genesis 1:1-31. Lembani mzere wolumikiza chithunzi chilichonse ndi vesi la m’Baibulo limene likugwirizana ndi chithunzicho. (Zithunzizi sizinaikidwe m’ndondomeko yake.)
KAMBIRANANI:
Kodi timadziwa bwanji kuti masiku amene Mulungu analenga dziko lapansi sanali masiku enieni a maola 24?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Genesis 2:4; Salimo 90:4.
Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene Yehova analenga?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Salimo 115:16; Aroma 1:20; 1 Yohane 4:8; Chivumbulutso 4:11.
ZOTI BANJA LICHITIRE PAMODZI:
Konzani zoti banja lanu lipite kumalo enaake. Mwina mungapite kumalo osungira nyama, kumalo enaake okongola kapena kumalo alionse kumene mungakaphunzireko zachilengedwe. Mukabwerako, mukambirane zimene mwaphunzira zokhudza Yehova
Sungani Kuti Muzikumbukira
KHADI LA BAIBULO 23 YONATANI
MAFUNSO
A. Yonatani anali mwana wamkulu wa ․․․․․.
B. Zoona kapena Zonama? Nthawi ina bambo ake a Yonatani anaponya mkondo kuti amulase.
C. Kodi Yonatani ankakonda kwambiri ndani, ndipo n’chifukwa chiyani ankamukonda?
ANALI NDANI?
Ndi amene ankayenera kulowa m’malo Mfumu Sauli. N’kutheka kuti anali wamkulu kwa Davide ndi zaka 30 ndipo anavomereza zimene Mulungu anasankha, zoti Davide ndi amene adzakhale mfumu. (1 Samueli 23:15-18) Yonatani anaika moyo wake pangozi chifukwa chofuna kuteteza Davide kuti asaphedwe ndi Sauli. (1 Samueli 20:1-42) Zimene Yonatani anachita zikutiphunzitsa kuti tiyenera kudzichepetsa komanso kusangalala Mulungu akachitira anthu ena zinthu zabwino.
MAYANKHO
A. Mfumu Sauli.—1 Samueli 14:47, 49.
B. Zoona.—1 Samueli 20:33.
C. Davide. Pamene Davide ankamenyana ndi Goliati, Yonatani anaona kuti Davide anali wolimba mtima komanso kuti ankakonda Yehova.—1 Samueli 17:1 mpaka 18:1-4.
Anthu ndi Mayiko
Mayina athu ndi Pyae Sone Aung ndi Hsu Myat Yadanar Lwin, ndipo tili ndi zaka 11 ndi 7. Timakhala ku Myanmar. Kodi mukudziwa kuti ku Myanmar kuli Mboni za Yehova zingati? Kodi ziliko 3,600; 6,300, kapena 10,000?
Kodi ndi kadontho kati kamene kakusonyeza dziko limene ifeyo timakhala? Lembani mzere wozungulira kadonthoko. Kenako jambulani kadontho kosonyeza kumene inuyo mumakhala, kuti muone kuyandikana kwa dziko lanu ndi la Myanmar.
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Pezani zithunzi izi m’magazini ino. Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
MAYANKHO A MAFUNSO
Chithunzi F chikugwirizana ndi 1.
Chithunzi B chikugwirizana ndi 2.
Chithunzi A chikugwirizana ndi 3.
Chithunzi E chikugwirizana ndi 4.
Chithunzi C chikugwirizana ndi 5.
Chithunzi D chikugwirizana ndi 6.
3,600.
D.