Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 2/13 tsamba 3
  • Zochitika Padzikoli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zochitika Padzikoli
  • Galamukani!—2013
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Israel
  • Australia
  • Greece
  • United States
  • Madagascar
  • Kodi Mumalidziŵa Bwino Motani Baibulo?
    Nsanja ya Olonda—1991
  • Ndife Otsimikiza Kutumikira Yehova
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mafunde Sangapose Zimenezi Ngakhale Atatalika Motani
    Galamukani!—2007
  • Anatchona Kofunafuna Golide
    Galamukani!—2011
Galamukani!—2013
g 2/13 tsamba 3

ZOCHITIKA PADZIKOLI

Israel

Lipoti la pa webusaiti ina linanena kuti “ana amene anabadwa ndi chilema chomwe madokotala akanatha kuchitulukira anawo asanabadwe,” sakuloledwanso kutengera kukhoti madokotalawo chifukwa cholola makolo awo kuwabereka m’malo mongochotsa mimbayo. Komabe makolo a anawo akhoza kupempha boma kuti liwapatse chipukutamisozi chowathandiza kusamalira ana awo kwa moyo wawo wonse.​—⁠Haaretz.com.

Australia

Ku Australia, mabanja 8 pa 10 alionse anayamba kukhalira limodzi asanakwatirane.

Greece

Lipoti lina limene unduna wa zaumoyo wa ku Greece unatulutsa, linasonyeza kuti chiwerengero cha anthu amene anadzipha m’dzikolo chinawonjezeka ndi 40 peresenti kuyambira m’mwezi wa January mpaka May, 2011. Chiwerengero chimenechi n’chokwera poyerekezera ndi chiwerengero cha anthu omwe anadzipha m’miyezi yomweyi, chaka cha 2010. Chiwerengerochi chinakwera kwambiri panthawi imenenso m’dzikolo munali mavuto azachuma.

United States

Nthambi yaboma yosamalira zachilengedwe ku United States inanena kuti 40 peresenti ya chakudya cha m’dzikolo chimawonongeka. Mwachitsanzo 7 peresenti ya chakudya chimangosiyidwa m’munda osakololedwa, 17 peresenti ya chakudya cha m’malesitanti chimatsala komanso 25 peresenti ya chakudya m’mabanja ambiri chimatayidwa.

Madagascar

Chaposachedwapa, anthu apeza mtundu winawake wa tianamzikambe tating’ono kwambiri ku Madagascar. Tianamzikambeti timakhala tatitali mainchesi 1.1, moti timakwana pachikhadabo cha munthu. Anthu ena akuona kuti tianamzikambe timeneti tili m’gulu la nyama zimene zatsala pang’ono kutheratu.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena