Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 2/15 tsamba 6-7
  • Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Chikondi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse—Chikondi
  • Galamukani!—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Kutsatira Mfundo Zosasinthasintha
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Zamkatimu
    Galamukani!—2015
  • Mmene Tingakhalire ndi Chikondi Chenicheni
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Magwero Apamwamba Kwambiri a Nzeru
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 2/15 tsamba 6-7

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MFUNDO ZA M’BAIBULO N’ZOTHANDIZABE MASIKU ANO?

Mfundo Zake N’zothandiza Nthawi Zonse​—Chikondi

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Valani chikondi, pakuti chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.”—Akolose 3:14.

UBWINO WOSONYEZA CHIKONDI: Chikondi chimene chimatchulidwa m’Baibulo kawirikawiri, si chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi. Koma ndi chikondi chomwe timasonyeza chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo. Munthu amene ali ndi chikondichi amakhala ndi makhalidwe monga, chifundo, kukhululuka, kudzichepetsa, kukhulupirika, kukoma mtima, kufatsa ndi kuleza mtima. (Mika 6:8; Akolose 3:12, 13) Chikondi chimene chimakhalapo pakati pa mwamuna ndi mkazi chikhoza kuzirala mkupita kwa nthawi. Koma chikondi chomwe timasonyeza chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo, sichitha.

Brenda, yemwe wakhala m’banja kwa zaka pafupifupi 30 anati: “Anthu akangokwatirana kumene amaona kuti akukondana kwambiri. Koma akakhala m’banja zaka zambiri, amaona kuti m’pamene akukondana kwambiri kuposa poyamba paja.”

Sam, yemwe wakhala m’banja kwa zaka zoposa 12 anati: “Ine ndi mkazi wanga timaona kuti malangizo a m’Baibulo ndi othandiza komanso si ovuta kuwatsatira. Zimenezi zimatichititsa chidwi kwambiri. Ndimaona kuti ndikamatsatira malangizo a m’Baibulo zinthu zimandiyendera bwino. Komabe nthawi zina ndikatopa, ndikakhala kuti ndili ndi nkhawa kapena ndikhala kuti ndikungoganizira za ineyo, ndimalephera kutsatira malangizo a m’Baibulo. Zikatere ndimapempha Yehova kuti andithandize. Kenako ndimamusonyeza mkazi wanga kuti ndimamukonda, basi n’kuiwala nkhaniyo.”

“Nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake”

Yesu Khristu anati “nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Zimene takambiranazi ndi umboni woti Baibulo lili ndi malangizo othandiza pa nkhani zosiyanasiyana. Zimene limaphunzitsa komanso mfundo zake n’zothandiza kwambiri ndipo sizitha ntchito. Zimagwira ntchito kwa anthu a zikhalidwe komanso mayiko osiyanasiyana. Zimenezi zimachita kusonyezeratu kuti nzeru zomwe zili m’Baibulo n’zochokera kwa Yehova Mulungu, yemwe ndi Mlengi wathu. Koma Baibulo lingamuthandize munthu pokhapokha ngati akutsatira mfundo zake, osati kungoliwerenga basi. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.” (Salimo 34:8) Tikukulimbikitsani kuti nanunso muyambe kutsatira mfundo za m’Baibulo kuti muone mmene zingakuthandizireni.

BAIBULO LANDITHANDIZA KWAMBIRI PA MOYO WANGA

Mayi wina dzina lake Linh, amakhala ku Southeast Asia. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe mmene Baibulo linamuthandizira.

Kodi poyamba munali m’chipembedzo chiti?

Banja lathu linali lachibuda ndipo tinkachita miyambo yamakolo. Sindinkadziwa chilichonse chokhudza Mulungu woona.

Kodi zinthu zinkayenda bwanji pa moyo wanu?

Sizinkayenda bwino kwenikweni. Ndinkakumana ndi mavuto ambiri. Mwachitsanzo, sindinkatha kugwiritsa ntchito bwino ndalama, ndinalibe anzanga apamtima komanso ndinkalephera kuthandiza makolo anga.

Ndiye n’chiyani chinathandiza kuti zinthu zisinthe?

Atsikana awiri a Mboni za Yehova anayamba kundiphunzitsa Baibulo. Ndikakhala ndi vuto ndinkawafotozera n’cholinga choti andithandize. Ngakhale kuti anali aang’ono kwa ineyo, ankandipatsa malangizo abwino. Koma sikuti ankangonena maganizo awo. Malangizowo ankakhala ochokera m’Baibulo.

Popeza ndaona kuti kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo n’kothandiza, ndimakhulupirira kuti bukuli ndi lochokera kwa Mulungu ndipo n’lothandiza kwa aliyense. Kukhala munthu wophunzira n’kwabwino koma zimene umaphunzira kusukulu sizingakuthandize ngati mmene Baibulo limachitira.

Mukutanthauza chiyani pamenepa?

Makolo anga ndi ophunzira kwambiri komanso ndi otchuka. Koma akakhala ndi mavuto sadziwa zimene angachite. Ndi anthu osasangalala ndipo ndikunena pano analekana. Komanso ndili ku koleji ndinaphunzira kuti kuchita zachiwawa kumathandiza kuti zinthu zisinthe m’dziko. Koma Baibulo limanena kuti anthu sangathetseretu mavuto. Zili choncho chifukwa Mulungu sanatilenge kuti tizidzilamulira. N’chifukwa chake ngakhale kuti anthu ayesa kukhazikitsa maboma osiyanasiyana, alephera ndipo nthawi zambiri m’mabomamo mumachitika zachinyengo. a Koma tikatsatira malangizo a Mulungu zinthu zimatiyendera bwino komanso timalimbikitsa ena kuchita zabwino.

Kodi Baibulo lakuthandizani bwanji?

Baibulo landithandiza kwabasi. Panopa sindida nkhawa kwambiri komanso ndili ndi anzanga apamtima. Ndaphunziranso kugwiritsa ntchito ndalama mwanzeru moti panopa ndimatha kukhala ndi ndalama zopitira kwinakwake kokasangalala. Chofunikanso kwambiri n’choti ndimatha kuthandiza anthu ovutika.

a Onani Mlaliki 8:9 ndi Yeremiya 10:23.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena