ZIMENE MUNGACHITE PA VUTO LA KUKWERA MITENGO KWA ZINTHU
Muziyembekezera Kuti Zinthu Zidzasintha
Kodi mitengo ya zinthu ikukwera kwambiri m’dziko lanu, koma ndalama zimene mumapeza sizikuwonjezereka? Kodi mumadera nkhawa mmene mungapezere zinthu zofunika pa moyo wanu komanso za anthu am’banja lanu? Ngati ndi choncho, mukhoza kumada nkhawa mukaganizira zam’tsogolo. Koma kukhala ndi chiyembekezo pa nthawi ngati imeneyi n’kothandiza kwambiri.
N’CHIFUKWA CHIYANI KUCHITA ZIMENEZI N’KOFUNIKA?
Munthu amene ali ndi chiyembekezo sikuti amangolakalaka zinthu zabwino zitachitika. Chiyembekezo chimatipatsa mphamvu ndipo chimatithandiza kuti tichite zinthu zimene zingatithandize pa mavuto athu. Mwachitsanzo, kafukufuku amasonyeza kuti anthu amene ali ndi chiyembekezo . . .
amatha kupirira mavuto
savutika kusintha
amasankha zinthu mwanzeru zomwe zimathandiza kuti akhale ndi moyo wabwino komanso wathanzi
ZIMENE MUNGACHITE
Choyamba, muziganizira mmene Baibulo lingakuthandizireni masiku ano. M’Baibulo muli malangizo amene angakuthandizeni kudziwa zochita pa vuto la kukwera mitengo kwa zinthu. Malangizowa angakuthandizeni kuona kuti sikuti palibiretu mtengo wogwira. Koma pali zimene mungachite panopa komanso zimene mungadzachite m’tsogolo ngati mavutowo atafika poipa kwambiri.
Chachiwiri, muziganizira zimene Baibulo limanena zokhudza m’tsogolo. Mukazindikira kuti nzeru zopezeka m’Baibulo n’zothandiza kwambiri, mudzafufuza zimene bukuli limanena zokhudza m’tsogolo. Mwachitsanzo, mudzazindikira kuti Mulungu amafuna kuti mukhale ndi “tsogolo labwino ndi chiyembekezo chabwino” ndipo wayala kale maziko oti zimenezi zitheke. (Yeremiya 29:11) Maziko amene tikunenawa ndi Ufumu wa Mulungu.
KODI UFUMU WA MULUNGU N’CHIYANI, NANGA UDZACHITA CHIYANI?
Ufumu wa Mulungu ndi boma lomwe lidzalamulire dziko lonse lapansi. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Ufumuwu uzidzalamulira kuchokera kumwamba ndipo udzathetsa umphawi ndi mavuto ena onse. Moti padzikoli padzakhala mtendere komanso zinthu zambiri, ngati mmene malemba ali m’munsiwa akusonyezera.
Anthu mamiliyoni ambiri amakhulupirira malonjezo amenewa podziwa kuti Mulungu “sanganame.” (Tito 1:2) Tikukulimbikitsani kuti inunso muwerenge zimene Baibulo limanena. Chiyembekezo chimene Baibulo limapereka chingakuthandizeni kupirira mavuto azachuma n’kumayembekezera kuti m’tsogolo zinthu zidzakhala bwino.