Mutu 40
Yesu Anapereka Moyo Wache kaamba ka Ife
INU muli ndi mabwenzi ena abwino, ati?—Koma tayerekezerani kuti iwo anali mu upandu weniweni. Bwanji ngati iwo akanakhala m’bwato limene linali kumamira? Kodi inuyo mukadafuna kuwapulumutsa iwo ngati inu mukadatha?—Kodi inu mukadachichita icho ngakhale ngati inu mwininu mungafe mukumawathandiza iwo?—Munthu amene akaupereka moyo wache kuwapulumutsa anthu ena amasonyeza kuti iye amawakonda iwo kwambiri.
Yesu anasonyeza kuti iye anali ndi mtundu umenewo wa chikondi kaamba ka ife. Iye anali wofunitsitsa kuchoka kumwamba ndi kutumizidwa ku dziko lapansi kudzatifera ife. Kodi inu munadziwa kuti iye anatifera ife?—
Kodi inu mungafune kumva mmene iye anachichitira chimenechi?—Tiyeni ife tikhale ngati kuti tiri pomwepo ndipo tingathe kuona chimene chikuchitika.
Uli usiku kwambiri usiku wina wa nthawi ya ngululu pa Yerusalemu. Mwezi ukuwala ndala wonse. Pamene ife tikuyang’ana pa mzindawo ife tikumuona Yesu ndi atumwi ache akuyenda kudzera pa chipata chachikuru ndi kuchoka mu mzindawo. Iwo akudza ku phiri lina limene limachedwa Phiri la Azitona ndipo akulowa m’munda. Kodi tiwatsatire iwo?—
Pamene ife tikuyang’ana, tikumuona Yesu akumachoka pakati pa ophunzira ache nagwada kupemphera kwa Atate wache. Iye akuchichita chimenechi katatu. Ndipo ulendo uli wonse iye akubwelera nawauza ophunzira ache kuti iwo ayenera kumapempheranso. Kodi chifukwa ninji? Kodi kudzachitikanji?—
Taonani! Kodi mukuwaona anthu awo omadza kulinga ku mundawo? Ena a iwo ali ndi nyali. Enanso ali ndi zibonga. Pali asilikari okhala ndi malupanga. Iwo akuonekera kukhala opanda ubwenzi kwambiri. Ndithudi Yesu ayenera kuwaona iwo akudza. Kodi iye sanayenera kuyesa kuthawa?—
Yesu akuwaona iwo, koma iye sakuthawa. Tsopano asilikariwo akufika ndi kumgwira Yesu. Kodi iye adzawalola iwo kuti amtenge? Iye akadatha kupfuulira kwa Atate wache. Mulungu akadatha kumtumizira iye zikwi zambiri za angelo. Iwo akadatha kuwaononga anthu amenewo pasanapite nthawi. Ngati inu mukadakhala Yesu, kodi inuyo mukadawaitanitsa angelowo?—
Koma Yesu akuwalola anthuwo kumtenga iye. Chifukwa ninji?—Chifukwa chakuti iye ali kufunitsitsa kutifera ife. Pali chifukwa china chofunika kwambiridi. Iye akumuuza wophunzira Petro kuti: ‘Mau a Mulungu ayenera kukwaniritsidwa.’ Eetu, kunali kutalembedwa kale m’Baibulo kuti Yesu akaupereka moyo wache kaamba ka mtundu wa anthu.
Ophunzira a Yesu tsopano anagwidwa mantha nathawa. Asilikariwo anamtengeranso Yesu ku mzindawo. Tiyeni tiwatsatire iwo ndi kuona chimene chikuchitika.
Iwo akumtengera Yesu pamaso pa akulu a ansembe. Ansembe amenewa akumuda Yesu chifukwa chakuti iye wakhala akumawasonyeza anthu kuti ansembewo sakuphunzitsa Baibulo.
Ansembewo akumzenga mlandu. Iwo akuwatengeramo anthu amene akunena bodza ponena za Yesu. Iwo akumfunsa Yesu mafunso kuyesa kutsimikiziradi kuti iye wachita kanthu kena kolakwa. Koma iwo sangathe kutsimikizira kanthu motsutsana naye. Kenako ansembewo akuti kwa Yesu: ‘Kodi inu ndinu Mwana wa Mulungu?’ Yesu akuti: ‘Ndine amene.’ Ansembewo akupsya mtima ndi kuti: ‘Iye ali ndi liwongo! Iye ayenera kuphedwa!’ Ena onsewo akubvomereza. Ena a anthuwo pamenepo anayamba kumamtonza Yesu. Iwo anamlabvulira iye malobvu ndi kummenya iye ndi nkhonya zao. Kodi Yesu akuyamba kumva chisoni kuti iye waphunzitsa choonadi kuchokera m’Baibulo? Kodi inuyo mukadamva bwanji?—
Eya, Yesu sali ndi chisoni ndipo iye sakudandaula kumene kapena kubwezera.
Tsopano kukucha. Yesu sanagone usiku wonsewo. Ansembewo tsopano alamulira kuti Yesu amangidwe, ndipo iwo akumtsogolera iye kunka kwa Pilato, kazembeyo.
Iwo akumuuza Pilato kuti: ‘Yesu ali wotsutsana ndi boma. Iye ayenera kuphedwa.’ Koma Pilato akuona kuti ansembewo ali kunena bodza. Chotero Pilato akuwauza iwo kuti: ‘Ine sindikupeza cholakwa chiri chonse ndi munthu ameneyu. Ndizamlola iye apite.’ Koma ansembewo limodzi ndi ena akupfuula kuti: ‘Ai! Mupheni!’
Pambuyo pache, Pilato akuyesa kachiwiri kuwauza anthuwo kuti iye adzamlola Yesu apite mwaufulu. Koma ansembewo anawachititsa makamuwo kupfuula kuti: ‘Ngati inu mummasula iye inunso muli kutsutsana ndi boma! Mupheni!’ Kukufikira kukhala kwaphokoso kwambiri. Kodi nchiani chimene Pilato adzachita?
Iye akugonjera. Choyamba iye akulamulira kuti Yesu akwapulidwe. Ndiyeno iye akumpereka iye kwa asilikari kuti aphedwe.
Iwo akumpatsa Yesu mtanda waukuru kapena mtengo kuti anyamule. Potsirizira pache iwo akufika ku malo ochedwa Malo a Bade kunja kwa mzindawo. Kumeneko iwo akuwakhomera manja ndi mapazi a Yesu ku mtengowo. Kenako iwo akuuimika uwo kotero kuti Yesu akupachikika pa uwo. Iye akuchucha mwazi. Ululuwo uli waukuru kwambiri.
Yesu sakufa nthawi yomweyo. Iye akungopachikika pamenepo pa mtengowo. Akulu a ansembewo akumtonza iye. Iwo akuti: “Ngati inu muli mwana wa Mulungu, tsikani pa mtengo wozunzirapowo!” Koma Yesu akuchidziwa chimene Atate wache wamtumiza iye kuchichita. Iye akudziwa kuti iye ayenera kuupereka moyo wache wangwiro kotero kuti ife tingathe kukhala ndi mwai wa kupeza moyo wosatha. Potsirizira pache, pafupifupi ora lachitatu madzulo amenewo, Yesu apfuulira kwa Atate wache ndipo amwalira.—Mateyu 26:36-27:50; Luka 22:39-23:46; Yohane 18:1-19:30, NW.
Ha, ndi wosiyana chotani nanga mmene analiri Yesu ndi Adamu! Adamu sanasonyeze chikondi kaamba ka Mulungu. Iye sanamumvere Mulungu. Adamu sanasonyezenso chikondi kaamba ka ife. Chifukwa chakuti iye anachimwa, tonsefe tabadwa ndi uchimo uli mwa ife. Koma Yesu anasonyeza chikondi kaamba ka Mulungu ndi kaamba ka ife. Iye anamumvera Mulungu masiku onse. Ndipo iye anaupereka moyo wache kotero kuti akathe chibvulazo chimene Adamu anatichitira ife.
Kodi inu mukuchiyamikira chinthu chodabwitsa chimene Yesu anachichita?—Pamene inu mupemphera kwa Mulungu, kodi inu mumamthokoza iye kaamba ka chimene Mwana wache anachichita?—Chimenecho chidzasonyeza kuti inu mukuchiyamikira icho. Ndipo ngati ife tichichitadi chimene Mphunzitsi Wamkuruyo amachinena, ife tidzasonyeza moonjezerekadi mmene ife tikuyamikilira kuti iye anaupereka moyo wache kaamba ka ife.
(Kuti muonjezere chiyamikiro kaamba ka chimene Yesu anatichitira ife, werengani Yohane 3:16; Aroma 5: 8, 19; 1 Timoteo 2:5, 6; Mateyu 20:28.)