Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • te mutu 39 tsamba 159-162
  • ‘Wodala Ali Amene Akudza monga Mfumu’

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • ‘Wodala Ali Amene Akudza monga Mfumu’
  • Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ufumu wa Mulungu ndi Chiyani? Zimene Tingachite Posonyeza Kuti Tikuufuna
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Boma la Mulungu la Mtendere
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo
te mutu 39 tsamba 159-162

Mutu 39

‘Wodala Ali Amene Akudza monga Mfumu’

KODI INU mukulidziwa pemphero la Ambuye?—Ndifuna ndimve inu mukulinena ilo.—Ngati simukulikumbukira ilo, tidzaliwerenga pamodzi kuchokera m’Baibulo pa Mateyu chaputara chachisanu ndi chimodzi, vesi la chisanu ndi chinai kufikira la khumi ndi chitatu.

Tsopano, m’pemphero limenelo ilo limati, “Ufumu wanu udze.” Kodi ufumu nchiani? Kodi inu mukuchidziwa?—

Ufumu ndiwo boma. Ndipo inu mukuchidziwa chimene chiri boma, eti?—Boma ndilo kagulu ka anthu amene amalilamulira dziko.

Mu boma mumakhala munthu wina amene ali wamkuru kapena wolamulira. M’maiko ena munthu ameneyu amachedwa prezidenti. Koma kodi inu mukuchidziwa chimene wolamulira wa boma la Mulungu akuchedwa?—Iye ndi mfumu.

Ponena za ufumu wa Mulungu Yehova mwiniyo waisankha mfumu. Kodi inu mukumdziwa amene ali mfumu imeneyo?—Iye ndi Yesu Kristu. Iye ali bwino kwambiri koposa wolamulira ali yense amene anthu amamsankha. Yesu ali ndi mphamvu yaikuru koposa ali yense wa olamulira amenewo. Ndipo Yesu amamkondadi Mulungu, chotero iye masiku onse amachita chimene chiri choyenera.

Kalekale mu Israyeli mafumu atsopano ankalowa m’Yerusalemu atakwera pa mwana wa buru kudzisonyeza okha kwa anthuwo. Ichi ndicho chimene Yesu anachichita.

Kunja pang’ono kwa Yerusalemu kunali mudzi waung’ono. Pamene Yesu anauyandikira uwo, iye anati kwa awiri a ophunzira ache: ‘Lowani m’mudzi uja, ndipo inu mudzampeza mwana wa buru. Mmasuleni iye ndi kudza naye kwa ine.’

Ophunzirawo anachita monga momwe Yesu ananenera. Ndipo pamene iwo anadza naye mwana wa buruyo kwa Yesu, iye anakhala pa iye. Pamene iye anayandikira Yerusalemu, khamu lalikuru la anthu linaturuka kudzamchingamira iye.

Pamene Yesu analinkuyenda ali pa buru, ochuruka a khamulo anayamba kumayala zobvala zao pa mseuwo patsogolo pache. Ena anagwetsa nthambi kuchokera m’mitengo naziika zimenezi pa mseuwo. Mwa chimenechi iwo anasonyeza kuti iwo anamfuna Yesu monga mfumu.

Anthuwo anali okondwa kumlandira Yesu. Iwo anapfuula kuti: “Wodala ali Amene akudza monga Mfumu m’dzina la Yehova!”

Koma osati munthu ali yense anali wokondwa kuti Yesu anali kumalowa m’Yerusalemu ali pa buru monga mfumu. Ena ananenadi kwa Yesu kuti, ‘Uzani ophunzira anu akhale chete.’—Luka 19:28-40.

Kodi inu mukulingalira bwanji ponena za kumakhala ndi Kristu monga mfumu?—Ngati inuyo mukadakhala muli ndi moyo pamene Yesu analowa m’Yerusalemu ali pa buru, kodi inuyo mukadamlandira iye monga amene anatumidwa ndi Yehova kwa anthu ache?

Eya, Yesu sali pa dziko lapansi lero lino, kodi sichoncho?—Iye ali kumwamba. Kuli kuchokera kumwamba kumeneko chakuti iye amalamulira monga mfumu. Ngakhale kuli kwakuti ife sitingamuone iye, iye angathe kumuona ali yense wa ife pano pa dziko lapansi. Ife sitingamnyenge iye. Iye amaziona zimene ife timazichita, ndipo iye amazidziwadi zimene ife tiri kumaziganiza. Ngati ife timamkondadi Yehova, iye amachidziwa chimenecho. Ndipo ngati ife tiri kumayesayesa zolimba kuchita chimene Baibulo limachinena, iye adzatithandiza ife. Kodi inu mukafuna kukhala ndi iye monga mfumu yanu kosatha?—

Si munthu ali yense amene amamfuna Kristu kukhala mfumu. Iwo anganene kuti iwo amakhulupilira Mulungu, koma iwo samaufuna ufumu wache. Iwo samamfuna Mulungu kapena Kristu kumawauza iwo cha kuchichita. Iwo amafuna maboma ao a iwo eni pa dziko lapansi pano. Motero kodi mukuchidziwa chimene chidzawachitikira iwo?—

Baibulo limatipatsa ife yankho pa Danieli chaputara chachiwiri, vesi la makumi anai mphambu anai. Tiyeni titenge Mabaibulo athu ndi kubandakula pamenepo limodzi. Lemba limeneli liri kulankhula za tsiku lathu la ife eni pamene ilo limati: “M’masiku a mafumu awo Mulungu wa kumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzaonongedwa konse. Ndipo ufumuwo sudzasiyidwira anthu ena ali onse. Uwo udzaphwanya ndi kutha maufumu onse amenewa, ndipo uwo wokha udzakhala kosatha.” (NW)

Kodi munachimvetsetsa chimenecho?—Baibulo limanena kuti boma la Mulungu lidzawaononga maboma onse a pa dziko lapansi amenewa. Chifukwa ninji?—Chifukwa chakuti iwo sakumumvera uyo amene Mulungu wampanga kukhala mfumu.

Dziko lonse lapansi nla Mulungu. Iye analipanga ilo kuphatikizapo chilengedwe chonse. Chotero iye ali ndi kuyenera kwa kusankha mtundu wa boma umene uyenera kulamulira. Ndipo boma lache liri labwino kopambana. Posachedwapa ufumu wa Mulungu udzakhala boma lokha liripo.

Kodi inu mukufuna kukhala ndi moyo kosatha pansi pa ufumu wa Mulungu?—Ine ndikufuna. Koma ife tifunikira kusonyeza chimenecho kwa Mulungu. Kodi mukudziwa kuchita kwache?—Ndiko mwa kumawaphunzira malamulo a Mulungu ndi kumawamvera iwo tsiku liri lonse.

Tsopano, Mulungu akuti ufumu wache udzawaononga maboma a anthu. Koma kodi iye amatiuza ife kuti ife tiyenera kuchita chimenecho?—Ai. Baibulo limanena kuti ife tiyenera kuwamvera malamulo a anthu, kufikira pamene Mulungu awalola maboma amenewo kulamulira.

Koma ngati ife timamfunadi Kristu monga mfumu, ife tiyenera kuchita zoposa zimenezo. Ife tiyenera kuzimvera zinthu zonse zimene Kristu ananena. Iye ananena kuti ife sitiyenera kukhala “mbali ya dziko lapansi.” Kodi ife tikadakhala tikumamumvera iye ngati ife tidayesayesa kukhala mbali ya maboma a dziko lapansi?—Yesu ndi atumwi ache anatalikirana ndi zinthu zoterozo.—Yohane 17:14, NW.

Kodi nchiani chimene iwo anachichita m’malo mwache?—Iwo analankhula kwa anthu ena ponena za ufumu wa Mulungu. Imeneyo inali nchito yaikuru m’miyoyo yao. Kodi ife tingathe kuichitanso imeneyo?—Inde, ndipo ife tidzaichita iyo ngati ife timachitanthauza chimene ife timachinena pamene ife timaupempha ufumu wa Mulungu kuti udze.

(Khalani ndi mphindi zina pang’ono tsopano kuti muwerenge malemba ena awa amene amasonyeza mmene ife tiyenera kumuonera uyo amene Mulungu wampanga kukhala mfumu: Yesaya 9:6, 7; Danieli 7:13, 14; Yohane 18:36; Mateyu 6:33.)

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena