Mutu 38
Chikondi kaamba ka Nyumba ya Mulungu
KODI INU mumakonda pamene ife taitanidwa kupita ku nyumba ya munthu wina kaamba ka chakudya chamadzulo?—Bwanji ngati ife tikanaitanidwa ku nyumba ya Mulungu, kodi inu mukadafuna kupita?—
Tsopano, inu munganene kuti Mulungu samakhala m’nyumba. Ndipo nzoona kuti Mulungu samakhala m’nyumba m’njira imene ife timachitira.
Koma Mphunzitsi Wamkuruyo ananena kuti Mulungu anali ndi “nyumba.” Ndipo Yesu anazolowera kupita ku nyumba ya Mulungu, ngakhale pamene iye anali mnyamata wamng’ono. Nyumba imeneyo inali kachisi wokongola wa Yehova mu mzinda wa Yerusalemu. Kachisi ameneyo anali wa Mulungu. Iye anali kumagwiritsiridwa nchito kaamba ka kulambira kwache. Chotero iye ankachedwa “nyumba ya Yehova.”
Pamene Yesu anali mnyamata, iye anali kukhala kutali kwambiri ndi “nyumba ya Yehova.” Palibe munthu ali yense anali ndi galimoto m’masiku amenewo, ndipo kunalibe matreni amene iwo akadatha kukwera. Kuti afike ku kachisiyo, iwo akadafunikira kuyenda pansi. Uwo sunali ulendo wa ora limodzi lokha kapena kupitilirapo kuchokera kumene iwo anali kukhala. Iwo ankafunikira kuyenda pansi kwa pafupifupi masiku atatu kuti afike kumeneko. Ndipo ulendo wobwelera ukatenga masiku ena atatu. Kodi unali woyenelera kuyesayesa konseko kuupanga ulendo woterowo? Kodi inuyo mukadayenda utali woterowo kukakhala mu “nyumba ya Mulungu”?—
Anthu amene anaikonda “nyumba ya Mulungu” sanganize kuti iyo inali kutali kwambiri. Chaka chiri chonse makolo a Yesu ankapita ku Yerusalemu kukalambira. Ndipo Yesu anatsagana nawo.
Chaka china, pamene iwo anauyamba ulendo wobwelera kwao, Yesu sanali limodzi ndi banja lache. Palibe ali yense amene anadziwa kufikira iwo atayenda ulendo wautali. Pamenepo makolo ache anabwelera m’mbuyo kukamfunafuna iye. Kodi inu mukuganizira kuti iye anali kuti?—
Iwo anampeza iye m’kachisi mwenimwenimo. Iye anali kumamvetsera kwa aphunzitsiwo. Iye anali kumafunsa mafunso. Ndipo pamene iwo anamfunsa iye kanthu kena, iye ankayankha. Iwo anadabwa ndi mayankho abwino kwambiri amene iye anawapereka.
Ndithudi, pamene makolo ache anampeza iye potsirizira pache, iwo anamva bwino kwambiri. Koma Yesu sanakhale wodera nkhawa. Iye anadziwa kuti kachisiyo anali malo abwino kukhalapo. Chotero iye anafunsa kuti: “Kodi inu simunadziwe kuti ine ndiyera kukhala m’nyumba ya Atate wanga?” Iye anadziwa kuti kachisi anali “nyumba ya Mulungu.” Ndipo iye anakonda kukhala kumeneko.- Luka 2:41-49, NW.
Sikunali kokha kamodzi pa chaka pamene Yesu ndi makolo ache anapita ku misonkhano kaamba ka kulambira. Mlungu uli wonse kunali misonkhano kaamba ka kulambira m’tauni kumene iwo anakhala.
Pa misonkhano imeneyo munthu wina ankaimilira ndi kuwerenga Baibulo. Iwo sanakhale nalo lonse m’bukhu limodzi. Ilo linalembedwa pa mipukutu yaitali. Chotero iwo anaufunyulula uwo kufika ku malo amene iwo anawafuna ndipo kenako kuyamba kuwerenga. Pambuyo pa chimenecho ilo linkafotokozedwa. Baibulo limanena kuti chinali “chizolowezi” cha Yesu kufika pa misonkhano imeneyi. Chimenecho chikutanthauza kuti iye anapita mokhazikika.—Luka 4:16, NW.
Ife tiyeneranso kuchita chimenecho. Koma kodi “nyumba ya Mulungu” iri kuti lero lino? Kodi ife tiyenera kupita kuti kukamlambira iye?—
Kachisi kumene Yesu anapita m’Yerusalemu kulibenso kumeneko. Iye anaonongedwa. Chotero ife sitingathe kupita kumeneko.
Koma Mulungu ali nayobe “nyumba.” Iyo siiri nyumba imene yamangidwa ndi miyala. Iyo yapangika ndi anthu. Kodi chimenecho chikatheka bwanji? Eya, nyumba ndiyo malo okhalamo. Ndipo Mulungu amanena kuti iye ali ndi anthu ache. Iye samachoka kumwamba ndi kutsikira ku dziko lapansi. Koma Mulungu ali pafupi kwambiri ndi anthu ache chakuti iwo amaona ngati kuti ali pomwepo limodzi ndi iwo.—1 Petro 2:5; Aefeso 2:22; 1 Timoteo 3:15.
Chotero, pamene ife tipita ku “nyumba ya Mulungu,” kodi ife tiyenera kupita kuti?—Ife tiyenera kupita kumene anthu a Mulungu asonkhana kaamba ka kulambira. Kungakhale m’nyumba yaikuru. Kungakhale mu yaing’ono. Kapena kungakhale m’nyumba ya munthu wina. Chinthu chofunika ndicho chakuti iwo akhaledi anthu a Mulungu. Koma kodi ife tingathe kudziwa bwanji ngati iwo ali anthu ache?—
Eya, kodi nchiani chimene iwo amachichita pa misonkhano yao? Kodi iwo amaphunzitsadi chimene chiri m’Baibulo? Kodi iwo amaliwerenga ilo ndi kulikambitsirana ilo? M’menemo ndimo mmene ife timamvetselera kwa Mulungu, ati?—Ndipo pa “nyumba ya Mulungu” ife tikayembekezera kumva chimene Mulungu amachinena, ati?—
Koma bwanji ngati anthu anena kuti inu simufunikira kukhala ndi moyo m’njira imene Baibulo limanena? Kodi inuyo mukananena kuti iwo ali anthu a Mulungu?—
Naka kanthu kenanso kakukaganizira. Baibulo limanena kuti anthu a Mulungu akakhala “anthu kaamba ka dzina lache.” Kodi dzina la Mulungu ndani?—Ndilo Yehova. Chotero ife tingawafunse anthu ngati Mulungu wao ali Yehova. Ngati iwo anena kuti “Ai,” pamenepo ife tidziwa kuti iwo sali anthu ache.—Machitidwe 15:14, NW.
Koma sikuli kokwanira kungonena kuti Yehova ndiye Mulungu wao. Kodi umboni uli kuti? Iwo ayenera kumalankhula za iye kwa anthu ena. Iwo ayenera kumawauza anthu ponena za ufumu wa Mulungu. Iwo ayenera kukhala ndi chikhulupiliro mwa Mwana wache. Iwo ayenera kusonyeza chikondi chao kaamba ka Mulungu mwa kumawasunga malamulo ache.—Yesaya 43:10.
Kodi ife tikuwadziwa anthu amene amazichita zinthu zonse zimenezo?—Pamenepo ife tiyenera kumasonkhana nawo kaamba ka kulambira. Ndipo ife tiyenera kufikako mokhazikika. Ife tiyenera kumamvetsera kwa awo amene amaphunzitsa, ndi kumawayankha mafunso pamene iwo afunsidwa. Chimenecho ndicho chimene Yesu anachichita pamene iye anali mu “nyumba ya Mulungu.” Ngati ife tichichita chimenecho, ife timasonyeza kuti ife, nafenso, timaikondadi “nyumba ya Mulungu.”
(Ife tiyenera kukondwera ndi kumafika pa misonkhano mokhazikika limodzi ndi anthu a Mulungu. Werengani chimene chanenedwa ponena za ichi pa Salmo 122:1 [121:1, MO]; Ahebri 10:23-25.)