Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ts mutu 4 tsamba 26-36
  • Kodi Ukalamba ndi Imfa Zinakhalako Motani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Ukalamba ndi Imfa Zinakhalako Motani?
  • Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI N’CHIFUKWA NINJI ZOFANANA’ZO?
  • MOYO WODALIRA PA KUMVERA
  • CHIFUKWA CHACHIKULU—UCHIMO
  • Cifukwa Cace Timakalamba ndi Kufa
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Kodi N’chifukwa Chiyani Timakalamba Komanso Kufa?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Mdani Wathu Womalizira Adzawonongedwa
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Yesu Anafa Ndi Kuukitsidwa—Kuti Tidzapeze Moyo Wosatha
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
ts mutu 4 tsamba 26-36

Mutu 4

Kodi Ukalamba ndi Imfa Zinakhalako Motani?

NGAKHALE kuli kwakuti zimalandiridwa mofala monga zachibadwa, ukalamba ndi imfa zikuthetsa anthu nzeru. Chimene’chi chiri choonekera bwino kuchokera m’cheni-cheni chakuti kwa zaka mazana ambiri miyambi yasiyiranidwa-siyiranidwa yoyesa kulongosola chifukwa chake anthu amakalamba ndi kufa.

Bukhu lina la nthanthi yakale Yachigriki limasimba za mkazi wochedwa Pandora amene anatsegula bokosi kapena mphika wa maluwa limene iye anauzidwa kusalitsegula. Kukunenedwa kuti, kachitidwe kamene’ka, kanatulutsa “Ukalamba,” “Kudwala,” “Misala” ndi “Matenda” ena zimene zimapitirizabe kukantha mtundu wa anthu.

Mu Australia, mafuko osiyana-siyana a anthu ochedwa Aborigines amakhulupirira kuti poyambirira anthu analinganizidwa kukhala ndi moyo kosatha. Koma iwo anayenera kutalikirana ndi mtengo wina wa mphako. Pamene njuchi zinapanga mtengo umene’wu kukhala malo ao okhala, akazi analakalaka kwambiri uchi wake. Monyalanyaza chenjezo la amuna, mkazi wina anagwiritsira ntchito kankhwangwa kake pa mtengo’wo. Atatero, mleme wamkulu anauluka, umatero mwambi’wo. Mleme amene’yo anali “Imfa.” Atatulutsidwa mu mtengo’wo, anamka napha onse amene anawakhudza ndi mapiko ake.

N’kwapadera kuti miyambi ya mitundu ina, yotalikirana kwambiri imanena mofananamo kuti imfa iri yochititsidwa ndi kusamvera, kawiri-kawiri mkazi akumalowetsedwamo choyamba.

KODI N’CHIFUKWA NINJI ZOFANANA’ZO?

Powerenga nthanthi zotero’zo, anthu ena angayedzamire ku kuika kulongosola kwa Baibulo chochititsa ukalamba ndi imfa m’gulu limodzi-modzi’lo. Iwo angasonyeze’di kuti m’mbali zina nthanthi zimaonekera kukhala zikufanana ndi kulongosola kwa Baibulo. Koma kodi n’chifukwa ninji pali zofanana zimene’zi? Kodi n’kothekera kuti miyambi imene’yi iri ndi maziko eni-eni amene angopotozedwa?

Baibulo leni-leni’lo limasonyeza mayankho a mafunso amene’wa. Limasonyeza Babulo wakale m’Kaldayo kukhala malo kumene anthu amene anapandukira Mulungu mwa kunyoza lamulo lake anamwazidwa. (Genesis 11:2-9) Ndandanda za Baibulo za mibadwo zimasonyeza kuti kumene’ku kunachitika pa nthawi imene amuna ena anali ndi moyo amene, monga atumiki okhulupirika a Mulungu, anadziwa choonadi chonena za moyo ndi chochititsa imfa. (Genesis 6:7, 8; 8:20, 21; 9:28; 10:1-9; 11:10-18; 1 Mbiri 1:19) Komabe, unyinji, popeza kuti iwo eni’wo anali kusonyeza kunyalanyaza choonadi chonena za chifuno cha Mulungu kwa munthu, sakanayembekezeredwa’di kusunga molondola choonadi chonena za m’mene imfa inakhalirako. Pamene iwo anafalikira, ndipo limodzi ndi kupita kwa nthawi, zeni-zeni zinapotozedwa ndi kuonjezeredwamo zonama; nthanthi zinabuka. Pali kusiyana-siyana kwambiri m’malongosoledwe ao a nthanthi onena za chochititsa ukalamba ndi imfa, komabe maziko amodzi akulu ngozindikirika.

Kumene’ku si kuyerekezera chabe. Umboni umene ulipo umasonyeza bwino lomwe kuti nthanthi zachipembedzo, kuphatikizapo zija zonena za imfa, zimachokera ku magwero amodzi. M’bukhu lake lakuti The Worship of the Dead, Colonel J. Garnier akulongosola kuti:

“Osati kokha Aigupto, Akaldayo, Afoinike, Agrikindi Aroma, koma’nso Ahindi, Abuda a ku China ndi a ku Tibeti, Ajeremani, Angelezi, Abritishi, Ameresiko ndi Aperu, Aborijini a ku Australia, ndipo ngakhale anthu osatsungula a m’Zisumbu za Kumwela kwa Nyanja ya Pacific, onse ayenera kukhala atatenga malingaliro ao achipembedzo ku magwero amodzi ndi pa phata limodzi. Kuli konse timapeza kufanana kwambiri mu nsembe, madzoma, miyambo, miyambi, ndi m’maina ndi zigwirizano za milungu ndi milungu yao yachikazi.”

Ndipo kodi ndi malo otani amene ali magwero amodzi amene’wa? Kodi umboni umasonyeza Kaldayo, monga mowe Baibulo limasonyera? Profesala George Rawlinson amati:

“Kufanana kwakululu kwa dongosolo la Akaldayo ndi kuja kwa nthanthi [kwakukulu-kulu za Agriki ndi Aroma] kumaonekera kukhala koyenera kuonedwa mwapadera. Kufanana kumene’ku kuli kofala kwambiri, ndi kogwirizana kwambiri m’mbali zina, kosati n’kutheketsa kuyerekezera kuti ngozi chabe yachititsa kufanana’ko. Mu Akachisi a ku Grisis ndi Roma, ndi mu aja a Kaldayo, kuikidwa m’gulu limodzi kofanana’ko [kwa milungu ndi milungu yachikazi] kuyenera kuzindikiridwa; kutsatizana-tsatizana kwa mibadwo kofanana’ko kulondoledwa; ndipo m’zochitika zina ngakhale maina aulemu odziwika a milungu Yachigriki ndi Yachiroma amabvomereza fanizo ndi kulongosola kwachilendo kwambiri kuchokera kwa Akaldayo.”

Kodi iye chifukwa cha chimene’cho akunenanji?

“Sitingakaikire kusiyapo kuti, mwa njira zosiyana-siyana, panali kusinthana zikhulupiriro—kupatsirana-patsirana m’nthawi zakale kwambiri’zo, kuchokera ku gombe la Chidikha cha Peresiya [kumene Babele wakale anali] kumka ku maiko a ku gome la Mediterranean kwa maganizo ndi malingaliro anthanthi.”

Motero chimene Baibulo limasonyeza ponena za kubuka kwa malingaliro achipembedzo chikupezeka kukhala chogwirizana ndi umboni wina wa mu mbiri. Ngati Baibulo limasunga’di molondola choonadi chimene nthanthi zachipembedzo pambuyo pake zinachipotoza, cholembedwa cha Baibulo chiyenera kukondweretsa malingaliro athu. Cholembedwa’cho chiyenera kumveka bwino. Kodi chimamveka?

MOYO WODALIRA PA KUMVERA

Polongosola zochititsa ukalamba ndi imfa, bukhu loyamba la Baibulo, Genesis silimanena mwa kanenedwe kakuti “kale-kale” mu “nthano yongoyerekezera,” koma limapereka cholembedwa cheni-cheni. Limanena za malo eni-eni, Edene, malo ake eni-eni ofala akumadziwikitsidwa ndi mitsenje inai. Iwiri ya imene’yi, Filate ndi Tigrisi (Hidikeli), ikudziwika kufikira lero lino. (Genesis 2:1-14; New English Bible) Nthawi’yo ingathe kutsimikiziridwa ndi kuwerengera nthawi kwa Baibulo kukhala chaka cha 4026 B.C.E. kapena mwamsanga pambuyo pake. Ndipon’so, kuchula kwa Baibulo anthu awiri oyambirira kuli komveka bwino mwasayansi. Bukhu lakuti The Races of Mankind limati:

“Nkhani ya Baibulo yonena za Adamu ndi Hava, atate ndi amai a pfuko lonse la anthu, inalongosola zaka mazana ambiri zapita’zo choonadi chimodzi-modzi’cho chimene sayansi yasonyezera lero lino: chakuti mitundu yonse ya pa dziko lapansi iri banja limodzi ndipo iri ndi magwero amodzi.”

Chitalongosola m’mene munthu woyamba anakhalirako, cholembedwa cha Baibulo chimasonyeza kuti Mlengi, Yehova Mulungu, anayambitsa mtundu wa anthu m’malo okhala okongola. Iye anaika pamaso pa munthu chiyembekezo cha moyo wopanda mapeto, pamene pa nthawi imodzi-modzi’yo akumapangitsa kusangalala nawo kwake kukhala kodalira pa kanthu kena. Mulungu kwa mwanuna’yo anati: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umene’wo chifukwa tsiku lomwe udzadya umene’wo udzafa ndithu.”—Genesis 2:16, 17.

Limene’lo linali lamulo losabvuta. Komabe kodi zimene’zi sindizo zimene tiyenera kuyembekezera? Mwamuna’yo Adamu anali yekha pa nthawi’yo. Moyo unali wosabvuta ndi wosacholowana-cholowana. Panalibe mabvuto m’kupeza chakudya. Panalibe zitsenderezo zochokera ku dongosolo laumbombo lamalonda. Malamulo obvuta sanali ofunika kuti aletse zikhoterero za uchimo zokhala m’kati mwa mwamuna woyamba’yo. Monga munthu wangwiro, Adamu analibe zizolowezi za uchimo.

Losabvuta monga momwe lamulo limene’li linaliri, linalowetsamo mikangano ya mikhalidwe yokhala ndi chotulukapo choopsya. Kusamvera lamulo la Mulungu kwa anthu oyambirira kukanatanthauza kum’pandukira monga Wolamulira. Kodi ziri choncho motani?

Kunali kuletsa kwa Mulungu kumene kunapangitsa kudya chipatso cha “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa” kukhala kolakwa. Munalibe mankhwala akupha m’chipatsomo. Chipatso’cho chinali chabwino, kweni-kweni ‘chabwino kudya.’ (Genesis 3:6) Chifukwa cha chimene’cho, kuletsa kwa Mulungu mtengo’wo kunagogomezera kudalira koyenera kwa munthu pa Mlengi wake monga Wolamulira. Mwa kumvera mwamuna ndi mkazi oyamba’wo akadasonyeza kuti iwo analemekeza kuyenera kwa Mulungu kwa kuwadziwitsa chimene chinali “chabwino,” kapena chobvomerezedwa mwaumulungu, ndi chimene chinali “choipa,” kapena chotsutsidwa mwaumulungu. Chifukwa cha chimene’cho kusamvera kwao kukatanthauza kupandukira ulamuliro wa Mulungu.

Yehova Mulungu analongosola chilango cha chipanduko chotero’cho kukhala imfa. Kodi chimene’cho chinali chilango chopambanitsa? Eya, kodi mitundu yambiri ya dziko lapansi simakulingalira kukhala kuyenera kwao kucha maupandu ena kukhala machimo ofunikira chilango cha imfa? Komabe mitundu imene’yi singathe kupereka kapena kuchirikiza kosatha moyo wa ali yense. Koma Mlengi wa munthu angathe. Ndipo chinali chifukwa cha chifuniro chake kuti Adamu ndi Hava anakhalako. (Chivumbulutso 4:11) Chotero kodi sikunali koyenera kwa Wopereka ndi Wochirikiza moyo kusonyeza kusamumvera kukhala koyenerera imfa? Kunali koyenera’di! Ndiyeno’nso, iye yekha, anazindikira mokwanira kuopsya kwa zotulukapo zobvulaza zimene zikachokera m’kusamvera lamulo lake.

Mwa kumvera lamulo loletsa’lo, anthu awiri oyamba’wo, Adamu ndi Hava, akanasonyeza chiyamikiro ndi chithokozo chao kwa Mulungu kaamba ka zonse zimene iye adawachitira. Kumvera kosonkhezeredwa moyenera kukanawaletsa kukhala adyera ndi kunyalalanyaza Wochitira zabwino wao, Mulungu.

Lamulo’lo linali la mtundu umene tikauyembekezera kuchokera kwa Mulungu wachikondi ndi chilungamo. Silinali losayenera. Iye sanawamane zofunika za moyo. Panali mitengo ina yambiri imene iwo akanatha kukhutiritsa nayo njala yao ya chakudya. Chifukwa cha chimene’cho, ngakhale Adamu kapena Hava analibe chifukwa choonekera kukhala ofunikira chipatso cha “mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.”

Komabe, cholembedwa’cho chimasonyeza kuti tsiku lina, pamene sanali limodzi ndi mwamuna wake, Hava anagonjera ku chinyengo ndi kudya chipatso chokanizidwa’cho.a Pambuyo pake iye anapambana m’kuumiriza mwamuna wake kugwirizana naye m’kuswala lamulo la Mulungu.—Genesis 3:1-6.

Tsopano, kunganenedwe kuti Mulungu akanatha kutenga mkhalidwe wolekerera chipanduko cha anthu oyamba chimene’chi. Kungalingaliridwe kuti iye akanangonyalanyaza kulakwa kwao, akumakusiya kopanda chilango. Koma kodi imene’yo ikanakhala njira yabwino kopambana? Kodi si zoona kuti kulephera kuchirikiza lamulo pakati pa anthu lero lino kwachititsa kusalemekeza malamulo olugama ndi kuonjezeka kwa upandu ndi chiwawa? Kwa Mulungu kusiya cholakwa cha Adamu ndi Hava popanda chilango kukanatanthauza kuwalimbikitsa ndi ana ao kupititizabe kusayeruzika. Kumene’ku kukanapangitsa Mulungu kugawana nawo thayo la machitidwe otero’wo.

Ndiyeno’nso, kulekerera’ko kukanapereka chikaikiro pa kudalirika kwa mau a Mulungu. Kukanakupangitsa kuonekera kuti iye samatanthauza zimene iye amanena ndi kuti chifukwa cha chimene’cho malamulo ake angathe kuswedwa popanda chilango.

Motero kukukhala koonekera bwino kuti chinali chinthu chokha choyenera ndi cholungama kwa Mulungu kuchirikiza lamulo lake ndi kulola anthu oyamba kulandira zotulukapo zoyenera za kusamvera kwao kwadala ndi kofuna okha. Chosati n’kunyalanyazidwa ndicho chakuti palibe umboni wakulapa kuli konse kwa iwo. Iwo sanapereke umboni wa kusintha kwa mtima.

CHIFUKWA CHACHIKULU—UCHIMO

Mwa kupandukira kwao Mulungu, Adamu ndi Hava anadzidula ku unansi wabwino ndi iye. Iwo analibe moyo wosaonongeka ndi wosakhoza kufa. Baibulo limanena kuti mwa njira ya mphamvu yake ‘anazikhazikitsa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi ku nthawi za nthawi.’ (Salmo 148:3-6) Chimodzi-modzi’nso, ndi anthu awiri oyambirira’wo. Iwo anali odalira pa Mulungu kaamba ka moyo wopitirizabe.

Mwa kukana kugonjera ku lamulo la Mulungu, Adamu ndi Hava anadzichotsera mphamvu yake yochirikiza. Ndipo’nso, pokhala atatalikirana ndi Mulungu, iwo anali opanda chitsogozo ndi chilangizo chake chaumulungu. Pamenepo, m’nthawi yake, uchimo umene unatalikiranitsa Adamu ndi Hava ndi Mulungu unachititsa imfa yao.

Komabe, pambuyo pa kuchimwira kwao Mulungu iwo anali nakobe mwa iwo eni kuthekera kwakukulu kwa moyo. Chimene’chi chiri choonekera bwino kuchokera m’cholembedwa cha mu mbiri, chimene chimasonyeza kuti Adamu anakhala ndi moyo zaka 930. (Genesis 5:5) Komabe, limene linakwaniritsidwa pa Adamu linali chenjezo lakuti: “Tsiku lomwe udzadya umene’wo [mtengo wa kudziwitsa zabwino ndi zoipa] udzafa ndithu,” pakuti Mulungu anaweruzira Adamu ku imfa pa tsiku limene’lo.—Genesis 2:17.

Mwa kusamvera kwake, Adamu, monga kholo la banja la anthu, anadzetsa imfa, osati kokha kwa iye mwini, koma’nso kwa ana ake osabadwa. Ndicho chifukwa chake Baibulo limanena kuti: “Uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse chifukwa kuti onse anachimwa.”—Aroma 5:12.

Pokhala atataya ungwiro, Adamu sakanatha kuupitirizira kwa ana ake. Kuyambira pachiyambi ana ake anabadwa ndi zofooka. Kugwira ntchito kwa uchimo m’thupi lake kunapangitsa kukhala kosatheka kwa iye kubala ana opanda zirema ndi zofooka. Chimene’chi chimagwirizana ndi mau a Baibulo pa Yobu 14:4: “adzatulutsa choyera m’chinthu chodetsa ndani? nnena mmodzi yense.” Chifukwa cha chimene’cho, kukalamba ndi kufa kwa anthu lero lino zingathe kutsatiridwa kuyambira pachiyambi kufikira ku uchimo wolandiridwa kuchokera kwa Adamu. Monga ana ake, iwo akulandira mphotho imene uchimo umapereka—imfa.—Aroma 6:23.

Kodi imfa imasonyeza mapeto a njira yonse ya moyo, kapena kodi pali mbali ina ya munthu imene imapitirizabe kukhala ndi moyo? Kodi kukhalako kozindikira kumapitirizabe pambuyo pa imfa ya thupi?

[Mawu a M’munsi]

a Nsonga zonena za chinyengo chimene’chi ndi wochiyambitsa wake zikulongosoledwa m’chaputala 10.

[Mapu patsamba 28]

(Onani m’buku lenileni kuti mumvetse izi)

NTHANTHI ZA MAIKO AMBIRI ZINAYAMBIRA PA BABELE

GRISI

BABELE

AFIRIKA

INDIA

[Chithunzi patsamba 32]

Baibulo limanena kuti Mulungu anapatsa anthu oyamba’wo chiyembekezo cha kukhala ndi moyo wopanda mapeto

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena