Mutu 3
Mzimu Wochirikiza Dongosolo Lakale Liripo’li
1. Kodi ndi funso lotani limene likubuka ponena za mzimu umene walowerera dongosolo lakale la zinthu liripo’li, ndipo kodi tiyenera kunenanji?
DONGOSOLO la zinthu liripo’li liri lakale—lakale zaka zikwi zambiri. M’kati mwa zaka zonse zikwi zambiri za nthawi zimene’zo mzimu umodzi walowerera dongosolo laumunthu la zinthu. Kodi wakhala mzimu woyera? Palibe munthu ali yense akalankhula mosemphana kwambiri ndi zenizeni za mbiri kwakuti n’kunena kuti mzimu woyera wochokera kwa Yehova Mulungu wakhala mphamvu yosaoneka yomagwiritsa ntchito chitaganya chonse cha anthu m’ntchito zake, kapena mu mkhalidwe wake wa moyo. Ukadakhala kuti unali mzimu woyera umene nthawi yonse’yi wakhala ukuchirikiza ndi kusonkhezera dongosolo la zinthu lakale’li, zotulukapo zake zikanakhala zosiyana kwambiri ndi mkhalidwe wa zinthu wa dziko lero lino.
2. (a) Kodi anthu amene amayendera limodzi ndi dongosolo lakale’li alamulidwa ndi mtundu wotani wa malamulo? (b) Kodi ndi ziti zimene ziri “ntchito za thupi,”ndipo kodi “zipatso za mzimu” zapangika ndi chiani?
2 Mzimu woyera wochokera kwa Yehova Mulungu, pamene ukugwira ntchito m’miyoyo ya anthu, umatulutsa zipatso zodziwikitsa. Litatsimikiziridwa ndi zipatso zimene zakhala ndi nthawi yokwanira kuzitulutsa, dongosolo lakale’li silikutsongozedwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Unyinji wa anthu umene umagwirizana ndi dongosolo lakale’li umadzisonyeza kukhala anthu ofunikira kuletsedwa ndi malamulo amene amalinganizidwira anthu okhala ndi maganizi a upandu, malamulo amene chifukwa cha chimene’cho amawalamula kupewa mitundu yonse ya kulakwa. Zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo panali munthu amene anatuluka mu mpambo wa malamulo wotero’wo. Iye analemba kalata kusonyeza kuti tifunikira kukhala ndi chisonkhezero chabwino kwambiri, mphamvu yapamwamba kwambiri kuti ikhale yogwira ntchito m’miyoyo yathu, ngati tikufuna kukhala osiyana ndi dingosolo lakale liripo’li. Tifunikira mzimu, mphamvu yosaoneka yogwira ntchito imene imachokera kwa Uyo amene ali wabwino kopambana mwamakhalidwe koposa dongosolo la dziko lakale’li, wabwino kopambana koposa wopereka lamulo wina ali yense wa chitaganya chaumunthu. Mphamvu yoyera imene ingatichititse kugwira ntchito zoyenera wolemba kalata’yo anaisonyeza, nati:
“Muyendeyende ndi Mzimu, ndipo musafitse chilakolako cha thupi. Pakuti thupi lilakalaka potsutsana naye Mzimu, ndi Mzimu potsutsana nalo thupi; pakuti izi si ilingana; kuti zimene muzifuna musazichite. Ngati Mzimu akutsogolerani, simuli omvera lamulo.
“Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsya mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
“Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso chiletso; pokana zimene’zi palibe lamulo.”—Agalatiya 5:16-23; onani’nso 1 Timoteo 1:8-11.
3. Awo oyembekezera kulandira madalitso a ufumu wa Mulungu samachita ntchito zotani?
3 Mpambo ndithu wa zosiyana, kodi si choncho? Ndithudi awo amene amatulutsa zipatso za mzimu wa Mulungu samachita zinthu zochedwa “ntchito za thupi.” Iwo akuyembekezera ufumu wa Mulungu ndi chikhumbo choona mtima cha kulandira madalitso ake.
4. Kodi n’chifukwa ninji ife enife sitikufunikira kusonyeza zolakwa za dongosolo lakale, ndipo kodi n’chifukwa ninji dongosolo lakale limene’lo silidzathandiza anthu kulowa ufumu wa Mulungu?
4 Komabe bwanji ponena za dongosolo lakale liripo’li? Sititofunikira kusonyeza zolakwa zake. Zimene’zo zikuchitidwa kaamba ka ife ndi malipoti ake, a m’nyuzipepa, nkhani za m’magazini ake, zolembedwa zake za polisi, kupanda chisungiko konse kochititsidwa ndi kukwerakwera kwa chiwerengero cha upandu, zipatala zokwera mtengo za odwala misala kudza’nso matenda oopedwa a anthu, zitsenderezo za ndale za dziko limodzi ndi chiopsyezo chomakulakula cha nkhondo ya nyuklea ya pa dziko lonse lapansi. Zinthu zina zosawerengeka zikatha kuchulidwa kutsutsa dongosolo lakale’li kukhala lokhala ndi “ntchito za thupi” zochuluka. Dongosolo lakale limene’li silidzathandiza kons anthu “kulowa ufumu wa Mulungu.” Liribe chigwirizano chiri chonse ndi ufumu wa Mulungu. Siliri lomwerekeretsedwa, losonkhezeredwa kapena kuchirikizidwa ndi mzimu woyera wochokera kwa Mulungu. Siliri konse loyera, ngakhale’nso mbali yake imene ikuchedwa Chikristu cha Dziko siri yoyera.
5, 6. Kodi n’chifukwa ninji chikhumbo chachibadwa cha thupi cha kuchita zinthu zimene ziri zotsutsa mzimu wa Mlengi sichiri chochokera kwa Mulungu?
5 Kodi ndi motani m’mene kuliri kuti mzimu wa Mulungu sukuchirikiza mbali iri yonse ya dongosolo lakale’li? Kodi ndi motani m’mene thupi la munthu linalowera mu mkhalidwe umene mwachibadwa limakhumba kuchita ntchito zimene ziri zosemphana ndi mzimu wa Mulungu? Thupi la munthu silinali lotero pa chiyambi chake. Pa nthawi imene’yo linasonkhezeredwa ndi mzimu wa Mlengi wake. Mulungu sakanaika mwa munthu wolengedwa chatsopano’yo chija chimene chiri choipa ndi chotsutsana naye. Iye sali magwero a choipa. Monga ngwazi yochirikiza njira yolungama, mneneri Mose anachotsera Yehova Mulungu thayo lonse kaamba ka zizolowezi zolakwa za m’matupi a anthu. Mose anati: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika. Anam’chitira zobvunda si ndiwo ana ake, chirema n’chao.”—Deuteronomo 32:4, 5.
6 Chirema mwa anthu sichiri chochokera kwa Mulungu. Iye anapanga munthu woyambirira wangwiro, thamo ku luso Lake la kulenga. Kwa Mulungu kulibe chirema. Mogwirizana ndi Mwana wake wobadwa yekha, Mulungu analenga mwamuna woyamba “m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu.” Munthu woyambirira, Adamu, anali chifanizo cha ungwiro wa Mulungu, ndipo chotero, kuti akhale chifanizo chenicheni, iye anayenera kukhala wangwiro.—Genesis 1:26-28; 2:7, 8.
7. Pa nthawi imene Adamu anali mu Edene, kodi ndi mkhalidwe wotani umene unalipo pakati pa kumwamba ndi dziko lapansi kupangitsa Mulungu kukondwa?
7 M’Munda waparadaiso wa Edene mwamuna woyambirir anayenda mogwirizana ndi mzimu woyera wa Mulungu. Pa chochitika china iye anakhala ndi kukambitsirana ndi Mulungu. M’jira yosaoneka ndi maso a munthu ndipo komabe yozindikirika kwa munthu’yo Adamu, Mulungu anayenda m’Munda wa Edene wokongola umene’ wo Panali umodzi pakati pa Mulungu ndi munthu. Pa nthawi imene’yo panali umodzi pakati pa zinthu zakumwamba ndi zinthu za pa dziko lapansi. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti mzimu wa Mulungu unalowerera konsekonse. Zonse’zi zinapangitsa Yehova Mulungu kukhala wachimwemwe. Iye ali “Mulungu wachimwemwe.”—1 Timoteo 1:11, NW.
8. Kodi ndi chifukwa cha mtundu wotani wa uchimo tiribe pa dziko lapansi lero lino dongosolo langwiro, ndipo kodi chimo limene’lo linachitidwa ndi yani?
8 Pano, tsopano, panali maziko a kupangidwa kwa dongosolo la zinthu langwiro limene silikhala konse lakale ndi kukonzekera kuchoka. Koma lero lino tiribe dongosolo loyera, lolungama ndi langwiro la zinthu. Kodi n’chifukwa ninji ziri choncho? Chiri chifukwa chakuti panachitika kuchimwira mzimu woyera. Kochitidwa ndi yani? Kochitidwa ndi munthu amene Yesu Kristu anam’dziwikitsa pamene anali kulankhula ndi anthu amene anali ofunitsitsa kum’pha chifukwa cha kunena choonadi cha Mulungu. Kwa odzakhala akupha amene’wa Yesu anati: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wabodza.”—Yohane 8:44.
9. Kodi ndani amene ali atate wauzumu wa wochita chimo, ndipo chifukwa ninji?
9 Wochimwira mzimu woyera woyamba akudziwikitsidwa’nso ndi wophunzira wa Yesu wochedwa Yohane, amene akulemba kuti: “Iye wochita chimo ali wochokera mwa Mdierekezi, chifukwa Mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi.” (1 Yohane 3:8) Wochita chimo sakakhala ndi atate wina wauzimu koposa uyo amene anamuyambitsa.
10. Kodi ndi motani m’mene wabodza woyambirira anadzipangira kukhala Mdierekezi?
10 Kucha wabodza woyambirira m’chilengedwe chonse amene’yu kukhala mdierekezi kumasonyeza kuti bodza lake’lo linali lotsutsa Mulungu, pakuti dzina’lo Mdierekezi limatanthauza Wonamizira. Iye anasiya choonadi ndipo anakulitsa mwa iye mwini lingaliro la bodza—M’kutsutsa koneneza zimene Mulungu anauza Adamu, Mdierekezi anauza mkazi wa Adamu, Hava, kuti chilango cha kudya zochokera ku mtengo woletsedwa’wo sichikakhala imfa: “Kufa simudzafai; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umene’ wo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa.” (Genesis 3:1-5) Wabodza’yo anadzipanga kukhala Mdierekezi, makamaka ponena za Mulungu.
11. Kodi ndi motani m’mene Mdierekezi ayenera kukhala atalinganizira kuchititsa Mulungu kulephera kikwaniritsa mau ake ngati Adamu ndi Hava atachimwa?
11 Woneneza Mulungu’yo sakanatsimikiziritsa Adamu ndi Hava kuti iwo sakafa’di ngati iwo atadya chipatso chokanizidwa’cho cha mtengo wa kudziwitsa zabwino ndi zoipa. Mau ake sanali amphamvu kwambiri koposa a Mulungu. (Ahebri 4:12; Genesis 2:16, 17) Koma mosakaikira Mdierekezi analingalira kuti iye akachititsa Yehova Mulungu kulowa mu mkhalidwe wobvuta kwambiri kumene kukakhala kusanena chimodzi kwa Mulungu kupha Adamu ndi Hava, makamaka ngati Mdierekezi akachititsa awiri okwatirana ochimwa’wo kudya “mtengo wamoyo” chiweruzo cha Mulungu chisanaperekedwe pa iwo. Genesis 2:9; 3:22, 23.
12. Kodi ndi motani m’mene Mdierekezi anakhalira wambanda, ndipo kodi n’chiani chimene chikumuyembekezera tsopano?
12 Mosasamala kanthu za kuyendetsa zinthu konse’ku, Mdierekezi anasanduka wabodza. Onyengedwa ake’wo anafa monga miyoyo yaumunthu, pakuti Yehova Mulungu Woweruza’yo anawapatsa chiweruzo cha imfa ndipo anawachititsa kusafika ku “mtengo wa moyo” mwa kuwathamangitsa m’Munda waparadaiso wa Edene. (Genesis 3:17-24) Chifukwa cha kuchititsa mopanda chikondi imfa ya munthu woyamb ndi mkazi wake, Mdierekezi anakhala “wambanda.”Chifukwa cha chimene’chi iye ali woyenerera kuphedwa malinga ndi kunena kwa lamulo lolongosoledwa ndi Woyambitsa Chikristu: “Ali yense amene achititsa kamodzi ka tiana iti tokhulupirira ine kuchimwa, kukakhala bwino kwambiri kwa iye ngati mphero yaikulu itakolowekedwa m’khosi mwake ndi kuponyedwa m’nyanja. (Marko 9:42, Revised Standard Version) Ziri’di choncho, chionongeko chosatha chikuyembekezera wambanda’yo, Mdierekezi.
13. Kodi Yehova anayerekezera Mdierekezi ndi yani, ndipo amene’yu asanaphedwe kodi iye akuloledwa kutulutsa chiani?
13 Mapeto otero’wo kwa Mdierekezi anasonyezedwa pamene Woweruza wa onse, Yehova, anamuyerekezera ndi chinjoka chimene chinagwiritsiridwa nchito kunyenga mkazi kudya chipatso chokanizidwa mosemphana ndi lamulo la Mulungu. Polunjikitsa mau’wo kwenikweni kwa Chinjoka chophiphiritsira’cho. Yehova anati: “Chifukwa kuti wachita ichi, wotembereredwa ndiwe wopambana ndi zinyama zonse ndi zamoyo zonse za m’thengo: uziyenda ndi pamimba pako, uzidya pfumbi masiku onse a moyo wako: ndipo ndidzaika udani pakati pa iwe ndi mkazi’yo, ndi pakati pa mbeu yako ndi mbeu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.” (Genesis 3:14, 15) Motero Mdierekezi anakhala wotembereredwa ndi Mulungu. Chotero ziri kwa Mulungu kuchititsa wotembereredwa amene’yu kuphedwa. Koma kumene’ku sikukachitika Chinjoka chotembereredwa’cho chisanakhale ndi mwai wa kubala “mbeu” ana m’njira yophiphiritsira kapena yauzimu. Monga mzimu, Mdierekezi alibe mphamvu zakubala zobadwa nazo mofanana ndi munthu.
14. Kodi ndi chiani chimene kukwawa ndi mimba kunatanthauza kwa Mdierekezi monga Chinjoka Chachikulu, ndipo kodi iye anagwirizana ndi yani m’kutsitsidwa kwake?
14 Yehova anayerekezera Mdierekezi ndi chinjoka chimene chimakwawa ndi mimba yake ndipo chikudya chakudya chodetsedwa ndi zidutswa za pfumbi. Motero iye anasonyeza mkhalidwe wotsika kwambiri mu umene Mdierekezi wotembereredwa anaponyedwamo tsopano. Popeza kuti anali malo otsika kopambana m’chilengedwe, anayerekezeredwa ndi malo amene anafikira kuchedwa Tartarus. M’kupita kwa nthawi Mdierekezi anagwirizana m’malo ake amene’wa ndi mizimu ina, ndi angelo ena amene anakana Utate wa Mululngu nalandira utate wa Mdierekezi. Mizimu imene’yi inakhala “mbeu” yake.
15. Kodi Petro ndi Yuda akunenanji ponena za angelo amene anagwirizana ndi Chinjoka Chachikulu m’kuchimwa?
15 Ponena za mbeu yauzimu ya Chinjoka chakale lomwe imene’yi, mtumwi Wachikristu Petro analemba kuti: “Mulungu sanaleka kulanga angelo amene anachimwa, koma mwa kumawaponya iwo mu Dzenje, anawapereka iwo ku maenje a mdima waukulu kuti akasungidwe kaamba ka chiweruzo.” (2 Petro 2:4, NW) Wophunzira Wachikristu Yuda akuchula “mbeu” yaungelo imodzimodzi’yo ya Cinjoka, pamene iye akulemba kuti: “Angelo’nso amene sanasunga chikhalidwe chao choyamba, komatu anasiya pokhala pao pao, adawasunga m’dende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.”—Yuda 6.
16. Kodi n’chifukwa ninji Mdierekezi anachita yekhayekha kunyenga Hava kulowa mu uchimo, ndipo kodi n’chifukwa ninji ena amalingalira kuti iye anali kerubi?
16 Pa nthawi imene Mdierekezi ananyenga mkazi wa Adamu, Hava, kuti apandukire Mulungu Atate wake wakumwamba, panalibe “mbeu” ya Chinjoka Chachikulu. Mdierekezi anachita yekhayekha. Iye sanasankhe kukhala ndi mnzake waungelo amene akakhala wopikisana naye m’kuchita ulamuliro pa ana a Adamu ndi Hava. Iye anachitira nsanje ulamuliro wotheratu pa anthu onse. Malo a ntchito amene iye anali nao m’gulu loyambirira la Mulungu sitikuwadziwa kwenikweni. Ophunzira Baibulo ambiri amva ulose wa Ezekieli 28:11-19 wonena za mfumu ya Turo wakale kunena’nso Satana Mdierekezi, ndipo chifukwa cha chimene’cho iwo amalingalira kuti Mdierekezi wodzipanga yekha’yo poyamba anali “kerubi” pakati pa “ana a Mulungu” akumwamba. Ngati zimene’zi ziri choncho, pamenepo ukulu wa kutsitsidwa kwake monga Chinjoka Chachikulu uli waukulu kwambiri.
17. Kodi angelo opanduka akukhalira limodzi motani ndi Mdierekezi mu mdima wa Tartarus?
17 Opandukira Mulungu ena aungelo, amene anakhala ‘mbeu” ya Chinjoka, akukhala naye mu ndima wa Tartarus, monga njoka zotembereredwa. Iwo alibe’nso kuunika kwa chiyanjo cha Mulungu ndi uphungu. Pa kupanduka kwao Mulungu anachotsa pa iwo mzimu wake woyera.
18. (a) Kodi n’chifukwa ninji m’tsogolo muli mwa mdima waukulu kwambiri kwa Mdierekezi ndi angelo ake? (b) Kodi ndi funso la chinsinsi lotani limene tsopano linafunsidwa?
18 M’tsogolo muli mwa ndima waukulu kwambiri kwa Chinjoka Chachikulu’cho ndi “mbeu” yake yaungelo. Tsiko la Mulungu la Chiweruzo likuwayembekezera, limodzi ndi chiyembekezo cha ‘kuzunzundidwa mutu.’ Mulungu adzagwiritsira ntchito “mbeu” ya “mkazi” wake kuti ichite kuzunzunda’ko. (Genesis 3:15) Kuzunzunda’ko sindiko chironda cha pamutu chabe. Kuli kuphwanyidwa mutu, kumene kukuchititsa imfa ya Chinjoka Chachikulu’cho ndi “mbeu” yake. Sipayenera kukhala kukumva molakwa, pakuti pa Aroma 16:20 ophunzira a Kristu akulemberedwa kuti: “Mulungu wamtendere adzaphawanya Satana pansi pa mapazi anu tsopano lino.” Chimene’chi ndi chifukwa chabwino kwa Satana ndi “mbeu” yake chodanira ndi “mbeu” ya “mkazi” wa Mulungu. Pa kuchula kwa Mulungu “mbeu” ya “mkazi” wake, chinsinsi chinayang’anizana ndi kumwamba ndi dziko lapansi lomwe. Chinsinsi kapena chinsinsi chopatulika chimene tsopano chinadzutsa chidwi m’chilengedwe chonse chinali chakuti, Kodi ndani amene ali mbeu ya mkazi imene’yi?
“MBEU” YA PA DZIKO LAPANSI YA CHINJOKA
19. Kodi ndi chifukwa ninji Akristu akulangizidwa kukhala osiyana ndi Kaini, mwana woyamba kubadwa wa mtundu wonse wa anthu?
19 “Mbeu” yachinsinsi ya “mkazi” wa Mulungu sinatsimikizire kukhala mwana wachisamba wa Hava, amene iye anam’cha Kaini. Kukhala kwa Kaini mwana wachisamba wa anthu onse sikunam’patse kuyenera kwa kutumikira monga “mbeu” yolonjezedwa imene’yo. Ndipo’nso chitende cha Kaini sichinazunzundidwe ndi Chinjoka Chachikulu, Mdierekezi. Ponena za kuzunzunda wina mutu, Kaini anapha mbale wake woopa Mulungu Abele, mwina mwake mwa kumenya mutu ndi nkhonya yakupha. M’malo mwa kudalitsidwa ndi Mulungu ndi kulandira mzimu woyera wa Mulungu, Kaini anakhala wachiwiri m’Baibulo kuchedwa “wotembereredwa,” Chinjoka chophiphiritsira kapena Mdierekezi chikumakhala choyambirira. (Genesis 3:14; 4:11) M’jira imene’yi Kaini anadzipanga kukhala mbali ya dziko lapansi ya “mbeu” ya Chinjoka, Mdierekezi, amene iye anam’tsanzira m’kunama ndi kuchita mbanda. Iye sanakonde kaya mbale wake, amene iye akanatha kumuona, kapena Mulungu, amene iye sakanatha kumuona. Atsatiri a Kristu akulangizidwa kukhala osiyana ndi, Kaini m’mau otsatirapo awa:
“Tikondane wina ndi mnzake: osati monga Kaini anali wochokera wa woipa’yo namupha mbale wake. Ndipo anamupha Iye chifukwa ninji? Popeza ntchito zake zinali zoipa, ndi za mbale wake zolungama” (1 Yohane 3:11, 12) “Tsoka kwa iwo! pakuti anayenda m’njira ya Kaini.”—Yuda 11.
20, 21. Kodi Kaini anatsanzira Mdierekezi m’kuchita chimo la mtundu wotani, ndipo kodi ndi polingalira chisonyezero chotani chimene’chi chinali chothekera kwa Kaini?
20 Kaini anatsanzira Mdierekezi, atate wake wauzimu “woipa’ yo,” m’kuchimwira mzimu woyera wa Mulungu. Zimene’zi sizikutanthauza kuti Kaini, mwana wamwamuna wachisamba wa Adamu ndi Hava, anakhalapo ndi mzimu woyera. Makolo ake a pa dziko lapansi anataya mzimu woyera chifukwa cha kuswa dala lamulo la Mulungu. Koma Kaini anaona kugwira ntchito kwa mzimu woyera. Kodi ndi liti ndipo motani?
21 Imene’yo inali nthawi imene Kaini anapereka kwa Mulungu nsembe yochokera ku zolima zake, pamene mng’ono wake Abele anapereka kwa Mulungu nsembe ya nyama zochokera m’gulu la nkhosa. Kodi nsembe za abale onse’wa zinali zolandiridwa ndi Mulungu? Genesis 4:4-7 amatiuza kuti: “Yehova ndipo anayang’anira Abele ndi nsembe yake: koma sanayang’anira Kaini ndi nsembe yake. Kaini ndipo anakwiya kwambiri, nigwa nkhope yake. Ndipo Yehova anati kwa Kaini, Ukwiyiranji? Yagweranji nkhope yako? Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzam’lamulira iye.”
22. Kodi ndi chisonyezero cha mzimu woyera chotani chimene Kaini anaona?
22 Ndithudi, Mulungu sanaonekere kwa Kaini ndi Abele pa chochitika chimmene’chi. M’mene iye anayang’anira mwa chiyanjo pa Abele ndi nsembe yake, sitikuuzidwa. Koma payenera kukhala panali umboni wina wooneka wa kumene’ku. Kumene’ku kunali kugwira ntchito kwa mzimu woyera wa Mulungu. Kaini anaona zimenezi ndipo’nso, popanda mau ochokera kwa Mulungu. Chotero anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa. Iye sanayankhe mwaulemu modzichepetsa ndi molapa pa kugwira ntchito kooneka kwa mzimu woyera wochokera kwa Mulungu kwa amene iye anali kupereka nsembe yosalandirika.
23. Kodi chimo la Kaini lochimwira mzimu woyera linali la mpangidwe wotani, ndipo chifukwa ninji?
23 Mwachionekere, Kaini sanali kuchita choyenera. Mau a Mulungu ochokera kosaoneka anam’longosolera mkhalidwe’wo. Pokhala wonyada kosati n’kudzichepetsa, Kaini sanalape ndi kutembenukira ku kuchita zabwino, ngakhale kuli kwakuti uchimo unali kubwatama monga ngati pa khomo pa nyumba yake ndi kufunafuna kum’gwira monga wogwidwa nawo. Iye sanafune kuulamulira, mosasamala kantu zimene mzimu woyera wa Mulungu unam’sonyeza. Posafuna kutukula nkhope yake, iye analinganizira chiwembu uyo amene anabvomerezedwa ndi Mulungu ndi kum’pha. Motero iye anachimwira mzimu woyera.
24. Kodi n’chiani chimene chinganenedwe ponena zakuti kaya uyo tsopano wochedwa Mdierekezi anali ndi mzimu woyera ndipo anaona kugwira ntchito kwa mzimu woyera?
24 Zimene’zi zinaipira Mulungu ndipo zinachititsa temberero lake pa Kaini. Koma zinakondweretsa Chinjoka, Mdierekezi, pakuti iye tsopano anaona mwana wake wa pa dziko lapansi amene anachita mofanana ndendende ndi atate wake wauzimu. Mdierekezi iye mwini anachimwira mzimu woyera. Kuphatikiza pa kuona Mulungu iye mwini, anachimwira mzimu woyera. Kophatikiza pa kuona Mulungu iye mwini, uyo tsopano wochedwa Mdierekezi anali ataona ntchito zonse za mzimu woyera ponena za malo akumwamba ndi ponena za kulengedwa kwa dziko lapansi ndi ponena za munthu wangwiro wokhala pa iro. (Yobu 38:7) M’kati mwa nthawi ya kukhala wopanda chisonkhezero chadyera, iye mwini anali ndi mlingo woyenera wa mzimu wa Atate wake wakumwamba. Zimene mzimu woyera umene’wu unatheketsa iye kuchita, iye anadziwa. Iye anaona’nso “mzimu wa chisomo” wosonyezedwa ndi Mulungu kulinga kwa Adamu ndi Hava m’kuwalinganizira kusangalala ndi moyo waumunthu wangwiro m’paradaiso wa pa dziko lapansi. Ndipo komabe kodi n’chiani chimene ‘mwana wa Mulungu’ wakumwamba’yo anachita?—Ahebri 10:29.
25. Kodi ndi motani m’mene ‘mwana wa Mulungu’ amene’yo anapitirizirabe kachitidwe kochimwira mzimu woyera ndipo motero kodi iye anadzipanga kukhala chiani?
25 Iye ananamizira “mzimu wa chisomo” mwa kuuza Hava kuti chinasokhezeredwa ndi dyera la Mulungu. Ndipo’nso, kuti chiletso chimene Mulungu anaika pa kudya mtengo wa kudziwitsa zabwino ndi zoipa chinasonkhezeredwa ndi kuopa kwa Mulungu kuti zolengedwa zaumunthu zingapeze luso la kupanga zosankha mosadalira iye, zosankha zonena za chimene chiri choyenera ndi chimene chiri cholakwa, chimene chiri chabwino ndi chimene chiri choipa. Chotero, pamene ‘mwana wa Mulungu’ wauzimu’yo mwadala ndi molinganiza anapotoza zinizeni zomvekera bwino za nkhani’yo ndi kunama kuti anyenge Hava kuti achimwe, iye anachimwira mzimu woyera, chimo limene liribe chikhululukiro. Iye anadzichititsa kulola kunyengeka ndi chiyembekezo chadyera cha kupeza ulamuliro pa dziko lapansi ndi anthu ake okhalapo ndiy eno anachitapo kanthu kuti atenge ulamuliro umene’wo. Pamenepo iye anataya mzimu woyera wa Mulungu. Zipatso za mzimu wa Mulungu m’moyo wake zinanyala ndi kufa. Iye anadzipanga kukhala Mdierekezi, wongoyenerera chionongeko.—Ahebri 12:29; 6:7, 8.
26. Kodi ndi motani m’mene Mdierekezi anakhalira “wolamulira wa ziwanda” ndipo kodi n’chifukwa ninji awo ochita kulankhula ndi mizimu sadzakhala ndi phande mu ufumu wa Mulungu?
26 Woyambirira kuchimwira mzimu woyera amene’yu anadzipanga kukhala chiwanda. “Ana a Mulungu” aungelo amene pambuyo pake anagwirizana naye m’kupandukira Mulungu anakhala ziwanda mofanana ndi Mdierekezi. Ziwanda zimene’zi zinakhala “mbeu” ya Chinjoka, ndipo motero Mdierekezi anakhala “wolamulira wa ziwa nda,” amene anadzakhala Beelzebule. (Mateyu 12:24-27, NW) Zimene’zi ndizo zopititsa patsogolo uchiwanda, kutembenuza anthu kuwachotsa ku kulambira Mulungu mmodzi wamoyo ndi woona, Yehova. Izo zimachedwa “mizimu yoipa.” (Mateyu 10:1, 8; 12:43-45) Kachitidwe ka kulankhula ndi mizimu mosonkhezeredwa ndi ziwanda zimene’zi kangachititse kokha uchisi wauzimu kwa wochita’yo ndi kum’panga kukhala wauchisi pamaso pa Mulungu. Kachitidwe ka kulankhula ndi mizimu kali imodzi ya ntchito za thupi lochimwa ndipo kadzalepheretsa munthu kukhala ndi phande liri lonse mu ufumu wa Mulungu ndi madalitso ake. Mizimu yoipa’yo imatsutsa mzimu woyera wa Mulungu, ndipo iye amatsutsa munthu chifukwa cha kukhala ndi chigwirizano chiri chonse ndi mizimu yoipa.—Deuteronomo 18:9-14; Agalatiya 5:19, 20; Chivumbulutso 9:20, 21; 21:8.
MTUNDU WA “MZIMU” UMENE UWO ULI
27. Kodi n’chifukwa ninji pa tsopano lino tiyenera kukhala okhoza kutsimikizira mtundu wa mzimu umene uli kutseri kwa dongosolo lakale lirip’oli?
27 Kuli kofunika kopambana kwa ife kudziwa zinthu zapamwambapo’zo. Mwa kuzidziwa tingathe kuzindikira chifukwa mkhalidwe wa anthu ulipo’wu. Pano lero lino, tiri m’zaka zathu za zana la makumi awiri, zaka zana zimene zinayamba bwino lomwe mwa lingaliro la anthu. Mwa kuwerengera nthawi malinga ndi kuena kwa Malemba Opatulika, tatha zaka zikwi zisanu ndi chimodzi kuyambira pamene ‘mwana wa Mulungu’ wofuna zake zokha anapandukira ulamuliro wa chilengedwe chonse wa Yehova ndipo anatsogolera Adamu ndi Hava m’kusamvera Mulungu kofananako. Pambuyo pa kutulutsidwa kwa anthu awiri opanduka amene’wa m’paradaiso wa Edene dongosolo latsopano laumunthu linakhazikitsidwa pa dziko lapansi, losiyana ndi limene Mulungu Mlengi wao walinganizira chiunda chathu’chi Dziko lapansi. Chotero tsopano lino tiyenera kukhala okhoza kutsimikizira mtundu wa mzimu umene uli kutseri kwa dongosolo limene tsopano liri lakake.
28. Ponena za mzimu kutseri kwa dongosolo lakale’li, kodi tikutanthauzanji mwa kumati “mzimu”?
28 Pakuti “mzimu” tikutanthauza mphamvu yogwira ntchito yosaoneka, mphamvu yosonkhezera, yofulumizitsa ndi yopatsa nyonga imene imasonkhezera chitaganya chonse cha anthu. Imasonkhezera njira yao m’moyo. Imawasonkhezere m’njira ina ya onse. Motero anthu onse amachita m’njira yofanana kwambiri pafupifupi mosadziwa, popanda kukulingalira kwenikweni. Zinthu zimene iwo amachita zimakhala pafupifupi zachibadwa, zochitisidwa ndi chisonkhezero cham’kati kotero kuti atsatire njira yokhazikika ndi kupanga chitsanzo china cha moyo. Pangakhale masiyanidwe ochepa kumadalira pa masiyanidwe a anthu mu umunthu, komabe moyo ndi zolinga zake ziri ndi mbali zofanana zimene zimazisonyeza kukhala mkhalidwe wa chitaganya cha anthu chimene tsopano chiri pansi pa dongosolo la zinthu liripo’lo.
29, 30. (a) Kodi ndani amene ali wolamulira wosaoneka wa dongosolo lakale’li, ndipo kodi iye wakhala yekha mu ulamuliro wotero’wo? (b) Kodi ziyambukiro za ulamuliro wosaoneka wotero’wo zakhala za mtundu wotani?
29 Mzimu wotero’wo kutseri kwa dongosolo la zinthu lakale la lero lino wayambukiridwa kwakukulu ndi anthu oposa anthu osaoneka okhala ndi maumunthu oposa anthu amene amalamulira dongosolo la zinthu iri ndipo latenga ulamuliro wake. Sipangakhale chikaikiro ponena za amene wolamulira woyamba’yo ali amene akulamulira dongosolo lonse lathunthu. Kalekale’lo m’zaka za zana lachisanu la dongosolo lakale, Yesu Kristu analengeza kuti Satana Mdierekezi ndiye “wolamulira wa dziko lino,” amene iye analibe naye zochita zaubwezi. Pa usiku wotsirizira wa moyo wake monga munthu pa dziko lapansi, Yesu Kristu kwa atumwi ake anati: “Mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine.” (Yohane 12:31; 14:30; 16:11) M’kulamulira anthu kosaoneka Satana Mdierekezi sali yekha. Iye ali ndi angelo auchiwanda ogwirizana naye monga mfumu yao. Mphamvu zonse za ziwanda zimene’zi zinakhala ndi mbali m’zochitika za dongosolo lakale liripo’li la chitaganya chaumunthu.
30 Ziyambukiro za ulamuliro wao wauzimu zakhala zobvulaza. Potsimikizira zimene’zi pali ulosi wolembedwa ndi mtumwi Yohane ponena za wogwetsa ziwanda kuchokera ku miyamba yoyera wam’tsogolo pa nthawi’yo. Ulosi umene’wu, monga momwe ukupezekera m’ Chibvumbulutso 12:7-12, timawerenga kuti:
“Ndipo munali nkhondo m’mwamba. Mikayeli ndi angelo ake akuchita nkhondo ndi chinjoka; chinjoka’nso ndi angelo ake chinachita nkhondo; ndipo sichinalakika, ndipo sanapezeka’nso malo ao m’mwamba. Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalamba’yo, iye wochedwa Mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyenda pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi. . . . Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdierekezi watsikira kwa inu, wokhala nao udani waukulu, podziwa kuti kam’tsalira kanthawi.”
31. Malinga ndi kunena kwa Chibvumbulutso 13:4, kodi Satana “chinjoka’cho” akusocheretsera dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu m’kulambira chiani?
31 Chimodzdi cha zinthu zimene Wonyenga’yo, Satana Mdierekezi, wasocheretsa nacho dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu ndicho kulambiridwa kwa iye mwini. Anthu oona mtima koma onyengedwa angabvutike maganizo ndi chibvumbulutso chotero’cho, koma Chibvumbulutso 13:4 ponena za anthu amene amalowa m’ndale za dziko za dziko lino chimati: “Analambira chinjoka, chifukwa chinachipatsa ulamuliro chirombo’cho; ndipo analambira chirombo.”
32. Kodi amene ali “mulungu wa dongosolo iri la zinthu” akuonekera bwino lomwe mwa kachitidwe kake kotani kulinga ku kuunika kwa mbiri yabwino?
32 Tiri’nso ndi mau a mtumwi Paulo onena za icho, akuti Mdierekezi, ndiye wamkulu wolambiridwa ndi dziko la mtundu wa anthu, modziwa kapena mosadziwa. Paulo anati: “Ngati’nso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika; mwa amene mulungu wa nthawi yino ya pansi pano unachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.” (2 Akorinto 4:3, 4) Dongosolo lino la zintu liri ndi “mulungu.” Umulungu wake wake wa dziko ndithudi uyenera kuyambukira mzimu kutseri kwa dongosolo lakale la zinthu liripo’li.
33. Kodi ndi motani m’mene tonsefe mwachibadwa tayambukiridwira ndi zimene “mulungu wa dongosolo iri la zinthu” anachita pafupi ndi chiyambi cha mbiri ya anthu?
33 Pafupi ndi chiyambi cha mbiri ya anthu uyo amene tsopano ali ‘mulungu wa dongosolo iri la zinthu’ anachititsa kuchimwa kwa makolo anthu oyambirira. Adamu ndi Hava anapanikizidwa kulowa m’kusamvera Mlengi wao. Zimene’zi zinali ife tisanabadwe. Ife tonse taona ziyambukiro zoipa za chimene’chi. Mu Aroma 5:12 mtumwi Paulo akunena mogwirizana ndi zenizeni pamene iye akulemba kuti: “Monga uchimo unalowa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” Tinalowa m’chitsutso cha imfa chifukwa cha kulandira mwachibadwa kupanda ungwiro, kukhala ochimwa ndi kuipa kwa makhalidwe. Tinali monga ngati kuti tinali akufa. Kwa Mulungu sitinali amoyo.
34, 35. Kodi ndi motani m’mene ife pa nthawi imene’yo tinaliri ngati akufa kwa Mulungu, ndipo kodi n’chiani chimene chinanenedwa kukhala chikugwira ntchito mwa ife?
34 Mwacahibadwa, tinali olandira mkwiyo wa Mulungu, “ana a mkwiyo.” Tinali “oyesedwa alendo pa moyo wa Mulungu.” (Aefeso 4:18) Monga momwe Akolose 1:21, NW, amanerera’so kuti: “Inu . . . pa nthawi ina munali alendo ndi adani chifukwa chakuti maganizo anu anali pa zinthu zimene ziri zoipa.” Chifukwa cha mkhalidwe wa zinthu umene’wo ndipo pa nthawi imene’yo, Yehova Mulungu sanali kugwira ntchito mwa ife. Chabwino, nangano, ndani kapena n’chiani chimene chinali kugwira ntchito?
35 M’kuyankha funso limene’lo, mau a Aefeso 2:1-5, olemberedwa kwa Akristu otembenuzidwa, amatiuza kuti: “Munali akufa, mwa zolakwa ndi machimo m’zimene munali kukhala pamene munali kutsatira njira ya dziko lino, mukumamvera wolamulira amene akulamulira mlengalenga, mzimu umene ukugwira nchito mwa opanduka. Ife tonse tinali pakati pao’nso kale, tikumakhala ndi miyoyo ya chilakolako, olamulidwa kotheratu ndi zikhumbo zathu zakuthupi ndi malingaliro a ife eni; kotero kuti mwa chibadwa tinali mu mkwiyo wa Mulungu mongofanana ndi mbali ina yonse ya dziko. Koma Mulungu anatikonda kwambiri ndi chikondi chochuluka kwakuti iye anali woolowa manja ndi chifundo chake: pamene tinali akufa mwa machimo athu.”—The Jerusalem Bible; An American Translation.
36. Malinga ndi kunena kwa otembenuza Baibulo ena, kodi “mzimu wonenedwa mu Aefeso 2:2 umatanthauza chiani, ndipo kodi uwo uli mu ulamuliro wa yani?
36 Kodi n’chiani chimene chiri “mzimu umene ukugwira ntchito mwa opanduka”? Iye ndiye wopandukira Yehovah Mulungu, woyambirira wamkulu wochedwa, Mdierekezi, “njoka ya kale lomwe.” Koma pano tiyenera kuona kuti, mu Aefeso 2:2 liu’lo “mzimu” limaonedwa ndi otembenuza Baibulo ena kukhala likutathauza kantu kena kosakhala munthu. Iwo amauona kukhala mphamvu yogwira ntchito yosaoneka imene ikuyendetsedwa ndi “wolamulira amene akulamulira mlengalenga” ndi amene akugwira ntchito m’kati mwa awo amene ali osamvera Yehova Mulungu. Mwa chitsanzo, katembenuzidwe ka Young ka Afeso 2:2 kamati: “M’mene inu munayendamo pa nthawi ina monga mwa utali wa nthawi ya dziko lino, monga mwa wolamulira wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu umene tsopano ukugwira ntchito mwa ana a kusamvera.” (Onani’nso katembenuzidwe ka Rotherham.) “Mzimu” wosakhala munthu wotero’wo ukakhala uli mu ulamuliro wa wogwiritsira ntchito woipa wa “mlengalenga.” Ukapatsa nyonga awo amene amachita “monga mwa dongosolo la zinthu la dziko lino,” osamvera Mulungu.
37, 38. Kodi ndi motani m’mene 1 Yohane 2:15-17 amasonyezera njira im ene mzimu kutseri kwa dongosolo lakale’li umadzisonyezera?
37 Kodi tingapeze kuti lingaliro lina lotsimikizirika lonena za mzimu umene uli kutseri kwa dongosolo la zinthu lakale liripo’li kapene m’mene umadzisonyezera? Eya, tiyeni tiyang’ane pa zimene mtumwi Yohane akulemba. Pochenjeza Akristu za mzimu wa dziko umene’wo iye akulemba kuti: “Musakonde dziko lapansi, kapena za m’dziko lapansi. Ngati wina akonda dziko lapansi, chikondi cha Atate sichiri mwa iye. Pakuti chiri chonse cha m’dziko lapansi, chilakolako cha thupo ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma ku dziko lapansi. Ndipo dziko lapansi lipita, ndi chilakolako chake.”—1 Yohane 2:15-17.
38 Chifukwa cha ichi mzimu wa dongosolo lakale umasonkhezera anthu audziko kukhumba zinthu zokondweretsa kwambiri maso ao ndi kukhumba zinthu zimene zimakhala zokondweretsa ku thupi; ndipo, moyenerera, zikhumbo zotero’zo zimatsogolera ku kachitedwe kadyera. Chifukwa cha kukhumba kwambiri mwadyera chimene chimakondweretsa maso ndi thupi lochimwa, anthu audziko amene’wo amakundika zinthu zochuluka zimene zimapanga njira zao zokhalira ndi moyo, kaamba ka kusangalala kwao ndi moyo. Monyadira kukhala kwao ndi zinthu, iwo amakonda kumaonetsera chuma chao kotero kuti akhutiritse ena. Kumeneku kumasonkhezera anthu amene alibe zinthu zotero’zo kufuna kukhala ndi zinthu zorero’zo nawo’nso.
39. Kodi Ayuda a m’zaka za zana loyamba anakana kulandira mzimu wa Mulungu mwa njira yotani, ndipo,malinga ndi kunena kwa Aroma 1:26-32, kodi n’chiani chimene chinatulukapo kwa iwo chifukwa cha kuloledwa kuchita monga momwe afunira?
39 Kalekale m’zaka za zana loyamba za Nyengo yathu Ino panali Ayuda amene anasankha kulowereredwa ndi mzimu wokhala kutseri kwa dongosolo la dziko lonse la zinthu. Kachisi womangidwa ndi Mfumu Herode anali chikhalirebe pa malikulu a mtunda wao a Yerusalemu, ndipo iwo anali odziwa mpambo wa Chilamulo woperekedwa kupyolera mwa mneneri Mose. Iwo sanafune kulandira mzimu wa Mulungu umene unali kusonyezedwa m’Chikristu choyera chimene pa nthawi imene’yo chinali kulengezedwa pa dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu. Chifukwa cha chimene’cho Yehova Mulungu anawalola kuyenda monga momwe afunira, mofanana ndi Israyeli wopatuka wakale. Limodzi ndi chotulukapo chotani kwa iwo? Mu Aroma 1:26-32, mtumwi Paulo akutiuza, kuti:
“Chifukwa cha ichi Mulungu anawapereka iwo ku zilakolako za manyazi; pakuti angakhale akazi ao anasandutsa machitidwwe ao a chibadwidwe: akhale machitidwe osalingana ndi chibadwidwe: ndipo chimodzimodzi’nso amuna anasiya machitidwe a chibadwidwe cha akazi, natenthetsana ndi chilakolako chao wina ndi mnzake, amuna okha okha anachitirana chamanyazi, ndipo analandira mwa iwo okha mphotho yakuyenera kulakwa kwao. Ndipo monga iwo anakana kukhala naye Mulungu m’chidziwitso chao, anawapereka Mulungu ku mtima wokanika, kukachita zinthu zosayenera; anadzala ndi zosalungama zonse kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani; akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao, opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo; amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndipo’nso abvomerezana ndi iwo akuzichita.”
40, 41. Limodzi ndi kufalikira kwa Chikristu, kodi mzimu kutseri kwa dongosolo lakale unaikidwa pa malo olakwa, ndipo kodi Paulo ananeneratu chiani mu 2 Timoteo 3:1-5,12?
40 M’nyengo ya atumwi ya m’zaka za zana loyamba C.E. chikhulupiriro chenicheni Chachikristu chinali kumalengezedwa, ndipo chotero kodi mzimu woyera wa Mulungu sukalowa m’malo mwa mzimu wokhala kutseri kwa dongosolo la zinthu lakale pamene Chikristu chinafalikira? Ndipo kodi chimene’chi sichinali choncho pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa Chikristu cha Dziko ndi mfumu Yachiroma, Konsitantini Wamkulu, m’zaka za zana lachinai C.E.? Kodi pa nthawi’yo mzimu watsopano woyera wamakhalidwe, woyera mwachipembedzo, sunalowetsedwe m’chitaganya chaumunthu chomapita patsogolo’cho? Ai, sizinali choncho malinga ndi kunena kwa zimene mtumwi woikidwa m’ndende’yo Paulo analemba, pafupi-fupi m’chaka cha 65 C.E. kapena m pambuyo pake. M’kalata yake yotsirizira, yonga imene inalemberedwa kwa mnzake wa nthawi yaitali, Timoteo, iye ananeneratu kuti:
41 “Masiku otsiriza zidzafika ntawi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; . . . Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m’moyo mwa Kristu Yesu, adzamva mazunzo.”—2 Timoteo 3:1-5, 12.
42. Kodi n’chifukwa ninji sitikufuna kukhala ndi mzimu unene uli kutseri kwa ochirikiza dongosolo lakale?
42 Kusonyezedwa konse kwapitako kwa mikhalidwe kumasonyeza mzimu umene umasonkhezera unyinji wa anthu onse pamene iwo akuchirikiza dongosolo la zinthu lakale. Kodi umen’ewo ndiwo mtundu wa mzimu umene ife timafuna kukhala nao monga mphamvu yosonkhezera ndi yotsogoza ya miyoyo yathu? Ai; ngati ife titi titsimikizire zipatso za mzimu wao zimene ochirikiza dongosolo lakale akututa lero lino! Ife moona mtima tikufuna kukhala ndi mzimu wosiyana, mzimu umene ukugwira ntchito kaamba ka dongosolo la zinthu labwino kwambiri. Chimene’chi chimafunikira kuti tikhale ndi mzimu wina wokha umene ulipo—mzimu woyera.