Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • go mutu 9 tsamba 149-160
  • Chizindikiro” cha Kuyandikira kwa Boma la Dziko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chizindikiro” cha Kuyandikira kwa Boma la Dziko
  • Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • PACHIMAKE PA “CHIZINDIKIRO” CHAMAKONO PALI PAFUPI
  • “DZIWANI KUTI IYE ALI PAFUPI PA KHOMO”
  • NSONGA YOTI IPHUNZIRIDWE TSOPANO
  • Atumwi Anapempha Chizindikiro
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • “Kuyenera Kuti Izi Zioneke”
    Nsanja ya Olonda—1999
  • “Kodi Nchiyani Chidzakhala Chizindikiro cha Kukhalapo Kwanu”?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Kodi Kukhalapo kwa Khristu Kumatanthauza Chiyani kwa Inu?
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
go mutu 9 tsamba 149-160

Mutu 9

Chizindikiro” cha Kuyandikira kwa Boma la Dziko

1, 2. (a) Kodi umboni wa kuyandikira kwa boma la dziko la Mulungu ukuperekedwa m’chiani? (b) Kodi n’chiani chimene chifunikira kuchitidwa “chisautso chachikulu” chisanachitike?

HA, NDI achimwemwe chotani nanga m’mene tingakhalire kuti ulamuliro wa dziko lonse lapansi wochitidwa ndi maboma a ndale za dziko a anthu opanda ungwiro ukuyandikira mapeto ake! Pa nthawi imodzi-modzi’yo langwiro la dziko lolonjezedwa ndi Mulungu likuyandikira. Umboni wa chimene’chi ulipo lero lino. Chiyambire chaka cha 1914 taona kuyamba kuchitika, kwa “chizindikiro” chosalakwika cha chimene’chi. Zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo mneneri wamkulu kwambiri koposa Danieli anafotokoza “chizindikiro” chimene’cho mwatsatane-tsatane. Tsopano tingathe kuwerenga tanthauzo lake ngati tikufuna. Wofotokoza “chizindikiro” cha pa nthawi yake chimene’chi anachula zinthu zonenedweratu m’Danieli, chaputala cha khumi ndi chiwiri. Mwa chitsanzo, m’kati mwa ulosi wake waukulu’wo iye anati kwa atumwi ake khumi ndi awiri pa Phiri la Azitona:

2 “Ndipo mbiri yabwino imene’yi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika. Chifukwa cha chimene’cho, pamene muona chinthu chonyansa chimene chichititsa chipululutso, monga chinanenedwa kupyolera mwa mneneri Danieli, chikuima m’malo oyera, (wowerenga’yo agwiritsire ntchito kuzindikira,) pamenepo awo amene ali m’Yudeya ayambe kuthawira ku mapiri. Munthu amene ali pa chindwi asatsike kukatulutsa katundu m’nyumba mwake; ndipo munthu amene ali m’munda asabwerere ku nyumba kukatenga chovala chake cha kunja. Tsoka kwa akazi okhala ndi pakati ndi awo oyamwitsa khanda m’masiku amene’wo! Pitirizanibe kupemphera kuti kuthawa kwanu kusachitike m’nthawi yachisanu, kapena pa tsiku la sabata; pakuti pa nthawi imene’yo padzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde, ndipo sichidzachitika’nso. Kunena zoona, ngati akadapanda kufupikitsidwa masiku amene’wo, palibe munthu ali yense amene akadapulumutsidwa; koma chifukwa cha osankhidwa’wo masiku amene’wo adzafupikitsidwa.”—Mateyu 24:14-22, NW; Marko 13:14-20.

3. Kodi ndi liti pamene Ayuda opangidwa kukhala Akristu’wo anathawa pa “malo oyera”? Chifukwa ninji?

3 Kale’lo m’masiku a atumwi a Yesu Kristu “malo oyera” anali mzinda wa Yerusalemu limodzi ndi kachisi wake wokongola kwambiri wolambiriramo Yehova Mulungu. Yudeya anali chigawo Chachiroma, chimene Yerusalemu anali malikulu ake achipembedzo. “Chinthu chonyansa chimene chichititsa chipululutso,” monga momwe chinachulidwira pa Danieli 12:11, chinali magulu ankhondo a Ufumu wa Roma, Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chimodzi wa ulosi wa Baibulo. Mwa chiukiro chachiwawa cha magulu ankhondo “chinthu chonyansa” cha m’nthawi imene’yo ‘chinali “chitaima” kwa kanthawi ‘m’malo oyera’ m’mphakasa ya chaka cha 66 C.E. Kumene’ko kunali chizindikiro chochenjeza kwa Ayuda opangidwa kukhala. Akristu’wo amene anali chikhalirebe m’Yerusalemu. Chotero, “chinthu chonyansa” chitachoka kwa kanthawi m’Yerusalemu, tsopano Akristu ochenjezedwa moyenerera’wo momvera anathawa m’malo oyera oyembekezera kuonongedwa’wo. Ambiri a othawa amene’wa anathawira ku “mapiri” m’chigawo Chachiroma cha Pereya patsidya pa Mtsinje wa Yordano.

4. Kodi ndi zinthu zotani zimene zinadza monga momwe kunanenedweratu pa mbadwo Wachiyuda umene’wo?

4 Zinali bwino kuti Ayuda opangidwa kukhala Akristu amene’wo anatero, pakuti, zaka zinai pambuyo pake, “chinthu chonyansa’cho” chinabwerera’nso. Icho chinapasula chigawo chonse cha Yudeya ndi kutsiriza kupasula’ko mwa kuononga Yerusalemu ndi kachisi wake wopatulika mu “chisautso chachikulu” chimene chinabvutitsa maganizo Ayuda m’kati ndi kunja kwa Ufumu Wachiroma. Ayuda opangidwa kukhala Akristu okhala m’malo osungika othawira’ko kunja kwa Yudeya anapulumuka chionongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. “Anthu” ena Achiyuda amene anakhalabe mu mzinda wopanduka’wo anapulumuka’nso, koma kokha kuti atengedwe ukakpolo ndi Aroma. Chotero mbadwo umene’wo wa Ayuda osapangidwa kukhala Akristu sunachitepo kanthu pa “chizindikiro” chimene Yesu Kristu anachineneratu. Kaamba ka mbadwo umene’wo iye anali ataneneratu nkhondo, njala, miriri, zibvomezi, chizunzo cha Akristu, kusaweruzika, kulalikidwa kwa Ufumu pa dziko lonse, ndi kuima kwa “chinthu chonyansa” m’malo oyera.’ Zinthu zonse’zi zinadza p ambadwo umene’wo wa Ayuda monga “chizindikiro” kwa iwo cha chionongeko chinalinkudza mofulumira’cho cha dongosolo la zinthu Lachiyuda.—Mateyu 24:3-22; Luka 21:10-23.

PACHIMAKE PA “CHIZINDIKIRO” CHAMAKONO PALI PAFUPI

5. Kodi n’chifukwa ninji boma la dziko la Mulungu silinatsatirepo pa kupasulidwa kwa Yerusalemu?

5 Komabe, kodi kuonongedwa kwa Yerusalemu mu 70 C.E. kunatsatiridwa ndi boma la dziko la Mulungu lokhala m’manja mwa Yesu Kristu, Mbadwa yoyenerera ya Mfumu Davide? Ai! Ufumu Wachiroma unapitirizabe monga Ulamuliro wa Dziko Wachisanu ndi Chimodzi ndipo unapitirizabe kumaonjezeka kupeza ulamuliro wake waukulu kopambana m’kulamulira kwa Mfumu Trajan. Chotero Nthawi za Akunja za utali wa zaka 2,520 zinali kumayendabe kumka ku kutsirizika kwake mu 1914 C.E. Mbiri inayenda monga momwe kunanedweratu ndi Yesu kuti: “Yerusalemu adzaponderezedwa ndi mitundu [Yachikunja] kufikira nthawi zoikirwiratu za amitundu zitakwanira.” (Luka 21:24, NW) Ulamuliro Wachikunja Wachisanu ndi Chiwiri wa Dziko unali usanabukebe mu mpangidwe wa Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri wa Angelezi ndi Amereka, kuyambira mu 1763 C.E. Uwo ukugwirabe ntchito, ndipo Amereka chiwalo cha Ulamuliro wa Dziko wa Uwiri unachita phwando lokumbukira chaka chake cha mazana awiri, phwando lokumbukira chaka chake cha mazana awiri, phwando lake la kamodzi pa zaka mazana awiri, pa July 4, 1976. Phwando limene’lo linali pafupi-fupi zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu ziwiri pambuyo pa kutha kwa Nthawi za Akunja m’chaka cha 1914.

6. Kodi ndi mitundu yotani imene imakana kuzindikira ufumu wobadwa chatsopano wa Mulungu?

6 Si United States of America yekha ndi Mitundu ya British Commonwealth koma mitundu Yachikunja ina yonse inakana kuzindikira ufumu wa Mulungu Waumesiya, umene kubadwa kwake anauzidwa mobwereza-bwereza.—Chibvumbulutso 12:1-5.

7. Kodi Kristu adzapirira kwa utali wotani ndi mitundu yokana’yo?

7 “Kukhala pafupi” kapena parousia wa Mesiya wolemekezedwa’yo Yesu mu ulamuliro Waufumu kuli cheni-cheni chotsimikiziridwa chiyambire m’1914! Kodi ndi kwa utali wotani Mfumu Yaumesiya ya Yehova yolongedwa pa mpando wachifumu ndi yobvekedwa chipewa chachifumu’yo idzapitirazabe kupirira kukana kogwirizana kwa mboma a ndale za dziko a dziko lapansi tsopano popeza kuti kubwereka kwao ulamuliro wa dziko popanda chidodometso cha Mulungu kwatha? Si kwa nthawi yaitali kwambiri, ngati titi titsimikizire ndi nsonga zonena za “chizindikiro cha kukhala pafupi [parousia] kwa Kristu ndi cha mapeto a dongosolo la zinthu.”—Mateyu 24:3, NW.

8. Kodi liu’lo “mbadwo” m’Mateyu 24:34 limagwira ntchito pa yani?

8 Yesu Kristu anali kulingalira mbadwo wathu’wo kudza’nso mbadwo Wachiyuda wa m’nthawi yake, pamene iye anati: “Indetu ndinena kwa inu, mbadwo uwu sudzatha kuchoka kufikira zinthu zonse’zi zidzachitidwa. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka ai.”—Mateyu 24:34, 35, NW.

9. Kodi n’chiani chimene “mbadwo uno” waona kale chikukwaniritsidwa chiyambire 1914?

9 Chabwino, pamenepa, kodi ife a “mbadwo uno” tikuyembekezerabe chiani? Ife taona, kumva, ndipo takumana ndi nkhondo za m’mitundu yonse, njala, miriri, zibvomezi, chizunzo cha pa dziko lonse cha mboni Zachikristu za Yehova, kuonjezeka kwa kusaweruzika, kuzirala kwa kukonda Mulungu kwa auyinji, ndi kulalikira “mbiri yabwino imene’yi ya ufumu” kochitidwa ndi mboni Zachikristu za Yehova chiyambire 1914 C.E Takumanandi zinthu zimene’zi ku mlingo wokwanira koposa m’mene unachitira “mbadwo” Wachiyuda zaka mazana khumi ndi asanu ndi anai zapita’zo. Ife taona kuchotsedwa kwa “nsembe yachikhalire” ya kulambiridwa kwa Yehova m’kati mwa Nkhondo Yoyamba ya Dziko ndi zizunzo zounjikidwa pa alambiri a Yehova ndi mitundu yochita nkhondo’yo. Taona’nso “kuima kwa chinthu chonyansa chimene chichititsa chipululutso” m’kukhazikitsidwa’ kwa cholowa m’malo chopangidwa ndi anthu cha ufumu wa Mulungu Waumesiya, ndiko kuti, Chigwirizano cha Mitundu, mu 1919, ndi cholowa m’malo chake, Mitundu Yogwirizana, mu 1945. (Mateyu 24:4-15, NW; Danieli 12:11) Chotero kodi n’chiani chimene “mbadwo uno” uyenera kuchiyembekezera posachedwapa?

“DZIWANI KUTI IYE ALI PAFUPI PA KHOMO”

10-12. Kaamba ka “mbadwo uno” wa lero lino’wu, kodi n’chiani chimene Mateyu 24:23-31 amanena?

10 Ndi kulumphidwa kofulumira kwa zaka mazana ambiri za pakati pa Nyengo yathu Ino, Yesu analumpha “chisautso chachikulu” chimene chinachititsa chionongeko cha Yerusalemu mu 70 C.E. kudzafika ku nyengo yathu yobvuta ino, “nthawi ya mapeto.” (Danieli 12:4) Iye anati:

11 “Pamenepo ngati ali yense anena kwa inu, “Taonani! Kristu ali pano,’ kapena ‘uko!’ musakhulupirire. Pakuti Akristu onyengandi aneneri onyenga adzauka ndipo adzapereka zizindikiro zazikulu ndi zodabwitsa kotero kuti akasocheretse, ngati n’kotheka, ngakhale osankhidwa omwe. Taonani! Nadkuchenjezeranitu. Chifukwa chake, ngati anthu anena kwa inu, ‘Taonani! Iye ali m’chipululu,’ musapiteko; ‘Taonani! Iye ali m’zipinda za m’kati,’ musakhulupirire. Pakuti monga momwe mphezi ichokera ku mbali za kum’mawa niwala ku mbali za kumadzulo, chotero kudzakhala kukhala pafupi [parousia] kwa Mwana wa munthu. Kuli konse kumene kuli mtembo, kumene’ko miimba idzasonkhana.

12 “Mwamsanga chitapita chisautso cha masiku amene’wo dzuwa lidzadetsedwa, ndipo mwezi sudzaonetsa kuunika kwake, ndipo nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Ndipo pamenepo chizindikiro cha Mwana wa munthu chidzaonekera kumwamba, ndipo pamenepo mafuko onse a dziko lapansi adzadzimenya pachifukwa mwachisoni, ndipo iwo adzaona mwana wa munthu alinkudza ndi mitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Ndipo iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera ku mphepo zinai, kuchokera ku malekezero amodzi a kumwamba kumka ku malekezero ake ena.”—Mateyu 24:23-31, NW; Marko 13:21-27.

13. Kodi tikudziwa motani kuti otsalira a “osankhidwa” ali nafe?

13 Mofanana ndi “kulira kwakukulu kwa lipenga” uthenga wonenedweratu m’Mateyu 24:14, NW, “mbiri yabwino imene’yi ya ufumu,” yalengezedwa moonjezereka-onjezereka pa dziko lonse chiyambire chaka cha 1919 ndi otsalira amakono a “osankhidwa ake.” Pamene “osankhidwa’ amene’wa amene asonkhanitsidwa kuchokera ku mbali zazikulu zinai (“mphepo zinai”) akhala ochuluka, ndi pamene’nso mfuu ya lipenga la “mbiri yabwino” yakhala yaikulu kwambiri ndi yofalikira kwambiri. Kaamba ka chifukwa chimene’chi tikudziwa kuti “osankhidwa’wo” amene ali oyenerera kukhala ndi malo mu ufumu wa kumwamba ali nafe mu “nthawi ya mapeto” ino. Sitinaone moonekera angelo ali onse auzimu akuwasonkhanitsira pamodzi, koma tikuona chiyambukiro cha ntchito za angelo zimene’zo mogwirizana ndi chifuniro cha Mwana wa Munthu wolemekezedwa’yo. Mwa kulalikira kwao kwapoyera ndi kwa ku nyumba ndi nyumba, otsalira a “osankhidwa” osonkhanitsidwa’wo adzipangitsa kuonedwa ndi kumvedwa.

14. Kodi angelo asonkhanitsira “osankhidwa’wo” m’chiani?

14 Ai, iwo sanasonkhanitisdwe pansi pa chitsogozo cha angelo kulowa m’malo ali onse m’dziko lina liri lonse limodzi. M’malo mwake, iwo asonkhanitsidwa kukhala mu umodzi wa pa dziko lonse walingaliro ndi ntchito malinga ndi kunena kwa Malemba Oyera omatseguka’wo, ndipo iwo nthawi zonse amasonkhana pamodzi mokhazikika m’mipingo yao, m’nyumba kapena m’Making’idomu Holo. Ngakhale pamene aletsedwa ndi maboma audziko audani, iwo amapitirizabe m’kusonkhana pamodzi, “mobisa,” titero kunena kwake, kulimbikitsana wina ndi mnzake m’chikhulupiriro Chachikristu ndi kulinganiza zoyesa-yesa zao za kulalikira. Pa phwando lao la chaka ndi chaka la Chakudya Chamadzulo cha Ambuye, kukumbukiridwa kwa imfa ya Kristu pa Nisan 14 (kalendala ya Baibulo), iwo amadyako zizindikiro za mkate ndi vinyo. Pa April 14 (Nisan 14), wa chaka cha 1976, 10,187 a “osankhidwa” otero’wo motero anachita phwando ndi kudyako zizindikiro.

15. Kodi otsalira osonkhanitsidwa’wo tsopano akufuna-funa kuonekera kwa “chizindikiro” chotani?

15 “Osankhidwa” okhulupirika amene’wa akuyembekezera “chizindikiro cha Mwana wa munthu” kumwamba pamene iye akudza m’ntchito yake ya kukhala Wakupha wa Mulungu kudzaononga mitundu yonse imene ikupitirizabe kutsutsa ufumu wake Waumesiya pa dziko lonse lapansi. N’zosadabwitsa kuti, pamene iye apangitsa kukhala pafupi kwake kumvedwa mwa machitidwe ake a kuononga, kudzakhala monga ngati kuti iwo anamuona kweni-kweni “akudza pa mitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” Chifukwa chabwino’di kwambiri kwa iwo ‘chodzimenyera pachifukwa mwachisoni.’—Mateyu 24:30; Chibvumbulutso 1:7.

NSONGA YOTI IPHUNZIRIDWE TSOPANO

16. Kodi n’chiani chimene chimasonyeza m’mene tingadziwire kuti iye ali pafupi pa khomo?

16 Ife tiri, kapena pafupi-fupi ife tonse tiyenera, kukhala, okondweretsedwa kudziwa kaya ngati mapeto akulu a zochitika adzadza m’nthawi yathu. Kodi ndi motani m’mene tingadziwire kuthekera kwa zimene’zi ndi kutsogozedwa moyenerera? Kaamba ka chitsogozo cha ife amene tiri ndi moyo lero lino, Yesu monga Mneneri ponena za “mapeto a dongosolo la zinthu” anapitirizabe kunena ndi atumwi ake khumi ndi awiri kuti: “Tsopano phunzirani ndi mtengo wa mkuyu monga fanizo la nsonga imene’yi: Pamene mungoona nthambi yatsopano ikuphuka ndipo ikuphuka masamba, mumadziwa kuti dzinja liri pafupi. Chomwecho inu’nso, pamene muona zinthu zimene’zi, dziwani kuti iye ali pafupi pa khomo. Ndithudi ndinena kwa inu mbadwo uno sudzachoka konse kufikira zinthu zonse’zi zitachitika. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mau anga sadzachoka konse.”—Mateyu 24:32-35, NW; yerekezerani ndi Luka 21:27-33.

17. Ife amene tinaona zinthu zimene’zi zikuyamba, tikuchita chiani ndi kudziwa chiani?

17 “Osankhidwa” awo amene ali ndi moyo lero lino amene anaona kuulika kwa Nkhondo Yoyamba ya Dziko mu 1914 angathe kukumbukira m’mene tonsefe tikusangalalira chifukwa chakuti taona “zinthu zimene’zi zikuyamba kuchitika.” Tikudziwa kuti Kristu wokhazikitsidwa pa mpando wachifumu chatsopano’yo anali “pafupi pa khomo” kaamba ka ntchito yake ya kupha motsutsana ndi “dongosolo la zinthu” loipa’li. Tikusangalala chifukwa chakuti “ufumu wa Mulungu uli pafupi” kaamba ka kutenga ulamuliro wotheratu wa dziko ndi kugwira ntchito monga boma la dziko. Sitinatope nako kukumbutsidwa mobwereza-bwereza m’kati mwa zaka makumi asanu ndi limodzi ndi zoposa zapita zimene’zi kuti ufumu wa Mulungu Waumesiya uli “pafupi pa khomo.” Kutikumbutsa kumene’ku sikunakhale kwachikale ndi kutaya mphamvu yake ndi nyonga yake yosonkhezera moyo kwa ife. Tikudziwa kuti ife tiri a “mbadwo” umene unaona chiyambi cha zinthu zimene’zi mu 1914 pa mapeto a Nthawi za Akunja, ndipo timakhulupirira chitsimikiziritso cha Yesu chakuti “mbadwo” wathu umodzi-modzi’wu udzaona kutha kwa zinthu zofunika zimene’zi, zonse’zi zikumafika pachimake m’kulowa malo kotheratu mwa Ufumu wopambana kwa zochitika za anthu zonse.

18. Kodi kuchenjeza kwathu anthu kuli kuwaopsyeza chabe kuti achite choyenera?

18 Tsoka la pa dziko lonse lapansi loyambukira anthu ochuluka kwambiri ndi magulu koposa m’mene chigumula cha m’tsiku la Nowa chinayambukirira latsala pang’ono kuulika pa “dziko la anthu opanda umulungu’li.” (2 Petro 2:5, NW) Limene’li lifunikira-liyenera-kumvedwa mobwereza-bwereza ndi “osankhidwa” ndi ena onse amene ali okondweretsedwa ndi boma langwiro ndi lolungama la dziko. Imene’yi sindiyo nkhani ya kuopsyeza anthu ndi chochititsa mantha chonyenga chofanana ndi chija cha chipunzitso chonyoza Mulungu cha “chizunzo chamuyaya mu helo wa moto weni-weni ndi sulfule” m’malo mwakuti aumirize kutembenuka ndi kufika kwao pa chalichi. Osati kokha moyo, koma moyo wamuyaya, wa anthu okhala paupandu’wo uli pa ngozi, ndipo monga ‘alonda’ oikidwa ndi Mulungu, tiri ndi thayo la kuchenjeza anthu oona mtima, okonda chilungamo. (Ezekieli 3:17-21; 33:6-20) Sitikufuna kukhala osakwaniritsa mathayo athu kwa Mulungu. Sitikudziopsyeza kuti tigwire ntchito pamene tikulingalira nkhani imene’yi mwamphamvu. Cholinga chathu ndicho kusonyeza chikondi kwa Mulungu ndi kwa anthu anzathu, maka-maka abale athu Achikristu.

19, 20. Kodi Yesu anafuna kuti chenjezo lake likhale losaphula kanthu pa atumwi ake?

19 Yesu Kristu iye mwini sanafune kulalikira ndi kunenera popanda chifuno. Iye sanafune chenjezo lake kukhala losaphula kanthu kwa ophunzira ake, pamene iye anati kwa iwo: “Ponena za tsiku iro ndi ora palibe munthu adziwa, ngakhale angelo a kumwamba kapena Mwana, koma Atate yekha. Pakuti monga momwe zinaliri m’masiku a Nowa, kudzakhala chimodzi-modzi’nso pa kukhala pafupi [parousia] kwa Mwana wa munthu. Pakuti monga momwe iwo analiri masiku amene’wo chisanafike chigumula, analinkudya ndi kumwa, amuna anali kukwatira ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikira tsiku [!] limene Nowa analowa m’chingalawa; ndipo iwo sanazindikire kufikira chigumula chinadza ndi kuwasesa onse, kudzakhala motero kukhala pafupi kwa Mwana wa munthu. Pamenepo amuna awiri adzakhala m’munda: wina adzatengedwa ndi wina kusiyidwa; akazi awiri adzakhala akupera pa mphero: mmodzi adzatengedwa ndi wina kusiyidwa. Chifukwa cha chimene’cho, khalani maso, chifukwa chakuti simudziwa tsiku limene Mbuye wanu akudza.

20 Koma dziwani chinthu chimodzi, kuti ngati mwini nyumba akadadziwa nthawi imene mbala ikadza, iye akanakhala maso ndi kusalola nyumba yake kuswedwa. Chifukwa chake inu’nso dzitsimikizireni kukhala okonzekera, chifukwa chakuti pa ora limene simuganizira kukhala iro, Mwana wa munthu akadza.”—Mateyu 24:36-44, NW.

21. Kodi ndi mafunso ndi chigomeko chotani zimene fanizo la Yesu likudzutsa?

21 Kodi fanizo la Yesu lonena za mwini nyumba limatanthauza kuti, ngati alola ophunzira a lero linofe kudziwiratu tsiku ndi ora la kudza kwake kudzathetsa nkhani, akatsimikizira kutipeza tonse tiri ogalamuka ndi odikira? Chifukwa cha chimene’cho kodi sitiyenera kupatsidwa chidziwitso chapasadakhale chonena za tsiku ndi ora leni-leni? Imene’yo ikakhala njira imene timachitira zinthu lero lino: patsani wolandira alendo wathu chidziwitso chapasadakhale m’malo mwakuti asadzidzimutsidwe koma akonzekere zinthu zonse ndi kusachititsidwa manyazi.

22. Kodi n’chifukwa ninji Yesu sakupereka chidziwitso cha nthawi idakalipo chonena za kudza kwake?

22 N’zosiyana ndi Yesu Kristu, pakuti ophunzira ake ali kweni-kweni akapolo ake ogulidwa. Pa nthawi zonse iye amawafuna kukhala okondweretsedwa ndi kudza kwake kudzapereka ziweruzo ndipo chotero kukhala oti n’kugwiritsiridwa ntchito nthawi zonse, mwa kum’konda. Iye samawafuna kukhala achinyengo okoma pamaso, obvala kaonekedwe ka kukhala wokangalika nthawi zonse mu utumiki nthawi itangotsala pang’ono yakuti afike. Mwa kukhala osadziwitsidwiratu pasadakhale nthawi yeni-yeni imene iye adzafika, chikondi ndi kumvera kwa ophunzira’wo kwa iye zachititsidwa kuyesedwa nthawi ndi nthawi. Kodi iwo ali okondweretsedwa nthawi ndi nthawi. Kodi iwo ali okondweretsedwa moona mtima ndi ufumu wake ndipo kodi iwo amakhala ndi nthawi ya kulowa m’zochitika zaudziko, tinene kuti, m’ndale za dziko zaudziko? Mfumu Yesu Kristu amaipidwa ndi utumiki wofunda, kumvetsera kusakondweretsedwa. Iye samafuna onyenga mu ufumu wake.

23, 24. Kodi Yesu anagogomezera nsonga yapamwambapo’yo ndi mafanizo otani?

23 Nsonga yofunika kwambiri imene’yi ikugogomezeredwa ndi Yesu Kristu m’mafanizo onena za “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” ndi “kapolo woipa uja,” mafanizo amene iye anawapereka atangotha kumene kufulumiza ophunzira ake ‘kudzitsimikizira kukhala okonzekera’ nthawi zonse. (Mat. 24:45-51, NW) Pali mphotho yaikulu yosungidwira ophunzira a Yesu Kristu amene akudzitsimikizira kukhala akapolo ake okhulupirika, ochenjera ndi achikondi, odzipereka mosabwerera m’mbuyo ku kuyendetsa kwake boma la dziko lolonjezedwa’lo. Ife tikum’tumikira osati kokha kaamba ka mphotho. Komabe, iye akulonjeza mphotho yaikulu mwa chiyamikiro chake. Kodi ife tikufuna mphotho imene’yo? Iri chosemphana ndi chilango cha osakhulupirika. (Luka 12:35-46) Mwa kukonda kwathu Mfumu yodzozedwa ya Yehova tikufuna mphotho ya kukhala okhulupirika, kodi si choncho? Yankho lathu pokhala Inde! Pamenepo tiyeni tichite zimene Mfumu Yesu Kristu amatiuza:

24 “Chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.”—Marko 13:32-37; Luka 21:36.

25. Chotero, kodi tsopano maso athu ayenera kusumikidwa pa chiani, ndipo chifukwa ninji?

25 Tiyeni odikira tonsefe tisumike maso athu pa “chizindikiro” chimene chakhala chokhoza kuoneka chiyambire 1914 C.E. (Mateyu 24:3, NW) Zitisonkhezeretu nthawi zonse kukhala maso, pakuti boma Laumesiya la dziko lonse liri pafupi!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena