Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • uw mutu 22 tsamba 169-175
  • Pitirizanibe Kulankhula Mawu a Mulungu Mtima Molimbika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Pitirizanibe Kulankhula Mawu a Mulungu Mtima Molimbika
  • Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Osadalira Nyonga ya Ife Eni
  • Cholembedwa cha Kuchitira Umboni Molimba Mtima
  • Pitirizani Kulankhula Mawu a Mulungu Molimbika Mtima
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Tsanzirani Yesu mwa Kulalikira Molimba Mtima
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Mudzakhala Mboni Zanga”
    Nsanja ya Olonda—2014
  • “Mpaka Kumalekezero a Dziko Lapansi.”
    ‘Kuchitira Umboni Mokwanira za Ufumu wa Mulungu’
Onani Zambiri
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
uw mutu 22 tsamba 169-175

Mutu 22

Pitirizanibe Kulankhula Mawu a Mulungu Mtima Molimbika

1. (a) Kodi ndimbiri yabwino yotani imene ophunzira a Yesu analengeza kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., koma kodi nchiyani chimene chinali kachitidwe ka olamulira ndi akulu a Ayuda? (b) Kodi ndimafunso otani amene tingadzifunse ponena za izi?

ZOCHITIKA zofunika koposa m’zaka zoposa 4 000 zapita m’mbiri ya anthu zachitika. Mwana weniweni wa Mulungu, Yesu Kristu, wadzozedwa monga Mfumu yamtsogolo padziko lonse lapansi. Mosasamala kanthu za kuphedwa kwa Yesu mosonkhezeredwa ndi adani achipembedzo, Yehova waukitsa Mwana wake kwa akufa. Kupyolera mwa iye chipulumutso chinali chothekera limodzi ndi lingaliro lamoyo wosatha. Koma pamene ophunzira okhulupirika a Yesu analengeza poyera mbiri yabwino imeneyi, chitsutso chowopsa chinaulika. Choyamba, awiri a atumwi ake anaikidwa m’ndende, kenako onse. Anakwapulidwa ndi kulamulidwa kuleka kulankhula zonena za Dzina la Yesu. (Mac. 4:1-3, 17; 18, 40) Kodi iwo akanayenera kuchitanji? Kodi inu mukanachitanji? Kodi inu mukanapitirizabe kuchitira umboni molimbika?

2. (a) Kodi ndi uthenga wodabwitsadi wotani umene ufunikira kulengezedwa m’tsiku lathu? (b) Kodi ndani amene ali ndi thayo lakuuchita?

2 M’chaka cha 1914 C.E. chochitika chodabwitsadi kwambiri chofunika m’chilengedwe chonse chinachitika. Ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Yesu Kristu unakhazikitsidwadi kumwamba. Kenako, Satana ndi ziwanda zake anaponyeredwa pansi kudziko lapansi. (Chiv. 12:1-5, 7-12) Masiku otsiriza a dongosolo loipa lazinthu anali atayamba. Mbadwo umene unawona zochitika za 1914 usanathe kufa, Mulungu adzaphwanya dongosolo lonse la Satana lazinthu. (Mat. 24:34) Opulumuka adzakhala ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya pamaso pawo. M’kukwaniritsidwa kwa chifuno choyambirira cha Mulungu, dziko lonse lapansi lidzakhala Paradaiso. Ngati inu mwavomereza kale mbiri yabwino imeneyi, muli ndi thayo la kuigawira ena. (Mat. 24:14) Koma kodi ndikulabadira kotani kumene mungayembekezere?

3. (a) Kodi ndimotani mmene anthu amalabadirira uthenga wa Ufumu? (b) Chotero, kodi ndifunso lotani limene tiyenera kuyang’anizana nalo?

3 Pamane kuli kwakuti anthu ena angakulandireni mwaubwenzi monga wolengeza wa Ufumu, unyinji udzakhaladi wamphwayi. (Mat. 24:37-39) Ena angakusekeni kapena angakutsutseni kwambiri. Yesu anachenjeza kuti chitsutso china chingadze kuchokera kwa achibale anu. (Luka 21:16-19) Icho chingachokerenso kumalo anu antchito kapena kusukulu. M’mbali zambiri zadziko lapansi Mboni za Yehova zafika ngakhale pa kuletsedwa ndi boma mosalungama. Pamene mukumana ndi ina ya mikhalidwe yotero kapena yonseyo, kodi mudzapitirizabe kulankhula Mawu a Mulungu molimbika?

4. Kodi chitsimikizo chathu chimatsimikiziritsa kuti tidzapitirizabe kutumikira Mulungu mokhulupirika?

4 Mosakaikira, mukufuna kukhala mtumiki wolimba mtima wa Mulungu. Komabe, ena amene ankalingalira kuti palibe chimene chikanawabwezera m’mbuyo asiya kukhala olengeza Ufumu. Mosiyana, ena, kuphatikizapo anthu amene ali ndi chibadwa cha mantha pang’ono, apitirizabe mosaleka kukhala atumiki a Mulungu achangu. Kodi ndimotani mmene mungatsimikizirire kukhala munthu amene “amachirimika m’chikhulupiriro”?—1 Akor. 16:13.

Osadalira Nyonga ya Ife Eni

5. (a) Kuti tidzitsimikizire ife eni kukhala atumiki okhulupirika a Mulungu, kodi nchiyani chimene chiri chofunika chachikulu? (b) Kodi nchifukwa ninji misonkhano iri yofunika kwambiri?

5 Ndithudi, pali zochititsa zambiri zophatikizidwa m’kukhala mtumiki wokhulupirika wa Mulungu. Koma chachikulu pazonsezo ndicho kudalira Yehova ndi makonzedwe ake. Kodi ndimotani mmene timasonyezera chidaliro chimenecho? Njira imodzi iri mwa kufika pamisonkhano yampingo. Malemba amatilimbikitsa kusainyalanyaza. (Aheb. 10:23-25) Awo amene apitirizabe kukhala mboni zokhulupirika za Yehova, kaya atayang’anizana ndi mphwayi ya anthu kapena chizunzo, adzigwiritsira ntchito kukhala okhazikika m’kufika pamisonkhano ndi olambira anzawo. Pamisonkhano imeneyi chidziwitso chathu cha Malemba chimawonjezeredwa, koma sindiko kukondweretsedwa chabe ndi zinthu zatsopano kumene kumatichititsa kufikapo. (Yerekezerani ndi Machitidwe 17:21.) Chiyamikiro chathu cha chowonadi chodziwika bwino chimakula, ndipo kuzindikira kwathu mmene tingazigwiritsirire ntchito chikhala chakuthwa. Chitsanzo chimene Yesu anatipatsa chimakhomerezeka kwambiri pamaganizo ndi mtima wathu. (Aef. 4:20-24) Timakokedwera pafupi ndi abale athu Achikristu m’kulambira kogwirizana ndipo timalimbikitsidwa mwachindunji kupitirizabe kuchita chifuniro cha Mulungu. Mzimu wa Yehova umagawira chitsogozo kupyolera mwa mpingo, ndipo mwanjira ya mzimu umenewo Yesu amakhala pakati pathu pamene tisonkhana m’dzina lake.—Chiv. 3:6; Mat. 18:20.

6. Kumene Mboni za Yehova ziri zoletsedwa, kodi nchiyani chimene chimachitidwa ponena za misonkhano?

6 Kodi inu mumafika pamisonkhano yonse mokhazikika ndipo kodi mumagwiritsira ntchito kwa inu mwini zimene mumamva zikukambitsiridwa? Nthawi zina, mkati mwa kuletsedwa, kwakhala kofunika kuchita misonkhano m’timagulu tochepa m’nyumba za anthu. Malo ndi misonkhano zingasinthe ndipo sizingakhale zoyenerera nthawi zonse, misonkhano ina ikumachitidwa pakati pa usiku. Koma, mosasamala kanthu za kusapeza bwino kwaumwini kapena upandu, abale ndi alongo okhulupirika amapanga kuyesayesa kwaphamphu kukhalapo pamsonkhano uliwonse.

7. (a) Kodi timasonyeza kudalira kwathu Yehova mwanjira inanso yotani? (b) Kodi ndimotani mmene iyi ingatithandizire kupitirizabe kulankhula molimba mtima?

7 Kudalira Yehova kumasonyezedwanso mwa kutembenukira kwa iye m’pemphero mokhazikika—osati monga chizolowezi chabe cha mwambo, koma ndi kuzindikira kochokera pansi pa mtima kuti tifunikira chithandizo cha Mulungu. Kodi mumachita zimenezo? Yesu anapemphera mobwerezabwereza mkati mwa uminisitala wake wa padziko lapansi. (Luka 3:21; 6:12, 13; 9:18, 28; 11:1; 22:39-44) Ndipo pausikuwo kupachikidwa kwake kusanachitike analimbikitsa ophunzira ake kuti “dikirani, pempherani, kuti mungalowe m’kuyesedwa.” (Marko 14:38) Ngati tikumana ndi kuchitira mphwayi kwambiri uthenga wa Ufumu, pangakhale chiyeso cha kuchepetsa liwiro mu uminisitala wathu. Ngati anthu atiseka kapena ngati palidi chizunzo chowonjezereka, tingalowe m’chiyeso chalingaliro la kukhala chete kotero kuti tichipewe. Koma ngati tipemphera mwaphamphu kuti mzimu wa Mulungu utithandize kupitirizabe kulankhula molimbika, tidzatetezeredwa ku kugonjera m’chiyeso chimenecho.—Luka 11:13; Aef. 6:18-20.

Cholembedwa cha Kuchitira Umboni Molimba Mtima

8. (a) Kodi nchifukwa ninji cholembedwacho m’Machitidwe chiri chokondweretsa mwapadera kwa ife? (b) Yankhani mafunso operekedwa pamapeto a ndime ino, mukumagogomezera mmene mawuwo angatipindulitsire.

8 Cholembedwa chimene chiri m’bukhu la Machitidwe chiri chokondweretsa mwapadera kwa ife tonse. Chimasimba mmene atumwi ndi ophunzira ena oyambirira, anthu amene anali ndi malingaliro ofanana ndi athu, analakira zopinga ndi kutsimikizira kukhala mboni za Yehova zokhulupirika ndi zolimba mtima. Tiyeni tipende gawo lacholembedwa chimenecho mothandizidwa ndi mafunso ndi malemba olembedwa otsatirawa. Pamene tikutero, lingalirani mmene inu mwininu mungapindulire ndi zimene mukuwerenga.

Kodi atumwi anali anthu ophunzira kwambiri? Kodi iwo anali anthu amene mwachibadwa anali opanda mantha, mosasamala kanthu za zimene zinachitika? (Mac. 4:13; Yoh. 18:17, 25-27; 20:19)

Kodi nchiyani chimene chinakhozetsa Petro kulankhula molimba mtima pamaso pa bwalo lamilandu Lachiyuda limene linali litaweruzira Mwana wa Mulungu mwiniyo ku imfa osati milungu yambiri yapitayo? (Mac. 4:8; Mat. 10:19, 20)

Kodi atumwi anali kuchitanji mkati mwa milunguyo asanadzawonekere pamaso pa Bwalo lamilandu? (Mac. 1:14; 2:1, 42)

Pamene olamulirawo anawalamula kuleka kulalikira m’dzina la Yesu, kodi Petro ndi Yohane anayankhanji? (Mac. 4:19, 20)

Atamasulidwa, kodi nkwayani kumene kachiwirinso iwo anayang’ana kaamba ka chithandizo? Kodi iwo anam’pempha kuletsa chizunzocho, kapena chiyani? (Mac. 4:24-31)

Kodi Yehova anagawira chithandizo m’njira yotani pamene otsutsa anayesa kuletsa ntchito yolalikira? (Mac. 5:17-20, 33-40)

Kodi ndimotani mmene atumwi anasonyezera kuti anazindikira chifukwa chimene analanditsidwira? (Mac. 5:21, 41, 42)

Ngakhale pamene unyinji wa ophunzirawo unabalalitsidwa chifukwa cha kukula kwa chizunzo, kodi iwo anapitirizabe kuchita chiyani? (Mac. 8:3, 4; 11:19-21)

9. (a) Kodi nzotulukapo zochititsa chidwi zotani zimene zinachokera mu uminisitala wa ophunzira oyambirira amenewo? (b) Kodi ndimotani mmene tafikira kukhala olowetsedwamo?

9 Ntchito yawo mogwirizana ndi mbiri yabwino sinali yosaphula kanthu. Pafupifupi ophunzira 3 000 anali atabatizidwa pa Pentekoste wa 33 C.E. “Okhulupirira mwa Ambuye anapitirizabe kuwonjezeredwa, ambirimbiri amuna ndi akazi omwe.” (Mac. 2:41; 4:4; 5:14, NW) M’kupita kwa nthawi kumasimbidwa kuti ngakhale mmodzi wa ozunza wachangu kwambiri, Saulo wa ku Tariso, anali atakhala Mkristu ndipo iyemwiniyo analikuchitira umboni chowonadi molimba mtima. Anadziwika monga mtumwi Paulo. (Agal. 1:22-24) Ntchito imene inayamba m’zaka za zana loyamba sinayime. Yawonjezera liwiro mu “masiku otsiriza” ano ndipo yafika mbali zonse zadziko lapansi. Tiri ndi mwayi wa kukhalamo ndi phande, ndipo pamene tikutero tingaphunzire kuchokera ku chitsanzo choperekedwa ndi mboni zokhulupirika zimene zinatumikira ife tisanakhaleko.

10. (a) Kodi ndimipata yotani imene Paulo anagwiritsira ntchito kuchitira umboni? (b) Kodi ndim’njira zotani m’zimene inu mumafalitsa uthenga wa Ufumu kwa ena?

10 Pamene Paulo anaphunzira chowonadi chonena za Yesu Kristu, iye sanazengereze. “Pomwepo . . . anayamba kulalikira Yesu, kuti iye ndiye Mwana wa Mulungu.” (Mac. 9:20) Anayamikira chisomo cha Mulungu kwa iye ndipo anazindikira kuti aliyense anafunikira mbiri yabwino imene iye anali atalandira. Mogwirizana ndi mwambo wa panthawiyo, popeza kuti iye anali Myuda anapita ku masunagoge, amene anali malo Achiyuda osonkhanako anthu onse, kukapereka umboni. Iye analalikiranso kunyumba ndi nyumba ndi kulankhula ndi anthu pa msika. Ndipo anali wofunitsitsa kusamukira m’magawo atsopano kukafalitsa mbiri yabwino.—Mac. 17:17; 20:20; Aroma 15:23, 24.

11. (a) Kodi ndimotani mmene Paulo anasonyezera kuti, ngakhale anali wolimba mtima, analinso waluntha m’njira imene anachitira nayo umboni? (b) Kodi ndimotani mmene ife tingasonyezere mkhalidwe umenewo pochitira umboni kwa achibale, ogwira nawo ntchito kapena anzathu a kusukulu?

11 Paulo anali wolimba mtima, komanso waluntha, monga momwe tiyenera kukhalira. Kwa Ayuda analankhula nawo za malonjezo opangidwa ndi Mulungu kwa makolo awo. Kwa Agiriki analankhula za zinthu zimene anali ozolowerana nazo. Nthawi zina anagwiritsira ntchito chokumana nacho cha iyemwini m’kuphunzira chowonadi monga njira yoperekera umboni. Monga momwe analongosolera kuti: “Ndichita zonse chifukwa cha uthenga wabwino, kuti ndikakhale oyanjana nawo.”—1 Akor. 9:20-23; Mac. 22:3-21.

12. (a) Ngakhale kuti anali wolimba mtima, kodi nchiyani chimene Paulo anachita kotero kuti apewe kulowa m’mikangano yosalekeza ndi otsutsa? (b) Kodi ndiliti pamene mwanzeru tingatsanzire chitsanzo chimenecho, ndipo motani? (c) Kodi mphamvu yopitirizira kulankhula molimba mtima imachokera kuti?

12 Pamene chitsutso cha mbiri yabwino chinakuchititsa kuwonekera kukhala kwabwino koposa kukalalikira kumalo ena kapena kusamukira kumagawo ena kwa kanthawi, Paulo anachita zimenezo m’malo mwa kudzilowetsa m’mikangano ndi adani a chowonadi. (Mac. 14:5-7; 18:5-7; Aroma 12:18) Koma iye sanachite manyazi konse ndi mbiri yabwino. (Aroma 1:16) Ngakhale kuli kwakuti Paulo anapeza kuti kuchitiridwa mwachipongwe, ngakhale mwachiwawa, ndi otsutsa kunali kosakondweretsa, iye anapeza “kulimbika mtima mwa Mulungu wathu” napitirizabe kulalikira. Mosasamala kanthu ndi mikhalidwe yovuta mu imene analowamo, anati: “Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse.” (1 Ates. 2:2; 2 Tim. 4:17) Mutu wa mpingo Wachikristu, Ambuye Yesu, akupitirizabe kugawira mphamvu yofunika m’kuchita ntchito imene adaneneratu kaamba ka tsiku lathu.—Marko 13:10.

13. Kodi nchiyani chimene chimapereka umboni wa kulimba mtima Kwachikristu, ndipo kodi nchiyani chimene chiri maziko ake?

13 Tiri ndi chifukwa chirichonse chopitirizira kulankhula molimba mtima Mawu a Mulungu, monga momwedi Yesu Kristu ndi atumiki ena okhulupirika a Mulungu m’zaka za zana loyamba anachitira. Ichi sichitanthauza kukhala wankhalwe kapena wachipongwe m’makhalidwe athu. Palibe chifukwa chokhalira wosalingalira kapena kukakamizira uthenga pa awo amene saufuna. Koma sitimaleka chifukwa chakuti anthu ali amphwayi, ndiponso sitimaopsedwa ndi chitsutso ndi kukhala chete. Mofanana ndi Yesu, timasonya ku Ufumu wa Mulungu monga boma loyenerera ladziko lonse lapansi. Timalankhula ndi chidaliro chifukwa tikuimira Yehova, Mfumu ya Chilengedwe chonse, ndipo uthenga umene timalengeza sumachokera kwa ife koma kwa iye.—Afil. 1:27, 28; 1 Ates. 2:13.

Makambitsirano Openda

● Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kupereka uthenga wa Ufumu kwa aliyense wothekera? Koma kodi ndikachitidwe kotani kamene tiyenera kuyembekezera?

● Kodi ndimotani mmene tingasonyezere kuti sitikuyesayesa kudalira pa nyonga ya ife eni potumikira Yehova?

● Kodi ndiphunziro lofunika lotani limene timapeza kuchokera m’bukhu la Machitidwe?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena