Nyimbo 158
Umodzi Wathu Wachikristu
1. Ndani ali ngati Yehova,
Magwerodi a umodzi!
Anatumizatu Mwana wake
Kudzatimasula ife.
Maziko a umodziwo
Anawaika mwa Kristu.
Kukhalatu monga banja limodzi
Ndi onse omvera Mawu.
2. Kodi ogwirizana n’Kristu
Tiri nalo thayo lanji?
Tikhale ndi khalidwe labwino,
Chifunocho chichitike.
Nkana tiri achisoni,
Mzimu umasangalatsa.
Muli chimwemwedi zedi m’kupatsa,
Potsanziratu Mulungu.
3. Wonani! teokrase Wake
E, atitchinjirizatu.
M’kulandira chowonadi chake,
Tidzakhala muumodzi.
M’lungu afunanji nafe?
Tisonye khalidwe lanji?
Kuchita chilungamo ndi chifundo,
Kuyenda modzichepetsa.