Nyimbo 213
Kugwirira Ntchito Pamodzi m’Chigwirizano
1. Tichite mogwirizana.
Tipeŵe kudziimira.
Chiyanjano ndi umodzi
Zidzetsa mtendere (wambiridi).
Umodzi udala.
Tiuwonadi (weniwenidi).
Tikakhala ndi maluso,
Sibwinodi kudzikweza.
Tikhale odzichepetsa,
Titamande M’lungu.
2. Makanitu ndi kaduka,
M’dziko lino laudani.
Tifunefune mtendere.
Uli ngati mame (ngati mame).
Mtendere ndi mame.
Utsitsimula (umaterodi).
Mikangano imabuka;
Tiri opanda ungwiro!
Kuithetsa nkwaphindudi.
Tisunge umodzi.
3. Pogwira ntchito limodzi,
Tisonyeze umodziwo.
Nkokoma ndipo kwabwino.
Tiusunge bwino (bwinobwino).
Umodzi tisunge,
Uli wabwino (tidziterodi).
Umodzi upindulitsa
—Timakhala ndi Yehova.
Watibwezera mtendere,
mwa Mbuye Mfumuyo.