Mutu 4
Mtundu wa Moyo Umene Ukuyembekezera Opulumuka
NGAKHALE kuti “tsiku la Yehova” lirinkudzalo lidzakhala lowopsa, silidzasiya dziko lapansi litawonongeka kosakhoza kukhalidwa ndi anthu. Ziyambukiro zake sizidzakhala zofanana ndi za chipiyoyo chanyukliya, chimene chikuwopedwa kuti chikawononga mpweya wa malo okhala ndi kuchititsa opulumuka kuvutika ndi ziyambukiro zowopsa zochokera m’misisi. Mmalo mwa kuwononga dziko lapansi kuti lisakhalidwe ndi anthu, Mlengi “adzawononga iwo akuwononga dziko.”—Yoweli 2:30, 31; Chivumbulutso 11:18.
2 Mulibe chikaikiro ngakhale chochepetsetsa m’maganizo mwa atumiki okhulupirika a Yehova chakuti Mulungu angakhoze kuwapulumutsa mosasamala kanthu za mphamvu yowononga imene panthaŵiyo adzatulutsa mowakweteza. Iwo akudziŵa kuti pamene Sodomu ndi Gomora anaipa mwamakhalidwe anawonongedwa ndi ‘sulfure ndi moto zochokera kumwamba,’ angelo a Yehova anapulumutsa Loti ndi ana ake aakazi aŵiri. (Genesis 19:15-17, 24-26) Iwo akuzindikiranso kuti pamene ana achisamba a Igupto anawonongedwa onse m’masiku a Mose, mngelo wa Yehova wowononga analambalala nyumba za Aisrayeli, nyumba zimene zinaikidwa chizindikiro cha mwazi wa mwana wankhosa wa Paskha. (Eksodo 12:21-29) Choteronso, pamene mkwiyo wowononga wa chisautso chachikulu uwulika, Yehova adzapulumutsa iwo amene ampanga kukhala ngaka yawo.—Salmo 91:1, 2, 14-16; Yesaya 26:20.
3 Zowona, chifukwa cha chiwonongeko chachikulu, dziko lapansi lidzati katakata ndi iwo ophedwa ndi Yehova. Koma palibe munthu amene akudziŵa bwinopo koposa Mulungu chimene chifunikira kuchitidwa kutetezera thanzi la opulumuka. Akutiuza kuti adzaitanira mbalame zam’mwamba ndi zirombo zakuthengo ku ‘phwando lake lalikulu lamadzulo’ ndi kuti zidzakhuta nyama za iwo ophedwa. (Chivumbulutso 19:17, 18; Ezekieli 39:17-20) Zimene izo sizingadye angaziwononge ndi njira ina. Chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi monga momwe chinalongosoledwera mu Edene panthaŵiyo chidzapita patsogolo kukukwaniritsidwa kwake.
CHIMENE CHIFUNO CHOYAMBIRIRA CHA MULUNGU CHIMAVUMBULA
4 Chisonyezero cha chimene chiri mtsogolo kaamba ka opulumuka chisautso chachikulu chikupezeka mu mtundu wa chiyambi umene Yehova anapatsa banja la anthu mu Edene. Pokonza dziko lapansi kuti likhalidwe ndi anthu, Mlengi anatulutsa zomera zambiri, ndiponso nsomba, mbalame ndi nyama zapamtunda za mawonekedwe okongola osiyanasiyana. “Yehova Mulungu anabzala m’munda ku Edene cha kummaŵa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.” (Genesis 2:8) Koma Mulungu sanapange dziko lonse lapansi kukhala paradaiso ndiyeno kulisunga monga paki kaamba ka munthu. Mmalo mwake, Yehova anapatsa anthu aŵiri oyambirira chiyambi chabwino, anaika dalitso lake pa iwo naŵapatsa gawo lantchito. Pamaso pawo anawaikira ntchito imene ikanaŵakhozetsa kugwiritsira ntchito maluso awo mokwanira ndi kupeza chikhutiro m’zochita zawo. Izi zikadzaza miyoyo yawo ndi tanthauzo. Ha lawolo linali gawo lokondweretsa chotani nanga—kulera ana kuti asonyeze mikhalidwe yaumulungu, akumafutukulira Paradaiso ku malekezero a dziko lapansi ndi kumsamalira limodzi ndi zolengedwa zake zankhaninkhani! Ngati Adamu ndi Hava akanapitiriza kulemekeza ulamuliro wa Yehova, sakanafa. Akanasangalala ndi moyo wangwiro padziko lapansi kosatha.—Genesis 1:26-28; 2:16, 17.
5 Ndithudi, mikhalidwe padziko lapansi mwamsanga pambuyo pa chisautso chachikulu sidzafanana ndi ija ya mu Edene. Koma chifuno choyambirira cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi ndi anthu chidzakhala chosasintha. Paradaiso ayenera kukuta chiunda chonse, anthu adzakhala olisamalira, ndipo adzakhala ogwirizanitsidwa m’kulambira Mulungu wowona. Pamaso pawo padzakhala kuthekera kwa kukhala ndi moyo kosatha, akumasangalala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu.—Luka 23:42, 43; Chivumbulutso 21:3, 4; Aroma 8:20, 21.
6 Mosakaikira, pachiyambi mabwinja a dongosolo lakale adzafunikira kuchotsedwa. Zida zankhondo zimene zidzatsala zidzatembenuziridwa ku ntchito zamtendere. (Ezekieli 39:8-10; yerekezerani ndi Mika 4:3.) Mosakaikira dzinthu zimene zidzakhalabe m’munda zidzakololedwa kuti zichirikize opulumuka. Ndiyeno pamene mbewu zifesedwa ndipo zokolola zatsopano zitutidwa, lonjezolo lidzakwaniritsidwa: “Dziko lapansi labereka zipatso zake: Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.” (Salmo 67:6; yerekezerani ndi Deuteronomo 28:8.) Anthu adyera ndi ogaŵanitsa a dongosolo lakale pokhala atachoka, palibenso munthu amene adzakakamizika kukagona ndi njala usiku.—Salmo 72:16.
7 Limeneli lidzakhala dziko lopangika ndi anthu amene akuzindikira kufunika kwa kukhala ndi chitsogozo cha Yehova ndi dalitso. Ndipo zimenezi zidzaperekedwa m’njira imene ikusonyeza nzeru ya Mulungu ndi chikondi. Uyo amene Yehova wamuika kukhala Mfumu yatsopano yadziko lapansi ndiye Mwana wake, Yesu Kristu. Baibulo limavumbula kuti kupyolera mwa iye Mulungu analenga dziko lapansi ndi mitundu yonse yosiyanasiyana ya moyo pa ilo. (Akolose 1:15-17) Mwana wa Mulungu amazindikiradi chimene kupitirizabe kwa moyo padziko lapansi kumafunikira ndipo iye ali ndi chikondwerero chapadera cha zinthu zokhudzana ndi anthu.—Miyambo 8:30, 31.
8 Koposa zonse, Mwanayo amachirikiza mokhulupirika ulamuliro wa Yehova. Ponena za Yesu kunanenedweratu kuti: “Pa iye mzimu wa Yehova uyenera kukhala, mzimu wanzeru ndi wa kuzindikira, mzimu wa uphungu ndi wa mphamvu, mzimu wa kudziŵa ndi wa kuwopa Yehova; ndipo iye adzakondwera ndi kuwopa Yehova.” (Yesaya 11:2, 3, NW) Adzathandiza nzika zake zapadziko lapansi kupeza chikondwerero chofanana m’kugwirizanitsa miyoyo yawo ndi njira za Yehova. Pansi pa ufumu wake, opulumuka chisautso chachikulu adzabwezeretsedwa ku mtundu wa moyo umene Mulungu analinganizira anthu pamene makolo athu oyamba anapatsidwa Edene kukhala malo awo okhala.
CHIMENE UMINISITALA WA YESU UMAVUMBULA
9 Komabe, kuti tikhale ndi moyo wa mtundu umenewo, tifunikira kumasulidwa ku ziyambukiro zovutitsa zauchimo. Tonsefe talandira uchimo kuchokera kwa Adamu, amene anataya ungwiro wake pamene anasonyeza kunyozera kwakukulu ulamuliro wa Yehova. Zotulukapo za uchimo zikuwoneka m’njira zambiri. Zingachititse matenda, ulema, ndiponso chikhoterero cha kuganiza ndi kunena ndi kuchita zinthu mwa zolinga zolakwa. Potsirizira pake umabala imfa. (Aroma 5:12; 6:23) Mkati mwa uminisitala wake wapadziko lapansi, Yesu anachita zozizwitsa zambiri zimene zinasonyeza zimene adzachita kudzetsa chimasuko kwa iwo amene ali nzika za Ufumu wa Mulungu.
10 Koma pamene anthu ena aŵerenga zolembedwa zochititsa nthumanzi za Baibulo za zozizwitsa za Yesu, amakayikira. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti tikukhala m’dziko mmene kukayikira kwakhala kofala. Okayikirawo angalingalire kuti kuti zozizwitsa zikhulupiririke, asayansi lerolino ayenera kukhala okhoza kuzichitanso kapena kuzilongosola. Koma kodi nchifukwa ninji asayansi akupitirizabe kuwonongera yochuluka kwambiri ya nthaŵi ndi ndalama ku kufufuza? Chifukwa chakuti pali zambiri zimene sakuzindikira. Chimene chikuvuta kwenikweni m’lingaliro lathu ku uminisitala wa Yesu ndicho kusafunitsitsa kuvomereza kuloŵerera kwa Mulungu m’zochitika za anthu.
11 Kukhamu m’Yerusalemu mu 33 C.E., mtumwi Petro anatchula Yesu kukhala “mwamuna wosonyezedwa ndi Mulungu kwa inu poyera mwa ntchito zamphamvu ndi zozizwitsa ndi zizindikiro zimene Mulungu anachita mwa iye.” (Machitidwe 2:22, NW) Monga momwe panopo Petro anasonyezera, zozizwitsazo zinali, ntchito “zamphamvu,” osati zochita zimene anthu ena akanazichitanso kapena kulongosola, koma umboni wakuti mphamvu ya Mulungu inali kugwira ntchito mwa Yesu. Zinali “zizindikiro” zakuti iye analidi Mesiya, Mwana weniweni wa Mulungu. Zinalinso “zozizwa,” zochitika zimene zinasonya ku zinthu zosangalatsa.
12 Ŵerengani zolembedwa za Uthenga Wabwino m’Baibulo, ndipo pamene mukutero, kumbukirani kuti zozizwitsa zochitidwa ndi Yesu zimapereka kuwonedweratu kwa zimene iye adzachitira anthu amene adzakhala padziko lapansi mu Ufumu Waumesiya wa Mulungu. Imeneyo idzakhala nthaŵi pamene anthu okhala ndi nthenda zopundula zonga ngati khate adzayeretsedwa—monga momwedi Yesu anayeretsera amuna akhate khumi pamene anali paulendo wa ku Yerusalemu m’chaka cha 33 C.E. Anasonyeza kuti angathandize anthu otero ndi kuti iye amafunadi kutero. (Luka 17:11-19; Marko 1:40-42) Ochuluka akhala ogwidwa ndi nthenda ya manjenje. Kwa amenewanso, kuchiritsidwa kudzapezeka—monga momwe kunaliri kwa wamanjenje wokhala pa kama amene Yesu anachiritsa, akumagwirizanitsa kumeneku ndi kukhululukira machimo a munthuyo.—Marko 2:1-12.
13 Maso akhungu adzatsegudwa, makutu a gonthi adzadziulidwa ndipo iwo okhala ndi malema a kulankhula malirime awo adzamasuliridwa—monga momwedi Yesu anachitira zinthu zimenezi kwa anthu m’Galileya ndi m’Dekapoli m’zaka za zana loyamba. (Mateyu 9:27-30; Marko 7:31-37) Kwa anthu ambiri lerolino madokotala sangachiritse nthenda zawo. Umenewo unali nkhalidwe wa mkazi wina m’Kapernao amene anamvetsedwa “zowawa zambiri ndi asing’anga ambiri, nalipira zonse anali nazo osachira pang’ono ponse.” Koma Yesu anamchiritsa, ndipo adzachita zofananazo kwa ena ambiri onga iye. (Marko 5:25-29) Kensa, nthenda yamtima, malungo, likodzo—palibe idzakhala yovuta kwambiri, monga momwe anasonyezera pamene anachiritsa “nthenda iriyonse ndi zofooka zonse” mkati mwa uminisitala wake m’Galileya.—Mateyu 9:35.
14 Imeneyo idzakhalanso nthaŵi pamene padzakhala mpata wa akufa—osati iwo owonongedwa ndi Mulungu m’chisautso chachikulu, koma wa ena mabiliyoni ambirimbiri amene afa mkati mwa zaka mazana ambiri—kuti akhalenso ndi moyo, ndipo ndi ziyembekezo zimene ndi kale lonse zinali zosafikiridwa kwa iwo. Kodi zimenezo zidzatanthauzanji kwa opulumuka? Pafupi ndi mudzi wa Naini, Yesu anaphwetsa misozi yachisoni ya mayi wina wamasiye mwa kubwezeretsera kumoyo mwana wake mmodzi yekha. M’Kapernao anadzetsa chikondwerero chachikulu kwa makolo a buthu lina mwa kudzutsa mwana wawo wakufa. (Luka 7:11-16; Marko 5:35-42) Kodi mungafune kukhalapo pamene okondedwa anu abweranso kuchokera kwa akufa? Chimenecho chidzakhala chinthu chokondweretsa kwambiri cha opulumuka kuloŵa mu “dziko lapansi latsopano.”
15 Moyo panthaŵi imeneyo sudzakhala kubwerezedwa kwa mavuto ndi zisoni zimene mwakaŵirikaŵiri zikulemetsa anthu tsopano. Zimenezi zikusonyezedwa osati kokha ndi zozizwitsa za Yesu komanso ndi ziphunzitso zake, chifukwa chakuti iwo okha amene alidi ophunzira ake adzapulumuka kuloŵa mu “dziko lapansi latsopano.” (Yohane 3:36) Anaphunzitsa omtsatira kuika zinthu zauzimu patsogolo pa zinthu zakuthupi, kudalira pa Yehova, kuyang’ana kwa Iye kaamba ka chitsogozo ndi kuyamikira madalitso Ake. Mwa mawu ndi chitsanzo, Yesu anagogomezera kufunika kwa chikondi ndi kudzichepetsa, kudera nkhaŵa kwambiri ndi anthu ena ndi kudzipereka kwake mmalo mwawo. Kufikira tsopano, awo amene akukhala ophunzira a Kristu ndi amene akugwiritsiradi ntchito ziphunzitso zimenezi akupeza kale chitsitsimutso chachikulu cha miyoyo yawo ndipo iwo, nawonso, amabweretsa chitsitsimutso kwa ena. (Mateyu 11:28, 29; Yohane 13:34, 35) Uku ndiko kulaŵiratu chabe mtundu wa moyo umene udzakhala ndi iwo amene ali chikhalirebe amoyo pamene dziko lopanda chikondi liripoli lichoka. Ngati muchita mwanzeru tsopano, moyo umenewo ungakhale wanu.
[Mafunso]
1. Kodi nchifukwa ninji kudza kwa “tsiku la Yehova” sikudzasiya dziko lapansi liri bwinja? (Yesaya 45:18)
2. Kodi nchiyani chimene chimatipatsa chidaliro chakuti Yehova adzapulumutsa okhulupirika m’chisautso chachikulu?
3. Kodi nchifukwa ninji chiŵerengero chachikulu cha mitembo sichidzakhala upandu kuthanzi la opulumuka?
4. Kodi ndimtundu wanji wa chiyambi umene Yehova anapereka kwa anthu aŵiri oyamba, ndipo nchifukwa ninji chimenecho chiri chokondweretsa mwapadera kwa ife?
5. Chotero, kodi nziyembekezo zotani zimene zidzakhala pamaso pa opulumuka chisautso chachikulu?
6. (a) Kodi nchiyani chimene chidzachitika ku zida zonse zankhondo? (b) Kodi nchifukwa ninji palibe aliyense adzakakamizika kukhalanso ndi njala?
7. Kodi ndimotani mmene kusankha kwa Yehova Mfumu yatsopano yadziko lapansi kumasonyezera nzeru ya Mulungu ndi chikondi?
8. Kodi ndikulabadira kotani ku ulamuliro wa Yehova kumene Kristu adzathandiza nzika zake za padziko lapansi kukulitsa?
9. (a) Kodi nchiyani chimene chiri zina za ziyambukiro zoipa za uchimo wolandiridwa? (b) Kodi nchiyembekezo chotani chimene zozizwitsa za Yesu zimapereka?
10. Kodi nchifukwa ninji sikuli kosayenera kuti Yesu akanatha kuchita zozizwitsa zimene asayansi sangazichitenso?
11. Pa Machitidwe 2:22, kodi ndimawu otani amene agwiritsiridwa ntchito kulongosola zozizwitsa za Yesu, ndipo kodi ameneŵa amasonyezanji?
12. (a) Kodi nchifukwa ninji mumapeza zolembedwa zonena za kuyeretsedwa kwa anthu amene anali akhate kukhala zolimbikitsa? (b) Kodi nchiyani chimene makamaka chinali chapadera ponena za kuchiritsa kwa Yesu wamanjenje?
13. Simbani chimodzi cha zozizwitsa za Yesu chimene chimapereka chiyembekezo kwa (a) akhungu, (b) ogontha kapena osalankhula, (c) anthu amene apatsidwa mankhwala ndi madokotala ambiri popanda kupeza mpumulo. (d) Kodi mukudziŵa bwanji kuti Yesu adzakhala wokhoza kuchiritsa mitundu yonse ya nthenda ndi zofooka?
14. Kodi ndimotani mmene zolembedwa za kuukitsa kwa Yesu akufa zimasonyezera chimene chiukiriro chidzatanthauza kwa opulumuka?
15. (a) Kodi ndimotani mmene ziphunzitso za Yesu zimasonyezera mtundu wa anthu amene adzakhala ndi moyo padziko lapansi panthaŵiyo? (b) Kodi ndim’njira yotani imene tingakhalire ndi kulaŵiratu mtundu umenewo wa moyo tsopano?
[Bokosi/Chithunzi patsamba 33]
CHIFUNO CHOYAMBIRIRA CHA MULUNGU KWA ANTHU
Kudzaza dziko lapansi ndi anthu osonyeza mikhalidwe ya Mulungu
Kufutukula Paradaiso padziko lonse lapansi ndi kulisamalira ndi zinyama zake
Kusangalala ndi moyo padziko lapansi kosatha