Zitsanzo Zolosera ndi Malongosoledwe za Anthu Okhala ndi Moyo Tsopano Amene Adzalandira Gawo la Dziko Lapansi la Ufumu wa Mulungu
Ophiphiritsiridwa ndi magulu kapena anthu otsatiraŵa:
(1) Ana a Nowa ndi apongozi ake (Genesis 6-9).
(2) Loti ndi ana ake aakazi (Genesis 19).
(3) Abale a Yosefe khumi mwa amayi ena olapawo (Genesis 37, 42-45).
(4) Aigupto Okanthidwa ndi njala amene anadzigulitsa kwa Yosefe (Genesis 41; 47:13-26).
(5) Gulu losanganikirana limene linachoka mu Igupto limodzi ndi Israyeli (Eksodo 12:38).
(6) Mafuko khumi ndi aŵiri a osakhala a Alevi a Israyeli pa Tsiku Lachitetezero (Levitiko 16; Mateyu 19:28).
(7) Alendo ogonera a Israyeli (Levitiko 19:34).
(8) Hobabu mulamu wake wa Mose (Numeri 10:29-32).
(9) Rahabi wa ku Yeriko (Yoswa 2, 6).
(10) Agibeoni amene anafunafuna mtendere ndi Israyeli (Yoswa 9, 10).
(11) Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni (Oweruza 4, 5).
(12) Jonatani mwana wa Mfumu Sauli (1 Samueli 18; 23:16, 17).
(13) Alendo amene anamenya nkhondo limodzi ndi Davide (2 Samueli 15:18-22).
(14) Mfumu yaikazi ya ku Seba (1 Mafumu 10).
(15) Namani wochiritsidwa khate (2 Mafumu 5).
(16) Yehonadabu mwana wa Rekabu (2 Mafumu 10:15-28).
(17) Alendo amene anapemphera atayang’ana kukachisi wa Yehova (2 Mbiri 6:32, 33).
(18) Anetini ndi ana a atumiki osakhala Aisrayeli a Solomo (Ezara 2, 8).
(19) Arekabu (Yeremiya 35).
(20) Ebedi-meleki Mwitiyopiya (Yeremiya 38; 39:16-18).
(21) Anineve olapa (Yona 3).
Ndiponso ofotokozedwa molosera motere:
(1) Mabanja a dziko amene akudzidalitsa mwa njira ya Abrahamu kupyolera mwa mbewu yake. (Genesis 12:3; 22:18).
(2) Mitundu imene ikukondwera ndi anthu a Yehova (Deuteronomo 32:43).
(3) Olungama, oyembekezera Yehova (Salmo 37:9, 29).
(4) Anamwali anzake a mkwatibwi (Salmo 45:14).
(5) Owongoka ndi angwiro (Miyambo 2:21).
(6) Mitundu yophunzitsidwa panyumba ya Yehova ndi kuyenda m’mabande ake (Yesaya 2:2-4).
(7) Mitundu imene imatembenukira nifufuza ku Chizindikiro (Yesaya 11:10).
(8) Mitundu imene ikutuluka mu mdima (Yesaya 49:6, 9, 10).
(9) Mtundu umene sunadziŵike ndi kalelonse (Yesaya 55:5).
(10) Alendo otumikira Yehova nakonda dzina lake (Yesaya 56:6).
(11) “Unyinji wa nyanja,” “chuma cha amitundu,” awo akudza ‘nauluka monga mtambo wankhunda’ (Yesaya 60:5, 6, 8).
(12) Abusa amene amaŵeta magulu ankhosa a Israyeli, alendo amene ali alimi ndi okonza minda yampesa ake (Yesaya 61:5).
(13) Olembedwa chizindikiro pamphumi ndi mwamuna wokhala ndi cholembera cha inki cha mlembi (Ezekieli 9).
(14) Anthu amene amaitana dzina la Yehova ndi kupulumuka patsiku lake lochititsa mantha (Yoweli 2:32).
(15) Zinthu zofunika za mitundu yonse (Hagai 2:7).
(16) Mitundu imene “imaphatikizidwa kwa Yehova” (Zekariya 2:11).
(17) ‘Amuna khumi ogwira mkawo wa Myuda’ (Zekariya 8:23).
(18) Mitundu imene Mfumu imalankhulako mtendere (Zekariya 9:10).
(19) “Nkhosa” zimene zimachitira zabwino abale a Mfumu (Mateyu 25:31-46).
(20) Mwana woloŵerera wolapa (Luka 15:11-32).
(21) “Nkhosa zina” zimene zimamvera mawu a Mbusa Wabwino (Yohane 10:16).
(22) Anthu amene amasonyeza chikhulupiriro mwa Kristu ndi “amene sadzafa konse” (Yohane 11:26).
(23) Chilengedwe chimene chidzamasulidwa kuchokera ku ukapolo wachivundi kukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu (Aroma 8:20, 21).
(24) Awo a dziko amene apeza moyo wosatha chifukwa chakuti amasonyeza chikhulupiriro mwa Mwana wa Mulungu (1 Yohane 2:2; Yohane 3:16, 36).
(25) “Khamu lalikulu” limene limatumikira m’kachisi wa Yehova usana ndi usiku (Chivumbulutso 7:9-17).
(26) Aliyense wakumwa madzi a moyo ndi amene iyemwini akunena kwa ena kuti, “Idzani!” (Chivumbulutso 22:17).
Apamwambawa ndiwo okha amene afotokozedwa kapena kutchulidwa m’bukhu lino.