Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 323-tsamba 327
  • Mzimu wa Dziko

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mzimu wa Dziko
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Nkhani Yofanana
  • Landirani Mzimu wa Mulungu Osati wa Dziko
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Kodi Mukukaniza Mzimu wa Dziko?
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Olamulira Okhala m’Malo a Mizimu
    Nsanja ya Olonda—1995
  • N’zotheka Kugonjetsa Satana
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 323-tsamba 327

Mzimu wa Dziko

Tanthauzo: Mphamvu yosonkhezera imene imayambukira anthu amene saali atumiki a Yehova Mulungu, kuchititsa anthu amenewo kunena ndi kuchita zinthu mogwirizana ndi mchitidwe wapadera. Ngakhale kuli kwakuti anthu amachita mogwirizana ndi zikhumbo zawo, osonyeza mzimu wa dziko amapereka umboni wa mikhalidwe ina yaikulu, njira zochitira zinthu, ndi zolinga m’moyo zimene ziri zoŵanda m’dongosolo liripoli la zinthu limene Satana ali wolamulira ndi mulungu wake.

Kodi nchifukwa ninji kuipitsidwa ndi mzimu wa dziko kuli nkhani yodetsa nkhaŵa kwambiri?

1 Yoh. 5:19: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (Satana watulutsa mzimu umene umalamulira malingaliro ndi zochita za anthu amene saali atumiki ovomerezedwa a Yehova. Ndiwo mzimu wadyera ndi kunyada umene uli woluluzika kwambiri kotero kuti uli wofanana ndi mpweya umene anthu amapuma. Tifunikira kusonyeza chisamaliro chachikulu kusagonjera kumphamvu ya Satana mwakulola mzimu umenewo kuumba miyoyo yathu.)

Chiv. 12:9: “Chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.” (Kuyambira pamene zimenezi zinachitika pambuyo pakubadwa kwa Ufumu mu 1914, chisonkhezero cha Satana ndi ziŵanda zake chakula kwambiri pakati pa anthu. Mzimu wake wasonkhezera anthu kuchita dyera lowonjezereka ndi chiwawa. Makamaka kwakukulukulu ofunafuna kutumikira Yehova amapanikizidwa kwambiri kuti akhale mbali ya dziko, kuchita zimene ena amachita, ndi kuleka kulambira kowona.)

Kodi ndiiti imene iri ina ya mikhalidwe ya mzimu wa dziko imene tiyenera kukhala ochenjera nayo?

1 Akor. 2:12: “Koma sitinalandira ife mzimu wa dziko lapansi, koma mzimu wa kwa Mulungu, kuti tikadziŵe zimene zipatsidwa kwa ife ndi Mulungu kwaufulu.” (Ngati mzimu wa dziko uzika mizu m’maganizo ndi zikhumbo za munthu, zotulukapo zake zimawonekera mwamsanga m’zochita zimene zimasonyeza mzimu umenewo. Chotero, kuwonjoka ku mzimu wa dziko kumafunikiritsa osati kokha kupeŵa ntchito zosakhala Zachikristu ndi kuchita mopambanitsa komanso kufika magwero a nkhaniyo mwa kukulitsa makhalidwe amene amasonyeza mzimu wa Mulungu ndi kukonda kowona njira zake. Muyenera kukumbukira zimenezi pamene mupenda zisonyezero zotsatirapozi za mzimu wadziko.)

Kuchita chimene munthuyo afuna, popanda kuŵerengera chifuniro cha Mulungu

Satana anasonkhezera Hava kudzisankhira chabwino ndi choipa. (Gen. 3:3-5; mosiyanitsa wonani Miyambo 3:5, 6.) Ambiri amene amalondola njira ya Hava samadziŵa chimene chiri chifuniro cha Mulungu kwa anthu, ndiponso sali okondwerera kufuna kudziŵa. Iwo ‘amangochita zokhumba zawo,’ chabe monga momwe amanenera. Awo amene amadziŵa malamulo a Mulungu nayesa kuchita mogwirizana nawo amafunikira kukhala osamala kuti mzimu wadziko sukuwachititsa kunyalanyaza dala uphungu wa Mawu a Mulungu m’zimene angawone kukhala “zinthu zazing’ono.”—Luka 16:10; wonaninso “Kudziimira.”

Kulabadira mikhalidwe chifukwa cha kunyada

Anali Satana amene anayamba kulola kudziŵerengera kopambanitsa kuipitsa mtima wake. (Yerekezerani ndi Ezekieli 28:17; Miyambo 16:5.) Kunyada ndiko mphamvu yogaŵanitsa m’dziko limene iye amalamulira, kuchititsa anthu kudzilingalira kukhala abwino kwambiri kuposa a mafuko ena, mitundu, timagulu tazinenero, ndi mkhalidwe wa zachuma. Ngakhale otumikira Mulungu angafunikire kuchotsa mbali zotsala za malingaliro otero. Iwo afunikiranso kukhala osamala kotero kuti kunyada sikukuwachititsa kupanga nkhani zazikulu kuchokera ku nkhani zazing’ono, kapena kukhala chopinga kukuvomereza kwawo zolakwa za iwo eni ndi kuvomereza uphungu ndipo chotero kupindula ndi chithandizo chachikondi chachikulu chimene Yehova amagaŵira kupyolera mwa gulu lake.—Aroma 12:3; 1 Pet. 5:5.

Kusonyeza mkhalidwe wopandukira ulamuliro

Chipanduko chinayamba ndi Satana, amene dzina lake limatanthauza “Wotsutsa.” Mwakuchitira kwake mwano Yehova, Nimrodi, amene dzina lake lingatanthauze “Tiyeni Tipanduke,” anasonyeza kuti anali mwana wa Satana. Kupeŵa mzimu umenewo kudzatetezera anthu owopa Mulungu kusakhala amwano kwa olamulira a dziko (Aroma 13:1); kudzathandiza achichepere kugonjera ulamuliro woperekedwa ndi Mulungu wamakolo awo (Akol. 3:20); kudzakhala chitetezo chakusamverera chisoni ampatuko, amene amanyozera anthu amene Yehova waikizira thayo m’gulu lake lowoneka.—Yuda 11; Aheb. 13:17.

Kugonjera mosavuta ku zikhumbo za thupi lakugwa

Chisonkhezero cha zimenezi chingawonedwe ndi kumvedwa kulikonse. Pali kufunikira kosalekeza kwa kukhala wochenjera nacho. (1 Yoh. 2:16; Aef. 4:17, 19; Agal. 5:19-21) Maganizo ndi zikumbo zimene zingatsogolere ku maumboni ake okulira kwambiri zingawonekere m’nkhani ya munthuyo, njerengo zake, nyimbo zimene amamvetsera, mtundu wa dansi imene amavina, kapena m’kuwonerera kwake maprogramu amene amasonyeza chisembwere. Mbali imeneyi ya mzimu wa dziko imadzisonyeza m’kugwiritsira ntchito molakwa mankhwala ogodomalitsa, uchidakwa, chigololo, dama la chigololo, ndi kugonana kwa anthu a ziŵalo zofanana. Umawonekeranso pamene munthuyo asudzula mnzake wa muukwati popanda chifukwa chamalemba, koma mwinamwake amatero mwalamulo, nakwatira wina.—Mal. 2:16.

Kulola moyo wa munthuwe kulamulidwa ndi chikhumbo cha kukhala ndi zimene uwona

Chinali chikhumbo chotero chimene Satana anakulitsa mwa Hava, kumsonkhezera kuchita chinthu chimene chinawononga unansi wake ndi Mulungu. (Gen. 3:6; 1 Yoh. 2:16) Yesu anakana mwamphamvu chiyeso chotero. (Mat. 4:8-10) Awo ofuna kukondweretsa Yehova afunikira kukhala maso kotero kuti sakulola dziko la zamalonda kukulitsa mzimu wotero mwa iwo. Chisoni chachikulu ndi chivulazo chauzimu zimakhala zotulukapo kwa ogwidwa nacho.—Mat. 13:22; 1 Tim. 6:7-10.

Kuwonetsera chuma cha munthuwe ndi zoyerekezeredwa kukhala zipambano

Chizoloŵezi chimenechinso, “chichokera kudziko lapansi” ndipo chifunikira kulekedwa ndi awo amene akhala atumiki a Mulungu. (1 Yoh. 2:16) Chiri chozikidwa m’kunyada, ndipo mmalo mwakulimbikitsa ena mwauzimu chimaika zikhumbo zakuthupi ndi malingaliro achipambano chaudziko pamaso pawo.—Aroma 15:2.

Kugonjera kumalingaliro a kulankhula konyansa ndi achiwawa a munthuwe

Zimenezi ziri “ntchito za thupi” zimene anthu ambiri ayenera kulimbana nazo. Mwachikhulupiriro chowona ndi chithandizo cha mzimu wa Mulungu iwo angathe kugonjetsa dziko mmalo mwa kulola mzimu wake kuwalamulira.—Agal. 5:19, 20, 22, 23; Aef. 4:31; 1 Akor. 13:4-8; 1 Yoh. 5:4.

Kuika ziyembekezo za munthuwe ndi mantha a zimene anthu ali okhoza kuchita

Munthu wakuthupi amalingalira zimene akhoza kuwona ndi kukhudza kukhaladi zofunika. Ziyembekezo zake ndi mantha zimasumikidwa pamalonjezo ndi ziwopsezo za anthu ena. Amayang’ana kwa olamulira aumunthu kaamba ka chithandizo ndipo amathedwa nzeru pamene iwo alephera. (Sal. 146:3, 4; Yes. 8:12, 13) Kwa iye, umenewu ndiwo moyo wokha umene ulipo. Zithupsyo za imfa zimaloŵetsa mu ukapolo mosavuta. (Mosiyana, wonani Mateyu 10:28; Ahebri 2:14, 15.) Koma mphamvu yatsopano yosonkhezera maganizo a anthu amene amafikira pa kudziŵa Yehova, amene amadzaza maganizo awo ndi mitima ndi malonjezo ake ndi amene amaphunzira kutembenukira kwa iye kaamba ka chithandizo m’nthaŵi iriyonse ya kusoŵa.—Aef. 4:23, 24; Sal. 46:1; 68:19.

Kupereka kwa anthu ndi zinthu ulemu wa kulambira umene uli wa Mulungu

“Mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” Satana Mdyerekezi, amalimbikitsa zizoloŵezi za mitundu yonse zimene zimasocheza chikhoterero cha munthu choperekedwa ndi Mulungu cha kulambira. (2 Akor. 4:4) Olamulira ena achitiridwa ngati milungu. (Mac. 12:21-23) Mamiliyoni ambiri amagwadira mafano. Mamiliyoni ena ambiri amalambira akatswiri ovina ndi akatswiri odziŵa kuthamanga. Kaŵirikaŵiri mapwando amapereka ulemu wosayenerera kwa anthu alionse paokha. Mzimu umenewo ngwofalikira kwambiri kotero kuti awo amene amakondadi Yehova ndi amene amafuna kumpatsa kudzipereka kotheratu afunikira kukhala maso kuchisonkhezero chake tsiku ndi tsiku.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena