Mutu 45
Wophunzira Wosayembekezeredwa
NDICHOCHITITSA mantha chotani nanga chimene Yesu akuwona pamene afika pagombe! Amuna aŵiri owopsa kwambiri akutuluka kuchokera munsitu wapafupiwo namthamangira. Iwo ngogwidwa ndi ziŵanda. Popeza kuti mwinamwake mmodzi wa iwo ali wachiŵawa kwambiri koposa winayo ndipo wavutika nthaŵi yaitali kwambiri atagwidwa ndi chiŵanda, akusumika maganizo pa iye.
Kwanthaŵi yayitali munthu womvetsa chisoni ameneyu wakhala akukhala maliseche pakati pa manda. Usana ndi usiku, amafuula mosalekeza ndi kudzitematema ndi miyala. Iye ngwachiwawa kwambiri kotero kuti palibe munthu amene ali wolimba mtima kudzera njira imeneyo yamsewu. Zoyesayesa zapangidwa zakummanga, koma iye amadula maunyolo nadula matangadza pamapazi ake. Palibe munthu amene ali ndi nyonga ya kumgonjetsa.
Pamene munthuyo akufika kwa Yesu nagwada pamapazi ake, ziŵanda zomlamulira zikumchititsa kufuula kuti: “Ndiri ndi chiyani ine ndi inu, Yesu, Mwana wa Mulungu Wamkulukulu? Ndikulumbirirani pa Mulungu, musandizunze.”
“Tuluka iwe, mzimu wonyansa, kwa munthuyu,” Yesu akupitirizabe kunena. Komano Yesu akufunsa kuti: “Dzina lako ndani?”
“Dzina langa ndine Legio; chifukwa tiri ambiri,” ndilo yankho. Ziŵandazo zimasangalala kuwona kuvutika kwa awo amene ali ogwidwa nazo, mwachiwonekere zikusangalalira kuwasonkhanira ali mumkhalidwe wamantha. Koma zitayang’anizana ndi Yesu, zikupempha kuti zisaponyedwe kuphompho. Kachiŵirinso tikuwona kuti Yesu ali ndi mphamvu yaikulu; anali wokhoza kugonjetsa ngakhale ziŵanda zowopsa. Izi zikuvumbulanso kuti ziŵanda zikudziŵa kuti kuikidwa kwawo kuphompho limodzi ndi mtsogoleri wawo, Satana Mdyerekezi, ndicho chiweruzo chawo chotsirizira chochokera kwa Mulungu.
Msambi wapafupifupi nkhumba 2,000 zikudya chapafupi ndi paphiri. Chotero ziŵandazo zikuti: “Titumizeni ife m’nkhumbazo, kuti tiloŵe mu izo.” Mwachiwonekere ziŵandazo zimapeza chisangalalo chachilendo, chauchinyama kuchokera m’kuukira matupi azolengedwa zathupi. Pamene Yesu alola kuti ziloŵe m’nkhumba, 2,000 zonsezo zikuthamanga kudumpha therezi ndi kumira m’nyanja.
Pamene osamalira nkhumbazo awona izi, iwo mofulumira akukasimba mbiriyo m’mizinda ndi kumilaga. Pamenepo, anthu akutuluka kudzawona zimene zinachitika. Pamene iwo akufika, akuwona munthu amene ziŵanda zinatulukamo. Eya, iye wavala ndipo maganizo ake ngolama, ndipo wakhala pamapazi a Yesu!
Mboni zowona ndi maso zikusimba mmene munthuyo anachiritsidwira. Iwo akusimbiranso anthu imfa yachiwawa ya nkhumbazo. Pamene anthu amva za chochitikachi, akugwidwa ndi mantha aakulu, ndipo akupempha mochonderera kwa Yesu kuti achoke m’chigawo chawo. Chotero iye akuvomereza nakwera ngalaŵa. Amene poyamba anali wogwidwa ndi ziŵandayo akupempha Yesu kuti amlole kutsagana naye. Koma Yesu akumuuza kuti: “Muka kwanu kwa abale ako, nuwauze zinthu zazikulu anakuchitira Ambuye, ndi kuti anakuchitira chifundo.”
Kaŵirikaŵiri Yesu akuuza awo amene wawachiritsa kusauza aliyense, popeza kuti safuna kuti anthu anene zinthu zozikidwa pamphekesera. Koma chochitika ichi chokha chiri choyenerera chifukwa chakuti amene kale anali wogwidwa ndi ziŵandayo adzakhala akuchitira umboni pakati pa anthu amene Yesu tsopano mwinamwake sadzakhala ndi mpata wa kuwafikira. Ndiponso, kukhalapo kwa munthuyo kukupereka umboni wonena za mphamvu ya Yesu ya kuchita zabwino, kutsutsa lipoti lirilonse losayenerera limene lingafalitsidwe ponena za kutayika kwa nkhumba.
Mogwirizana ndi malangizo a Yesu, amene poyamba anali wogwidwa ndi ziŵanda akuchoka. Iye akuyamba kulengeza mu Dekapoli yense zinthu zonse zimene Yesu anamchitira, ndipo anthu akuzizwa kwambiri. Mateyu 8:28-34; Marko 5:1-20; Luka 8:26-39; Chivumbulutso 20:1-3.
▪ Kodi nchifukwa ninji, mwinamwake chisamaliro chasumikidwa pa munthu mmodzi wogwidwa ndi chiŵanda pamene kuli kwakuti pali aŵiri?
▪ Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti ziŵanda zimadziŵa za kuikidwa m’phompho kumene kulinkudza?
▪ Mwachiwonekere, kodi nchifukwa ninji, ziŵanda zimafuna kuti zigwire anthu ndi zinyama?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yesu akuchita mosiyana ndi amene kale anali wogwidwa ndi ziŵanda, akumamuuza kukauza ena ponena za zimene Iye anamchitira?