Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 46
  • Anakhudza Chovala Chake

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Anakhudza Chovala Chake
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Anakhudza Chovala Chake
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Anachira Atagwira Malaya a Yesu
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Yesu Aukitsa Akufa
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Tingauke kwa Akufa!
    Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 46

Mutu 46

Anakhudza Chovala Chake

MBIRI ya kubwerera kwa Yesu kuchokera ku Dekapoli ikufika ku Kapernao, ndipo khamu lalikulu likusonkhana pafupi ndi nyanja kudzamchingamira. Mosakayikira iwo amva kuti iye anatontholetsa namondwe nachiritsa amuna ogwidwa ndi ziŵanda. Tsopano, pamene akufika pagombe, iwo akusonkhana momzungulira, achidwi ndi oyembekezera.

Mmodzi wa amene ali ndi chidwi kufuna kuwona Yesu ndiye Yairo, mtsogoleri wa sunagoge. Iye akugwera pamapazi a Yesu nampempha mobwerezabwereza kuti: “Kamwana kanga kabuthu kalimkutsirizika; ndikupemphani inu mufikeko, muike manja anu pa iko, kuti apulumuke, ndi kukhala ndi moyo.” Popeza kuti mwanayo ndiye mmodzi yekha ndipo ngwazaka 12 zokha zakubadwa, iye mwapadera ngwamtengo wapatali kwambiri kwa Yairo.

Yesu akulabadira, ndipo moperekezedwa ndi khamulo, akumka kunyumba ya Yairo. Tingathe kuyerekezera chidwi cha anthu pamene ayembekezera chozizwitsa china. Koma chisamaliro cha mkazi wina m’khamulo chikusumikidwa pavuto lake lalikulu.

Kwazaka 12, mkazi ameneyu wavutika ndi kuchucha mwazi. Iye wapita kwa asing’anga osiyanasiyana, akumawononga ndalama zake zonse kufunira mankhwala. Koma sanapeze thandizo; mmalomwake, vuto lake lafikira kukhala loipirapo.

Monga momwe mwinamwake mungazindikirire, kuwonjezera pakumfoketsa kwambiri, nthenda yake irinso yochititsa manyazi ndi yoluluza. Kaŵirikaŵiri munthuwe sumalankhula poyera ponena za nthenda yotere. Ndiponso, pansi pa Chilamulo cha Mose kuchucha mwazi kumapangitsa mkazi kudetsedwa, ndipo aliyense womkhudza kapena zovala zake zokhathamira ndi mwazi amafunikira kusamba ndi kukhala wodetsedwa kufikira madzulo.

Mkaziyo wamva za zozizwitsa za Yesu ndipo tsopano wampeza. Polingalira za kudetsedwa kwake, iye akuloŵerera m’khamulo mwakachetechete kwambiri monga momwe kungathekere, akumati kwa iye mwini: “Ngati ndikakhudza ngakhale zovala zake ndidzapulumutsidwa.” Pamene iye atero, nthaŵi yomweyo akumva kuti kuchucha kwake mwazi kwalekeka!

“Wandikhudza ine ndani?” Mmene mawu a Yesu amenewo ayenera kukhala atamchititsira mantha nanga! Kodi iye wadziŵa bwanji? ‘Mphunzitsi,’ Petro akutsutsa, ‘khamuli likuzingani, ndipo likukukankhanikankhani, ndipo munena bwanji kuti, “Wandikhudza ine ndani?” ’

Ataunguzaunguza kufuna mkaziyo, Yesu akufotokoza kuti: “Wina wandikhudza ine pakuti ndazindikira ine kuti mphamvu yatuluka mwa ine.” Ndithudi, sikuli kukhudza wamba, chifukwa chakuti kuchiritsidwa kochitika kukutulutsa mphamvu mwa Yesu.

Powona kuti iye wawonekera, mkaziyo akufika nagwera pamapazi a Yesu, wamantha ndi kunthunthumira. Pamaso pa anthu onse, iye akusimba nkhani yonseyo ponena za matenda ake ndi mmene tsopano lomweli wachiritsidwira.

Mosonkhezeredwa ndi kuulula kwake konseko, Yesu mokoma mtima akumtonthoza kuti: “Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako.” Mmene kuliri kwabwino nanga kudziŵa kuti Uyo amene Mulungu wamsankha kulamulira dziko lapansi ali munthu wokoma mtima, ndi wachifundo chotero, amene ponse paŵiri amasamalira anthu ndipo ali ndi mphamvu yakuwathandiza! Mateyu 9:18-22; Marko 5:21-34; Luka 8:40-48; Levitiko 15:25-27.

▪ Kodi Yairo ndani, ndipo nchifukwa ninji wadza kwa Yesu?

▪ Kodi ndivuto lanji limene mkazi wina ali nalo, ndipo kodi nchifukwa ninji kudza kwa Yesu kuti apeze chithandizo kuli komvuta kwambiri?

▪ Kodi mkaziyo akuchiritsidwa motani, ndipo kodi ndimotani mmene Yesu akumtonthozera?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena