Mutu 48
Kuchoka Panyumba ya Yairo ndi Kukachezanso ku Nazarete
TSIKULO lakhala lotanganitsidwa kwa Yesu—ulendo wa panyanja kuchokera ku Dekapoli, kuchiritsa mkazi wochucha mwazi, ndi kuukitsa mwana wamkazi wa Yairo. Komatu tsikulo silinathe. Mwachiwonekere pamene Yesu achoka panyumba ya Yairo, amuna akhungu aŵiri akutsatira m’mbuyo, akumafuula kuti: “Mutichitire ife chifundo, mwana wa Davide.”
Mwakutchula Yesu kuti “mwana wa Davide,” amuna ameneŵa panopa akusonyeza chikhulupiliro chakuti Yesu ndiye woloŵa nyumba pampando wachifumu wa Davide, chotero iye ndiye Mesiya wolonjezedwayo. Komabe, Yesu, mwachiwonekere akunyalanyaza mfuu zawo zopempha chithandizo, mwinamwake kuti ayese khama lawo. Koma amunawo sakuleka. Iwo akulondola Yesu kumene akukhala, ndipo pamene iye aloŵa m’nyumba, iwo akumlondola m’nyumbamo.
Mmenemo Yesu akufunsa kuti: “Mukhulupilira kodi kuti ndikhoza kuchita ichi?”
“Inde, Ambuye,” iwo akuyankha mwachidaliro.
Chotero, pokhudza maso awo, Yesu akuti: “Chichitidwe kwa inu monga chikhulupiliro chanu.” Mwadzidzidzi iwo akutha kuwona! Pamenepo Yesu akuwauzitsa kuti: “Yang’anirani, asadziŵe munthu aliyense.” Koma podzazidwa ndi chikondwerero, iwo akunyalanyaza lamulo la Yesu nanena za iye m’chigawo chonsecho.
Pamene amuna ameneŵa akuchoka, anthu akubweretsa munthu wina wogwidwa ndi chiŵanda amene chiŵanda chamletsa kulankhula. Yesu akutulutsa chiŵandacho, ndipo pomwepo munthuyo akuyamba kulankhula. Makamuwo akuzizwa ndi zozizwitsa zimenezi, akumati: “Kale lonse sichinawonekere chomwecho mwa Israyeli.”
Nawonso Afarisi ali pompo. Iwo sangathe kulandula zozizwitsazo, koma m’kusakhulupilira kwawo koipako iwo akubwerezanso chinenezo chawo ponena za magwero a ntchito zamphamvu za Yesu, akumati: “Atulutsa ziŵanda ndi mphamvu zake za mfumu ya ziŵanda.”
Mwamsanga pambuyo pa zochitika zimenezi, Yesu akubwerera kutauni yakwawo ya Nazarete, panthaŵi ino limodzi ndi ophunzira ake. Pafupifupi chaka chimodzi chapitacho, iye anali atafika kusunagoge naphunzitsa kumeneko. Ngakhale kuti anthu poyambapo anazizwa ndi mawu ake okondweretsa, iwo pambuyo pake anaipidwa ndi kuphunzitsa kwake nayesayesa kumupha. Tsopano, mokoma mtima, Yesu akupanga kuyesayesa kwina kuthandiza amene kale anali anansi ake.
Pamene kuli kwakuti malo ena anthu akufika muunyinji wawo kwa Yesu, mwachiwonekere kunoku sakutero. Chotero, pa Sabata, iye akupita kusunagoge kukaphunzitsa. Ochuluka a amene akumumvetsera akuzizwa. “Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi zamphamvu izi?” iwo akufunsa. “Kodi uyu simwana wa mmisiri wamitengo? Kodi dzina la amake si Mariya? ndipo abale ake si Yakobo ndi Yosefe ndi Simoni ndi Yuda? Ndipo alongo ake sali ndife onsewa? Ndipo iyeyo adazitenga zinthu zonsezi kuti?”
‘Yesu ali kokha munthu wamba wa mommuno mofanana nafe,’ iwo akulingalira motero. ‘Tinamuwona akukula, ndipo timadziŵa banja lake. Kodi iye angakhale Mesiya motani?’ Chotero mosasamala kanthu za umboni wonsewo—nzeru yake yaikulu ndi zozizwitsa—iwo akumkana. Chifukwa cha kuzoloŵerana naye kwawo kwambiri, ngakhale abale a iye mwini akukhumudwa naye, zikumachititsa Yesu kunena kuti: “Mneneri sakhala wopanda ulemu, koma m’dziko la kwawo ndimo, ndi pakati pa abale ake ndi am’nyumba yake.”
Ndithudi, Yesu akudabwa chifukwa cha kupanda chikhulupiliro kwawo. Chotero iye sakuchita chozizwitsa chirichonse kumeneko kusiyapo kuika manja pa odwala oŵerengeka ndi kuwachiritsa. Mateyu 9:27-34; 13:54-58; Marko 6:1-6; Yesaya 9:7.
▪ Mwa kutchula Yesu kuti “mwana wa Davide,” kodi amuna akhunguwo akusonyeza kuti akukhulupilira chiyani?
▪ Kodi Afarisi akhala akufotokozanji ponena za zozizwitsa za Yesu?
▪ Kodi nchifukwa ninji kuli kukoma mtima kwa Yesu kuti abwerere kukathandiza anthu a ku Nazarete?
▪ Kodi ndikulandiridwa kotani kumene Yesu akukhala nako m’Nazarete, ndipo chifukwa ninji?