Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 49
  • Ulendo Wina Wokalalikira ku Galileya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ulendo Wina Wokalalikira ku Galileya
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Ulendo Wina Wolalikira wa ku Galileya
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Analalikira ku Galileya Komanso Anaphunzitsa Atumwi
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • “Mbiri Yabwino Iyenera Kulalikidwa Choyamba”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Sangalalani Ndi Ntchito Yotuta!
    Nsanja ya Olonda—2001
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 49

Mutu 49

Ulendo Wina Wokalalikira ku Galileya

PAFUPIFUPI zaka ziŵiri za kulalikira kwakukulu zitapita, kodi tsopano Yesu adzayamba kulefuka ndi kuchita mwapang’onopang’ono? Kutalitali, iye akufutukula ntchito yake yolalikira mwa kulinganiza ulendo winanso, wachitatu wopita ku Galileya. Iye akuyenda kumizinda yonse ndi midzi m’gawolo, akumaphunzitsa m’masunagoge ndi kulalikira mbiri yabwino Yaufumu. Zimene akuwona paulendo uno zikumkhutiritsa koposa ndi kalelonse ponena za kufunika kwa kukulitsa ntchito yolalikira.

Kulikonse kumene Yesu akupita, akuwona makamu ofunikira kuchiritsidwa mwauzimu ndi chitonthozo. Iwo ali ofanana ndi nkhosa zopanda mbusa, zokambululudwa ndi zomwazidwa, ndipo iye akuwachitira chisoni. Akuuza ophunzira ake kuti: “Zotuta zichulukadi, koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake, pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.”

Yesu akulinganiza za ntchitoyo. Iye akutuma atumwi 12, amene anali atawasankha pafupifupi chaka chimodzi poyambirirapo. Iye akuwagaŵa iwo aŵiriaŵiri, napanga timagulu tisanu ndi kamodzi ta olalikira, ndipo akuwapatsa malangizo. Iye akufotokoza kuti: “Musapite kunjira ya kwa anthu akunja, ndipo m’mudzi wa Asamariya musamaloŵamo; koma makamaka mupite kunkhosa zosokera za banja la Israyeli. Ndipo pamene mulikupita lalikani kuti Ufumu wakumwamba wayandikira.”

Ufumu umenewu umene iwo akawulalikira ndiwo umene Yesu anawaphunzitsa kuupempherera m’pemphero lachitsanzo. Ufumuwo wayandikira m’lingaliro lakuti Mfumu yosankhidwa ya Mulungu, Yesu Kristu, iripo. Kukhazikitsa ziyeneretso za ophunzira ake monga oimira a boma loposa laumunthu limenelo, Yesu akuwapatsa mphamvu ya kuchiritsa odwala ndipo ngakhale kuukitsa akufa. Iye akuwauza kuchita mautumiki ameneŵa kwaulere.

Kenako iye akuuza ophunzira ake kusakonzekera zinthu zakuthupi kaamba ka ulendo wawo wokalalikira. “Musadzitengere ndalama za golidi, kapena za siliva, kapena za kobiri m’malamba mwanu; kapena thumba la kamba la kunjira, kapena malaya aŵiri, kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira zakudya zake.” Awo amene amayamikira uthengawo adzalabadira ndi kupereka chakudya ndi malo ogona. Monga momwe Yesu akunenera kuti: “Ndipo m’mzinda uliwonse, kapena m’mudzi, muloŵamo, mufunitsitse ali woyenera momwemo; ndipo bakhalani komweko kufikira mutulukamo.”

Pamenepo Yesu akupereka malangizo onena za kufikira eni nyumba ndi uthenga wa Ufumu. “Ndipo poloŵa m’nyumba,” iye akulangiza, “muwalankhule; Ndipo ngati nyumbayo iri yoyenera, mtendere wanu udze pa iyo, koma ngati siiri yoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. Ndipo yemwe sadzakulandirani inu, kapena kusamva mawu anu, pamene mulikutuluka m’nyumbayo, kapena m’mudzimo sansani fumbi m’mapazi anu.”

Ponena za mzinda umene ukukana uthenga wawo, Yesu akuulula kuti chiweruzo pamzindawo chidzakhaladi chowopsa. Iye akufotokoza kuti: “Indetu ndinena kwa inu, kuti, tsiku la kuweruza, mlandu wawo wa Sodomu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mudzi umenewo.” Mateyu 9:35–10:15; Marko 6:6-12; Luka 9:1-5.

▪ Kodi ndiliti pamene Yesu akuyamba ulendo wachitatu wolalikira ku Galileya, ndipo kodi ukumkhutiritsa za chiyani?

▪ Potuma atumwi ake 12 kukalalikira, kodi ndimalangizo otani amene akuwapatsa?

▪ Kodi nchifukwa ninji kuli kolondola kuti ophunzira aphunzitse kuti Ufumuwo wayandikira?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena