Mutu 87
Linganizani Mtsogolo Mwanzeru Yogwira Ntchito
YESU wangotha kumene kusimba fanizo la mwana woloŵerera kukhamu limene likuphatikizapo ophunzira ake, okhometsa msonkho osawona mtima ndi ochimwa ena odziŵika, ndi alembi ndi Afarisi. Tsopano, polankhula ndi ophunzira ake, akusimba za fanizo la munthu wachuma amene walandira mbiri yoipa yonena za kapitawo wa m’nyumba yake kapena mdindo.
Malinga ndi kunena kwa Yesu, munthu wachumayo akuitana mdindo wake namuuza kuti akamchotsa ntchito. “Ndidzachita chiyani, chifukwa mbuye wanga andichotsera ukapitawo?” akudabwa mdindoyo. “Kulima ndilibe mphamvu, kupemphapempha kundichititsa manyazi. Ndidziŵa chimene ndidzachita, kotero kuti pamene anditulutsa muukapitawo, anthu akandilandire kunyumba kwawo.”
Kodi nchiyani chimene mdindoyo akulinganiza? Iye akuitana awo amene ali ndi mangaŵa kwa mbuye wake. “Unakongola chiyani kwa mbuye wanga?” iye akufunsa.
Woyamba akuyankha kuti, ‘Malitala 2,200 amafuta a azitona.’
‘Bwerera ndi pangano lako lolembedwalo ndipo kakhale pansi nulembepo mofulumira malitala 1,100,’ iye akumuuza.
Iye akufunsanso wina kuti: “Ndipo iwe uli nawo mangaŵa otani?”
Iye akuti, ‘Mitanga yatirigu yolemera malitala 22,000.’
‘Bwerera ndi pangano lako lolembedwa nukalembe 18,000.’
Mdindoyo akali ndi kuyenera kwake kwa kuchepetsa ngongole za mbuye wake, popeza kuti iye akali chikhalirebe ndi ulamuliro pachuma cha mbuyake. Mwa kuchepetsa mtengowo, akupanga mabwenzi ndi awo amene angamkomere mtima pamene atayikiridwa ndi ntchito yake.
Pamene mbuyeyo amva zimene zachitika, akuchita chidwi. Kwenikweni, ‘anayamikira mdindoyo, ngakhale kuti ngwosalungama, chifukwa chakuti anachita mwanzeru yogwira ntchito.’ Ndithudi, Yesu akuwonjezera kuti: “Chifukwa ana a nthaŵi ya pansi pano ali anzeru m’mbadwo wawo koposa ana a kuunika.”
Tsopano, posonyeza phunzirolo kwa ophunzira ake, Yesu akulimbikitsa kuti: “Mudziyesere nokha abwenzi ndi chuma chosalungama; kuti pamene chikusoŵani, iwo akalandire inu m’mahema osatha.”
Yesu sakuyamikira mdindoyo kaamba ka kusalungama kwake koma kaamba ka nzeru yake yogwira ntchito yowona patali. Kawirikawiri “ana a nthaŵi ya pansi pano” amagwiritsira ntchito mochenjera ndalama zawo kapena malo awo antchito kupanga mabwenzi ndi awo amene akawabwezera kuwakomera mtima. Chotero atumiki a Mulungu, “ana akuunika,” nawonso afunikira kugwiritsira ntchito chuma chawo chakuthupi, ‘chuma chawo chosalungama,’ mwanjira yanzeru kuti adzipindulitse.
Koma monga momwe Yesu akunenera, iwo ayenera kupanga mabwenzi kupyolera mwa chuma chimenechi ndi awo amene angawalandire “m’mahema osatha.” Kwa ziŵalo za kagulu kankhosa, malo ameneŵa ndiwo kumwamba; kwa “nkhosa zina,” ndiwo padziko lapansi la Paradaiso. Popeza kuti Yehova Mulungu yekha ndi Mwana wake ndiwo amene angalandire anthu mmalo ameneŵa, tiyenera kukhala akhama kukulitsa ubwenzi ndi iwo mwa kugwiritsira ntchito “chuma chosalungama” chirichonse chimene tingakhale nacho kuchirikizira zinthu Zaufumu. Ndiyeno, pamene chuma chakuthupi chilephera kapena chiwonongeka, monga momwedi chidzachitira, mtsogolo mwathu mosatha mudzakhala motsimikizirika.
Yesu akupitirizabe kunena kuti anthu okhulupirika posamalira zinthu zakuthupi, kapena zazing’ono, adzakhalanso okhulupirika posamalira zinthu zofunika kwambiri. “Chifukwa chake,” iye anapitirizabe kuti, “ngati simunakhala okhulupirika m’chuma chosalungama, adzakhulupilira inu ndani ndi chuma chowona [ndiko kuti, zinthu zauzimu, kapena Zaufumu]? Ndipo ngati simunakhala okhulupirika ndi zake za wina [zinthu Zaufumu zimene Mulungu amaikizira atumiki ake], adzakupatsani inu ndani za inu eni [mphotho yamoyo wosatha mmalo okhala osatha]?”
Ife sitingathe kukhala atumiki owona a Mulungu ndipo panthaŵi imodzimodziyo kutumikira chuma chosalungama, chuma chakuthupi, monga momwe Yesu akumalizira kuti: “Palibe mnyamata wa m’nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye aŵiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa chuma.” Luka 15:1, 2; 16:1-13; Yohane 10:16.
▪ Kodi ndimotani mmene mdindo wa m’fanizo la Yesu akupangira mabwenzi ndi awo amene angamthandize pambuyo pake?
▪ Kodi “chuma chosalungama” nchiyani, ndipo kodi tingapange bwanji mabwenzi kudzera mwa chumacho?
▪ Kodi ndani angatilandire “m’mahema osatha,” ndipo kodi malo ameneŵa nchiyani?