Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 86
  • Fanizo la Mwana Woloŵerera

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Fanizo la Mwana Woloŵerera
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Pamene Mwana Wotayikayo Apezeka
  • Pamene Mwana Wotayika Apezeka
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Nkhani ya Mwana Wotaika
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Mwana Wotayika Anabwerera
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Tate Yemwe Ali Wokonzeka Kukhululukira
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 86

Mutu 86

Fanizo la Mwana Woloŵerera

POKHALA atangotsiriza kumene kusimba mafanizo kwa Afarisi onena za kupezeka kwa nkhosa yotayika ndi ndalama zasiliva khumi zotayika, Yesu akupitirizabe tsopano ndi fanizo lina. Limeneli nlonena za atate wina wachikondi ndi kuchitira kwake ana ake aamuna aŵiri, amene aliyense wa iwo ali ndi zolakwa zazikulu.

Choyamba, pali mwana wamwamuna wamng’ono, mbali yaikulu yafanizolo. Iye akutenga choloŵa chake, chimene atate wake akumpatsa mosadodoma. Pamenepo iye akuchoka panyumba naphatikizidwa m’njira yamoyo wachisembwere kwambiri. Koma tamverani pamene Yesu akusimba fanizolo, ndi kuwona ngati mungadziŵe amene osimbidwawo akuimira.

“Munthu wina,” akuyamba motero Yesu, “anali ndi ana aamuna aŵiri; ndipo wamng’onoyo anati kwa atate wake, Atate, ndigaŵirenitu zanga za pa chuma chanu. Ndipo [atateyo] anagaŵira zamoyo wake.” Kodi mwana wamng’onoyu akuchitanji ndi zimene akulandira?

“Ndipo,” Yesu akufotokoza kuti, “pakupita masiku oŵerengeka, mwana wamng’onoyo anasonkhanitsa zonse, napita ulendo wake kudziko lakutali; ndipo komweko anamwaza chuma chake ndi makhalidwe a chitayiko.” Kwenikweni, iye akuthera ndalama zake mwa kukhala ndi mahule. Pambuyo pake nthaŵi zamavuto zifika, monga momwe Yesu akupitirizira kusimba kuti:

“Pamene anatha zake zonse, panakhala njala yaikulu m’dziko muja, ndipo iye anayamba kusoŵa. Ndipo anamuka nadziphatikiza kwa mfulu imodzi ya dziko lija; ndipo uyu anamtumiza kubusa kwake kukaŵeta nkhumba. Ndipo analakalaka kukhutitsa mimba yake ndi makoko amene nkhumba zimadya, ndipo palibe munthu anamninkha kanthu.”

Nkoluluza chotani nanga kukakamizidwira kuŵeta nkhumba, popeza kuti nyama zimenezi zinali zodetsedwa mogwirizana ndi Chilamulo! Koma chimene chinamvetsa ululu mwanayo chinali kuŵaŵa kwa njala imene inamchititsadi kukhumba chakudya chimene chinapatsidwa nkhumba. Chifukwa cha tsoka lake lowopsa limeneli, Yesu anati, “anakumbukira mumtima.”

Akumapitirizabe fanizo lake, Yesu akufotokoza kuti: “Anati [kwa iye mwini], Antchito olipidwa ambiri a atate wanga ali nacho chakudya chochuluka, ndipo ine ndiwonongeke kuno ndi njala? Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga, ndipo ndidzanena naye, Atate, ndinachimwira kumwamba ndi pamaso panu; sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu; mundiyese ine ngati mmodzi wa antchito anu. Ndipo iye ananyamuka nadza kwa atate wake.”

Kanthu kokalingalira ndi aka: Ngati atate wake akanamtembenukira ndi kumkalipira mwaukali pamene anachoka panyumba, mwachiwonekere mwanayo sakanakhala ndi ganizo lotsimikizirika ponena za chimene ayenera kuchita. Iye akanasankha kubwerera ndi kuyesa kukafunafuna ntchito kwina kwake m’dziko lakwawo kotero kuti sakayang’anizana ndi atate wake. Komabe, palibe lingaliro lotero limene linali m’maganizo mwake. Iye anafuna kukakhala kwawo!

Mwachiwonekere, atate wa m’fanizo la Yesu amaimira Atate wathu wachikondi, ndi wokoma mtima wakumwamba, Yehova Mulungu. Ndipo mwinamwake inu mukuzindikira kuti mwana wotayika, kapena woloŵerera, amaimira ochimwa odziŵika. Afarisi, amene Yesu akulankhula nawo poyambirira, asuliza Yesu chifukwa chakudya ndi anthu enieni amenewa. Koma kodi mwana wamkuluyo amaimira yani?

Pamene Mwana Wotayikayo Apezeka

Pamene mwana wotayika, kapena woloŵererayo, m’fanizo la Yesu abwerera kunyumba ya atate wake, kodi akulandiridwa motani? Mvetserani pamene Yesu akufotokoza:

“Koma pakudza iye kutali, atate wake anamuwona, nagwidwa chifundo, nathamanga, namkupatira pakhosi pake, nampsompsonetsa.” Ndiatate wokoma mtima chotani nanga, ndi wachifundo ameneyo woimira bwino lomwe Atate wathu wakumwamba, Yehova!

Mwachiwonekere atateyo anali atamva za moyo womwerekera m’chisembwere wa mwana wake. Komabe iye akumulandira kunyumba popanda kuyembekezera kaye mafotokozedwe atsatanetsatane. Yesu nayenso ali ndi mzimu wochingamira wotero, akumayamba kufika kwa ochimwa ndi okhometsa msonkho, amene akuimiridwa m’fanizoli ndi mwana woloŵerera.

Ndithudi, mosakayikira atate wa lunthayo m’fanizo la Yesu akudziŵa kanthu kena za kulapa kwa mwana wake mwa kuwona nkhope yake yachisoni, yakugwa pamene akubwerera. Koma kuchitapo kanthu kwachikondi kwa atateyo kukuchititsa kukhala kosavutirapo kwa mwanayo kulapa machimo ake, monga momwe Yesu akusimbira kuti: “Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu.”

Komabe, mawuwo asanathe kutuluka m’kamwa mwa mwanayo atate wake akuchitapo kanthu, akumalamulira akapolo ake kuti: “Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato ku mapazi ake; ndipo idzani naye mwana wang’ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere; chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa.” Pamenepo iwo akuyamba “kusekera.”

Pakali pano, ‘mwana wamkulu wa atatewo anali kumunda.’ Tiyeni tiwone ngati mungathe kudziŵa amene mwanayo amaimira mwa kumvetsera kumbali yotsala ya fanizolo. Yesu akuti ponena za mwana wamkuluyo: “Pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, anamva kuimba ndi kuvina. Ndipo anaitana mmodzi wa anyamata, namfunsa, Zinthu izi nzotani? Ndipo uyu anati kwa iye, Mng’ono wako wafika; ndipo atate wako anapha mwana wa ng’ombe wonenepa, chifukwa anamlandira iye wamoyo. Koma anakwiya, ndipo sanafuna kulowamo. Ndipo atate wake anatuluka namdandaulira. Koma anayankha nati kwa atate wake, Wonani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwira lamulo lanu nthaŵi iriyonse; ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwana wa mbuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga. Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiŵerewere, munamphera iye mwana mwana wa ng’ombe wonenepa.”

Kodi ndani, mofanana ndi mwana wamkuluyo, amene wakhala akusuliza kukoma mtima ndi chisamaliro zoperekedwa kwa ochimwa? Kodi sindiwo alembi ndi Afarisi? Popeza kuti kuli kusuliza kwawo Yesu chifukwa chakuti iye akulandira ochimwa kumene kukusonkhezera kusimbidwa kwa fanizo limeneli, mwachiwonekere iwo ayenera kukhala amene akuimiriridwa ndi mwana wamkulu.

Yesu akumaliza fanizo lake ndi chidandaulo cha atateyo kwa mwana wake wamkulu kuti: “Mwana wanga, iwe uli ndi ine nthaŵi zonse, ndipo zanga zonse ziri zako. Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng’ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.”

Motero Yesu akusiya kumasulira zimene potsirizira pake mwana wamkuluyo akuchita. Ndithudi, pambuyo pake, imfa ya Yesu ndi chiukiriro zitachitika, “khamu lalikulu la ansembe linamvera chikhulupirirocho,” mwinamwake kuphatikizapo ena a kagulu ka “mwana wamkulu” kameneka komwe Yesu akulankhula nako pano.

Koma kodi ndani m’nthaŵi zamakono amene ana aamuna aŵiri ameneŵa akuimira? Ayenera kukhala awo amene afikira pakudziŵa zifuno za Yehova mokwanira kukhala ndi maziko akuloŵa muunansi ndi iye. Mwana wamkulu amaimira ziŵalo zina za “kagulu kankhosa” kapena “mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m’mwamba.” Ameneŵa anatenga lingaliro lofanana ndi la mwana wamkulu. Analibe chikhumbo cha kulandira kagulu ka padziko lapansi, “nkhosa zina,” amene anawalingalira kukhala akuwabera kutchuka.

Kumbali ina, mwana woloŵererayo, amaimira anthu a Mulungu amene amachoka kukakondwera ndi zosangalatsa zimene dziko limapereka. Komabe, munthaŵi yokwanira, ameneŵa molapa amabwerera ndi kuyambiranso kukhala atumiki okangalika a Mulungu. Ndithudi, mmene Atate aliri wachikondi ndi wachifundo chotani nanga kwa awo amene amazindikira kufunikira kwawo chikhululukiro ndi kubwerera kwa iye! Luka 15:11-32; Levitiko 11:7, 8; Machitidwe 6:7; Luka 12:32; Ahebri 12:23; Yohane 10:16.

▪ Kodi nkwayani kumene Yesu akusimbirako fanizoli, kapena nkhani, ndipo nchifukwa ninji?

▪ Kodi munthu wosumikiridwa chisamaliro m’fanizoli ndani, ndipo chikumchitikira nchiyani?

▪ Kodi ndani m’tsiku la Yesu akuimiriridwa ndi atate ndi mwana wamng’onoyo?

▪ Kodi ndimotani mmene Yesu amatsanzirira chitsanzo cha atate wachifundo wa m’fanizo lake?

▪ Kodi nchiyani chimene chiri lingaliro la mwana wamkuluyo kulinga kukulandiridwa kwa mphwake, ndipo kodi Afarisi akuchita motani mofanana ndi mwana wamkuluyo?

▪ Kodi ndikugwira ntchito kotani kumene fanizo la Yesu liri nako m’tsiku lathu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena