Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 9/1 tsamba 30-31
  • Tate Yemwe Ali Wokonzeka Kukhululukira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Tate Yemwe Ali Wokonzeka Kukhululukira
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anatayika Napezedwanso
  • Zimene Tikuphunzirapo
  • Mwana Wotayika Anabwerera
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Fanizo la Mwana Woloŵerera
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Pamene Mwana Wotayika Apezeka
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Kulandiridwa Mwachikondi kwa Obwerawo
    Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 9/1 tsamba 30-31

Anachita Chifuniro cha Yehova

Tate Yemwe Ali Wokonzeka Kukhululukira

NDI zifukwa zabwino, latchedwa kuti nthano yaikulu yoposa zonse zomwe zinalembedwapo. Fanizo la Yesu lonena za chikondi cha atate kwa mwana wake woloŵerera lili ngati zenera lomwe tingaonerepo chifundo chapadera cha Mulungu kwa ochimwa olapa.

Anatayika Napezedwanso

Munthu wina anali ndi ana aŵiri. Wamng’onoyo anati kwa iye: “ndigaŵirenitu zanga za pa chuma chanu.” Tateyo anamvera, mwachionekere anampatsa limodzi la magawo atatu a chuma chake chonse​—monga mwalamulo kwa wamng’ono pa ana aŵiriwo. (Deuteronomo 21:17) Mnyamatayo mwamsanga anasonkhanitsa zake zonse napita kudziko lakutali kumene adakawononga ndalama zake zonse pochita makhalidwe oipa.​—Luka 15:11-13.

Ndiye kunagwa njala yoopsa. Posowa chochita, mnyamatayo analoŵa ntchito yoŵeta nkhumba​—ntchito yonyozeka kwa Myuda. (Levitiko 11:7, 8) Chakudya chinali chosoŵa mwakuti analakalaka kudya makoko amene nkhumba zimadya! Potsiriza, mnyamatayo anakumbukira. “Antchito olipidwa ambiri a atate wanga ali nacho chakudya chochuluka,” analingalira motero. ‘Ndidzanyamuka ndipite kwa atate wanga ndi kuulula machimo anga, ndipo ndikapempha kuti ndikhale mmodzi wa antchito awo.’a​—Luka 15:14-19.

Mwamsanga mnyamatayo anabwerera kwawo. Mosakayika maonekedwe ake anasintha kwambiri. Komabe, atate ake anamzindikira “pakudza iye kutali.” Atagwidwa chifundo, anamthamangira, namkupatira, ‘nampsompsona.’​—Luka 15:20.

Kumlandira bwino kumeneku kunapangitsa kukhala kosavuta kwa mnyamatayo kunena zakukhosi. Iye anati “Atate, ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu.” Atateyo anaitanitsa akapolo ake, nanena, “Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake; ndipo idzani naye mwana wa ng’ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere; chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwa.”​—Luka 15:21-24.

Phwando linayambika, ndipo panali kuimba ndi kuvina. Pamene anali kuchokera kumunda, mwana wamkulu anamva kuimba ndi kuvina. Pamene anazindikira kuti mng’ono wake wabwera ndipo ndicho chifukwa chake pali phwando, anakwiya. Iye anadandaula kwa atate ake kuti, ‘Ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri, ndipo sindinalakwira lamulo, simunandipatsepo kamwana ka mbuzi kuti ndisekere ndi mabwenzi anga. Koma pamene wadza mwana wanu uyu wokusakazirani chuma, mwamkonzera phwando.’ Koma atate akewo ananena naye, ‘Mwana wanga, iwe umakhala ndi ine, ndipo zanga zonse zili zako. Koma kudayenera kuti tisangalale chifukwa mng’ono wako anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.’​—Luka 15:25-32.

Zimene Tikuphunzirapo

M’fanizo la Yesuli, atate akuimira Mulungu wathu wachifundo, Yehova. Monga mwana wotayika, anthu ena kwa kanthaŵi amachoka m’malo achisungiko m’nyumba ya Mulungu koma pambuyo pake amabwereranso. Kodi Yehova amawaona motani amenewa? Amene amabwerera kwa Yehova atalapa ndi mtima wonse angatsimikizire kuti “Sadzatsutsana nawo nthaŵi zonse; ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha.” (Salmo 103:9) M’fanizoli, tate anathamanga kukalandira mwana wake. Mofananamo, sikuti Yehova akufuna chabe komanso ndi wokonzeka kukhululukira ochimwa olapa. Iye ndi “wokhululukira,” ndipo “adzakhululukira koposa.”​—Salmo 86:5; Yesaya 55:7; Zekariya 1:3.

M’fanizo la Yesu, chikondi chenicheni cha atate chinapangitsa kukhala kosavuta kwa mwana kulingalira zobwerera. Koma talingalirani: Chikadachitika nchiyani ngati atateyo akadamkana mnyamatayo kapena mwaukali akadamuuza kuti asadzabwerenso? Kachitidwe kotero mwachionekere kakanapangitsa mwanayo chisoni kosatha.​—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 2:6, 7.

Zikutanthauza kuti, atateyo anatheketsa kuti mwanayo adzathe kubwerera panthaŵi imene ankachoka. Nthaŵi zina masiku ano akulu achikristu amachotsa olakwa osalapa mumpingo. (1 Akorinto 5:11, 13) Potero, mwachikondi akhoza kuyamba kukonza njira yopangitsira wochimwa kubwerera mwakusonyeza njira zomwe angatsate kuti adzabwezeretsedwe mtsogolo. Kukumbukira za kulimbikitsidwa kotero kwapangitsa ambiri omwe adatayika mwauzimu kulapa pambuyo pake ndipo kwawapangitsa kubwerera kunyumba ya Mulungu.​—2 Timoteo 4:2.

Tateyo adasonyezanso chifundo pamene mwana wake anabwerera. Sizinamtengere nthaŵi yaitali kuti azindikire kulapa koona mtima kwa mnyamatayo. Kenaka, mmalo moumirira kufunsitsa kalikonse pa zolakwa za mwana wake, anangomlandira ndi manja aŵiri, ndipo adasangalala kwambiri kuchita zimenezo. Akristu ayenera kutengera chitsanzo chimenechi. Ayenera kusangalala kuti wotayika wapezeka.​—Luka 15:10.

Machitidwe a tateyo amasonyezeratu kuti ankafuna nkale kuti mwana wake woloŵererayo abwerere. Ndithudi, uku nkungochitira chithunzi mmene Yehova amalakalakira amene anachoka m’nyumba yake. Iye ‘safuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.’ (2 Petro 3:9) Amene amalapa machimo awo akhoza kutsimikizira kuti adzapeza madalitso mwa “nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye.”​—Machitidwe 3:19.

[Mawu a M’munsi]

a Pamene kapolo amaonedwa monga mmodzi wa pabanjalo, wantchito anali monga waganyu amene akhoza kuchotsedwa nthaŵi iliyonse. Mnyamatayo analingalira za kulola ngakhale ntchito yapansi kwambiri kunyumba kwa atate ake.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena