Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • su mutu 21 tsamba 160-166
  • Kulandiridwa Mwachikondi kwa Obwerawo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kulandiridwa Mwachikondi kwa Obwerawo
  • Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MWANA WOLOŴERERA ABWERERA
  • KODI FANIZOLO LIKUGWIRIRA NTCHITO MOTANI LEROLINO
  • KUMANGA PAMAZIKO OLIMBA
  • “Yehova, Mulungu Wachifundo ndi Wachisomo”
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Fanizo la Mwana Woloŵerera
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Tate Yemwe Ali Wokonzeka Kukhululukira
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Pamene Mwana Wotayika Apezeka
    Nsanja ya Olonda—1989
Onani Zambiri
Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
su mutu 21 tsamba 160-166

Mutu 21

Kulandiridwa Mwachikondi kwa Obwerawo

PALI anthu ambiri amene panthaŵi ina anali atamva mokwanira chowonadi Chabaibulo kudziŵa kuti Yehova ndi Mulungu wowona ndi kuzindikira kanthu kena ponena za zifuno zake. Ngakhale kuli kwakuti sali Mboni za Yehova, iwo angakhale ataphunzira Baibulo ndi Mboni. Kapena mwinamwake makolo awo anali Mboni. Unyinji wa amenewa wafika pamisonkhano ina pa Nyumba Yaufumu. Iwo angakhaledi atakhala ndi mbali m’kuuza ena uthenga Waufumu. Koma iwo sanapereke miyoyo yawo ku kuchita chifuniro cha Mulungu. Analekeranji?

2 Dziko limapereka zokopa zimene iwo amaganiza kuti amazifuna, zinthu zimene amalingalira kuti zidzawonjezera kusangalala kwawo ndi moyo, ndipo amachoka m’gulu la Yehova nakafunafuna zinthu zotero. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi, ena a amenewa amazindikira kuti sanapeze mtundu wa moyo umene anayembekezera. Amazindikira chenicheni chakuti ngati apitirizabe monga momwe akuchitira, adzawonongeka limodzi ndi dziko. Iwo sanaiŵale chisungiko ndi zakudya zauzimu zochuluka mu “nyumba” ya Yehova, ndipo iwo amafuna kubwereranso. Koma kodi Yehova adzawalandira?

MWANA WOLOŴERERA ABWERERA

3 Yankho likusonzedwa m’fanizo lodziŵika kwambiri la Yesu la mwana woloŵerera. Monga fanizo, Yesu anasimba za munthu amene anali ndi ana aŵiri. Wocheperapo anapempha atate wake gawo lake la chuma. Atalandira limeneli anapita ku dziko lakutali, kumene mosasamala anawawanya chirichonse m’moyo woipa. Chotero iye anachita momwaza. Pamene njala inakantha dzikolo, mnyamatayo, posoŵa kotheratu, anakakamizika kuŵeta nkhumba, koma sanaloledwe ngakhale kudya zakudya zake. Atagwedezedwa ndi mavuto amene anamkulira, anadzazindikira. Anakumbukira mmene moyo unaliri wabwino ngakhale kwa antchito olembedwa m’nyumba ya atate wake, ndipo anatsimikiza kubwerera. Iye akavomereza njira yake yolakwa ndi kupempha kuti alandiridwenso, osati monga mwana, koma monga mtumiki wolembedwa ntchito. (Luka 15:​11-19) Koma pambuyo pa zinthu zonse zimene anali atachita, kodi atate wake akamlola kubwerera? Kodi ndimotani mmene Yehova, amene anaphiphiritsiridwa ndi atate m’fanizoli akawonera kubwerera kwa munthu wotero?

4 Posonyeza bwino lomwe malingaliro a Yehova m’nkhaniyo, Yesu anapitiriza: “Koma pakudza iye [mwana wamng’onoyo] kutali, atate anamuwona, nagwidwa chifundo, nathamanga nam’kupatira pakhosi, nam’psopsonetsa. Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira kumwamba ndi pamaso panu, sindiyenera konse kutchulidwa mwana wanu. Koma atateyo ananena kwa akapolo ake, Tulutsani msanga mwinjiro wokometsetsa, nimumveke; ndipo mpatseni mphete kudzanja lake ndi nsapato kumapazi ake; ndipo idzani naye mwana wang’ombe wonenepa, mumuphe, ndipo tidye, tisekere; chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa, ndipo wakhalanso wamoyo; anali wotayika, ndipo wapezedwanso. Ndipo anayamba kusekera.”​—⁠Luka 15:​20-24.

KODI FANIZOLO LIKUGWIRIRA NTCHITO MOTANI LEROLINO

5 M’fanizoli mwana wamkuluyo, wachisamba, moyenerera akuyenerana ndi “mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m’mwamba.” (Ahebri 12:23) Kodi bwanji za mwana wamng’onoyo? Iye ayenera kuimira kagulu kena osati “kagulu ka nkhosa” kamene kali ndi chiyembekezo chakumwamba. Si “nkhosa zina” zonse za ambuye zikuyenerera ndi kulongosoledwa kwa mwana wamng’onoyo, koma ena amatero. Ngakhale kusonkhanitsidwa kwa “nkhosa zina” kusanadziŵike mwapadera, kuyambira mu 1935, panali anthu amene anadziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu wowona yekha. Iwo anadziŵa chiyembekezo cha moyo wa padziko lapansi mu Ufumu wake, ndipo analibe lingaliro lirilonse la kukhala a “mpingo wa obadwa oyamba” limodzi ndi ziyembekezo zakumwamba. Koma mmalo mwa kudzipereka ku utumiki wa Yehova, iwo analoŵerera m’zinthu zadziko. Iwo anatenga “zawo” zimene Mulungu adawapatsa, nthaŵi ndi moyo zimene anaŵalola kukhala nazo, nagwiritsira ntchito zimenezi kaamba ka kudzikhutiritsa iwo eni. Koma mu 1935 pamene atumiki a Yehova kwanthaŵi yoyamba anamvetsetsa kudziŵika kwa “khamu lalikulu,” ambiri amene anafanana ndi mwana wamng’onoyo anadzipereka ndi mtima wonse kaamba ka utumiki m’nyumba ya Atate. Inali nthaŵi ya kukondwera yonga imene Yesu analongosolera m’fanizo lake.

6 Nzowona kuti panthaŵiyo, sialiyense analoŵa m’chisangalalo chimenechi cha kufika kwa kagulu koimiridwa ndi mwana wamng’onoyo. M’fanizo lake Yesu anasonyeza kuti zimenezi zikakhala motero. Koma siotsalira onse a ‘kaguluko’ anasonyeza mzimu wotero, ndipo m’fanizo lake Yesu anasiya mpata wotsegukira awo amenedi poyamba anali osakondwera, kuti aloŵe m’chisangalalo chimene Yehova mwiniyo ali nacho pamene ochimwa otere alapadi.​—⁠Luka 15:​7, 10, 25-32.

7 Komabe, chiyambire zochitika za pakati pa ma 1930 zimenezo, ena azindikiranso kuti iwo, nawonso, m’mbali zina ngofanana ndi mwana woloŵerera ameneyo. Iwo akudziŵa bwino kwambiri nyumba yauzimu ya Yehova, gulu lake lowoneka, koma kakhalidwe kawo kawalekanitsa nalo, monga ngati ku “dziko lakutali.” Iwo sanatsutse atumiki a Yehova, koma kakhalidwe kawo sikanagwirizane ndi miyezo ya Mawu a Mulungu. Iwo angakhale atasumika moyo wawo wonse pantchito yawo yakuthupi ndi iwo eni koma analephera kupereka lingaliro lamphamvu kumathayo awo pamaso pa Mulungu ndi kuwopsa kwa nthaŵi zimene tikukhalamo ndi moyo. Ena anakhumudwa ndi zofooka za ena amene panthaŵiyo anagwirizana ndi mpingo ndipo sanayembekezere Yehova moleza mtima kuti awongole zinthu. Koma kodi ndim’mikhalidwe yotani imene onsewa aloŵamo pamene adzilekanitsa ndi banja lachikhulupiriro?

8 M’kupita kwa nthaŵi, ena azindikira kuti asauka mwauzimu. Awona kuti nyengo zazifupi zirizonse za chisangalalo zimene ali nazo sizikuwapatsa chimwemwe chosatha. Iwo angawonenso kuti kakhalidwe kawo kakuwavulaza mwakuthupi, mwa maganizo ndi mwauzimu. Mkati amawona kukhala opanda kanthu, monga momwe amachitira onse amene ali opanda Mulungu ndi opanda chiyembekezo. (Aefeso 2:12) Iwo amazindikira kuti nthaŵi yokha imene iwo analidi achimwemwe inali mu “nyumba” ya Yehova. Akufuna kubwerera. Kodi iwo ayenera kutero? Kodi ndimapindu otani othekera amene angakhalepo m’kupitiriza kwawo mu mkhalidwe wosauka? Kuzengereza kungakhale kwa ngozi. Ngati apitirizabe kudziphatikiza kudziko, pamene liwonongedwa adzataya moyo wawo.

9 Koma kodi anthu otere angabwerere? Mwachikondi Yehova akuwaitana kuti abwerere, ndipo gulu lake lowoneka likupereka chithandizo chachikondi kwa awo amene akutero. (Zekariya 1:​3, 4) Kodi chofunika nchiyani? Monga momwe kwasonyezedwera m’fananizo la Yesu, iwo ayenera kuzindikira, kuchitapo kanthu kubwerera ndi kuvomereza kuti iwo achimwira Mulungu. Ngati analoŵa m’khalidwe loipa kwambiri, ayenera kupereka umboni kwa akulu wokhutiritsa wakuti iwo tsopano aleka kakhalidwe kameneko ndipo alapa mowonadi. Chikhumbo chawo chaphamphu tsopano chiyenera kukhala kutumikira Yehova monga mbali ya gulu lake lowoneka. (Luka 15:​18-21; Miyambo 28:13) Ngati zimenezo ndizo zimene ziridi m’mtima mwawo, angatsimikizire kuti kusiya kwawo njira zoipa ndi maganizo ndi kubwerera kwa Yehova kudzapereka chisangalalo chachikulu. (Yesaya 55:⁠7) Komabe, kuti chisangalalo chawo chipitirire chikondwerero cha kulandiridwanso mwachikondi pa Nyumba Yaufumu, kulimbitsidwa kolama kwauzimu kukufunika.

KUMANGA PAMAZIKO OLIMBA

10 Kwenikweni nkofunika kwa aliyense amene akubwerera kubanja la Yehova kudziŵa bwino mbali zosiyanasiyana za umunthu wa Yehova ndi kukulitsa unansi weniweni naye. Iwo afunikira kuzindikira kuti zokha zimene Yehova amafuna kwa ife ziridi kaamba ka phindu lathu. Malamulo ake samachotsa chisangalalo m’moyo koma, mmalo mwake, amatitetezera kuchita zinthu zimene zingapereke chikondwerero chakanthaŵi koma kutsogolera ku zotulukapo zowawa. (Yesaya 48:17; Agalatiya 6:​7, 8) Pamene atilanga, chiri chifukwa chakuti amatikonda. (Miyambo 3:​11, 12) Phunziro laumwini lotsatiridwa ndi kusinkhasinkha zimene zaphunziridwa, pemphero laphamphu ndi kusonkhana nthaŵi zonse zidzatithandiza kuphunzira kuika chidaliro chathu chotheratu mwa Yehova, kuyang’ana kwa iye kaamba ka chitsogozo m’zonse zimene tichita.​—⁠Miyambo 3:​5, 6.

11 Awo amene anasokera angakhale atadziŵa chimene chinali cholungama ndi chimene chinali chosalungama. Koma tsopano ayenera kukulitsa kuda choipa ndipo ayenera kupitiriza kutero malinga ngati chiri pafupi nawo. (Salmo 97:10) Adzathandizidwa m’zimenezi ngati afunafuna osati chidziŵitso chokha komanso luntha. Choyambirira zimenezi zimaphatikizapo kuwona zinthu mogwirizana ndi Mulungu. Tifunikira kuzindikira njira zosiyanasiyana zimene amatilangizira nazo ndi mmene kachitidwe kathu ku uphungu wake kamayambukirira unansi wathu ndi iye. (Miyambo 4:7; 9:10) Tiyenera kuzindikira kufunika kwa kukhala osasintha, kugwiritsira ntchito miyezo ya Yehova nthaŵi zonse, m’zonse zimene timachita. (Tito 2:​11, 12; 1 Atesalonika 4:⁠7) Kusamala kuyeneranso kuchitidwa kulingalira osati kokha chisangalalo chakanthaŵi koma zimene zotulukapo za zosankha zathu zingadzakhale. (Yerekezerani ndi Miyambo 20:21; 23:​17, 18; Ahebri 11:​24-26) Tiyeneranso kukhala odera nkhaŵa mwachikondi ponena za chiyambukiro pa ena cha zinthu zimene timanena ndi kuchita.​—⁠Aroma 15:​1, 2.

12 Monga Akristu tidzalimbikitsidwa kwambiri mwa kuzindikira kuti tiri mkati mwa nkhondo yauzimu. Mdani wathu wamkulu ndiye Satana Mdyerekezi, limodzi ndi ziŵanda zake. Mwanjira iriyonse yotheka amafunafuna kutipatutsa pantchito yofunika Yaufumu imene Yehova watipatsa kuti tichite. Cholinga chake ndicho kutikopa kuika pambali miyezo ya Yehova, kukhala mbali ya dziko limene iye ali wolamulira. Kaŵirikaŵiri misampha yake imakondweretsa zikhumbo zachibadwa (za chimene, kupeza bwino kwathupi, chikondi ndi kukonda), koma amatisonkhezera kupatsa zikhumbo zoterozo kufunika kumene kumaipitsa chifuno chawo kapena kudzikhutiritsa m’njira yosayenera. Mwa kugwiritsira ntchito kokha mokwanira chovala chankhondo chauzimu chimene Mulungu amapereka tingapambane m’nkhondo imeneyi ya miyoyo yathu yauzimu.​—⁠Aefeso 6:​11-18.

13 Yesu ananena kuti ngati tikadza kwa iye ndi kunyamula “goli” lake, tikapeza mpumulo wa miyoyo yathu. (Mateyu 11:​29, 30) Kunyamula “goli” kumatanthauza kutumikira. Koma kutumikira Yehova motsanzira Mwana wake kumapereka mpumulo weniweni. Ziri choncho motani? Chifukwa chakuti kumapereka ufulu weniweni. Sitimakhalanso akapolo a uchimo, omangidwa nawo, kuchita zinthu zimene tikudziŵa kuti sitiyenera kuchita ndipo mwinamwake kufuna kuti sitikanakhala tikuzichita. (Yohane 8:​32, 34-36) Ngati umunthu wathu Wachikristu wamangidwa pa Yesu Kristu monga maziko, tidzazindikira malo ake antchito m’chifuno cha Yehova, tidzam’mvetsera ndi kuphunzira kwa iye. Iye anakondwera kuchita chifuniro cha Atate wake. Tidzaphunzira kuchita chimenechonso. (Yohane 4:34; Salmo 40:⁠8) Chifukwa cha kumamatira ku miyezo ya makhalidwe abwino ya Mulungu tidzakhala okhoza kukhala ndi chikumbumtima choyera. Mmalo mwa kudzikhalira moyo, tidzapeza chimwemwe chimene chimachokera m’kupatsa. (Machitidwe 20:35) Moyo udzafikira kukhala ndi chifuno chenicheni kwa ife. Koposa zonse, tidzakhala ndi chisangalalo cha kudziŵa kuti tiri ndi chivomerezo cha Yehova mwiniyo, Atate wa onse amene akukhala ana ake.​—⁠Miyambo 10:⁠22.

[Mafunso]

1. Kodi ndianthu amtundu wanji amene akukambitsiridwa m’mutu uno?

2. (a) Kodi nchifukwa ninji anachoka m’gulu la Yehova (b) Kodi nchifukwa ninji amayamba kukhumba kuti akanabwerera?

3. (a) M’fanizo la mwana woloŵerera, kodi ndimalongosoledwe otani amene Yesu anapereka a mkhalidwe wofanana? (b) Kodi atate amaphiphiritsira yani?

4. Kodi ndimotani mmene atate analandirira mwana wawo pamene anabwerera?

5. (a) Kodi ndani anachitiridwa chithunzi ndi mwana wamkuluyo m’fanizo la Yesu? (b) Pamenepa, kodi ndani anaphiphiritsiridwa ndi mwana wamn’gono, woloŵererayo?

6. M’kukwaniritsidwa, kodi ndimotani mmene anthu ena anasonyezera mkhalidwe wa mwana wamkuluyo, koma kodi zimenezo zinali choncho kwa otsalira onse?

7, 8. (a) M’zaka zaposachedwapa kwambiri, kodi nchiyani chimene chachititsa ena kulekana kwambiri ndi nyumba ya Yehova? (b) Kodi ndim’njira ziti zimene ena alingalirira mofanana ndi mwana woloŵerera? (c) Kodi nchifukwa ninji ayenera kubwerera?

9. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova amafuna anthu otero kuti abwerere? (Ezekieli 18:23) (b) Kodi nchiyani chimene chikufunidwa kwa iwo?

10. (a) Kodi ndimkhalidwe wotani kulinga ku malamulo a Yehova umene olapawo afunikira kukulitsa? (b) Kodi ndimotani mmene iwo angakulitsire unansi weniweni ndi Yehova?

11. Kodi ndimotani mmene osokerawo adzathandizidwira ndi (a) kukulitsa kuda choipa? (b) kufunafuna luntha? (c) kukhala osasintha m’kugwiritsira ntchito miyezo ya Mulungu? (d) kuphunzira kulingalira chotulukapo cha chirichonse chimene akulinganiza kuchita? (e) kusonyeza kudera nkhaŵa kwachikondi kulinga kwa ena?

12. (a) Kodi ndikuzindikira chiyani ponena za Satana ndi njira zake kumene kudzathandiza kutitetezera? (b) Kodi nchiyani chimene chikufunika kuti tipambane m’nkhondo imeneyi?

13. (a) Kodi ndimotani mmene tingapezere mpumulo wa miyoyo yathu? (b) Kodi nchifukwa ninji kutumikira Yehova motsanzira Kristu Yesu kumatipatsadi chimwemwe?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena