Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ed tsamba 2
  • Chifuno cha Brosha Lino

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chifuno cha Brosha Lino
  • Mboni za Yehova ndi Maphunziro
Mboni za Yehova ndi Maphunziro
ed tsamba 2

Chifuno cha Brosha Lino

WAFILOSOFI Wachidatchi Spinoza analemba: “Ndayesa kusaseka zochita za munthu, kusalira nazo, ngakhale kusazida, koma kuzimvetsetsa.” Monga mphunzitsi, mukuyang’anizana ndi ntchito yovuta ya kumvetsetsa malingaliro, mbiri, ndi zikhulupiriro za ana a sukulu amene mukuphunzitsa, kuphatikizapo ana a sukulu amene ali ana a Mboni za Yehova. Nthaŵi zina, ana a sukulu amenewo angatenge kaimidwe kamene kamaoneka kukhala kachilendo pankhani zina. Koma pamene kuli koonekeratu kuti mwana wa sukulu akuchita zimenezo chifukwa cha zikhulupiriro zake za chipembedzo ndi makhalidwe abwino, muyenera kumvetsera. Brosha lino latulutsidwa ndi Watch Tower Bible and Tract Society (bungwe lofalitsa mabuku la Mboni za Yehova) ndipo lalembedwa kuti likuthandizeni kumvetsetsa bwino ana a sukulu amene ali Mboni. Tikhulupirira mudzapatula nthaŵi yoliŵerenga bwinobwino.

Kumvetsetsa zikhulupiriro za chipembedzo cha wina sikumafuna kuti muzilandire kapena kuzitsatira, ndipo kudziŵitsa wina sindiko kumtembenuza. Si cholinga cha broshali kukakamiza inu kapena ana a sukulu anu kulandira zikhulupiriro za chipembedzo cha Mboni. Zimene tifuna ndi kungokudziŵitsani za makhalidwe ndi zikhulupiriro zimene ana a sukulu anu ena akuphunzitsidwa ndi makolo awo kotero kuti musavutike kumvetsetsa ana a Mboni ndi kugwirizana nawo. Ndithudi, si nthaŵi zonse pamene ana amachita zimene amaphunzitsidwa, popeza mwana aliyense akuphunzira kukhala ndi chikumbumtima chakechake.

Monga makolo ochuluka, Mboni za Yehova zimafuna kuti ana awo apindule koposa ndi maphunziro awo. Chifukwa chake, amaphunzitsa ana awo kugwirizana ndi aphunzitsi awo. Nawonso makolo amene ali Mboni ndi ana awo omwe amayamikira kwambiri pamene aphunzitsi awakomera mtima ndi kuwalemekeza.

Mboni za Yehova ndi Akristu odziŵika padziko lonse. Komabe, nthaŵi zina amamvedwa molakwa. Chotero, tikhulupirira kuti broshali lidzakuthandizani kumvetsetsa bwino ana a Mboni amene mukuwaphunzitsa. Makamaka, tikhulupirira kuti mudzaona chifukwa chake, m’mikhalidwe ina, iwo angafune kukhala osiyana.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena