Mmene Mboni za Yehova Zimaonera Maphunziro
Monga makolo onse, Mboni za Yehova zimadera nkhaŵa mtsogolo mwa ana awo. Chotero zimaona maphunziro kukhala ofunika kwambiri. “Maphunziro ayenera kuthandiza anthu kukhala othandiza ena m’chitaganya. Ayeneranso kuwathandiza kudziŵa mwambo wawo ndi kukhala ndi moyo wokhutiritsa kwambiri.”
MONGA momwe mawu ogwidwawo mu The World Book Encyclopedia akusonyezera, chimodzi cha zolinga zazikulu za maphunziro ndicho kuphunzitsa ana moyo wa tsiku ndi tsiku, zimenezi zimaphatikizapo kuwaphunzitsa kusamalira zosoŵa za banja mtsogolo. Mboni za Yehova zimakhulupirira kuti limeneli ndi thayo lopatulika. Baibulo lenilenilo limati: “Ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m’banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.” (1 Timoteo 5:8) Zaka zimene ana amakhala pasukulu zimawakonzekeretsa kaamba ka mathayo amene adzakhala nawo m’moyo. Choncho, Mboni zimadziŵa kuti maphunziro ayenera kuonedwa kukhala ofunika kwambiri.
“Maphunziro ayenera kuthandiza anthu kukhala othandiza ena m’chitaganya. Ayeneranso kuwathandiza kudziŵa mwambo wawo ndi kukhala ndi moyo wokhutiritsa kwambiri.” —The World Book Encyclopedia
Mboni zimayesayesa kutsatira lamulo la Baibulo: “Zilizonse zimene muchita, zichiteni ndi mtima wanu wonse, ngati kuti munali kugwira ntchito ya Ambuye ndipo osati ya anthu.” (Akolose 3:23, Today’s English Version) Lamulo limeneli limagwira ntchito m’mbali zonse za moyo wa tsiku ndi tsiku, kuphatikizapo sukulu. Chotero, Mboni zimalimbikitsa ana awo kulimbikira ndi kuona ntchito zimene amapatsidwa kusukulu kukhala zofunika kwambiri.
“Zilizonse zimene muchita, zichiteni ndi mtima wanu wonse, ngati kuti munali kugwira ntchito ya Ambuye.”—Akolose 3:23, Today’s English Version
Baibulo limaphunzitsanso kumvera malamulo a dziko limene munthu akukhalamo. Chotero ngati lamulo limafuna kuti munthu apite kusukulu kufikira pa usinkhu wakutiwakuti, Mboni za Yehova zimatsatira lamulolo.—Aroma 13:1-7.
Pamene kuli kwakuti Baibulo silimachepetsa kufunika kwa kuphunzira za moyo wa tsiku ndi tsiku, ilo limasonyeza kuti chimenecho sindicho cholinga chokha kapena chachikulu cha maphunziro. Maphunziro achipambano ayeneranso kupatsa ana chimwemwe cha kukhala ndi moyo ndi kuwathandiza kupeza malo awo m’chitaganya monga anthu olemekezeka. Chotero, Mboni za Yehova zimaona kuti kusankha bwino zochita za kunja kwa kalasi nkofunika kwambiri. Zimakhulupirira kuti kupuma koyenera, nyimbo, zochita zapamtima, maseŵero olimbitsa thupi, kupita kumalaibulale ndi kumamyuziyamu, ndi zina zotero, zimathandiza kwambiri m’maphunziro oyenera. Ndiponso, zimaphunzitsa ana awo kulemekeza achikulire ndi kupeza mipata ya kuwatumikira.
Bwanji Nanga za Maphunziro Owonjezera?
Chifukwa cha sayansi yopanga zinthu yatsopano, mwaŵi wa ntchito ukusintha nthaŵi zonse. Chotero, achichepere ambiri amakakamizika kugwira ntchito imene sanaiphunzire. Popeza zili choncho, kagwiridwe kawo ka ntchito ndi kudziphunzitsa okha, makamaka kukhala wokhoza kusintha, zidzakhala zofunika kwambiri kwa iwo. Choncho, ndi bwino kuti ana a sukulu adzakhale achikulire a ‘mutu wogwira ntchito bwino m’malo mwa mutu wodzala bwino’ malinga ndi kunena kwa wolemba nkhani wa m’nyengo ya Renaissance, Montaigne.
Ulova, umene uli m’maiko olemera ndi osauka omwe, kaŵirikaŵiri umakhala ukuyembekeza achichepere osaphunzira kwambiri. Chifukwa chake, ngati ntchito zimafuna maphunziro owonjezera pa mlingo umene lamulo limafuna, zili kwa makolo kuthandiza ana awo kusankha maphunziro owonjezera, akumapenda mapindu amene angakhalepo ndi zimene maphunziro owonjezera amenewo angawatayitse.
Komabe, tikhulupirira mungavomereze kuti chipambano m’moyo sichimangodalira pa chuma chakuthupi. Posachedwapa amuna ndi akazi amene moyo wawo wonse unali pa ntchito zawo anataya chifuno cha moyo pamene anachotsedwa ntchito. Makolo ena alepa moyo wa mabanja awo ndi nthaŵi yocheza ndi ana awo, akumalephera kuwathandiza kukula, chifukwa chakuti iwo anamwerekera kwambiri ndi ntchito yolembedwa.
Mwachionekere, maphunziro oyenera ayenera kuphatikizapo mfundo yakuti si chuma chakuthupi chokha chimene chimatipatsa chimwemwe. Yesu Kristu anati: “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka m’kamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Monga Akristu, Mboni za Yehova zimazindikira kufunika kwa kukhala ndi makhalidwe abwino ndi mikhalidwe yauzimu limodzi ndi kudzikonzekeretsa iwo eni kusamalira zosoŵa zawo zakuthupi.