Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ed tsamba 10-13
  • Maprogramu a Maphunziro

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Maprogramu a Maphunziro
  • Mboni za Yehova ndi Maphunziro
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Sukulu Yautumiki Wateokrase
  • Sukulu Zina
  • Kodi Mwana Wanga Azipita ku Sukulu?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Amaphunzitsa Baibulo Komanso Kuwerenga ndi Kulemba
    Galamukani!—2015
  • Ntchito Yamaphunziro Yofala Kwambiri
    Galamukani!—2001
  • Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu
    Galamukani!—1994
Onani Zambiri
Mboni za Yehova ndi Maphunziro
ed tsamba 10-13

Maprogramu a Maphunziro

Mboni za Yehova ndi zodziŵika padziko lonse chifukwa cha ntchito yawo yophunzitsa Baibulo.

CHIFUKWA chakuti zimaona ntchito yawo yophunzitsa Baibulo kukhala yofunika kwambiri, anthu ena angaganize kuti izo sizimafuna maphunziro akusukulu. Koma zimenezo si zoona. Kuti mphunzitsi aphunzitse ena, iye ayenera kuphunzira choyamba, ndipo zimenezi zimafuna maphunziro ndi malangizo oyenera. Chotero kuwonjezera pa kugwiritsira ntchito bwino maphunziro akusukulu, Mboni za Yehova zapindula kwa zaka zambiri ndi maprogramu osiyanasiyana a maphunziro ndi sukulu zoyendetsedwa ndi Watch Tower Society. Zimenezi zathandiza Mboni ndi ena kuwongolera nzeru zawo, makhalidwe awo, ndi mkhalidwe wawo wa uzimu.

Mwachitsanzo, m’maiko ambiri Mboni zayang’anizana ndi vuto lapadera—mmene zingaphunzitsire anthu omwe sadziŵa kuŵerenga ndi kulemba amene anali ndi mwaŵi wochepa kapena amene analibiretu mwaŵi wa kulandira maphunziro oyenera. Kuti ikwaniritse chosoŵa chimenechi, Watch Tower Society yakonza makalasi ophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba.

Mwachitsanzo, ku Nigeria Mboni za Yehova zachititsa makalasi ophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba chiyambire 1949. Pofika mu 1961, Anaijeriya zikwizikwi anali ataphunzira kuŵerenga ndi kulemba, ndipo maumboni amene alipo asonyeza kuti pakati pa 1962 ndi 1994, achikulire ena okwanira 25,599 anaphunzitsidwa kuŵerenga ndi kulemba m’makalasi ameneŵa. Kufufuza kwaposachedwapa kunasonyeza kuti Mboni za Yehova zoposa 90 peresenti m’Nigeria zidziŵa kuŵerenga ndi kulemba, poyerekezera ndi yochepera 50 peresenti ya anthu ena onse. Ku Mexico, Watch Tower Society yachititsa makalasi ophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba chiyambire 1946. Mu 1994, anthu oposa 6,500 anaphunzitsidwa kuŵerenga ndi kulemba. Pakati pa 1946 ndi 1994, oposa 127,000 anathandizidwa kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba. Makalasi ophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba akonzedwanso m’maiko ena ambiri, onga Bolivia, Cameroon, Honduras, ndi Zambia.

Makalasi otero ophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba kaŵirikaŵiri azindikiridwa ndi akuluakulu a maphunziro m’maiko amene achitikirako. Mwachitsanzo, ku Mexico wantchito wa boma wina analemba: “Ndikuthokozani kwambiri kaamba ka kugwirizanika kwanu, ndipo moimira boma ndikupereka kwa inu chiyamikiro chawo chachikulu kwambiri pa ntchito yanu yabwino yopita patsogolo yopindulitsa anthu ya kuphunzitsa osadziŵa kuŵerenga ndi kulemba. . . . Ndikuti mupambanetu pa ntchito yanuyo ya kuphunzitsa.”

Sukulu Yautumiki Wateokrase

Popeza zimaona ntchito yawo yophunzitsa Baibulo kukhala yofunika kwambiri, Mboni za Yehova zimayesayesa kuwongolera luso lawo la kufotokozera ena ziphunzitso za Baibulo. Kuti chithandizo cha mtundu umenewu chiperekedwe, msonkhano wotchedwa Sukulu Yautumiki Wateokrase umachitidwa mlungu ndi mlungu m’mipingo yonse yoposa 75,000 padziko lonse. Olembetsa onse, Mboni ndi amene sali Mboni omwe, amasinthana kukamba nkhani pamaso pa omvetsera yozikidwa pa mutu wosankhidwa pasadakhale. Mosasamala kanthu za usinkhu wawo, ana a sukuluwo amalandira uphungu pambuyo pake woperekedwa ndi mlangizi ndi cholinga cha kuwaphunzitsa maluso a kuŵerenga ndi kulankhula poyera. Ngakhale achichepere kwambiri, atangodziŵa kuŵerenga, angalembetse ndi kulandira maphunziro ameneŵa, amene amawathandizanso m’mbali zina, kuphatikizapo m’maphunziro awo akusukulu. Aphunzitsi ambiri anena kuti ana a sukulu amene ali Mboni amadziŵa kufotokoza bwino zinthu.

Ndiponso, mpingo uliwonse wa Mboni za Yehova umalimbikitsidwa kukhala ndi laibulale ya mabuku ophunzirira Baibulo, madikishonale, ndi mabuku ena a maumboni m’Nyumba yawo Yaufumu, kapena malo olambirira. Onse amene amapezeka pamisonkhano pa Nyumba Yaufumu akhoza kugwiritsira ntchito laibulale imeneyi. Kuŵerenga kumalimbikitsidwa kwambiri m’mipingo yawo, ndiponso banja lililonse limalimbikitsidwa kukhala ndi laibulale ya banja ya zofalitsa zosiyanasiyana zokwaniritsa zosoŵa za ana ndi achikulire omwe.

Sukulu Zina

Watch Tower Society imachititsanso sukulu zophunzitsa amishonale amuna ndi akazi omwe, limodzinso ndi sukulu zophunzitsa amuna amene ali ndi mathayo a utumiki m’mipingo yawo. Sukulu zimenezi zili maumboni ena akuti Mboni za Yehova zimaona maphunziro kukhala ofunika kwambiri.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena