Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g94 3/8 tsamba 7-9
  • Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu
  • Galamukani!—1994
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu a Mulungu Lerolino
  • Kuphunzira Kuŵerenga
  • Kodi Mwana Wanga Azipita ku Sukulu?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Kupindula ndi Kuŵerenga Baibulo Tsiku ndi Tsiku
    Nsanja ya Olonda—1995
  • Chitani Khama pa Kuŵerenga
    Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Amaphunzitsa Baibulo Komanso Kuwerenga ndi Kulemba
    Galamukani!—2015
Onani Zambiri
Galamukani!—1994
g94 3/8 tsamba 7-9

Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu

M’NTHAŴI zakale anthu ambiri a Mulungu anali ophunzira. Pafupifupi zaka 3,500 zapitazo, Mose analemba mabuku asanu oyambirira a Baibulo. Yemwe anatenga malo ake, Yoswa, analamulidwa kuŵerenga Malemba “usana ndi usiku” kuti apeze chipambano m’ntchito imene Mulungu anampatsa. Ndipo Mulungu analamula kuti mafumu Achiisrayeli, ataloŵa ufumu, adzilembere kope la Chilamulo ndi kuliŵerenga tsiku ndi tsiku.—Yoswa 1:8; Deuteronomo 17:18, 19.

Atsogoleri a mtunduwo sindiwo okha amene anali kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba. Ngakhale kuti mwachionekere anali ophiphiritsira, malangizo opatsidwa kwa Aisrayeli a ‘kulemba’ malamulo a Mulungu pamphuthu za nyumba zawo anasonyeza kuti anthuwo anali ophunzira. Amosi anali mbusa wa nkhosa, ndipo Mika anali mneneri wa kumudzi wakutali; komabe, aŵiriwo analemba mabuku a Baibulo.—Deuteronomo 6:8, 9; Amosi 1:1; Mika 1:1.

Yesu anali wokhoza kusanthula mipukutu yonse youziridwa ya Malemba Achihebri m’masunagoge, kumene, panthaŵi ina, anaŵerenga poyera ndi kutanthauzira lembalo pa iye mwini. Atumwi ake nawonso anali ophunzira, akumagwira mawu ndi kuloza ku Malemba Achihebri nthaŵi mazanamazana m’zolembedwa zawo.—Luka 4:16-21; Machitidwe 17:11.

Anthu a Mulungu Lerolino

Yesu anauza otsatira ake ‘kuphunzitsa anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene [anawalamulira].’ Analoseranso kuti “uthenga uwu wabwino wa ufumu [ukalalikidwa] padziko lonse lapansi.”—Mateyu 24:14; 28:19, 20.

Mofanana ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba, Mboni za Yehova lerolino zachita malangizo ameneŵa mwa kuphunzitsa mwachangu ndi kulalikira ndi pakamwa. Ndiponso zafalitsanso mbiri yabwino ya Ufumu ndi zofalitsidwa. Chiyambire 1920, Mboni za Yehova zatulutsa ndi kufalitsa m’zinenero zoposa 200 Mabaibulo, mabuku, magazini, ndi timabuku zoposa mamiliyoni zikwi zisanu ndi zinayi.

Anthu mamiliyoni padziko lonse lapansi alabadira mwachiyanjo, akumakhala ophunzira a Kristu. Mwa iwo muli amuna ndi akazi amene satha kuŵerenga kapena kulemba. Osaphunzira ameneŵa sali Akristu onyozeka—ambiri atumikira Mulungu mokhulupirika kwa zaka makumi ambiri, apirira zizunzo zachipembedzo, ndipo asonyeza chikondi chawo kwa Yehova mwa kusunga malamulo ake.—1 Yohane 5:3.

Ambiri a iwo amalakalaka kuŵerenga ndi kulemba, pozindikira kuti kuphunzira ndiko mfungulo imene imatsegula njira yakutengamo mbali kwambiri m’kulambira kwawo Mulungu. Pamisonkhano, amafuna kutsatira pamene Baibulo ndi zofalitsidwa Zachikristu zikuŵerengedwa, ndipo amafuna kuŵerenga mawu a nyimbo kotero kuti aziimbira limodzi ndi abale ndi alongo awo auzimu. Panyumba, amalakalaka kudzilimbitsa iwo eni ndi mabanja awo kupyolera m’phunziro la Baibulo. Muutumiki, amalakalaka kuphunzitsa ena chowonadi cha Mawu a Mulungu popanda kudalira wina kuwaŵerengera.

Kuphunzira Kuŵerenga

Zikumachitapo kanthu pa kusoŵa kumeneku, Mboni za Yehova zapanga makonzedwe othandizira kupititsa patsogolo kuphunzira m’mipingo yawo ndi kwa munthu payekha. Padziko lonse, zaphunzitsa amuna ndi akazi osaŵerengeka. M’Nigeria mokha, Mboni za Yehova zaphunzitsa anthu oposa 23,000 kuŵerenga ndi kulemba. Mmodzi wa ameneŵa ndi Effor. Iye akusimba kuti:

“Ndinayamba kuŵerenga ndi kulemba mu 1950 pamene ndinali ndi zaka 16 zakubadwa. Kalasi lophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba linachititsidwa ndi Mboni za Yehova. Tinkagwiritsira ntchito buku lofalitsidwa ndi Watch Tower Society, ndipo tinkapatsidwa magawo okaŵerengera kunyumba.

“Ndinaona kusaphunzira kwanga monga nthenda. Ndinafuna kufotokozera Baibulo abale anga ndi mabwenzi, koma pokhala wosakhoza kuŵerenga ndi kulemba, sindinathe kuchita zimenezo bwino lomwe. Chimene chinandisonkhezera kuphunzira chinali chikhumbo changa cha kulalikira ndi kuphunzitsa ena kuti akhale ophunzira a Kristu. Ndinali kulemba pa chilichonse chimene ndinapeza, ngakhale pamasamba a nthochi. Chikhumbo changa cha kuŵerenga ndi kulemba chinali chachikulu kwambiri kwakuti ndinali kulota ndikuyeseza. Ndinapempha ena kundithandiza; sindinachite manyazi. Ndikumbukira ndikumalembera makalata mabwenzi anga ndi kupatsa makalatawo kwa amene anapita kusukulu kuti awawongolere.

“Kuphunzira m’kalasi lophunzitsa kuŵerenga ndi kulemba la mpingo kunanditengera chaka. Pambuyo pake ndinapatsidwa gawo lophunzitsa kalasilo. Zimenezo zinandipatsa mpata wakuthandiza ena ambiri.

“Sukulu imeneyo inandithandiza kwambiri kwakuti mkati mwa zaka zambiri, ndinapatsidwa mwaŵi wa kutembenuza madrama a Sosaite kuchokera m’Chingelezi kupita m’Chiisoko, chinenero changa. Ndiponso, ndatumikira monga woyang’anira mpingo chiyambire ma 1960. M’ma 1980, ndinatumikira monga woyang’anira dera wogwirizira wa Mboni za Yehova. Ndinalinso ndi mwaŵi wa kuchititsa Sukulu Yautumiki Waupainiya [sukulu ya atumiki anthaŵi yonse] ndipo kaŵiri ndinaphunzitsa pa Sukulu Yautumiki Waufumu [sukulu ya akulu Achikristu]. Ndidziŵa kuti ngati ndinali wosaphunzira, sindikanapatsidwa mwaŵi wonsewu.

“Mmene ndimayamikirira nanga makonzedwe ameneŵa akuphunzitsa ofatsa kuŵerenga ndi kulemba! Nthaŵi zina pamene ndipita kukagona usiku, ndimayamikabe Yehova kuti sindilinso wosaphunzira m’dziko lamakonoli.”

Mlengi wathu, Yehova Mulungu, mwachisomo wapatsa mtundu wa anthu luso lakuŵerenga ndi kulemba. Koma maluso ameneŵa samapezeka popanda kuyesayesa. Mphoto yaikulu koposa ya kuphunzira kuŵerenga ndi kulemba ndiyo kukhoza kutenga Mawu a Mulungu ndi kumvera chilangizo chaumulungu chakuti: “Ulingiriremo usana ndi usiku.”—Yoswa 1:8.

[Bokosi patsamba 9]

Mmene Mungathandizire Ana Anu Kukulitsa Chikondi cha Kuŵerenga

● Perekani chitsanzo inu mwini mwa kuŵerenga nthaŵi zonse. Makolo amene amaŵerenga mothekera adzakhala ndi ana amene amaŵerenga.

● Lankhulani ndi mwana wanu kuyambira ukhanda wake. Kumvetsera chinenero chatanthauzo kumathandiza ana kuzindikira mawu ndi malingaliro amene adzachititsa kuphunzira kuŵerenga kukhala kosavuta.

● Nthaŵi zonse ŵerengerani ana anu. Pamene muwafukata ndi kuwaŵerengera, makanda amalandira uthenga wakuti mawu ndi mabuku ngabwino, ngakhale ngati sanakulebe mokhoza kuzindikira nkhani imene ikuŵerengedwa. Pitirizani kuŵerengera ana anu pambuyo pakuti iwo eniwo aphunzira kuŵerenga. Aphunzitsi kusukulu amathandiza ana kudziŵa mmene angaŵerengere, koma makolo angachite zochuluka kuwathandiza kukonda kuŵerenga. Ana amakonda kumvetsera nkhani zawo zapamtima mobwerezabwereza.

● Khalani ndi mabuku oti ana anu adziŵerengera panyumba.

● Limbikitsani ana anu kulemba. Kaŵirikaŵiri mwana amene amalemba amaŵerenganso.

● Sankhani nyengo ya kuŵerenga yotsimikizirika ya banja. Sinthanani kuŵerenga, ndiyeno kambitsiranani nkhaniyo pamodzi. Nthaŵi zimenezi ziyenera kukhala zosangalatsa ndi zomangirira.

[Chithunzi patsamba 8]

Anthu akale owopa Mulungu anali kudziŵa kuŵerenga ndi kulemba

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena