Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g 8/15 tsamba 10-11
  • Amaphunzitsa Baibulo Komanso Kuwerenga ndi Kulemba

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Amaphunzitsa Baibulo Komanso Kuwerenga ndi Kulemba
  • Galamukani!—2015
  • Nkhani Yofanana
  • Maprogramu a Maphunziro
    Mboni za Yehova ndi Maphunziro
  • Kuphunzira Pakati pa Anthu a Mulungu
    Galamukani!—1994
  • Kodi Mwana Wanga Azipita ku Sukulu?
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Ntchito Yamaphunziro Yofala Kwambiri
    Galamukani!—2001
Onani Zambiri
Galamukani!—2015
g 8/15 tsamba 10-11
Wa Mboni za Yehova akuphunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba

Timabuku tambirimbiri takuti Dziperekeni pa Kuwerenga ndi Kulemba tapangidwa m’zilankhulo zoposa 100

Amaphunzitsa Baibulo Komanso Kuwerenga ndi Kulemba

Bungwe linaa loona za maphunziro linanena kuti: “Munthu aliyense ali ndi ufulu wophunzira ndipo akaphunzira, zinthu zimamuyendera bwino pa moyo wake.”

MALIPOTI akusonyeza kuti padziko lonse, anthu oposa 700 miliyoni azaka zoposa 15, sadziwa kuwerenga ndi kulemba. Choncho sangaphunzire paokha zinthu zosiyanasiyana zomwe zimalembedwa. Sangawerengenso mfundo za m’Baibulo zimene “zinalembedwa kuti zitilangize.” (Aroma 15:4) A Mboni za Yehova m’mayiko ambiri amaphunzitsa Baibulo komanso kuwerenga ndi kulemba ndipo amachita zonsezi kwaulere. Kodi ntchito imeneyi ikuthandizadi anthu?

Kuti tiyankhe, tiyeni tikambirane za ku Mexico. M’dzikoli, anthu ambiri amalankhula Chisipanishi ndipo kuyambira mu 1946, a Mboni aphunzitsa anthu oposa 152,000 kuwerenga ndi kulemba. Ena mwa anthuwa anayambanso kuphunzitsa anzawo. Boma la Mexico lalemba makalata ambiri othokoza Mboni za Yehova chifukwa cha ntchito imeneyi. M’kalata ina linalemba kuti: “Anthu inu mukuchita bwino kwambiri. Akuluakulu a zamaphunziro akudziwa ntchito yaikulu imene mukugwira pophunzitsa anthu kuwerenga ndi kulemba.”

Ana ndi achikulire omwe akuthandizidwa chifukwa cha sukulu imeneyi. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Josefina analowa sukuluyi ali ndi zaka 101 ndipo anadziwa kuwerenga ndi kulemba pambuyo pa zaka ziwiri.

Ngakhale kuti m’dzikoli anthu ambiri amalankhula Chisipanishi, ntchito yophunzitsa kuwerenga ndi kulembayi imachitikanso m’zilankhulo zina. Mu 2013, sukuluyi inachitika m’zilankhulo zokwana 8 ndipo anthu anaphunzira kuwerenga ndi kulemba m’zilankhulo zawo.

Kunena zoona, kuwerenga ndi kulemba n’kothandiza m’njira zambiri.Koma chofunika kwambiri n’chakuti kumathandiza anthu kuphunzira Baibulo. Tikutero chifukwa chakuti munthu akaphunzira Baibulo amatha kusiya makhalidwe oipa ndiponso kukhulupirira zinthu za bodza.—Yohane 8:32.

a United Nations Educational, Scientific, and Cultural Organization.

ANTHU A M’BANJA LAKE ANADABWA

Munthu wovutika kumva dzina lake Daniel akulemba notsi pamene akuonera DVD ya chilankhulo cha manja cha ku Mexico

Daniel anaphunzira chilankhulo chamanja cha ku Mexico pogwiritsa ntchito ma DVD

Munthu wina dzina lake Daniel anali ndi vuto lakumva komanso kulankhula. Izi zinkachititsa kuti azikhala wokhumudwa n’kumangokalipira achibale ake. Atafika zaka 23, wa Mboni wina dzina lake Josué, yemwenso anali ndi vuto la kumva, anayamba kuphunzira naye Baibulo. Iye ankagwiritsa ntchito manja ndi zithunzi basi. Kenako Daniel anaphunzira chilankhulo chamanja cha ku Mexico pogwiritsa ntchito ma DVD.b

Daniel atamvetsa mfundo za m’Baibulo anayamba kukhala ndi makhalidwe atsopano monga ‘chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kuleza mtima.’ (Akolose 3:10, 12) Anayambanso kutsatira lamulo la m’Baibulo lakuti tizilemekeza makolo athu. (Aefeso 6:1, 2) Anthu a m’banja lake ataona mmene wasinthira, anadabwa kwambiri. Mayi ake anayamikira Josué chifukwa chothandiza mwana wawo kudziwa Mulungu ndipo ankamuthokoza misozi ikulengeza m’maso. Mu 2007, Daniel anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova.

b Mabuku okwana 46 anamasuliridwa m’chilankhulo chamanja cha ku Mexico ndipo akupezeka m’ma DVD. Pa webusaiti yathu ya jw.org pamapezekanso zinthu zosiyanasiyana m’zilankhulo zamanja zokwana 80. Timapanganso mabuku ena m’zilembo za anthu osaona.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena