Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
Taganizirani zodabwitsa izi: M’dziko lina lotukuka, anthu oposa 90 peresenti amaona kuti ali ndi moyo wachimwemwe kwambiri kapena wachimwemwe chokwanira ndithu. Koma mitundu ya mankhwala itatu pa mitundu khumi yogwiritsidwa ntchito kwambiri m’dzikomo imaperekedwa kaamba ka vuto la kuvutika maganizo. M’dziko lokhalokhalo, 91 peresenti ya anthu amaona kuti moyo wa banja lawo uli wokhutiritsa. Chikhalirechobe, pafupifupi theka la maukwati kumeneko amatha!
Ndipo kufufuza anthu m’mayiko 18, okwana pafupifupi theka la chiŵerengero cha anthu onse padziko lapansi, kumaonetsa kuti “anthu ambiri padziko lapansi akuopa za m’tsogolo.” Choncho, n’chachidziŵikire kuti ambiri sali ndi moyo wokhutiritsa. Nanga inuyo bwanji? Kabukuka kalembedwa kuti kakuthandizeni kupanga moyo wanu kukhala wokhutiritsa kwenikweni.