Mutu 1
Moyo Wokhutiritsa—Kodi Ndi Wongoyerekeza Chabe?
1-3. Kodi ndi mavuto otani amene timakumana nawo tsiku ndi tsiku?
MU Dziko lotukuka, nyumba yokhala ndi zonse zofunikira zosangalatsa moyo ingapereke chithunzi chakuti moyo m’nyumbamo ndi wachimwemwe ndi wokhutiritsa. Koma kodi mutaloŵamo mungapeze zotani? Mkhalidwe wosasangalatsa ndi womvetsa chisoni. Mayankhidwe a ana achinyamata kwa makolo awo ndi ongodula, kumangoti “Inde,” kapena “Ayi,” basi. Mayi akusoŵa chikondi cha mwamuna wake. Ndipo bamboyo sakufuna wina kum’sokoneza. Makolo okalamba a banjali pokhala okha kumalo akutali, akulakalaka kuona banja limeneli chifukwa sanaonane nawo kwa miyezi yambiri. Komabe, mabanja ena omwe akumana ndi mavuto ngati ameneŵa akhala okhoza kuwathetsa ndipo alidi achimwemwe. Kodi mukudabwa kuti zimenezi zimatheka bwanji?
2 Taganizirani za banja lina lokhala m’dziko limene likutukuka kumene, mwinamwake kudera lakutali kumidzi. Anthu onse seveni m’banjamo akukhala m’kanyumba kamaudzu kamene kangagwe nthawi iliyonse. Sakudziŵa kuti chakudya chotsatira chichokera kuti—inde, ichi n’chikumbutso chomvetsa chisoni chakuti munthu sanathe kuthetsa njala ndi umphaŵi padziko lapansi. Komabe, alipo mabanja ambiri padziko lapansi amene ali achimwemwe ngakhale kuti ali paumphaŵi wofananawo. Chifukwa chiyani?
3 Ngakhale m’mayiko olemera, mavuto azachuma akhoza kukhalapo. Banja lina ku Japan linagula nyumba pangongole ya loni pamene chuma cha dzikolo chinali pabwino. Pokhala ndi chidaliro chakuti malipiro adzawonjezedwa, iwo anavomereza kumapereka ndalama zambiri zobweza ngongole yaikuluyo. Komabe, pamene chuma cha dzikolo chinatsika, iwo sanathenso kubweza ngongoleyo ndipo pamapeto pake anaumirizika kugulitsa nyumba yawoyo pamtengo wotsika kwambiri poyerekeza ndi zimene anali atalipirako kale. Ngakhale kuti sakukhalanso m’nyumbayo, banjalo likulipirabe ndalama za loni ya nyumbayo. Kuwonjezeranso pavutolo, iwo akulimbana ndi kulipira ngongole zimene ali nazo chifukwa chogwiritsa ntchito mosasamala khadi logulira zinthu pangongole lotchedwa credit card. Bambo wa banjalo amachita njuga ya mpikisano wa mahachi, ndipo ngongole za banjalo zikuchulukachulukabe. Komabe, mabanja ambiri akhala okhoza kusintha ndi kukhala osangalala. Kodi mungafune kudziŵa chimene chawathandiza kusintha?
4. Kodi kukhala ndi anthu anzanu kumakukhudzani motani?
4 Kulikonse kumene mungakhale, kukhala ndi anthu nthaŵi zina kumachititsa vuto lopitirira la kuvutika maganizo, limene limapangitsa moyo kukhala wosakhutiritsa. Kuntchito anthu angamakuchitireni miseche. Mwina inuyo chifukwa chochita bwino m’zinthu zina, ena angakuchitireni nsanje ndi kumakusulizani. Mwinanso munthu amene mumakhala naye tsiku ndi tsiku angamakukhumudwitseni chifukwa cha kudzitukumula kwake. Mwana wanu angamavutitsidwe ndi anzake kusukulu, kumam’nyoza, kapena kumam’nyalanyaza. Ngati ndinu kholo lopanda mwamuna kapena mkazi, mukudziŵa kuti zimenezo n’zosathandiza pamoyo wanu pokhala ndi anthu ena. Mavuto onsewo amawonjezera vuto la kuvutika maganizo pamiyoyo ya amuna ndi akazi ambiri lerolino.
5. Kodi mukuona kuti chimene chimachititsa anthu kukhala ndi vuto la kuvutika maganizo m’dziko lerolino n’chiyani?
5 Zotsatira za kuvutika maganizo zikhoza kuwonjezeka m’kupita kwa nthaŵi mpaka zitafika poipa, popanda kuperekeratu zizindikiro. Ndiye chifukwa chake kuvutika maganizo kwatchedwa matenda akupha mwakachetechete, ndipo kuvutika maganizo kopitirira kwatchedwa, poizoni wakupha pang’onopang’ono. Pulofesa Robert L. Veninga, wa pa Yunivesite ya Minnesota, ananena kuti: “Lerolino, kuvutika maganizo limodzi ndi matenda ake otsatira kumapeza ogwira ntchito pafupifupi kulikonse padziko lapansi.” Akuti matenda oyambitsidwa ndi kuvutika maganizo amawonongera dziko la United States ndalama zokwanira madola akumeneko 200 biliyoni pachaka. Amanenanso kuti kuvutika maganizo ndi katundu amene dziko la America layamba kutumiza kwambiri kunja, ndipo mawu akuti “kuvutika maganizo” tsopano akumveka m’zinenero zazikulu zambiri padziko lapansi. Pamene mwavutika maganizo ndipo mukulephera kuchita zinthu zimene mwakonzekera, mungayambe kudziona kukhala wamlandu. Kufufuza kwaposachedwapa kwasonyeza kuti anthu ambiri amatha maola aŵiri patsiku akuvutika ndi malingaliro podziona kukhala amlandu. Komabe, ena akhala okhoza kuthana ndi vuto la kuvutika maganizo ndipo akhala ochita bwino pamiyoyo yawo.
6. Kodi nzeru ya anthu m’maiona motani pokuthandizani kukhala ndi moyo wokhutiritsa?
6 Kodi mavuto a tsiku ndi tsiku ngati amenewo mungathane nawo bwanji ndi kukhalabe ndi moyo wokhutiritsa? Ena amafufuza chithandizo m’mabuku odziŵerengera pawekha ndi zolemba zina za akatswiri. Kodi mabuku oterowo ndi odalirika? Dr. Benjamin Spock, amene buku lake lonena za kulera ana alimasulira m’zinenero 42 ndipo lagulitsidwa kufika pa chiŵerengero chokwanira pafupifupi 50 miliyoni ananena kuti “kulephera kulanga ana . . . ndilo vuto la makolo ambiri ku America lerolino.” Kenako anapitiriza kunena kuti akatswiri, kuphatikizapo iye mwiniyo, ndiwo oyenera kuimbidwa mlandu. Iye anavomereza kuti: “Tinazindikira mochedwa kwambiri, kuti maganizo athu oonetsa kuti timadziŵa zonse akulepheretsa makolo kukhala odzidalira mwa iwo okha.” Choncho funso ndi lakuti: Kodi ndi uphungu wa ndani umene tingautsatire ndi chidaliro chakuti tikhala ndi moyo wokhutiritsa lero ndi m’tsogolo?